Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ma’idah ayat 116 - المَائدة - Page - Juz 7
﴿وَإِذۡ قَالَ ٱللَّهُ يَٰعِيسَى ٱبۡنَ مَرۡيَمَ ءَأَنتَ قُلۡتَ لِلنَّاسِ ٱتَّخِذُونِي وَأُمِّيَ إِلَٰهَيۡنِ مِن دُونِ ٱللَّهِۖ قَالَ سُبۡحَٰنَكَ مَا يَكُونُ لِيٓ أَنۡ أَقُولَ مَا لَيۡسَ لِي بِحَقٍّۚ إِن كُنتُ قُلۡتُهُۥ فَقَدۡ عَلِمۡتَهُۥۚ تَعۡلَمُ مَا فِي نَفۡسِي وَلَآ أَعۡلَمُ مَا فِي نَفۡسِكَۚ إِنَّكَ أَنتَ عَلَّٰمُ ٱلۡغُيُوبِ ﴾
[المَائدة: 116]
﴿وإذ قال الله ياعيسى ابن مريم أأنت قلت للناس اتخذوني وأمي إلهين﴾ [المَائدة: 116]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo (kumbukirani) pamene Allah adzanena: “Iwe Isa (Yesu) mwana wa Mariya: Kodi iwe udauza anthu kuti: ‘Ndiyeseni ine ndi mayi wanga monga milungu iwiri m’malo mwa Allah?” (Mneneri Isa {Yesu}) adzaati: “Ulemelero ukhale pa Inu. Sikoyenera kwa ine kunena zomwe sizili zoyenera (kwa ine mawu amenewa ngabodza). Ngati ndikadanena, ndiye kuti mukadadziwa. Inu mukudziwa zomwe zili mu mtima mwanga, pomwe ine sindidziwa zomwe zili mwa Inu. Ndithudi, Inu ndinu Wodziwa zamseri.” |