×

Surah Al-Maidah in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Maidah

Translation of the Meanings of Surah Maidah in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Maidah translated into Chichewa, Surah Al-Maidah in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Maidah in Chichewa - نيانجا, Verses 120 - Surah Number 5 - Page 106.

بسم الله الرحمن الرحيم

يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا أَوْفُوا بِالْعُقُودِ ۚ أُحِلَّتْ لَكُم بَهِيمَةُ الْأَنْعَامِ إِلَّا مَا يُتْلَىٰ عَلَيْكُمْ غَيْرَ مُحِلِّي الصَّيْدِ وَأَنتُمْ حُرُمٌ ۗ إِنَّ اللَّهَ يَحْكُمُ مَا يُرِيدُ (1)
oh inu anthu okhulupirira! Kwaniritsani mapangano anu. Ndi zololedwa kwa inu kudya nyama zonse kupatula zimene tsopano zili kuletsedwa kwa inu. Kusaka nyama ndi koletsedwa pamene muli paulendo wa Hajji. Ndithudi Mulungu amalamula zimene Iye afuna
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تُحِلُّوا شَعَائِرَ اللَّهِ وَلَا الشَّهْرَ الْحَرَامَ وَلَا الْهَدْيَ وَلَا الْقَلَائِدَ وَلَا آمِّينَ الْبَيْتَ الْحَرَامَ يَبْتَغُونَ فَضْلًا مِّن رَّبِّهِمْ وَرِضْوَانًا ۚ وَإِذَا حَلَلْتُمْ فَاصْطَادُوا ۚ وَلَا يَجْرِمَنَّكُمْ شَنَآنُ قَوْمٍ أَن صَدُّوكُمْ عَنِ الْمَسْجِدِ الْحَرَامِ أَن تَعْتَدُوا ۘ وَتَعَاوَنُوا عَلَى الْبِرِّ وَالتَّقْوَىٰ ۖ وَلَا تَعَاوَنُوا عَلَى الْإِثْمِ وَالْعُدْوَانِ ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۖ إِنَّ اللَّهَ شَدِيدُ الْعِقَابِ (2)
oh inu anthu okhulupirira! Musaphwanye kupatulika kwa zizindikiro za Mulungukapenaza MweziWoyera kapenazanyamazimene zimabweretsedwa kukhala nsembe kapena zizindikiro zimene zimaikidwa pa izo kapena za anthu amene amadza ku Nyumba Yoyera kudzafuna chisomo ndi chisangalalo cha Ambuye wawo. Koma mukatsiriza miyambo ya Hajji, mukhoza kusaka ndipo musalole chidani cha anthu ena amene anakuletsani kulowa mu Mzikiti Woyera kuti chikuchimwitseni. Thandizanani wina ndi mnzake pa ntchito zabwino koma musathandizane mu ntchito ya uchimo ndi yoswa malamulo. Muopeni Mulungu. Ndithudi Mulungu amalanga kwambiri
حُرِّمَتْ عَلَيْكُمُ الْمَيْتَةُ وَالدَّمُ وَلَحْمُ الْخِنزِيرِ وَمَا أُهِلَّ لِغَيْرِ اللَّهِ بِهِ وَالْمُنْخَنِقَةُ وَالْمَوْقُوذَةُ وَالْمُتَرَدِّيَةُ وَالنَّطِيحَةُ وَمَا أَكَلَ السَّبُعُ إِلَّا مَا ذَكَّيْتُمْ وَمَا ذُبِحَ عَلَى النُّصُبِ وَأَن تَسْتَقْسِمُوا بِالْأَزْلَامِ ۚ ذَٰلِكُمْ فِسْقٌ ۗ الْيَوْمَ يَئِسَ الَّذِينَ كَفَرُوا مِن دِينِكُمْ فَلَا تَخْشَوْهُمْ وَاخْشَوْنِ ۚ الْيَوْمَ أَكْمَلْتُ لَكُمْ دِينَكُمْ وَأَتْمَمْتُ عَلَيْكُمْ نِعْمَتِي وَرَضِيتُ لَكُمُ الْإِسْلَامَ دِينًا ۚ فَمَنِ اضْطُرَّ فِي مَخْمَصَةٍ غَيْرَ مُتَجَانِفٍ لِّإِثْمٍ ۙ فَإِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (3)
Zoletsedwa kwa inu kudya ndi nyama yofa yokha, liwende, nyama ya nkhumba ndi nyama iliyonse imene yaphedwa m’dzina la mulungu wina osati Mulungu weniweni. Inu muli kuletsedwa kudya nyama zophedwa pomangirira chingwe pakhosi ndi kukoka ndiponso izo zimene zamenyedwa mpaka kufa, nyama zimene zaphedwa chifukwa chakugwa kapena yaphedwa ndi nyama inzake ndiponso imene yadyedwa ndi chilombo cha m’thengo, kupatula ngati inu mwaimaliza kupha ndiponso nyama zimene zaphedwa pamwala ndi kuperekedwa ku milungu ya mafano. Inu mwaletsedwa kufuna kudziwa chinsinsi pochita mayere a maula. Amenewa ndi machitidwe oipa . Lero anthu osakhulupirira achita mantha ndi chipembedzo chanu. Motero musawaope iwo koma opani Ine. Lero ndakonza chipembedzo chanu ndipo ndamaliza ubwino wanga pa inu ndipo Ine ndakusankhirani Chisilamu kuti chikhale chipembedzo chanu. Koma iye amene wakakamizidwa ndi njala osati ndi cholinga chochimwa, ndithudi, Mulungu ali wokhululukira ndi wachisoni
يَسْأَلُونَكَ مَاذَا أُحِلَّ لَهُمْ ۖ قُلْ أُحِلَّ لَكُمُ الطَّيِّبَاتُ ۙ وَمَا عَلَّمْتُم مِّنَ الْجَوَارِحِ مُكَلِّبِينَ تُعَلِّمُونَهُنَّ مِمَّا عَلَّمَكُمُ اللَّهُ ۖ فَكُلُوا مِمَّا أَمْسَكْنَ عَلَيْكُمْ وَاذْكُرُوا اسْمَ اللَّهِ عَلَيْهِ ۖ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۚ إِنَّ اللَّهَ سَرِيعُ الْحِسَابِ (4)
Iwo amakufunsa iwe za zinthu zimene zili zololedwa kwa iwo. Nena: “Zinthu zonse zimene ndi zabwino ndi zololedwa kwa inu ndiponso zinthu zimene mwaphunzitsa, mbalame ndi nyama zosaka kuti zizigwira, kuziphunzitsa monga momwe Mulungu adakuphunzitsirani. Motero idyani zimene izo zakugwirirani koma tchulani dzina la Mulungu pa izo ndipo opani Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi wachangu powerengera.”
الْيَوْمَ أُحِلَّ لَكُمُ الطَّيِّبَاتُ ۖ وَطَعَامُ الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ حِلٌّ لَّكُمْ وَطَعَامُكُمْ حِلٌّ لَّهُمْ ۖ وَالْمُحْصَنَاتُ مِنَ الْمُؤْمِنَاتِ وَالْمُحْصَنَاتُ مِنَ الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ مِن قَبْلِكُمْ إِذَا آتَيْتُمُوهُنَّ أُجُورَهُنَّ مُحْصِنِينَ غَيْرَ مُسَافِحِينَ وَلَا مُتَّخِذِي أَخْدَانٍ ۗ وَمَن يَكْفُرْ بِالْإِيمَانِ فَقَدْ حَبِطَ عَمَلُهُ وَهُوَ فِي الْآخِرَةِ مِنَ الْخَاسِرِينَ (5)
Zinthu zonse zabwino, tsiku lalero, zaloledwa kuti mukhoza kuzigwiritsa ntchito. Chakudya cha anthu m’Buku ndi chololedwa kwa inu ndiponso chakudya chanu ndi chololedwa kwa iwo. Muloledwa kukwatira akazi okhulupirira ndi akazi angwiro kuchokera ku gulu la anthu a m’Buku pamene muwapatsa mphatso yawo ya ukwati ndi kukhala molemekezeka ndi iwo osachita chiwerewere kapena kuwasandutsa iwo ngati zibwenzi zanu. Ndipo aliyense amene sakhulupirira mwa Mulungu mmodzi, ntchito zake zidzakhala zopanda pake ndipo m’dziko limene lili nkudza, iye adzakhala olephera kwambiri
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِذَا قُمْتُمْ إِلَى الصَّلَاةِ فَاغْسِلُوا وُجُوهَكُمْ وَأَيْدِيَكُمْ إِلَى الْمَرَافِقِ وَامْسَحُوا بِرُءُوسِكُمْ وَأَرْجُلَكُمْ إِلَى الْكَعْبَيْنِ ۚ وَإِن كُنتُمْ جُنُبًا فَاطَّهَّرُوا ۚ وَإِن كُنتُم مَّرْضَىٰ أَوْ عَلَىٰ سَفَرٍ أَوْ جَاءَ أَحَدٌ مِّنكُم مِّنَ الْغَائِطِ أَوْ لَامَسْتُمُ النِّسَاءَ فَلَمْ تَجِدُوا مَاءً فَتَيَمَّمُوا صَعِيدًا طَيِّبًا فَامْسَحُوا بِوُجُوهِكُمْ وَأَيْدِيكُم مِّنْهُ ۚ مَا يُرِيدُ اللَّهُ لِيَجْعَلَ عَلَيْكُم مِّنْ حَرَجٍ وَلَٰكِن يُرِيدُ لِيُطَهِّرَكُمْ وَلِيُتِمَّ نِعْمَتَهُ عَلَيْكُمْ لَعَلَّكُمْ تَشْكُرُونَ (6)
Oh inu anthu okhulupirira! Pamene mukonzeka kuti mupemphere, sambitsani nkhope zanu ndiponso manja anu mpaka pa kasukusuku ndipo pakani ku mutu kwanu ndipo sambitsani mapazi anu mpaka molekezera phazi lanu. Ngati mwadetsedwa, dziyeretseni. Koma ngati muli kudwala kapena muli paulendo, kapena wina wa inu abwera kuchokera ku chimbudzi kapena munagona ndi akazi anu ndipo mwasowa madzi, tengani mchenga woyera ndi kupukuta m’manja mwanu ndi ku nkhope kwanu. Mulungu safuna kukukundikirani mtolo wolemera koma Iye afuna kukuyeretsani ndi kukwaniritsa zokoma zake kwa inu kuti inu mukhale oyamika
وَاذْكُرُوا نِعْمَةَ اللَّهِ عَلَيْكُمْ وَمِيثَاقَهُ الَّذِي وَاثَقَكُم بِهِ إِذْ قُلْتُمْ سَمِعْنَا وَأَطَعْنَا ۖ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (7)
Ndipo kumbukirani zabwino zimene Mulungu wakupatsani inu ndi lonjezo limene adakumangani nalo pamene inu mudanena kuti: “Tamva ndipo tidzatsatira.” Ndipo muopeni Mulungu. Ndithudi Iye amadziwa maganizo amene ali mu mtima mwanu
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا كُونُوا قَوَّامِينَ لِلَّهِ شُهَدَاءَ بِالْقِسْطِ ۖ وَلَا يَجْرِمَنَّكُمْ شَنَآنُ قَوْمٍ عَلَىٰ أَلَّا تَعْدِلُوا ۚ اعْدِلُوا هُوَ أَقْرَبُ لِلتَّقْوَىٰ ۖ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۚ إِنَّ اللَّهَ خَبِيرٌ بِمَا تَعْمَلُونَ (8)
oh inu anthu okhulupirira! Limbikirani chifukwa cha Mulungu ndipo perekani umboni woona wokhawokha ndipo musalole chidani chimene chilipo ndi anthu ena kuti chikusokonezeni kuchita chilungamo. Chitani chilungamo chifukwa chilungamo chili kufupi ndi kuyera mtima ndipo opani Mulungu. Ndithudi Mulungu amadziwa ntchito zonsezimenemumachita
وَعَدَ اللَّهُ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ ۙ لَهُم مَّغْفِرَةٌ وَأَجْرٌ عَظِيمٌ (9)
Mulunguwalonjezaonseamene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, kuti kwa iwo kuli chikhululukiro ndiponso mphotho yaikulu
وَالَّذِينَ كَفَرُوا وَكَذَّبُوا بِآيَاتِنَا أُولَٰئِكَ أَصْحَابُ الْجَحِيمِ (10)
Iwo amene sakhulupirira ndipo amakana chivumbulutso chathu, amenewa adzakhala eni ake a Gahena
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا اذْكُرُوا نِعْمَتَ اللَّهِ عَلَيْكُمْ إِذْ هَمَّ قَوْمٌ أَن يَبْسُطُوا إِلَيْكُمْ أَيْدِيَهُمْ فَكَفَّ أَيْدِيَهُمْ عَنكُمْ ۖ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۚ وَعَلَى اللَّهِ فَلْيَتَوَكَّلِ الْمُؤْمِنُونَ (11)
oh inu anthu okhulupirira! Kumbukirani ubwino wa Mulungu pa inu pamene anthu ena adafuna kukutambasulirani manja awo koma Mulungu adatchinjiriza manja awo kufika kwa inu. Motero opani Mulungu. Ndipo mwa Mulungu, alekeni anthu okhulupilira kuti aike chikhulupiriro chawo
۞ وَلَقَدْ أَخَذَ اللَّهُ مِيثَاقَ بَنِي إِسْرَائِيلَ وَبَعَثْنَا مِنْهُمُ اثْنَيْ عَشَرَ نَقِيبًا ۖ وَقَالَ اللَّهُ إِنِّي مَعَكُمْ ۖ لَئِنْ أَقَمْتُمُ الصَّلَاةَ وَآتَيْتُمُ الزَّكَاةَ وَآمَنتُم بِرُسُلِي وَعَزَّرْتُمُوهُمْ وَأَقْرَضْتُمُ اللَّهَ قَرْضًا حَسَنًا لَّأُكَفِّرَنَّ عَنكُمْ سَيِّئَاتِكُمْ وَلَأُدْخِلَنَّكُمْ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ ۚ فَمَن كَفَرَ بَعْدَ ذَٰلِكَ مِنكُمْ فَقَدْ ضَلَّ سَوَاءَ السَّبِيلِ (12)
Ndithudi Mulungu adalandira lonjezo la ana a Israyeli ndipo Ife tidadzutsa pakati pawo atsogoleri khumi ndi awiri. Ndipo Mulungu adati: “Ine, ndithudi, ndili pamodzi ndi inu ngati inu mupemphera moyenera, mupereka chopereka chothandiza anthu osauka ndipo mukhulupirira mwa Atumwi anga ndipo muwathandiza ndiponso mukongoza Mulungu ngongole yabwino. Ndithudi Ine ndidzakukhululukirani machimo anu ndi kukulowetsani ku minda yothiriridwa ndi madzi ya m’mitsinje. Koma ngati wina wa inu, pambuyo pake sakhulupilira, Iye wasochera ku njira yoyenera.”
فَبِمَا نَقْضِهِم مِّيثَاقَهُمْ لَعَنَّاهُمْ وَجَعَلْنَا قُلُوبَهُمْ قَاسِيَةً ۖ يُحَرِّفُونَ الْكَلِمَ عَن مَّوَاضِعِهِ ۙ وَنَسُوا حَظًّا مِّمَّا ذُكِّرُوا بِهِ ۚ وَلَا تَزَالُ تَطَّلِعُ عَلَىٰ خَائِنَةٍ مِّنْهُمْ إِلَّا قَلِيلًا مِّنْهُمْ ۖ فَاعْفُ عَنْهُمْ وَاصْفَحْ ۚ إِنَّ اللَّهَ يُحِبُّ الْمُحْسِنِينَ (13)
Koma chifukwa chakuti iwo adaphwanya lonjezo lawo, Ife tidawatemberera ndi kuumitsa mitima yawo. Iwo adasintha mawu ndi kuwachotsa m’malo mwake ndi kusiya zambiri zimene zidatumizidwa kwa iwo. Siudzasiya kuona ntchito za chinyengo mwa iwo kupatula owerengeka okha. Koma akhululukire ndipo uwalekerere. Ndithudi Mulungu amakonda anthu ochita zabwino
وَمِنَ الَّذِينَ قَالُوا إِنَّا نَصَارَىٰ أَخَذْنَا مِيثَاقَهُمْ فَنَسُوا حَظًّا مِّمَّا ذُكِّرُوا بِهِ فَأَغْرَيْنَا بَيْنَهُمُ الْعَدَاوَةَ وَالْبَغْضَاءَ إِلَىٰ يَوْمِ الْقِيَامَةِ ۚ وَسَوْفَ يُنَبِّئُهُمُ اللَّهُ بِمَا كَانُوا يَصْنَعُونَ (14)
Ndipo kuchokera kwa iwo amene amadzitcha kuti ndi Akhirisitu. Ife tidachita nawo lonjezo koma iwo adasiya zambiri zimene zidatumizidwa kwa iwo. Kotero tidadzutsa pakati pawo udani ndi chizondi chimene chidzakhala mpaka patsiku louka kwa akufa ndipo Mulungu adzawauza iwo zonse zimene amachita
يَا أَهْلَ الْكِتَابِ قَدْ جَاءَكُمْ رَسُولُنَا يُبَيِّنُ لَكُمْ كَثِيرًا مِّمَّا كُنتُمْ تُخْفُونَ مِنَ الْكِتَابِ وَيَعْفُو عَن كَثِيرٍ ۚ قَدْ جَاءَكُم مِّنَ اللَّهِ نُورٌ وَكِتَابٌ مُّبِينٌ (15)
oh inu anthu a m’Buku! Ndithudi Mtumwi wathu wadza kudzakuuzani inu zambiri zimene mwakhala mukuzibisa za m’Buku la Mulungu ndi kuzisiya osafotokoza bwino. Ndithudi kwadza kuwala kwa inu kuchokera kwa Mulungu ndi Buku la choonadi
يَهْدِي بِهِ اللَّهُ مَنِ اتَّبَعَ رِضْوَانَهُ سُبُلَ السَّلَامِ وَيُخْرِجُهُم مِّنَ الظُّلُمَاتِ إِلَى النُّورِ بِإِذْنِهِ وَيَهْدِيهِمْ إِلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (16)
Limene Mulungu amatsogolera, kunjira ya mtendere, onse amene amafuna chikondwerero cha Iye. Mulungu amawatulutsa, mwachifuniro chake, kuchoka ku mdima ndi kunka kowala, ndipo amawatsogolera kunjira yoyenera
لَّقَدْ كَفَرَ الَّذِينَ قَالُوا إِنَّ اللَّهَ هُوَ الْمَسِيحُ ابْنُ مَرْيَمَ ۚ قُلْ فَمَن يَمْلِكُ مِنَ اللَّهِ شَيْئًا إِنْ أَرَادَ أَن يُهْلِكَ الْمَسِيحَ ابْنَ مَرْيَمَ وَأُمَّهُ وَمَن فِي الْأَرْضِ جَمِيعًا ۗ وَلِلَّهِ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَمَا بَيْنَهُمَا ۚ يَخْلُقُ مَا يَشَاءُ ۚ وَاللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (17)
Ndithudi ndi chifukwa chopanda chikhulupiliro chimene iwo amati: “Mulungu ndi Messiya, mwana wa Maria.” Nena: “Kodi ndani amene angamuletse Mulungu ngati Iye atafuna kuononga Messiya mwana wa Maria, Mai wake ndi zonse zimene zili m’dziko lapansi?” Mwini ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo ndi Mulungu. Iye amalenga chimene afuna. Ndipo Iye ali ndi mphamvu pa chinthu chilichonse
وَقَالَتِ الْيَهُودُ وَالنَّصَارَىٰ نَحْنُ أَبْنَاءُ اللَّهِ وَأَحِبَّاؤُهُ ۚ قُلْ فَلِمَ يُعَذِّبُكُم بِذُنُوبِكُم ۖ بَلْ أَنتُم بَشَرٌ مِّمَّنْ خَلَقَ ۚ يَغْفِرُ لِمَن يَشَاءُ وَيُعَذِّبُ مَن يَشَاءُ ۚ وَلِلَّهِ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَمَا بَيْنَهُمَا ۖ وَإِلَيْهِ الْمَصِيرُ (18)
Ndipo Ayuda ndi Akhirisitu amati: “Ife ndife ana a Mulungu ndiponso wokondedwa ake.” Nena: “Nanga bwanji amakulangani chifukwa cha zolakwa zanu?” Iyayi, inu ndinu anthu amene mudalengedwa ndi Iye. Mulungu amakhululukira aliyense amene Iye wamufuna ndipo amalanga aliyense amene Iye wamufuna. Mwini ufumu wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zili m’menemo ndi Mulungu. Ndipo kwa Iye ndiko kobwerera
يَا أَهْلَ الْكِتَابِ قَدْ جَاءَكُمْ رَسُولُنَا يُبَيِّنُ لَكُمْ عَلَىٰ فَتْرَةٍ مِّنَ الرُّسُلِ أَن تَقُولُوا مَا جَاءَنَا مِن بَشِيرٍ وَلَا نَذِيرٍ ۖ فَقَدْ جَاءَكُم بَشِيرٌ وَنَذِيرٌ ۗ وَاللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (19)
oh inu anthu otsatira Buku! Tsopano mtumwi wathu wadza kwa inu kudzaulula poyera chifuniro chathu patapita nthawi yaitali imene kudalibe Atumwi, kuti mwina mungadzanene kuti: “Sikudabwere kwa ife wodzatiuza nkhani zabwino kapena kudzatichenjeza.” Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse
وَإِذْ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوْمِهِ يَا قَوْمِ اذْكُرُوا نِعْمَةَ اللَّهِ عَلَيْكُمْ إِذْ جَعَلَ فِيكُمْ أَنبِيَاءَ وَجَعَلَكُم مُّلُوكًا وَآتَاكُم مَّا لَمْ يُؤْتِ أَحَدًا مِّنَ الْعَالَمِينَ (20)
Ndi pamene Mose adawauza anthu ake: “Oh Anthu anga! Kumbukirani zokoma zimene Mulungu wakuchitirani inu pamene adaika Atumwi pakati panu, adakupangani inu kukhala mafumu ndipo adakupatsani zimene sadampatsepo wina aliyense mu zolengedwa zonse.”
يَا قَوْمِ ادْخُلُوا الْأَرْضَ الْمُقَدَّسَةَ الَّتِي كَتَبَ اللَّهُ لَكُمْ وَلَا تَرْتَدُّوا عَلَىٰ أَدْبَارِكُمْ فَتَنقَلِبُوا خَاسِرِينَ (21)
Oh anthu anga! Lowani m’dziko loyera limene Mulungu wakupatsani ndipo musabwerere m’mbuyo chifukwa mudzabwezedwa ngati olephera pa zochita
قَالُوا يَا مُوسَىٰ إِنَّ فِيهَا قَوْمًا جَبَّارِينَ وَإِنَّا لَن نَّدْخُلَهَا حَتَّىٰ يَخْرُجُوا مِنْهَا فَإِن يَخْرُجُوا مِنْهَا فَإِنَّا دَاخِلُونَ (22)
Iwo adati: “Iwe Mose! Kumeneko kuli anthu amphamvu ndipo ife sitidzalowa m’dziko limeneli pokhapokha iwo atachoka ndipo ngati iwo atatuluka, ife tidzalowamo.”
قَالَ رَجُلَانِ مِنَ الَّذِينَ يَخَافُونَ أَنْعَمَ اللَّهُ عَلَيْهِمَا ادْخُلُوا عَلَيْهِمُ الْبَابَ فَإِذَا دَخَلْتُمُوهُ فَإِنَّكُمْ غَالِبُونَ ۚ وَعَلَى اللَّهِ فَتَوَكَّلُوا إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ (23)
Anthu awiri amene amaopa ndiponso amene Mulungu adaonetsa chisomo chake adati: “Amenyeni kudzera pa chipata, chifukwa ngati inu mulowa, mudzapambana ndipo ikani chikhulupiliro chanu mwa Mulungu ngati inu ndinu wokhulupilira.”
قَالُوا يَا مُوسَىٰ إِنَّا لَن نَّدْخُلَهَا أَبَدًا مَّا دَامُوا فِيهَا ۖ فَاذْهَبْ أَنتَ وَرَبُّكَ فَقَاتِلَا إِنَّا هَاهُنَا قَاعِدُونَ (24)
Iwo adati: “Iwe Mose! Ife sitidzalowa m’menemo ngati iwo akhalabe ali momwemo. Motero pita iwe pamodzi ndi Ambuye wako, kukamenyana nawo. Ife tikhala pompano.”
قَالَ رَبِّ إِنِّي لَا أَمْلِكُ إِلَّا نَفْسِي وَأَخِي ۖ فَافْرُقْ بَيْنَنَا وَبَيْنَ الْقَوْمِ الْفَاسِقِينَ (25)
Iye adati: “Ambuye wanga! Ine ndili ndi mphamvu pa ine mwini ndi pa mbale wanga, motero tipatuleni kugulu la anthu oswa malamulo.”
قَالَ فَإِنَّهَا مُحَرَّمَةٌ عَلَيْهِمْ ۛ أَرْبَعِينَ سَنَةً ۛ يَتِيهُونَ فِي الْأَرْضِ ۚ فَلَا تَأْسَ عَلَى الْقَوْمِ الْفَاسِقِينَ (26)
Mulungu adati: “Motero iwo sadzalowa m’dziko ili mpaka patatha zaka makumi anayi ndipo adzakhala akuyendayenda wopanda malo enieni padziko lapansi. Motero usawadandaulire anthu oswa malamulo.”
۞ وَاتْلُ عَلَيْهِمْ نَبَأَ ابْنَيْ آدَمَ بِالْحَقِّ إِذْ قَرَّبَا قُرْبَانًا فَتُقُبِّلَ مِنْ أَحَدِهِمَا وَلَمْ يُتَقَبَّلْ مِنَ الْآخَرِ قَالَ لَأَقْتُلَنَّكَ ۖ قَالَ إِنَّمَا يَتَقَبَّلُ اللَّهُ مِنَ الْمُتَّقِينَ (27)
Ndipo auze iwo, mwachoonadi, nkhani za ana awiri a Adamu mmene aliyense adaperekera nsembe yake ndi kulandiridwa kwa nsembe ya mmodzi wa iwo pamene ya wina siidalandiridwe. Iye adati: “Ndithudi ine ndikupha.” Ndipo m’bale wake adati: “Mulungu amalandira nsembe ya anthu olungama.”
لَئِن بَسَطتَ إِلَيَّ يَدَكَ لِتَقْتُلَنِي مَا أَنَا بِبَاسِطٍ يَدِيَ إِلَيْكَ لِأَقْتُلَكَ ۖ إِنِّي أَخَافُ اللَّهَ رَبَّ الْعَالَمِينَ (28)
“Ngati iwe utambasula dzanja lako kuti undiphe, ine sindidzatambasula dzanja langa kuti ndikuphe chifukwa ine ndimaopa Mulungu, Ambuye wazolengedwa zonse.”
إِنِّي أُرِيدُ أَن تَبُوءَ بِإِثْمِي وَإِثْمِكَ فَتَكُونَ مِنْ أَصْحَابِ النَّارِ ۚ وَذَٰلِكَ جَزَاءُ الظَّالِمِينَ (29)
“Ndithudi ine ndikufuna kuti usenze machimo anga ndi ako ndipo udzakhala m’gulu la anthu a ku Moto ndipo imeneyi ndi mphotho ya anthu ochita zoipa.”
فَطَوَّعَتْ لَهُ نَفْسُهُ قَتْلَ أَخِيهِ فَقَتَلَهُ فَأَصْبَحَ مِنَ الْخَاسِرِينَ (30)
Motero mtima wake udamuumiriza kupha m’bale wake! Iye adamupha ndipo adakhala mmodzi wa anthu olephera
فَبَعَثَ اللَّهُ غُرَابًا يَبْحَثُ فِي الْأَرْضِ لِيُرِيَهُ كَيْفَ يُوَارِي سَوْءَةَ أَخِيهِ ۚ قَالَ يَا وَيْلَتَا أَعَجَزْتُ أَنْ أَكُونَ مِثْلَ هَٰذَا الْغُرَابِ فَأُوَارِيَ سَوْءَةَ أَخِي ۖ فَأَصْبَحَ مِنَ النَّادِمِينَ (31)
Ndipo atatero Mulungu adatumiza khwangwala amene adakumba pansi ndi kumulangiza mmene iye angakwiririre mtembo wa m’bale wake. Iye adati: “Kalanga ine! Ndalephera kukhala ngati khwangwala uyu ndi kukwirira mtembo wa m’bale wanga?” Ndipo iye adali mmodzi wa anthu onong’oneza bombono
مِنْ أَجْلِ ذَٰلِكَ كَتَبْنَا عَلَىٰ بَنِي إِسْرَائِيلَ أَنَّهُ مَن قَتَلَ نَفْسًا بِغَيْرِ نَفْسٍ أَوْ فَسَادٍ فِي الْأَرْضِ فَكَأَنَّمَا قَتَلَ النَّاسَ جَمِيعًا وَمَنْ أَحْيَاهَا فَكَأَنَّمَا أَحْيَا النَّاسَ جَمِيعًا ۚ وَلَقَدْ جَاءَتْهُمْ رُسُلُنَا بِالْبَيِّنَاتِ ثُمَّ إِنَّ كَثِيرًا مِّنْهُم بَعْدَ ذَٰلِكَ فِي الْأَرْضِ لَمُسْرِفُونَ (32)
Chifukwa cha chimenechi Ife tidakhazikitsa lamulo kwa ana a Israyeli kuti ngati wina apha munthu mnzake osati chobwezera imfa ya wina kapena kuyambitsa chisokonezo pa dziko adzakhala ngati wapha anthu onse, ndipo kuti ngati wina adzapulumutsa moyo wa munthu, adzakhala ngati kuti adapulumutsa anthu onse. Ndithudi adabwera kwa iwo Atumwi athu ndi zizindikiro zooneka komabe sipanapite nthawi mmene ena a iwo adachimwa machimo akuluakulu m’dziko
إِنَّمَا جَزَاءُ الَّذِينَ يُحَارِبُونَ اللَّهَ وَرَسُولَهُ وَيَسْعَوْنَ فِي الْأَرْضِ فَسَادًا أَن يُقَتَّلُوا أَوْ يُصَلَّبُوا أَوْ تُقَطَّعَ أَيْدِيهِمْ وَأَرْجُلُهُم مِّنْ خِلَافٍ أَوْ يُنفَوْا مِنَ الْأَرْضِ ۚ ذَٰلِكَ لَهُمْ خِزْيٌ فِي الدُّنْيَا ۖ وَلَهُمْ فِي الْآخِرَةِ عَذَابٌ عَظِيمٌ (33)
Mphotho ya iwo amene amamenya nkhondo yolimbana ndi Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo amafalitsa chisokonezo m’dziko ndi kuphedwa kapena kupachikidwa pa mtanda kapena kudulidwa manja ndi mapazi awo mosiyanitsa mbali kapena kuthamangitsidwa m’dziko. Zimenezo, kwa iwo, ndi zowachititsa manyazi m’dziko lino ndipo adzalangidwa kwambiri m’dziko limene lili kudza
إِلَّا الَّذِينَ تَابُوا مِن قَبْلِ أَن تَقْدِرُوا عَلَيْهِمْ ۖ فَاعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (34)
Kupatula okhawo amene alapa iwe usadawagonjetse. Motero dziwani kuti Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا اتَّقُوا اللَّهَ وَابْتَغُوا إِلَيْهِ الْوَسِيلَةَ وَجَاهِدُوا فِي سَبِيلِهِ لَعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ (35)
oh inu anthu okhulupirira! opani Mulungu ndipo funani njira yoyenera yopita kwa Iye ndipo limbikirani kwambiri m’njira ya Mulungu kuti mukhale opambana
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا لَوْ أَنَّ لَهُم مَّا فِي الْأَرْضِ جَمِيعًا وَمِثْلَهُ مَعَهُ لِيَفْتَدُوا بِهِ مِنْ عَذَابِ يَوْمِ الْقِيَامَةِ مَا تُقُبِّلَ مِنْهُمْ ۖ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (36)
Ndithudi anthu osakhulupirira, akadakhala nazo zonse zimene zili padziko ndi zina zoonjezera apa kuti adzipulumutsire nazo ku chilango cha patsiku louka kwa akufa, sizidzalandiridwa kuchokera kwa iwo ndipo chawo chidzakhala chilango chowawa
يُرِيدُونَ أَن يَخْرُجُوا مِنَ النَّارِ وَمَا هُم بِخَارِجِينَ مِنْهَا ۖ وَلَهُمْ عَذَابٌ مُّقِيمٌ (37)
Iwo adzayesetsa kuti achoke kumoto koma sadzatha kuchoka ayi ndipo chawo chidzakhala chilango chosatha
وَالسَّارِقُ وَالسَّارِقَةُ فَاقْطَعُوا أَيْدِيَهُمَا جَزَاءً بِمَا كَسَبَا نَكَالًا مِّنَ اللَّهِ ۗ وَاللَّهُ عَزِيزٌ حَكِيمٌ (38)
Kwa munthu wakuba, mwamuna kapena mkazi, m’duleni dzanja lake ngati malipiro a zimene wachita ndi chilango ngati chitsanzo chochokera kwa Mulungu. Ndipo Mulungu ndi mphamvu ndi waluntha
فَمَن تَابَ مِن بَعْدِ ظُلْمِهِ وَأَصْلَحَ فَإِنَّ اللَّهَ يَتُوبُ عَلَيْهِ ۗ إِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (39)
Koma aliyense amene alapa pambuyo pochimwa, ndipo achita ntchito zabwino, ndithu Mulungu adzalandira kulapa kwake. Ndithudi Mulungu ndi okhululukira ndi wachisoni chosatha
أَلَمْ تَعْلَمْ أَنَّ اللَّهَ لَهُ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ يُعَذِّبُ مَن يَشَاءُ وَيَغْفِرُ لِمَن يَشَاءُ ۗ وَاللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (40)
Kodi iwe siudziwa kuti Mulungu ndiye Mwini ufumu wa kumwamba ndipo dziko lapansi? Iye amalanga amene wamufuna ndipo amakhululukira aliyense amene wamufuna. Ndipo Mulungu ndi wamphamvu pa chinthu china chilichonse
۞ يَا أَيُّهَا الرَّسُولُ لَا يَحْزُنكَ الَّذِينَ يُسَارِعُونَ فِي الْكُفْرِ مِنَ الَّذِينَ قَالُوا آمَنَّا بِأَفْوَاهِهِمْ وَلَمْ تُؤْمِن قُلُوبُهُمْ ۛ وَمِنَ الَّذِينَ هَادُوا ۛ سَمَّاعُونَ لِلْكَذِبِ سَمَّاعُونَ لِقَوْمٍ آخَرِينَ لَمْ يَأْتُوكَ ۖ يُحَرِّفُونَ الْكَلِمَ مِن بَعْدِ مَوَاضِعِهِ ۖ يَقُولُونَ إِنْ أُوتِيتُمْ هَٰذَا فَخُذُوهُ وَإِن لَّمْ تُؤْتَوْهُ فَاحْذَرُوا ۚ وَمَن يُرِدِ اللَّهُ فِتْنَتَهُ فَلَن تَمْلِكَ لَهُ مِنَ اللَّهِ شَيْئًا ۚ أُولَٰئِكَ الَّذِينَ لَمْ يُرِدِ اللَّهُ أَن يُطَهِّرَ قُلُوبَهُمْ ۚ لَهُمْ فِي الدُّنْيَا خِزْيٌ ۖ وَلَهُمْ فِي الْآخِرَةِ عَذَابٌ عَظِيمٌ (41)
oh iwe Mtumwi! Asakudandaulitse anthu amene amafulumira kusakhulupirira ndipo amati: “Tikhulupirira” ndi milomo yawo pamene mitima yawo ilibe chikhulupiriro. Ndipo pakati pa Ayuda pali anthu amene amamvetsera mabodza ndi zimene anthu ena amene sadadze kwa iwe amakamba. Iwo amasintha mawu monga momwe adalili ndipo amati: “Ngati mwapatsidwa izi landirani ndipo ngati simudapatsidwe chenjerani.” Ndipo amene Mulungu afuna kumusocheretsa,iwe ulibe mphamvu ina iliyonse pa iye yopikisana ndi Mulungu. Awo ndi amene mitima yawo Mulungu safuna kuiyeretsa ndipo kwa awa kuli zinthu zochititsa manyazi m’dziko lino ndi chilango chachikulu m’dziko limene lili nkudza
سَمَّاعُونَ لِلْكَذِبِ أَكَّالُونَ لِلسُّحْتِ ۚ فَإِن جَاءُوكَ فَاحْكُم بَيْنَهُمْ أَوْ أَعْرِضْ عَنْهُمْ ۖ وَإِن تُعْرِضْ عَنْهُمْ فَلَن يَضُرُّوكَ شَيْئًا ۖ وَإِنْ حَكَمْتَ فَاحْكُم بَيْنَهُم بِالْقِسْطِ ۚ إِنَّ اللَّهَ يُحِبُّ الْمُقْسِطِينَ (42)
Iwo amakonda kumvera nkhani zabodza ndi kumadya zinthu zoletsedwa. Ndipo ngati iwo adza kwa iwe, uweruze pakati pawo kapena ungowasiya. Ngati iwe uwasiya, iwo sangathe kukupweteka ayi, koma ngati uwaweruza, weruza mwachilungamo pakati pawo. Ndithudi Mulungu amakonda iwo amene amachita chilungamo
وَكَيْفَ يُحَكِّمُونَكَ وَعِندَهُمُ التَّوْرَاةُ فِيهَا حُكْمُ اللَّهِ ثُمَّ يَتَوَلَّوْنَ مِن بَعْدِ ذَٰلِكَ ۚ وَمَا أُولَٰئِكَ بِالْمُؤْمِنِينَ (43)
Kodi iwo abwera bwanji kwa iwe kudzaweruzidwa pamene iwo ali ndi Buku la chipangano chakale limene muli chiweruzo cha Mulungu? Ndipo ngakhale zili tero iwo amatembenuka. Iwo si okhulupirira enieni
إِنَّا أَنزَلْنَا التَّوْرَاةَ فِيهَا هُدًى وَنُورٌ ۚ يَحْكُمُ بِهَا النَّبِيُّونَ الَّذِينَ أَسْلَمُوا لِلَّذِينَ هَادُوا وَالرَّبَّانِيُّونَ وَالْأَحْبَارُ بِمَا اسْتُحْفِظُوا مِن كِتَابِ اللَّهِ وَكَانُوا عَلَيْهِ شُهَدَاءَ ۚ فَلَا تَخْشَوُا النَّاسَ وَاخْشَوْنِ وَلَا تَشْتَرُوا بِآيَاتِي ثَمَنًا قَلِيلًا ۚ وَمَن لَّمْ يَحْكُم بِمَا أَنزَلَ اللَّهُ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْكَافِرُونَ (44)
Ndithudi Ife tidavumbulutsa chipangano chakale mmene muli chilangizo ndiponso kuwala, ndipo kudzera mu ilo, Atumwi amene anadzipereka kwa Mulungu, adaweruza Ayuda. Ndipo Ansembe ndi anthu oyera mtima chifukwa iwo adapatsidwa udindo osamala Buku la Mulungu, ndipo iwo adali mboni. Motero usamaope anthu koma opani Ine ndipo musasinthitse chivumbulutso changa ndi zinthu zopanda pake. Ndipo yense amene salamulira ndi zomwe adatumiza Mulungu, iwo ndi anthu osakhulupirira
وَكَتَبْنَا عَلَيْهِمْ فِيهَا أَنَّ النَّفْسَ بِالنَّفْسِ وَالْعَيْنَ بِالْعَيْنِ وَالْأَنفَ بِالْأَنفِ وَالْأُذُنَ بِالْأُذُنِ وَالسِّنَّ بِالسِّنِّ وَالْجُرُوحَ قِصَاصٌ ۚ فَمَن تَصَدَّقَ بِهِ فَهُوَ كَفَّارَةٌ لَّهُ ۚ وَمَن لَّمْ يَحْكُم بِمَا أَنزَلَ اللَّهُ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الظَّالِمُونَ (45)
Ndipo mu ilo, Ife tidalamula kuti moyo ku moyo, diso ku diso, mphuno ku mphuno, khutu ku khutu, dzino ku dzino ndi ululu ku ululu. Koma ngati munthu akhululuka chifukwa chowonetsa chisoni, chimenechi chidzakhala chikhululukiro. Ndipo aliyense amene saweruza ndi zomwe adavumbulutsa Mulungu, woteroyo ndi opanda chilungamo
وَقَفَّيْنَا عَلَىٰ آثَارِهِم بِعِيسَى ابْنِ مَرْيَمَ مُصَدِّقًا لِّمَا بَيْنَ يَدَيْهِ مِنَ التَّوْرَاةِ ۖ وَآتَيْنَاهُ الْإِنجِيلَ فِيهِ هُدًى وَنُورٌ وَمُصَدِّقًا لِّمَا بَيْنَ يَدَيْهِ مِنَ التَّوْرَاةِ وَهُدًى وَمَوْعِظَةً لِّلْمُتَّقِينَ (46)
Atapita awa, Ife tidatumiza Yesu, mwana wamwamuna wa Maria kudzatsimikiza za Buku la chipangano chakale limene lidavumbulitsidwa kale ndipo tidamupatsa Iye chipangano chatsopano m’mene muli ulangizi ndi muuni wotsimikiza zonse zimene zidavumbulutsidwa kale m’buku la chipangano chakale, ulangizi ndi chenjezo kwa anthu oyera mtima
وَلْيَحْكُمْ أَهْلُ الْإِنجِيلِ بِمَا أَنزَلَ اللَّهُ فِيهِ ۚ وَمَن لَّمْ يَحْكُم بِمَا أَنزَلَ اللَّهُ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْفَاسِقُونَ (47)
Anthu a m’Buku la chipangano chatsopano aweruze potsatira zimene Mulungu wavumbulutsa m’menemo. Ndipo aliyense amene saweruza molingana ndi chivumbulutso cha Mulungu ndi olakwa
وَأَنزَلْنَا إِلَيْكَ الْكِتَابَ بِالْحَقِّ مُصَدِّقًا لِّمَا بَيْنَ يَدَيْهِ مِنَ الْكِتَابِ وَمُهَيْمِنًا عَلَيْهِ ۖ فَاحْكُم بَيْنَهُم بِمَا أَنزَلَ اللَّهُ ۖ وَلَا تَتَّبِعْ أَهْوَاءَهُمْ عَمَّا جَاءَكَ مِنَ الْحَقِّ ۚ لِكُلٍّ جَعَلْنَا مِنكُمْ شِرْعَةً وَمِنْهَاجًا ۚ وَلَوْ شَاءَ اللَّهُ لَجَعَلَكُمْ أُمَّةً وَاحِدَةً وَلَٰكِن لِّيَبْلُوَكُمْ فِي مَا آتَاكُمْ ۖ فَاسْتَبِقُوا الْخَيْرَاتِ ۚ إِلَى اللَّهِ مَرْجِعُكُمْ جَمِيعًا فَيُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمْ فِيهِ تَخْتَلِفُونَ (48)
Ndipo kwa iwe, tavumbulutsa Buku mwachoonadi kutsimikiza Mabuku amene adadza kale, okhulupilika ndi a pamwamba. Kotero weruza pakati pawo ndi zimene wavumbulutsa Mulungu ndipo usatsatire zilakolako zawo kusiya choonadi chimene chavumbulutsidwa kwa iwe. Ife takhazikitsa lamulo ndipo takonza njira yoyenera. Ngati Mulungu akadafuna, akadakupangani inu kukhala mtundu umodzi wa anthu koma afuna kuti akuyeseni inu ndi zimene wakupatsani. Motero pikisanani pochita ntchito zabwino. Ndi kwa Mulungu kumene nonsenu mudzabwerera ndipo Iye adzakuuzani zonse zimene munali kutsutsana
وَأَنِ احْكُم بَيْنَهُم بِمَا أَنزَلَ اللَّهُ وَلَا تَتَّبِعْ أَهْوَاءَهُمْ وَاحْذَرْهُمْ أَن يَفْتِنُوكَ عَن بَعْضِ مَا أَنزَلَ اللَّهُ إِلَيْكَ ۖ فَإِن تَوَلَّوْا فَاعْلَمْ أَنَّمَا يُرِيدُ اللَّهُ أَن يُصِيبَهُم بِبَعْضِ ذُنُوبِهِمْ ۗ وَإِنَّ كَثِيرًا مِّنَ النَّاسِ لَفَاسِقُونَ (49)
Ndipo motero weruza pakati pawo molingana ndi chivumbulutso cha Mulungu ndipo usatsatire zilakolako zawo, ndipo chenjera nawo chifukwa akhoza kukubweza kugawo limene Mulungu wavumbulutsa kwa iwe. Koma ngati iwo akana chiweruzo chako, dziwani kuti chifuniro cha Mulungu ndi kuwalanga chifukwa cha zoipa zawo. Ndithudi anthu ambiri ndi oswa malamulo
أَفَحُكْمَ الْجَاهِلِيَّةِ يَبْغُونَ ۚ وَمَنْ أَحْسَنُ مِنَ اللَّهِ حُكْمًا لِّقَوْمٍ يُوقِنُونَ (50)
Kodi ndi malamulo a chikunja amene iwo afuna kuti aweruzidwe nawo? Kodi woweruza wabwino kwambiri ndani woposa Mulungu kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro cholimba
۞ يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَتَّخِذُوا الْيَهُودَ وَالنَّصَارَىٰ أَوْلِيَاءَ ۘ بَعْضُهُمْ أَوْلِيَاءُ بَعْضٍ ۚ وَمَن يَتَوَلَّهُم مِّنكُمْ فَإِنَّهُ مِنْهُمْ ۗ إِنَّ اللَّهَ لَا يَهْدِي الْقَوْمَ الظَّالِمِينَ (51)
oh inu anthu okhulupirira! Musasankhe Ayuda ndi Akhirisitu kuti akhale abwenzi anu. Iwo ndi abwenzi a wina ndi mnzake ndipo aliyense wa inu amene apalana nawo chibwenzi ndithudi adzakhala mmodzi wa iwo. Ndithudi Mulungu satsogolera anthu ochita zoipa
فَتَرَى الَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٌ يُسَارِعُونَ فِيهِمْ يَقُولُونَ نَخْشَىٰ أَن تُصِيبَنَا دَائِرَةٌ ۚ فَعَسَى اللَّهُ أَن يَأْتِيَ بِالْفَتْحِ أَوْ أَمْرٍ مِّنْ عِندِهِ فَيُصْبِحُوا عَلَىٰ مَا أَسَرُّوا فِي أَنفُسِهِمْ نَادِمِينَ (52)
Ndipo iwe umawaona anthu amene ali ndi matenda m’mitima mwawo ali kuwathamangira abwenzi awo nati: “Tili kuopa kuti mwina tsoka likhoza kutigwera ife.” Mwina Mulungu akhoza kubweretsa kupambana kapena lamulo mwachifuniro chake. Ndipo iwo adzadandaula chifukwa cha zimene adasunga ngati chinsinsi mwa iwo okha
وَيَقُولُ الَّذِينَ آمَنُوا أَهَٰؤُلَاءِ الَّذِينَ أَقْسَمُوا بِاللَّهِ جَهْدَ أَيْمَانِهِمْ ۙ إِنَّهُمْ لَمَعَكُمْ ۚ حَبِطَتْ أَعْمَالُهُمْ فَأَصْبَحُوا خَاسِرِينَ (53)
Ndipo anthu okhulupirira adzati; “Kodi awa ndi anthu omwe analumbira molimbika kuti, pali Mulungu, iwo ali pamodzi ndi inu?” Ntchito zawo zonse zidzakhala zopanda pake ndipo iwo akhala olephera
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا مَن يَرْتَدَّ مِنكُمْ عَن دِينِهِ فَسَوْفَ يَأْتِي اللَّهُ بِقَوْمٍ يُحِبُّهُمْ وَيُحِبُّونَهُ أَذِلَّةٍ عَلَى الْمُؤْمِنِينَ أَعِزَّةٍ عَلَى الْكَافِرِينَ يُجَاهِدُونَ فِي سَبِيلِ اللَّهِ وَلَا يَخَافُونَ لَوْمَةَ لَائِمٍ ۚ ذَٰلِكَ فَضْلُ اللَّهِ يُؤْتِيهِ مَن يَشَاءُ ۚ وَاللَّهُ وَاسِعٌ عَلِيمٌ (54)
Inu anthu okhulupirira! Aliyense wa inu amene asiya chipembedzo chake, Mulungu adzaika anthu wolowa m’malo mwake ndipo Mulungu adzawakonda anthuwo ndiponso anthuwo adzakonda Mulungu, odzichepetsa kwa anthu okhulupirira koma olimba kwa anthu osakhulupirira, omenya nkhondo munjira ya Mulungu ndipo osaopa zonena za anthu. Chimenechi ndicho chisomo cha Mulungu chimene Iye amachipereka kwa aliyense amene Iye wamufuna. Ndipo Mulungu ali ndi zonse zimene zolengedwa zake zimafuna, Iye amadziwa
إِنَّمَا وَلِيُّكُمُ اللَّهُ وَرَسُولُهُ وَالَّذِينَ آمَنُوا الَّذِينَ يُقِيمُونَ الصَّلَاةَ وَيُؤْتُونَ الزَّكَاةَ وَهُمْ رَاكِعُونَ (55)
Ndithudi bwenzi lanu lapamtima ndi Mulungu, Mtumwi wake ndi anthu okhulupirira amene amapemphera nthawi zonse ndipo amapereka zopereka ndipo amadzichepetsa akamapembedza
وَمَن يَتَوَلَّ اللَّهَ وَرَسُولَهُ وَالَّذِينَ آمَنُوا فَإِنَّ حِزْبَ اللَّهِ هُمُ الْغَالِبُونَ (56)
Ndipo amene amasankha Mulungu, Mtumwi wake ndi anthu onse okhulupirira kukhala omuteteza ayenera kudziwa kuti gulu la Mulungu lidzapambana
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَتَّخِذُوا الَّذِينَ اتَّخَذُوا دِينَكُمْ هُزُوًا وَلَعِبًا مِّنَ الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ مِن قَبْلِكُمْ وَالْكُفَّارَ أَوْلِيَاءَ ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ (57)
Oh inu okhulupirira! Musapalane chibwenzi ndi anthu amene amachita chipongwe chipembedzo chanu ndi kuchisandutsa kukhala choseweretsa, amene ali pakati pa anthu amene adapatsidwa mau a Mulungu kale inu musanadze kapena anthu osakhulupirira ndipo opani Mulungu ngati inu ndinu anthu okhulupirira
وَإِذَا نَادَيْتُمْ إِلَى الصَّلَاةِ اتَّخَذُوهَا هُزُوًا وَلَعِبًا ۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ قَوْمٌ لَّا يَعْقِلُونَ (58)
Ndipo ngati inu muitanira mapemphero, iwo amaganiza kuti ndi nthabwala ndiponso chinthu choseweretsa chifukwa iwo ndi anthu opanda nzeru
قُلْ يَا أَهْلَ الْكِتَابِ هَلْ تَنقِمُونَ مِنَّا إِلَّا أَنْ آمَنَّا بِاللَّهِ وَمَا أُنزِلَ إِلَيْنَا وَمَا أُنزِلَ مِن قَبْلُ وَأَنَّ أَكْثَرَكُمْ فَاسِقُونَ (59)
Nena: “oh inu anthu a m’Buku! Kodi inu muli kutitsutsa ife chifukwa chakuti takhulupirira mwa Mulungu ndi mwa zimene zavumbulutsidwa kwa ife ndiponso zimene zidavumbulutsidwa kale ndipo kuti ambiri a inu ndinu anthu ochita zoipa?”
قُلْ هَلْ أُنَبِّئُكُم بِشَرٍّ مِّن ذَٰلِكَ مَثُوبَةً عِندَ اللَّهِ ۚ مَن لَّعَنَهُ اللَّهُ وَغَضِبَ عَلَيْهِ وَجَعَلَ مِنْهُمُ الْقِرَدَةَ وَالْخَنَازِيرَ وَعَبَدَ الطَّاغُوتَ ۚ أُولَٰئِكَ شَرٌّ مَّكَانًا وَأَضَلُّ عَن سَوَاءِ السَّبِيلِ (60)
Nena: “Kodi ine ndikuuzeni chinthu chonyasa kuposa ichi chochokera kwa Mulungu? Iwo amene Mulungu adawatemberera ndipo adawakwiyira ndikuwasintha kukhala nyani ndi nkhumba, iwo amene amapembedza milungu yabodza. Awa ndi anthu apansi zedi ndipo ndi osochera kunjira yoyenera.”
وَإِذَا جَاءُوكُمْ قَالُوا آمَنَّا وَقَد دَّخَلُوا بِالْكُفْرِ وَهُمْ قَدْ خَرَجُوا بِهِ ۚ وَاللَّهُ أَعْلَمُ بِمَا كَانُوا يَكْتُمُونَ (61)
Ndi pamene iwo amadza kwa inu amati: “Ife takhulupirira.” Koma iwo amalowa ali osakhulupirira ndipo amatuluka ndi kusakhulupirira. Ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene amabisa
وَتَرَىٰ كَثِيرًا مِّنْهُمْ يُسَارِعُونَ فِي الْإِثْمِ وَالْعُدْوَانِ وَأَكْلِهِمُ السُّحْتَ ۚ لَبِئْسَ مَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (62)
Ndipo iwe umawaona ambiri a iwo ali kupikisana m’machimo ndi mu zinthu zodanitsa ndipo ali kudya zinthu zosaloledwa. Ndithudi ndi zoipa zimene iwo akhala ali kuchita
لَوْلَا يَنْهَاهُمُ الرَّبَّانِيُّونَ وَالْأَحْبَارُ عَن قَوْلِهِمُ الْإِثْمَ وَأَكْلِهِمُ السُّحْتَ ۚ لَبِئْسَ مَا كَانُوا يَصْنَعُونَ (63)
Kodi ndi chifukwa chiyani Abusa ndiponso anthu oyera, sawaletsa anthu kulankhula mawu amachimo kapena kudya zinthu zoletsedwa? Ndithudi zoipa ndi zimene iwo akhala ali kuchita
وَقَالَتِ الْيَهُودُ يَدُ اللَّهِ مَغْلُولَةٌ ۚ غُلَّتْ أَيْدِيهِمْ وَلُعِنُوا بِمَا قَالُوا ۘ بَلْ يَدَاهُ مَبْسُوطَتَانِ يُنفِقُ كَيْفَ يَشَاءُ ۚ وَلَيَزِيدَنَّ كَثِيرًا مِّنْهُم مَّا أُنزِلَ إِلَيْكَ مِن رَّبِّكَ طُغْيَانًا وَكُفْرًا ۚ وَأَلْقَيْنَا بَيْنَهُمُ الْعَدَاوَةَ وَالْبَغْضَاءَ إِلَىٰ يَوْمِ الْقِيَامَةِ ۚ كُلَّمَا أَوْقَدُوا نَارًا لِّلْحَرْبِ أَطْفَأَهَا اللَّهُ ۚ وَيَسْعَوْنَ فِي الْأَرْضِ فَسَادًا ۚ وَاللَّهُ لَا يُحِبُّ الْمُفْسِدِينَ (64)
Ayudaamanenakuti:“Manjaa Mulungundiomangika.” Manja awo ndiwo akhale omangika ndiponso iwo atembereredwe chifukwa cha zimene anena! Iyayi! Manja onse a Mulungu ndi otambasuka. Iye amapereka mmene wafunira. Ndithudi chimene Mulungu wavumbulutsa kwa iwe chimaonjezera udani ndi kusakhulupirira kwa anthu ambiri mwaiwo. Ife taika pakati pawo ndi kukhazikitsa udani mpaka patsiku louka kwa akufa. Nthawi zonse pamene iwo ayatsa moto wa nkhondo, Mulungu amauzima ndipo iwo amayesetsa kupanga zoipa padziko. Mulungu sakonda anthu oyambitsa chisokonezo
وَلَوْ أَنَّ أَهْلَ الْكِتَابِ آمَنُوا وَاتَّقَوْا لَكَفَّرْنَا عَنْهُمْ سَيِّئَاتِهِمْ وَلَأَدْخَلْنَاهُمْ جَنَّاتِ النَّعِيمِ (65)
Akadakhala kuti anthu a m’Buku adakhulupirira ndi kulewa zoipa, Ife tikadawakhululukira machimo awo ndi kuwalowetsa m’minda ya mtendere
وَلَوْ أَنَّهُمْ أَقَامُوا التَّوْرَاةَ وَالْإِنجِيلَ وَمَا أُنزِلَ إِلَيْهِم مِّن رَّبِّهِمْ لَأَكَلُوا مِن فَوْقِهِمْ وَمِن تَحْتِ أَرْجُلِهِم ۚ مِّنْهُمْ أُمَّةٌ مُّقْتَصِدَةٌ ۖ وَكَثِيرٌ مِّنْهُمْ سَاءَ مَا يَعْمَلُونَ (66)
Ndipo iwo akadatsatira Buku la chipangano chakale ndi chipangano chatsopano ndiponso zimene zavumbulutsidwa kwa iwo kuchokera kwa Ambuye wawo, iwo akadadya zinthu kuchokera kumwamba ndi pansi pa miyendo yawo. Ena mwa iwo ndi anthu a chilungamo koma ambiri a iwo ndi ochita zoipa
۞ يَا أَيُّهَا الرَّسُولُ بَلِّغْ مَا أُنزِلَ إِلَيْكَ مِن رَّبِّكَ ۖ وَإِن لَّمْ تَفْعَلْ فَمَا بَلَّغْتَ رِسَالَتَهُ ۚ وَاللَّهُ يَعْصِمُكَ مِنَ النَّاسِ ۗ إِنَّ اللَّهَ لَا يَهْدِي الْقَوْمَ الْكَافِرِينَ (67)
Oh iwe Mtumwi! Lalikira zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako. Ndipo ngati iwe siutero, ndithudi, iwe walephera kupereka uthenga wake. Mulungu adzakuteteza iwe kwa anthu. Ndithudi Mulungu satsogolera anthu osakhulupirira
قُلْ يَا أَهْلَ الْكِتَابِ لَسْتُمْ عَلَىٰ شَيْءٍ حَتَّىٰ تُقِيمُوا التَّوْرَاةَ وَالْإِنجِيلَ وَمَا أُنزِلَ إِلَيْكُم مِّن رَّبِّكُمْ ۗ وَلَيَزِيدَنَّ كَثِيرًا مِّنْهُم مَّا أُنزِلَ إِلَيْكَ مِن رَّبِّكَ طُغْيَانًا وَكُفْرًا ۖ فَلَا تَأْسَ عَلَى الْقَوْمِ الْكَافِرِينَ (68)
Nena: “oh inu anthu a m’Buku! Inu mulibe poimira mpaka pamene mutatsatira Buku la chipangano chakale ndi chipangano chatsopano ndi zimene zavumbulutsidwa kwa inu kuchokera kwa Ambuye wanu.” Ndithudi zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako ziwonjezera, mwa ambiri a iwo, machimo ndi kusakhulupirira. Motero iwe usamve chisoni ndi anthu osakhulupirira
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا وَالَّذِينَ هَادُوا وَالصَّابِئُونَ وَالنَّصَارَىٰ مَنْ آمَنَ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ وَعَمِلَ صَالِحًا فَلَا خَوْفٌ عَلَيْهِمْ وَلَا هُمْ يَحْزَنُونَ (69)
Ndithudi iwo amene amakhulupirira ndi iwo amene ndi Ayuda, Masabiyani ndi Akhirisitu, aliyense amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku la chimaliziro ndipo amachita zabwino, iwo sadzakhala ndi mantha ndipo sadzadandaula
لَقَدْ أَخَذْنَا مِيثَاقَ بَنِي إِسْرَائِيلَ وَأَرْسَلْنَا إِلَيْهِمْ رُسُلًا ۖ كُلَّمَا جَاءَهُمْ رَسُولٌ بِمَا لَا تَهْوَىٰ أَنفُسُهُمْ فَرِيقًا كَذَّبُوا وَفَرِيقًا يَقْتُلُونَ (70)
Ndithudi Ife tidalandira lonjezo kuchokera kwa ana a Israyeli ndipo tidatumiza Atumwi kwa iwo. Koma nthawi iliyonse imene Mtumwi amadza kwa iwo ndi uthenga umene mitima yawo siimafuna, iwo adali kunena kuti ena ndi onama pamene ena adali kuwapha
وَحَسِبُوا أَلَّا تَكُونَ فِتْنَةٌ فَعَمُوا وَصَمُّوا ثُمَّ تَابَ اللَّهُ عَلَيْهِمْ ثُمَّ عَمُوا وَصَمُّوا كَثِيرٌ مِّنْهُمْ ۚ وَاللَّهُ بَصِيرٌ بِمَا يَعْمَلُونَ (71)
Iwo adali kuganiza kuti padalibe chilango chimene chikadawatsata, motero iwo adakhala a khungu ndi osamva. Ndipo Mulungu adawakhululukira iwo komabe ambiri a iwo adali a khungu ndi osamva. Mulungu amaona zonse zimene akuchita
لَقَدْ كَفَرَ الَّذِينَ قَالُوا إِنَّ اللَّهَ هُوَ الْمَسِيحُ ابْنُ مَرْيَمَ ۖ وَقَالَ الْمَسِيحُ يَا بَنِي إِسْرَائِيلَ اعْبُدُوا اللَّهَ رَبِّي وَرَبَّكُمْ ۖ إِنَّهُ مَن يُشْرِكْ بِاللَّهِ فَقَدْ حَرَّمَ اللَّهُ عَلَيْهِ الْجَنَّةَ وَمَأْوَاهُ النَّارُ ۖ وَمَا لِلظَّالِمِينَ مِنْ أَنصَارٍ (72)
Ndithudi ndi osakhulupirira amene amati: “Mulungu ndi Messiya mwana wa mwamuna wa Maria.” Koma Messiya mwini wake adati: “o inu ana a Israyeli! Pembedzani Mulungu, Ambuye wanga amene ndi Ambuye wanu.”Ndithudi aliyense amene apembedza milungu ina m’malo mwa Mulungu yekha sadzalowa ku Paradiso ndipo malo ake ndi kumoto. Ndipo anthu ochita zoipa alibe owathandiza
لَّقَدْ كَفَرَ الَّذِينَ قَالُوا إِنَّ اللَّهَ ثَالِثُ ثَلَاثَةٍ ۘ وَمَا مِنْ إِلَٰهٍ إِلَّا إِلَٰهٌ وَاحِدٌ ۚ وَإِن لَّمْ يَنتَهُوا عَمَّا يَقُولُونَ لَيَمَسَّنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا مِنْهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (73)
Ndithudi osakhulupirira ndi anthu amene amati: “Mulungu ndi mmodzi mwa atatu.” Koma kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha. Ndipo ngati iwo sasiya zimene akunena, ndithudi chilango chowawa chidzagwa pa anthu osakhulupilira amene ali pakati pawo
أَفَلَا يَتُوبُونَ إِلَى اللَّهِ وَيَسْتَغْفِرُونَهُ ۚ وَاللَّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (74)
Kodi iwo sangalape kwa Mulungu ndi kufunsa chikhululukiro chake? Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha
مَّا الْمَسِيحُ ابْنُ مَرْيَمَ إِلَّا رَسُولٌ قَدْ خَلَتْ مِن قَبْلِهِ الرُّسُلُ وَأُمُّهُ صِدِّيقَةٌ ۖ كَانَا يَأْكُلَانِ الطَّعَامَ ۗ انظُرْ كَيْفَ نُبَيِّنُ لَهُمُ الْآيَاتِ ثُمَّ انظُرْ أَنَّىٰ يُؤْفَكُونَ (75)
Messiya, mwana wamwamuna wa Maria, sadali wina aliyense ayi koma Mtumwi, Atumwi ena adadza iye asadadze. Mayi wake adali mayi wokhulupilira. onse adali kudya chakudya. Taona mmene timaonetsera kwa iwo poyera chivumbulutso chathu ndipo taona mmene iwo amatembenuzira choonadi
قُلْ أَتَعْبُدُونَ مِن دُونِ اللَّهِ مَا لَا يَمْلِكُ لَكُمْ ضَرًّا وَلَا نَفْعًا ۚ وَاللَّهُ هُوَ السَّمِيعُ الْعَلِيمُ (76)
Nena: “Kodi inu muzipembedza, powonjezera pa Mulungu, chinthu chimene sichingathe kukuonongani kapena kukuthandizani?” Koma Mulungu ndiye amamva zonse ndiponso amadziwa zonse
قُلْ يَا أَهْلَ الْكِتَابِ لَا تَغْلُوا فِي دِينِكُمْ غَيْرَ الْحَقِّ وَلَا تَتَّبِعُوا أَهْوَاءَ قَوْمٍ قَدْ ضَلُّوا مِن قَبْلُ وَأَضَلُّوا كَثِيرًا وَضَلُّوا عَن سَوَاءِ السَّبِيلِ (77)
Nena: “Inu anthu a m’Buku! Musaonjezere china chilichonse m’chipembedzo chanu chosakhala choonadi ndipo musatsatire zilakolako za anthu amene adasokera kale, amene anasocheretsa anthu ochuluka ndiponso adadzisocheretsa iwo eni kunjira yoyenera.”
لُعِنَ الَّذِينَ كَفَرُوا مِن بَنِي إِسْرَائِيلَ عَلَىٰ لِسَانِ دَاوُودَ وَعِيسَى ابْنِ مَرْيَمَ ۚ ذَٰلِكَ بِمَا عَصَوا وَّكَانُوا يَعْتَدُونَ (78)
Iwo amene adali pakati pa ana a Israyeli, ndipo sanakhulupilire, anatembereredwa ndi lilime la Davide ndi la Yesu, mwana wa wamamuna wa Maria. Zimenezo ndi chifukwa chakuti adanyoza ndi kulumpha malire
كَانُوا لَا يَتَنَاهَوْنَ عَن مُّنكَرٍ فَعَلُوهُ ۚ لَبِئْسَ مَا كَانُوا يَفْعَلُونَ (79)
Iwo sanali kuletsana wina ndi mnzake kuchita zoipa zimene ankachita. Ndithudi ndi zoipa zimene adali kuchita
تَرَىٰ كَثِيرًا مِّنْهُمْ يَتَوَلَّوْنَ الَّذِينَ كَفَرُوا ۚ لَبِئْسَ مَا قَدَّمَتْ لَهُمْ أَنفُسُهُمْ أَن سَخِطَ اللَّهُ عَلَيْهِمْ وَفِي الْعَذَابِ هُمْ خَالِدُونَ (80)
Iwe umawaona anthu ambiri akupalana ubwenzi ndi anthu osakhulupirira. Ndithudi ndi zinthu zoipa zimene iwo adatsogoza ndipo chifukwa cha ichi mkwiyo wa Mulungu unagwa pa iwo ndipo adzalandira chilango chosatha
وَلَوْ كَانُوا يُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ وَالنَّبِيِّ وَمَا أُنزِلَ إِلَيْهِ مَا اتَّخَذُوهُمْ أَوْلِيَاءَ وَلَٰكِنَّ كَثِيرًا مِّنْهُمْ فَاسِقُونَ (81)
Ndipo iwo akadakhulupirira mwa Mulungu ndi mwa Mtumwi ndi zimene zavumbulutsidwa kwa iye, iwo sakadapalana nawo ubwenzi. Koma ambiri a iwo ndi anthu ochita zoipa
۞ لَتَجِدَنَّ أَشَدَّ النَّاسِ عَدَاوَةً لِّلَّذِينَ آمَنُوا الْيَهُودَ وَالَّذِينَ أَشْرَكُوا ۖ وَلَتَجِدَنَّ أَقْرَبَهُم مَّوَدَّةً لِّلَّذِينَ آمَنُوا الَّذِينَ قَالُوا إِنَّا نَصَارَىٰ ۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّ مِنْهُمْ قِسِّيسِينَ وَرُهْبَانًا وَأَنَّهُمْ لَا يَسْتَكْبِرُونَ (82)
Ndithudi udzaona kuti anthu odana kwambiri ndi anthuokhulupirirandiAyudandianthuopembedzamafano ndipo udzapeza amene amakhala kufupi pokondana ndi anthu okhulupirira ndiwo amene amati: “Ndife Akhirisitu.” Chifukwa chake ndi chakuti pali pakati pawo Ansembe ndi Abusa ndipo iwo sadzikweza
وَإِذَا سَمِعُوا مَا أُنزِلَ إِلَى الرَّسُولِ تَرَىٰ أَعْيُنَهُمْ تَفِيضُ مِنَ الدَّمْعِ مِمَّا عَرَفُوا مِنَ الْحَقِّ ۖ يَقُولُونَ رَبَّنَا آمَنَّا فَاكْتُبْنَا مَعَ الشَّاهِدِينَ (83)
Ndipo pamene iwo amamvetsera ku zimene zavumbulutsidwa kwa Mtumwi, udzaona misozi ili kuyengeza m’maso mwawo chifukwa cha choonadi chimene adziwa. Iwo amati: “Ambuye wathu! Ife takhulupirira motero tilembeni pamodzi ndi omwe akuikira umboni.”
وَمَا لَنَا لَا نُؤْمِنُ بِاللَّهِ وَمَا جَاءَنَا مِنَ الْحَقِّ وَنَطْمَعُ أَن يُدْخِلَنَا رَبُّنَا مَعَ الْقَوْمِ الصَّالِحِينَ (84)
“Kodi ife tisakhulupirire bwanji mwa Mulungu ndi chimene chadza kwa ife moonadi pamene ife tikufunitsitsa kuti Ambuye wathu akatilowetse pamodzi ndi anthu ochita zabwino?”
فَأَثَابَهُمُ اللَّهُ بِمَا قَالُوا جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا ۚ وَذَٰلِكَ جَزَاءُ الْمُحْسِنِينَ (85)
Motero, chifukwa cha zimene ananena, Mulungu adawalipira minda yothiriridwa ndi madzi ya m’mitsinje kumene adzakhaleko mpaka kalekale. Amenewa ndiwo malipiro a anthu olungama
وَالَّذِينَ كَفَرُوا وَكَذَّبُوا بِآيَاتِنَا أُولَٰئِكَ أَصْحَابُ الْجَحِيمِ (86)
Koma iwo amene sanakhulupirire ndipo amakana chivumbulutso chathu, iwo adzakhala eni ake aku Gahena
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تُحَرِّمُوا طَيِّبَاتِ مَا أَحَلَّ اللَّهُ لَكُمْ وَلَا تَعْتَدُوا ۚ إِنَّ اللَّهَ لَا يُحِبُّ الْمُعْتَدِينَ (87)
Oh inu anthu okhulupirira! Musaletse zabwino zimene Mulungu wakulolani kuti muchite, musadumphe malire. Ndithudi Mulungu sakonda anthu odumpha malire
وَكُلُوا مِمَّا رَزَقَكُمُ اللَّهُ حَلَالًا طَيِّبًا ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ الَّذِي أَنتُم بِهِ مُؤْمِنُونَ (88)
Ndipo idyani zinthu zololedwa ndi zabwino zonse zimene Mulungu wakupatsani ndipo opani Mulungu amene inu mumakhulupirira
لَا يُؤَاخِذُكُمُ اللَّهُ بِاللَّغْوِ فِي أَيْمَانِكُمْ وَلَٰكِن يُؤَاخِذُكُم بِمَا عَقَّدتُّمُ الْأَيْمَانَ ۖ فَكَفَّارَتُهُ إِطْعَامُ عَشَرَةِ مَسَاكِينَ مِنْ أَوْسَطِ مَا تُطْعِمُونَ أَهْلِيكُمْ أَوْ كِسْوَتُهُمْ أَوْ تَحْرِيرُ رَقَبَةٍ ۖ فَمَن لَّمْ يَجِدْ فَصِيَامُ ثَلَاثَةِ أَيَّامٍ ۚ ذَٰلِكَ كَفَّارَةُ أَيْمَانِكُمْ إِذَا حَلَفْتُمْ ۚ وَاحْفَظُوا أَيْمَانَكُمْ ۚ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ اللَّهُ لَكُمْ آيَاتِهِ لَعَلَّكُمْ تَشْكُرُونَ (89)
Mulungu sadzakulangani inu chifukwa cha kulumbira kwanu kosakonzekera. Koma Iye adzakulangani chifukwa cha malonjezo anu a bodza. Kulipira kwake ndi kudyetsa anthu khumi osowa ndi chakudya chimene inu mumadyetsa banja lanu kapena kuwaveka kapena kumasula kapolo mmodzi. Koma yense amene sangathe kukwaniritsa china cha izi, ayenera kusala masiku atatu. Kumeneko ndiko kulipira kwa malonjezo anu ngati mwalumbira. Motero sungani malonjezo anu. Mmenemo ndimo mmene Mulungu amaonetsera poyera chivumbulutso chake kuti mukhale oyamika
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِنَّمَا الْخَمْرُ وَالْمَيْسِرُ وَالْأَنصَابُ وَالْأَزْلَامُ رِجْسٌ مِّنْ عَمَلِ الشَّيْطَانِ فَاجْتَنِبُوهُ لَعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ (90)
Oh inu anthu okhulupirira! Zoledzeretsa, masewera a mwayi, kupembedza mafano ndi mipaliro ndi ntchito zoipa zopangidwa ndi Satana. Motero zipeweni kuti mukhale opambana
إِنَّمَا يُرِيدُ الشَّيْطَانُ أَن يُوقِعَ بَيْنَكُمُ الْعَدَاوَةَ وَالْبَغْضَاءَ فِي الْخَمْرِ وَالْمَيْسِرِ وَيَصُدَّكُمْ عَن ذِكْرِ اللَّهِ وَعَنِ الصَّلَاةِ ۖ فَهَلْ أَنتُم مُّنتَهُونَ (91)
Ndithudi cholinga cha Satana ndikudzetsa udani pakati panu pogwiritsa ntchito zoledzeretsa, masewera a mwayi ndiponso kukuletsani inu kuti muzikumbukira Mulungu ndi mapemphero. Kodi simungathe kuzisiya
وَأَطِيعُوا اللَّهَ وَأَطِيعُوا الرَّسُولَ وَاحْذَرُوا ۚ فَإِن تَوَلَّيْتُمْ فَاعْلَمُوا أَنَّمَا عَلَىٰ رَسُولِنَا الْبَلَاغُ الْمُبِينُ (92)
Ndipo mverani Mulungu ndi Mtumwi. Chenjerani ndipo opani Mulungu. Ngati inu mutembenuka dziwani kuti udindo wa Mtumwi wathu ndi kupereka uthenga momveka
لَيْسَ عَلَى الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ جُنَاحٌ فِيمَا طَعِمُوا إِذَا مَا اتَّقَوا وَّآمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ ثُمَّ اتَّقَوا وَّآمَنُوا ثُمَّ اتَّقَوا وَّأَحْسَنُوا ۗ وَاللَّهُ يُحِبُّ الْمُحْسِنِينَ (93)
Kwa onse amene akhulupirira ndi kuchita zabwino sipadzakhala mlandu pa nkhani ya chakudya chilichonse chimene adadya ngati iwo aopa Mulungu, akhulupirira mwa Iye ndi kuchita ntchito zabwino moyenera. Mulungu amakonda anthu ochita zabwino
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَيَبْلُوَنَّكُمُ اللَّهُ بِشَيْءٍ مِّنَ الصَّيْدِ تَنَالُهُ أَيْدِيكُمْ وَرِمَاحُكُمْ لِيَعْلَمَ اللَّهُ مَن يَخَافُهُ بِالْغَيْبِ ۚ فَمَنِ اعْتَدَىٰ بَعْدَ ذَٰلِكَ فَلَهُ عَذَابٌ أَلِيمٌ (94)
Oh inu anthu okhulupirira! Mulungu adzakuyesani inu ndi nyama zimene mukhoza kugwira ndi manja anu kapena kupha ndi mikondo yanu kuti Mulungu awadziwe onse amene amamuopa Iye mwamseri. Yense amene adumpha malire pambuyo pa izi adzakhala ndi chilango chowawa
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَقْتُلُوا الصَّيْدَ وَأَنتُمْ حُرُمٌ ۚ وَمَن قَتَلَهُ مِنكُم مُّتَعَمِّدًا فَجَزَاءٌ مِّثْلُ مَا قَتَلَ مِنَ النَّعَمِ يَحْكُمُ بِهِ ذَوَا عَدْلٍ مِّنكُمْ هَدْيًا بَالِغَ الْكَعْبَةِ أَوْ كَفَّارَةٌ طَعَامُ مَسَاكِينَ أَوْ عَدْلُ ذَٰلِكَ صِيَامًا لِّيَذُوقَ وَبَالَ أَمْرِهِ ۗ عَفَا اللَّهُ عَمَّا سَلَفَ ۚ وَمَنْ عَادَ فَيَنتَقِمُ اللَّهُ مِنْهُ ۗ وَاللَّهُ عَزِيزٌ ذُو انتِقَامٍ (95)
Oh inu anthu okhulupirira! Musaphe nyama za m’thengo pamene mutavala zobvala za Hajji kapena Umra. Yense wa inu amene apha nyama mwadala, adzapereka, ngati dipo lofika ku Kaaba, nyama yoweta yofanana ndi imene iye wapha, imene idzatsimikizidwa ndi anthu awiri olungama amene ali pakati panu kapena m’malo mwake adzadyetsa anthu osauka kapena kusala kuti alawe kuipa kwa ntchito zake. Mulungu wakhululukira zonse za m’mbuyo koma ngati wina abwerera ku uchimo, Mulungu adzamulanga kwambiri. Mulungu ndi wamphamvu ndipo ndi mwini kubwezera
أُحِلَّ لَكُمْ صَيْدُ الْبَحْرِ وَطَعَامُهُ مَتَاعًا لَّكُمْ وَلِلسَّيَّارَةِ ۖ وَحُرِّمَ عَلَيْكُمْ صَيْدُ الْبَرِّ مَا دُمْتُمْ حُرُمًا ۗ وَاتَّقُوا اللَّهَ الَّذِي إِلَيْهِ تُحْشَرُونَ (96)
Ndi chololedwa kwa inu kusodza m’nyanja ndi kudya za mnyanja, inu ndi iwo a paulendo. Koma mwaletsedwa kupha nyama za pa mtunda pamene mutabvala zobvala za Hajji kapena Umra. Opani Mulungu kumene nonse mudzasonkhanitsidwa
۞ جَعَلَ اللَّهُ الْكَعْبَةَ الْبَيْتَ الْحَرَامَ قِيَامًا لِّلنَّاسِ وَالشَّهْرَ الْحَرَامَ وَالْهَدْيَ وَالْقَلَائِدَ ۚ ذَٰلِكَ لِتَعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ يَعْلَمُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ وَأَنَّ اللَّهَ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (97)
Mulungu anapanga Ka’ba, Nyumba yolemekezeka, malo a chitetezo ndi Hajji ndi Umra, anthu ndiponso Miezi Yoyera ndi nyama zoperekedwa ngati nsembe ndiponso zizindikiro zimene amamangira pa izo, kuti mukhoza kudziwa kuti Mulungu amadziwa zonse zimene zili mlengalenga ndi dziko lapansi ndiponso kuti Mulungu amadziwa zonse
اعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ شَدِيدُ الْعِقَابِ وَأَنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (98)
Dziwani kuti Mulungu ali ndi chilango chowawa ndipo kuti Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha
مَّا عَلَى الرَّسُولِ إِلَّا الْبَلَاغُ ۗ وَاللَّهُ يَعْلَمُ مَا تُبْدُونَ وَمَا تَكْتُمُونَ (99)
Ntchito ya Mtumwi ndi kungopereka chenjezo. Ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene mumaonetsa ndi zimene mumabisa
قُل لَّا يَسْتَوِي الْخَبِيثُ وَالطَّيِّبُ وَلَوْ أَعْجَبَكَ كَثْرَةُ الْخَبِيثِ ۚ فَاتَّقُوا اللَّهَ يَا أُولِي الْأَلْبَابِ لَعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ (100)
Nena: “Zabwino ndi zoipa sizifanana ngakhale kuti kuchuluka kwa zoipa kumakusangalatsani kwambiri.” Opani Mulungu inu anthu ozindikira,kuti mukhale opambana
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَسْأَلُوا عَنْ أَشْيَاءَ إِن تُبْدَ لَكُمْ تَسُؤْكُمْ وَإِن تَسْأَلُوا عَنْهَا حِينَ يُنَزَّلُ الْقُرْآنُ تُبْدَ لَكُمْ عَفَا اللَّهُ عَنْهَا ۗ وَاللَّهُ غَفُورٌ حَلِيمٌ (101)
oh inu anthu okhulupirira! Musamafunse zinthu zimene ngati zitadziwika kwa inu zikhoza kukuvutitsani. Koma ngati mufunsa za izo pamene Korani ili kuvumbulutsidwa kwa inu, zidzafotokozedwa mwatsatanetsatane kwa inu. Mulungu wakhululuka ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi wopilira kwambiri
قَدْ سَأَلَهَا قَوْمٌ مِّن قَبْلِكُمْ ثُمَّ أَصْبَحُوا بِهَا كَافِرِينَ (102)
Anthu ena, anafunsa za izo, inu musanadze koma iwo adakhalaosakhulupirira
مَا جَعَلَ اللَّهُ مِن بَحِيرَةٍ وَلَا سَائِبَةٍ وَلَا وَصِيلَةٍ وَلَا حَامٍ ۙ وَلَٰكِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا يَفْتَرُونَ عَلَى اللَّهِ الْكَذِبَ ۖ وَأَكْثَرُهُمْ لَا يَعْقِلُونَ (103)
Si Mulunguameneadayambitsa Bahira (miyambo yosakama ngamira yaikazi kapena Saiba (ngamira yaikazi kuisiya yokha kuubusa) kapena Wasila (kupereka nsembe ya nyama ya ngamila imene ibereka ana akazi motsatizana) kapena Ham (mitheno ya ngamira imene yaletsedwa kugwira ntchito) koma ndi anthu osakhulupirira amene amapeka bodza lokhudza Mulungu ndipo ambiri a iwo alibe nzeru
وَإِذَا قِيلَ لَهُمْ تَعَالَوْا إِلَىٰ مَا أَنزَلَ اللَّهُ وَإِلَى الرَّسُولِ قَالُوا حَسْبُنَا مَا وَجَدْنَا عَلَيْهِ آبَاءَنَا ۚ أَوَلَوْ كَانَ آبَاؤُهُمْ لَا يَعْلَمُونَ شَيْئًا وَلَا يَهْتَدُونَ (104)
Pamene zinenedwa kwa iwo kuti: Bwerani ku chimene Mulungu wavumbulutsa ndi kwa Mtumwi. Iwo amati, “Chikhulupiriro chimene adatisiyira makolo athu ndi chotikwanira.” Ngakhale kuti makolo awo samadziwa chilichonse ndipo sadatsogozedwe bwino
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا عَلَيْكُمْ أَنفُسَكُمْ ۖ لَا يَضُرُّكُم مَّن ضَلَّ إِذَا اهْتَدَيْتُمْ ۚ إِلَى اللَّهِ مَرْجِعُكُمْ جَمِيعًا فَيُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (105)
Oh inu anthu okhulupirira! Dzisamaleni nokha. Iye amene wasokera sangakuchiteni kanthu kalikonse ngati inu muli ochita zabwino. Nonse mudzabwerera kwa Mulungu ndipo adzakuuzani zimene munali kuchita
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا شَهَادَةُ بَيْنِكُمْ إِذَا حَضَرَ أَحَدَكُمُ الْمَوْتُ حِينَ الْوَصِيَّةِ اثْنَانِ ذَوَا عَدْلٍ مِّنكُمْ أَوْ آخَرَانِ مِنْ غَيْرِكُمْ إِنْ أَنتُمْ ضَرَبْتُمْ فِي الْأَرْضِ فَأَصَابَتْكُم مُّصِيبَةُ الْمَوْتِ ۚ تَحْبِسُونَهُمَا مِن بَعْدِ الصَّلَاةِ فَيُقْسِمَانِ بِاللَّهِ إِنِ ارْتَبْتُمْ لَا نَشْتَرِي بِهِ ثَمَنًا وَلَوْ كَانَ ذَا قُرْبَىٰ ۙ وَلَا نَكْتُمُ شَهَادَةَ اللَّهِ إِنَّا إِذًا لَّمِنَ الْآثِمِينَ (106)
O inu anthu okhulupirira! Pamene imfa idza pa mmodzi wa inu panthawi yopereka mawu, anthu awiri olungama achitire umboni pakati panu; kapena anthu amuna awiri ochokera kumtundu wina osakhulupirira ngati muli paulendo padziko ndipo imfa yakupezani. Asungeni mpaka mutatha kupemphera ndipo ngati mukaika za kukhulupirika kwawo, afunseni kuti alumbire pali Mulungu kuti: “Ife sitigulitsa umboni wathu pamtengo wina uliwonse ngakhale kwa m’bale wathu weniweni. Ndipo ife sitibisa umboni wa Mulungu, ndithudi ife titatero tikhala mgulu la anthu ochimwa.”
فَإِنْ عُثِرَ عَلَىٰ أَنَّهُمَا اسْتَحَقَّا إِثْمًا فَآخَرَانِ يَقُومَانِ مَقَامَهُمَا مِنَ الَّذِينَ اسْتَحَقَّ عَلَيْهِمُ الْأَوْلَيَانِ فَيُقْسِمَانِ بِاللَّهِ لَشَهَادَتُنَا أَحَقُّ مِن شَهَادَتِهِمَا وَمَا اعْتَدَيْنَا إِنَّا إِذًا لَّمِنَ الظَّالِمِينَ (107)
Koma ngati zidziwika kuti anthu awiriwa ali ndi mlandu wina, sankhulani anthu ena awiri kuti aime m’malo mwawo, amene ali a chibale a munthu amene ali kufa. Iwo ayenera kulumbira pali Mulungu kuti: “Ife titsimikiza kuti umboni wathu ndi woona kuposa wa anthu awiriwo ndipo kuti ife sitinaperekepo umboni wabodza ndipo ngati ife tinama, ndiye kuti ndife olakwa.”
ذَٰلِكَ أَدْنَىٰ أَن يَأْتُوا بِالشَّهَادَةِ عَلَىٰ وَجْهِهَا أَوْ يَخَافُوا أَن تُرَدَّ أَيْمَانٌ بَعْدَ أَيْمَانِهِمْ ۗ وَاتَّقُوا اللَّهَ وَاسْمَعُوا ۗ وَاللَّهُ لَا يَهْدِي الْقَوْمَ الْفَاسِقِينَ (108)
Imeneyo ndiyo njira yapafupi yoti iwo akhoza kupereka umboni woona weniweni poopa kuti ena akhoza kulumbira pambuyo pakulumbira kwawo. Muopeni Mulungu ndipo mverani ulangizi wake. Mulungu satsogolera anthu ochita zoipa
۞ يَوْمَ يَجْمَعُ اللَّهُ الرُّسُلَ فَيَقُولُ مَاذَا أُجِبْتُمْ ۖ قَالُوا لَا عِلْمَ لَنَا ۖ إِنَّكَ أَنتَ عَلَّامُ الْغُيُوبِ (109)
Patsiku limene Mulungu adzasonkhanitsa Atumwi ake onse ndi kuwafunsa kuti: “Kodi mudayankhidwa bwanji?” Iwo adzati: “Ife sitidziwa. Ndithudi Inu nokha ndiye amene mumadziwa zonse zimene ndi zobisika.”
إِذْ قَالَ اللَّهُ يَا عِيسَى ابْنَ مَرْيَمَ اذْكُرْ نِعْمَتِي عَلَيْكَ وَعَلَىٰ وَالِدَتِكَ إِذْ أَيَّدتُّكَ بِرُوحِ الْقُدُسِ تُكَلِّمُ النَّاسَ فِي الْمَهْدِ وَكَهْلًا ۖ وَإِذْ عَلَّمْتُكَ الْكِتَابَ وَالْحِكْمَةَ وَالتَّوْرَاةَ وَالْإِنجِيلَ ۖ وَإِذْ تَخْلُقُ مِنَ الطِّينِ كَهَيْئَةِ الطَّيْرِ بِإِذْنِي فَتَنفُخُ فِيهَا فَتَكُونُ طَيْرًا بِإِذْنِي ۖ وَتُبْرِئُ الْأَكْمَهَ وَالْأَبْرَصَ بِإِذْنِي ۖ وَإِذْ تُخْرِجُ الْمَوْتَىٰ بِإِذْنِي ۖ وَإِذْ كَفَفْتُ بَنِي إِسْرَائِيلَ عَنكَ إِذْ جِئْتَهُم بِالْبَيِّنَاتِ فَقَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا مِنْهُمْ إِنْ هَٰذَا إِلَّا سِحْرٌ مُّبِينٌ (110)
Pamene Mulungu adzati: “Oh! iwe Yesu, mwana wamwamuna wa Maria! Kumbukira zokoma zanga zimene ndinakhazikitsa pa iwe ndi pa amayi ako; mmene ndidakulimbitsa iwe ndi Mzimu Woyera moti udalankhula kwa anthu pamene unali wakhanda ndiponso utakula msinkhu; mmene ndidakuphunzitsira iwe mawu a Mulungu ndi kukuonjezera luntha labuku la chipangano chakale ndi chipangano chatsopano; mmene ndi chilolezo changa udapanga kuchokera kudothi, chinthu cholingana ndi mbalame ndipo udachiuzira mpweya ndipo ndi chilolezo changa, icho chidasanduka mbalame ya moyo; ndipo mmene ndi chilolezo changa udachiritsa anthu a khungu ndi anthu a makate ndiponso ndi chilolezo changa unali kupereka moyo kwa anthu akufa; mmene ndidakutetezera iwe kwa ana a Israyeli pamene udadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka,” ndipo anthu osakhulupirira amene adali pakati pawo adati: “Ichi sichina chilichonse koma matsenga oonekera poyera.”
وَإِذْ أَوْحَيْتُ إِلَى الْحَوَارِيِّينَ أَنْ آمِنُوا بِي وَبِرَسُولِي قَالُوا آمَنَّا وَاشْهَدْ بِأَنَّنَا مُسْلِمُونَ (111)
Mmene ndidalamulira ophunzira ako kuti akhulupirire mwa Ine ndi mwa Mtumwi wanga, iwo adati: “Ife takhulupirira. Ndipo chitira umboni kuti ife tidzipereka kwathunthu kwa Mulungu.”
إِذْ قَالَ الْحَوَارِيُّونَ يَا عِيسَى ابْنَ مَرْيَمَ هَلْ يَسْتَطِيعُ رَبُّكَ أَن يُنَزِّلَ عَلَيْنَا مَائِدَةً مِّنَ السَّمَاءِ ۖ قَالَ اتَّقُوا اللَّهَ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ (112)
Pamene ophunzira adati: “oh iwe Yesu, mwana wamwamuna wa Maria! Kodi angathe, Ambuye wako, kutitumizira ife kuchokera kumwamba gome lodzala ndi chakudya?” Iye adati: “Muopeni Mulungu ngati inu ndinu okhulupirira.”
قَالُوا نُرِيدُ أَن نَّأْكُلَ مِنْهَا وَتَطْمَئِنَّ قُلُوبُنَا وَنَعْلَمَ أَن قَدْ صَدَقْتَنَا وَنَكُونَ عَلَيْهَا مِنَ الشَّاهِدِينَ (113)
Iwo adati: “Ife tifuna kudya kuchokera pa ilo kuti mitima yathu ikhazikike ndi kudziwa kuti zonse zimene udatiuza ife ndi zoona, ndipo kuti ife tikhoza kukhala mboni wa izo.”
قَالَ عِيسَى ابْنُ مَرْيَمَ اللَّهُمَّ رَبَّنَا أَنزِلْ عَلَيْنَا مَائِدَةً مِّنَ السَّمَاءِ تَكُونُ لَنَا عِيدًا لِّأَوَّلِنَا وَآخِرِنَا وَآيَةً مِّنكَ ۖ وَارْزُقْنَا وَأَنتَ خَيْرُ الرَّازِقِينَ (114)
Yesu, mwana wamwamuna wa Maria, adati: “oh Ambuye wathu! Titumizireni ife kuchokera kumwamba gome lodzala ndi chakudya kuti likhale phwando lathu ndi la iwo amene akudza mtsogolo; ndi chizindikiro chochokera kwa inu. Ndipo tipatseni chakudya. Ndipo Inu ndinu wabwino mwa onse opereka.”
قَالَ اللَّهُ إِنِّي مُنَزِّلُهَا عَلَيْكُمْ ۖ فَمَن يَكْفُرْ بَعْدُ مِنكُمْ فَإِنِّي أُعَذِّبُهُ عَذَابًا لَّا أُعَذِّبُهُ أَحَدًا مِّنَ الْعَالَمِينَ (115)
Mulungu adati: “Ine nditumiza gome kwa inu koma aliyense wa inu amene, ataona izi, sadzakhulupirira ndidzamulanga ndi chilango chimene sindidalangepo wina aliyense wa zolengedwa zanga.”
وَإِذْ قَالَ اللَّهُ يَا عِيسَى ابْنَ مَرْيَمَ أَأَنتَ قُلْتَ لِلنَّاسِ اتَّخِذُونِي وَأُمِّيَ إِلَٰهَيْنِ مِن دُونِ اللَّهِ ۖ قَالَ سُبْحَانَكَ مَا يَكُونُ لِي أَنْ أَقُولَ مَا لَيْسَ لِي بِحَقٍّ ۚ إِن كُنتُ قُلْتُهُ فَقَدْ عَلِمْتَهُ ۚ تَعْلَمُ مَا فِي نَفْسِي وَلَا أَعْلَمُ مَا فِي نَفْسِكَ ۚ إِنَّكَ أَنتَ عَلَّامُ الْغُيُوبِ (116)
Pamene Mulungu adzati: “O! iwe Yesu, mwana wamwamuna wa Maria! Kodi udawauza anthu kuti: Ndipembedzeni ine ndi Amai anga ngati milungu iwiri powonjezera pa Mulungu?” Iye adzayankha: “Ulemerero ukhale kwa Inu! Sikunali koyenera kuti ine ndinene zinthu zimene ndinalibe ulamuliro wonenera. Ngati ndikadanena choncho, ndithudi, inu mukadadziwa. Inu mumadziwa zimene zili mumtima mwanga pamene ine sindidziwa zimene zili mu mtima mwanu. Inu nokha mumadziwa zinthu zobisika.”
مَا قُلْتُ لَهُمْ إِلَّا مَا أَمَرْتَنِي بِهِ أَنِ اعْبُدُوا اللَّهَ رَبِّي وَرَبَّكُمْ ۚ وَكُنتُ عَلَيْهِمْ شَهِيدًا مَّا دُمْتُ فِيهِمْ ۖ فَلَمَّا تَوَفَّيْتَنِي كُنتَ أَنتَ الرَّقِيبَ عَلَيْهِمْ ۚ وَأَنتَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ شَهِيدٌ (117)
“Ine sindinawauze china chilichonse kupatula zimene Inu mudandilamula kuti ndinene zoti. ‘Pembedzani Mulungu, Ambuye wanga, amene ali Ambuye wanu.’ Ine ndidali mboni yawo pamene ndidali kukhala pakati pawo koma pamene Inu mudanditenga ine kudza kwa Inu, Inuyo ndiye amene mudali kuwayang’anira ndipo Inu ndinu mboni pa zinthu zonse.”
إِن تُعَذِّبْهُمْ فَإِنَّهُمْ عِبَادُكَ ۖ وَإِن تَغْفِرْ لَهُمْ فَإِنَّكَ أَنتَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (118)
“Ngati muwalanga, iwo ndi akapolo anu, koma ngati muwakhululukira, ndithudi, Inu ndinu wa mphamvu ndi Mwini nzeru.”
قَالَ اللَّهُ هَٰذَا يَوْمُ يَنفَعُ الصَّادِقِينَ صِدْقُهُمْ ۚ لَهُمْ جَنَّاتٌ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا أَبَدًا ۚ رَّضِيَ اللَّهُ عَنْهُمْ وَرَضُوا عَنْهُ ۚ ذَٰلِكَ الْفَوْزُ الْعَظِيمُ (119)
Ndipo Mulungu adzati: “Ili ndilo tsiku limene chilungamo chawo chidzawapindulira anthu olungama.” Iwo adzakhala nthawi zonse m’minda yothiriridwa ndi mitsinje yamadzi yoyenda pansi pake. Iwo adzakhalamo mpaka kalekale. Mulungu ndi osangalala ndi iwo ndipo iwo ndi Iye. Kumeneku ndiko kupambana kwakukulu
لِلَّهِ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَمَا فِيهِنَّ ۚ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (120)
Mulungu ndiye mwini wa Ufumu wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo ndipo Iye ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas