×

Ndithudi Mulungu adalandira lonjezo la ana a Israyeli ndipo Ife tidadzutsa pakati 5:12 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah Al-Ma’idah ⮕ (5:12) ayat 12 in Chichewa

5:12 Surah Al-Ma’idah ayat 12 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ma’idah ayat 12 - المَائدة - Page - Juz 6

﴿۞ وَلَقَدۡ أَخَذَ ٱللَّهُ مِيثَٰقَ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَبَعَثۡنَا مِنۡهُمُ ٱثۡنَيۡ عَشَرَ نَقِيبٗاۖ وَقَالَ ٱللَّهُ إِنِّي مَعَكُمۡۖ لَئِنۡ أَقَمۡتُمُ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتَيۡتُمُ ٱلزَّكَوٰةَ وَءَامَنتُم بِرُسُلِي وَعَزَّرۡتُمُوهُمۡ وَأَقۡرَضۡتُمُ ٱللَّهَ قَرۡضًا حَسَنٗا لَّأُكَفِّرَنَّ عَنكُمۡ سَيِّـَٔاتِكُمۡ وَلَأُدۡخِلَنَّكُمۡ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۚ فَمَن كَفَرَ بَعۡدَ ذَٰلِكَ مِنكُمۡ فَقَدۡ ضَلَّ سَوَآءَ ٱلسَّبِيلِ ﴾
[المَائدة: 12]

Ndithudi Mulungu adalandira lonjezo la ana a Israyeli ndipo Ife tidadzutsa pakati pawo atsogoleri khumi ndi awiri. Ndipo Mulungu adati: “Ine, ndithudi, ndili pamodzi ndi inu ngati inu mupemphera moyenera, mupereka chopereka chothandiza anthu osauka ndipo mukhulupirira mwa Atumwi anga ndipo muwathandiza ndiponso mukongoza Mulungu ngongole yabwino. Ndithudi Ine ndidzakukhululukirani machimo anu ndi kukulowetsani ku minda yothiriridwa ndi madzi ya m’mitsinje. Koma ngati wina wa inu, pambuyo pake sakhulupilira, Iye wasochera ku njira yoyenera.”

❮ Previous Next ❯

ترجمة: ولقد أخذ الله ميثاق بني إسرائيل وبعثنا منهم اثني عشر نقيبا وقال, باللغة نيانجا

﴿ولقد أخذ الله ميثاق بني إسرائيل وبعثنا منهم اثني عشر نقيبا وقال﴾ [المَائدة: 12]

Khaled Ibrahim Betala
“Ndipo ndithudi, Allah adamanga pangano ndi ana a Israyeli, ndipo tidawaikira Akuluakulu khumi ndi awiri mwa iwo. Ndipo Allah adati: “Ndithudi Ine ndili pamodzi ndi inu, ngati mupemphera Swala ndikupereka chopereka, ndikukhulupirira atumiki Anga, ndi kuwalemekeza ndi kumkongoza Allah Ngongole yabwino, ndithudi ndikufafanizirani zoipa zanu, ndikudzakulowetsani m’Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje. Koma amene akane mwa inu pambuyo pa (chipangano) ichi, ndithu wasochera njira yowongoka.”
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek