Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ma’idah ayat 5 - المَائدة - Page - Juz 6
﴿ٱلۡيَوۡمَ أُحِلَّ لَكُمُ ٱلطَّيِّبَٰتُۖ وَطَعَامُ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ حِلّٞ لَّكُمۡ وَطَعَامُكُمۡ حِلّٞ لَّهُمۡۖ وَٱلۡمُحۡصَنَٰتُ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ وَٱلۡمُحۡصَنَٰتُ مِنَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ مِن قَبۡلِكُمۡ إِذَآ ءَاتَيۡتُمُوهُنَّ أُجُورَهُنَّ مُحۡصِنِينَ غَيۡرَ مُسَٰفِحِينَ وَلَا مُتَّخِذِيٓ أَخۡدَانٖۗ وَمَن يَكۡفُرۡ بِٱلۡإِيمَٰنِ فَقَدۡ حَبِطَ عَمَلُهُۥ وَهُوَ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ مِنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ ﴾
[المَائدة: 5]
﴿اليوم أحل لكم الطيبات وطعام الذين أوتوا الكتاب حل لكم وطعامكم حل﴾ [المَائدة: 5]
Khaled Ibrahim Betala “Lero mwaloledwa zonse zabwino ndi chakudya cha omwe adapatsidwa buku nchololedwa kwa inu, ndiponso chakudya chanu nchololedwa kwa iwo, ndipo (mukuloledwa kuwakwatira) akazi abwino a mwa okhulupirira ndi akazi abwino a mwa omwe adapatsidwa ma buku kale, ngati mwawapatsa chiwongo chawo m’njira yomanga nawo ukwati, osati mochita nao chiwerewere, osatinso mochita nao zibwenzi. Ndipo amene akane kukhulupirira, ndiye kuti yaonongeka ntchito yake; ndipo iye tsiku lachimaliziro adzakhala mwa oluza (otaiyika) |