Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ma’idah ayat 6 - المَائدة - Page - Juz 6
﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا قُمۡتُمۡ إِلَى ٱلصَّلَوٰةِ فَٱغۡسِلُواْ وُجُوهَكُمۡ وَأَيۡدِيَكُمۡ إِلَى ٱلۡمَرَافِقِ وَٱمۡسَحُواْ بِرُءُوسِكُمۡ وَأَرۡجُلَكُمۡ إِلَى ٱلۡكَعۡبَيۡنِۚ وَإِن كُنتُمۡ جُنُبٗا فَٱطَّهَّرُواْۚ وَإِن كُنتُم مَّرۡضَىٰٓ أَوۡ عَلَىٰ سَفَرٍ أَوۡ جَآءَ أَحَدٞ مِّنكُم مِّنَ ٱلۡغَآئِطِ أَوۡ لَٰمَسۡتُمُ ٱلنِّسَآءَ فَلَمۡ تَجِدُواْ مَآءٗ فَتَيَمَّمُواْ صَعِيدٗا طَيِّبٗا فَٱمۡسَحُواْ بِوُجُوهِكُمۡ وَأَيۡدِيكُم مِّنۡهُۚ مَا يُرِيدُ ٱللَّهُ لِيَجۡعَلَ عَلَيۡكُم مِّنۡ حَرَجٖ وَلَٰكِن يُرِيدُ لِيُطَهِّرَكُمۡ وَلِيُتِمَّ نِعۡمَتَهُۥ عَلَيۡكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ ﴾
[المَائدة: 6]
﴿ياأيها الذين آمنوا إذا قمتم إلى الصلاة فاغسلوا وجوهكم وأيديكم إلى المرافق﴾ [المَائدة: 6]
Khaled Ibrahim Betala ““E inu amene mwakhulupirira! Pamene mwaimilira kuti mukaswali, sambitsani nkhope zanu, ndi manja anu mpaka mmagongono; ndipo pakani madzi pa mitu panu ndi kusambitsa mapazi anu mpaka mu akakolo. Ngati muli ndi janaba dziyeretseni (sambani thupi lonse); ndipo ngati muli odwala kapena muli paulendo, kapena mmodzi wanu wachokera kokadzithandiza kapenanso mwakhalira limodzi ndi mkazi, ndiye simudapeze madzi, chitani Tayammamu ndi dothi labwino ndipo pakani ku nkhope zanu ndi mmanja mwanu. Allah sakufuna kukuvutitsani, koma akufuna kukuyeretsani ndi kukwaniritsa chisomo chake pa inu kuti muthokoze |