Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ma’idah ayat 64 - المَائدة - Page - Juz 6
﴿وَقَالَتِ ٱلۡيَهُودُ يَدُ ٱللَّهِ مَغۡلُولَةٌۚ غُلَّتۡ أَيۡدِيهِمۡ وَلُعِنُواْ بِمَا قَالُواْۘ بَلۡ يَدَاهُ مَبۡسُوطَتَانِ يُنفِقُ كَيۡفَ يَشَآءُۚ وَلَيَزِيدَنَّ كَثِيرٗا مِّنۡهُم مَّآ أُنزِلَ إِلَيۡكَ مِن رَّبِّكَ طُغۡيَٰنٗا وَكُفۡرٗاۚ وَأَلۡقَيۡنَا بَيۡنَهُمُ ٱلۡعَدَٰوَةَ وَٱلۡبَغۡضَآءَ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ كُلَّمَآ أَوۡقَدُواْ نَارٗا لِّلۡحَرۡبِ أَطۡفَأَهَا ٱللَّهُۚ وَيَسۡعَوۡنَ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَسَادٗاۚ وَٱللَّهُ لَا يُحِبُّ ٱلۡمُفۡسِدِينَ ﴾
[المَائدة: 64]
﴿وقالت اليهود يد الله مغلولة غلت أيديهم ولعنوا بما قالوا بل يداه﴾ [المَائدة: 64]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo Ayuda adati: “Dzanja la Allah lafumbatika (sitikupeza chuma ngati kale). (Koma sichoncho); manja awo ndiwo afumbatika (posachita zabwino ndi kuchenjelera anthu). Ndipo atembeleredwa chifukwa cha zomwe anena. Koma manja ake (Allah) ngotambasuka. Amapatsa mmene wafunira. Ndithudi, zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako, ziwaonjezera ambiri a iwo (Ayuda) kulumpha malire ndi kusakhulupirira. Ndipo taika chidani ndi kusakondana pakati pawo mpaka tsiku la chimariziro. Nthawi iliyonse akayatsa moto wa nkhondo, Allah amauzimitsa. Ndipo amayesetsa kudzetsa chisokonezo pa dziko, (koma Allah sawathandiza). Ndipo Allah sakonda owononga |