Quran with Chichewa translation - Surah Al-hadid ayat 25 - الحدِيد - Page - Juz 27
﴿لَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا رُسُلَنَا بِٱلۡبَيِّنَٰتِ وَأَنزَلۡنَا مَعَهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡمِيزَانَ لِيَقُومَ ٱلنَّاسُ بِٱلۡقِسۡطِۖ وَأَنزَلۡنَا ٱلۡحَدِيدَ فِيهِ بَأۡسٞ شَدِيدٞ وَمَنَٰفِعُ لِلنَّاسِ وَلِيَعۡلَمَ ٱللَّهُ مَن يَنصُرُهُۥ وَرُسُلَهُۥ بِٱلۡغَيۡبِۚ إِنَّ ٱللَّهَ قَوِيٌّ عَزِيزٞ ﴾
[الحدِيد: 25]
﴿لقد أرسلنا رسلنا بالبينات وأنـزلنا معهم الكتاب والميزان ليقوم الناس بالقسط وأنـزلنا﴾ [الحدِيد: 25]
Khaled Ibrahim Betala “Ndithu tidatuma atumiki Athu pamodzi ndi zozizwitsa. Ndipo tidavumbulutsa pamodzi ndi iwo mabuku ndi muyeso wa choonadi kuti anthu achite chilungamo. Ndipo tidalenga chitsulo momwe muli mphamvu zambiri (pa nkhondo) ndiponso chithandizo kwa anthu (akakhala pa mtendere ndi kupindula nacho pochita zowathandiza pa moyo wawo). Ndi kuti Allah amuonetsere poyera, amene angachiteteze (chipembedzo Chake) ndi atumiki Ake (kupyolera m’chitsulocho) pomwe Iye sakumuona. Ndithu Allah Ngwamphamvu (pa chilichonse) Ngopambana |