×

سورة الحديد باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة الحديد

ترجمة معاني سورة الحديد باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة الحديد مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Hadid in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة الحديد باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 29 - رقم السورة 57 - الصفحة 537.

بسم الله الرحمن الرحيم

سَبَّحَ لِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (1)
Chilichonse chimwe chili kumwamba ndi padziko lapansi chimalemekeza Mulungu. Iye ndiye Mwini mphamvu, Mwini nzeru
لَهُ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ يُحْيِي وَيُمِيتُ ۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (2)
Wake ndi Ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi. Ndiye amene amapereka moyo ndi imfa ndipo ali ndi mphamvu pa zinthu zonse
هُوَ الْأَوَّلُ وَالْآخِرُ وَالظَّاهِرُ وَالْبَاطِنُ ۖ وَهُوَ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (3)
Iye ndi woyamba ndi womaliza, wapamwamba mwamba ndi wapafupi. Ndipo Iye amadziwa zinthu zonse
هُوَ الَّذِي خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ فِي سِتَّةِ أَيَّامٍ ثُمَّ اسْتَوَىٰ عَلَى الْعَرْشِ ۚ يَعْلَمُ مَا يَلِجُ فِي الْأَرْضِ وَمَا يَخْرُجُ مِنْهَا وَمَا يَنزِلُ مِنَ السَّمَاءِ وَمَا يَعْرُجُ فِيهَا ۖ وَهُوَ مَعَكُمْ أَيْنَ مَا كُنتُمْ ۚ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌ (4)
Ndiye adalenga kumwamba ndi dziko lapansi m’masiku asanu ndi limodzi ndipo adabuka pa mwamba pa mpando wake wa Chifumu. Iye amadziwa chilichonse chimene chimalowa m’nthaka ndi chilichonse chimene chimatuluka mu iyo, zonse zimene zimadza pansi kuchokera kumwamba ndi zonse zimene zimakwera kumwamba. Ndipo Iye ali nanu kulikonse kumene mungakhale. Ndipo Mulungu amaona zonse zimene mumachita
لَّهُ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ وَإِلَى اللَّهِ تُرْجَعُ الْأُمُورُ (5)
Wake ndi Ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo ndi kwa Iye kumene zonse zimabwerera
يُولِجُ اللَّيْلَ فِي النَّهَارِ وَيُولِجُ النَّهَارَ فِي اللَّيْلِ ۚ وَهُوَ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (6)
Iye amapanga usiku kulumikizana ndi usana ndi kupanga usana kulumikizana ndi usiku. Iye amadziwa zinsinsi zonse zili m’mitima
آمِنُوا بِاللَّهِ وَرَسُولِهِ وَأَنفِقُوا مِمَّا جَعَلَكُم مُّسْتَخْلَفِينَ فِيهِ ۖ فَالَّذِينَ آمَنُوا مِنكُمْ وَأَنفَقُوا لَهُمْ أَجْرٌ كَبِيرٌ (7)
Khulupirirani mwa Mulungu ndi Mtumwi wake. Perekani zopereka zaulere kuchokera ku zinthu zimene Mulungu wakupatsani kuti zikhale zanu. Iwo a inu amene akhulupilira ndipo apereka chaulere, yawo idzakhala mphotho yaikulu
وَمَا لَكُمْ لَا تُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ ۙ وَالرَّسُولُ يَدْعُوكُمْ لِتُؤْمِنُوا بِرَبِّكُمْ وَقَدْ أَخَذَ مِيثَاقَكُمْ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ (8)
Kodi ndi chifukwa chiyani kuti inu simukhulupirira mwa Mulungu? Pamene Mtumwi ali kukuitanani kuti mukhulupirire mwa Ambuye wanu ndipo Iye, ndithudi, walandira lonjezo lanu ngati inu ndinu anthu okhulupirira
هُوَ الَّذِي يُنَزِّلُ عَلَىٰ عَبْدِهِ آيَاتٍ بَيِّنَاتٍ لِّيُخْرِجَكُم مِّنَ الظُّلُمَاتِ إِلَى النُّورِ ۚ وَإِنَّ اللَّهَ بِكُمْ لَرَءُوفٌ رَّحِيمٌ (9)
Ndiye amene amatumiza kwa kapolo wake zizindikiro zooneka kuti akhoza kukutsogolerani inu kuchoka ku mdima waukulu kupita kowala. Ndipo, ndithudi, Mulungu, kwa inuyo, ndi wachifundo ndi wachisoni
وَمَا لَكُمْ أَلَّا تُنفِقُوا فِي سَبِيلِ اللَّهِ وَلِلَّهِ مِيرَاثُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ لَا يَسْتَوِي مِنكُم مَّنْ أَنفَقَ مِن قَبْلِ الْفَتْحِ وَقَاتَلَ ۚ أُولَٰئِكَ أَعْظَمُ دَرَجَةً مِّنَ الَّذِينَ أَنفَقُوا مِن بَعْدُ وَقَاتَلُوا ۚ وَكُلًّا وَعَدَ اللَّهُ الْحُسْنَىٰ ۚ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرٌ (10)
Kodi ndi chifukwa chiyani inu simufuna kupereka m’njira ya Mulungu? Mulungu ndiye Mwini wa zonse zili kumwamba ndi padziko lapansi. Palibe ofanana, pakati panu, ndi iwo amene amapereka chaulere ndipo adamenya nawo nkhondo poyamba kupambana kusanadze. Amenewa ndi a pamwamba kuposa iwo amene adapereka chaulere ndi kumenya nkhondo pambuyo pake. Koma kwa onsewa, Mulungu walonjeza mphotho yokoma. Ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita
مَّن ذَا الَّذِي يُقْرِضُ اللَّهَ قَرْضًا حَسَنًا فَيُضَاعِفَهُ لَهُ وَلَهُ أَجْرٌ كَرِيمٌ (11)
Kodi ndani amene adzakongoza Mulungu ngongole yabwino kuti Iye aipindulitse ndipo kuti iye adzakhale ndi mphotho ina yapamwamba
يَوْمَ تَرَى الْمُؤْمِنِينَ وَالْمُؤْمِنَاتِ يَسْعَىٰ نُورُهُم بَيْنَ أَيْدِيهِمْ وَبِأَيْمَانِهِم بُشْرَاكُمُ الْيَوْمَ جَنَّاتٌ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا ۚ ذَٰلِكَ هُوَ الْفَوْزُ الْعَظِيمُ (12)
Patsiku limeneli inu mudzaona amuna okhulupirira ndi akazi okhulupirira, nyali zawo zili kuyaka patsogolo pawo ndi kudzanja lawo lamanja, kulonjerana kwawo kudzakhala nkhani yabwino kwa inu lero lino! Minda imene pansi pake pamayenda madzi mudzakhala m’menemo mpaka kalekale. Kumeneko ndiko kupambana kwenikweni
يَوْمَ يَقُولُ الْمُنَافِقُونَ وَالْمُنَافِقَاتُ لِلَّذِينَ آمَنُوا انظُرُونَا نَقْتَبِسْ مِن نُّورِكُمْ قِيلَ ارْجِعُوا وَرَاءَكُمْ فَالْتَمِسُوا نُورًا فَضُرِبَ بَيْنَهُم بِسُورٍ لَّهُ بَابٌ بَاطِنُهُ فِيهِ الرَّحْمَةُ وَظَاهِرُهُ مِن قِبَلِهِ الْعَذَابُ (13)
Patsiku limene amuna a chinyengo ndi akazi a chinyengo adzanena kwa iwo okhulupirira:“Tidikirirenikutitikhozakulandirachilangali kuchokera ku muuni wanu.” Koma kudzanenedwa kuti: “Bwererani m’mbuyo kuti mukafune muuni wanu. Ndipo chipupa chidzakhazikitsidwa pakati pawo chokhala ndi khomo. Mbali ina ya chipupachi kudzakhala chisomo pamene mbali ina kudzakhala chilango.”
يُنَادُونَهُمْ أَلَمْ نَكُن مَّعَكُمْ ۖ قَالُوا بَلَىٰ وَلَٰكِنَّكُمْ فَتَنتُمْ أَنفُسَكُمْ وَتَرَبَّصْتُمْ وَارْتَبْتُمْ وَغَرَّتْكُمُ الْأَمَانِيُّ حَتَّىٰ جَاءَ أَمْرُ اللَّهِ وَغَرَّكُم بِاللَّهِ الْغَرُورُ (14)
Iwo adzalira kwa iwo. “Kodi inu sitinali kukhalira limodzi?” Okhulupilira adzayankha kuti: “Zoonadi koma inu mudadzisocheretsa nokha. Inu mudanyengedwa, mudakayikira ndipo zilakolako zanu zidakunyengani inu mpaka pamene chilango cha Mulungu chinachitika. Ndipo wonyenga adakunyengani inu pa nkhani zokhudza Mulungu.”
فَالْيَوْمَ لَا يُؤْخَذُ مِنكُمْ فِدْيَةٌ وَلَا مِنَ الَّذِينَ كَفَرُوا ۚ مَأْوَاكُمُ النَّارُ ۖ هِيَ مَوْلَاكُمْ ۖ وَبِئْسَ الْمَصِيرُ (15)
Motero lero palibe chiphuphu chimene chidzalandiridwa kuchokera kwa inu kapena iwo amene adakana Mulungu. Malo anu okhala ndi kumoto, amenewo ndiwo malo okhawo amene mudzalandiridwako ndipo ndi malo oipitsitsa kukhalamo
۞ أَلَمْ يَأْنِ لِلَّذِينَ آمَنُوا أَن تَخْشَعَ قُلُوبُهُمْ لِذِكْرِ اللَّهِ وَمَا نَزَلَ مِنَ الْحَقِّ وَلَا يَكُونُوا كَالَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ مِن قَبْلُ فَطَالَ عَلَيْهِمُ الْأَمَدُ فَقَسَتْ قُلُوبُهُمْ ۖ وَكَثِيرٌ مِّنْهُمْ فَاسِقُونَ (16)
Kodi nthawi siinakwane yoti okhulupirira enieni apereke mitima yawo modzichepetsa ndipo kuti azikumbukira Mulungu ndi choonadi chimene chavumbulutsidwa kwa iwo ndipo kuti asakhale ngati iwo amene adapatsidwa Buku nthawi ya kale? Koma patapita nthawi, mitima yawo idalimba. Ndipo ambiri a iwo ndi ophwanya malamulo
اعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ يُحْيِي الْأَرْضَ بَعْدَ مَوْتِهَا ۚ قَدْ بَيَّنَّا لَكُمُ الْآيَاتِ لَعَلَّكُمْ تَعْقِلُونَ (17)
Dziwani kuti Mulungu amapereka moyo ku nthaka ikafa. Ndithudi taonetsa chivumbulutso chathu poyera kwa inu kuti mukhoza kuzindikira
إِنَّ الْمُصَّدِّقِينَ وَالْمُصَّدِّقَاتِ وَأَقْرَضُوا اللَّهَ قَرْضًا حَسَنًا يُضَاعَفُ لَهُمْ وَلَهُمْ أَجْرٌ كَرِيمٌ (18)
Ndithudi iwo amene amapereka chopereka chaulere, amuna kapena akazi, iwo amasunga gawo lawo kwa Mulungu lomwe lidzaonjezeredwa mopitiriza muyeso ndipo adzakhala ndi mphotho yolemekezeka
وَالَّذِينَ آمَنُوا بِاللَّهِ وَرُسُلِهِ أُولَٰئِكَ هُمُ الصِّدِّيقُونَ ۖ وَالشُّهَدَاءُ عِندَ رَبِّهِمْ لَهُمْ أَجْرُهُمْ وَنُورُهُمْ ۖ وَالَّذِينَ كَفَرُوا وَكَذَّبُوا بِآيَاتِنَا أُولَٰئِكَ أَصْحَابُ الْجَحِيمِ (19)
Ndipo iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi mwa Mtumwi wake, iwo ndi olungama ndi okhulupirira pamaso pa Ambuye wawo. Iwo adzalandira mphotho yawo pamodzi ndi muuni. Ndipo iwo amene sakhulupirira ndipo amakana chivumbulutso chathu, amenewa ndiwo a ku moto wa ku Gahena
اعْلَمُوا أَنَّمَا الْحَيَاةُ الدُّنْيَا لَعِبٌ وَلَهْوٌ وَزِينَةٌ وَتَفَاخُرٌ بَيْنَكُمْ وَتَكَاثُرٌ فِي الْأَمْوَالِ وَالْأَوْلَادِ ۖ كَمَثَلِ غَيْثٍ أَعْجَبَ الْكُفَّارَ نَبَاتُهُ ثُمَّ يَهِيجُ فَتَرَاهُ مُصْفَرًّا ثُمَّ يَكُونُ حُطَامًا ۖ وَفِي الْآخِرَةِ عَذَابٌ شَدِيدٌ وَمَغْفِرَةٌ مِّنَ اللَّهِ وَرِضْوَانٌ ۚ وَمَا الْحَيَاةُ الدُّنْيَا إِلَّا مَتَاعُ الْغُرُورِ (20)
Dziwani kuti moyo wa padziko lino lapansi ndi masewera ndi wotailako nthawi, chionetsero ndi kunyada ndi mpikisano pakati pa wina ndi mnzake wofuna chuma ndi ana. Fanizo lake lili ngati mvula ndi zomera zimene zimadza chifukwa cha zimene zimabweretsa chisangalalo kwa ozilima. Pasanapite nthawi izo zimafota ndi kuoneka za chikasu. Ndipo zimauma ndi kugwa pansi. Koma m’moyo umene uli kudza, kuli chilango chowawa kwa anthu ogona m’machimo ndi chikhululukiro chochokera kwa Mulungu ndiponso chisangalalo chake kwa iwo amene amadzipereka kwa Mulungu. Kodi moyo wa padziko lino lapansi ndi chiyani kupatula chinyengo chabe
سَابِقُوا إِلَىٰ مَغْفِرَةٍ مِّن رَّبِّكُمْ وَجَنَّةٍ عَرْضُهَا كَعَرْضِ السَّمَاءِ وَالْأَرْضِ أُعِدَّتْ لِلَّذِينَ آمَنُوا بِاللَّهِ وَرُسُلِهِ ۚ ذَٰلِكَ فَضْلُ اللَّهِ يُؤْتِيهِ مَن يَشَاءُ ۚ وَاللَّهُ ذُو الْفَضْلِ الْعَظِيمِ (21)
Kotero fulumirani kupeza chikhululukiro cha Mulungu ndi munda wa Paradiso umene kutalika kwake kuli ngati kukula kwa kumwamba ndi dziko lapansi umene udakonzedwera iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Atumwi ake. Chimenechi ndicho chisomo cha Mulungu chimene amapereka kwa amene Iye wamufuna. Mulungu ndi Ambuye wa chisomo chosatha
مَا أَصَابَ مِن مُّصِيبَةٍ فِي الْأَرْضِ وَلَا فِي أَنفُسِكُمْ إِلَّا فِي كِتَابٍ مِّن قَبْلِ أَن نَّبْرَأَهَا ۚ إِنَّ ذَٰلِكَ عَلَى اللَّهِ يَسِيرٌ (22)
Palibe vuto limene limadza padziko kapena pa inu limene silinakhazikitsidwe kale Ife tisanalibweretse. Ndithudi chimenechi ndi chosavuta kwa Mulungu
لِّكَيْلَا تَأْسَوْا عَلَىٰ مَا فَاتَكُمْ وَلَا تَفْرَحُوا بِمَا آتَاكُمْ ۗ وَاللَّهُ لَا يُحِبُّ كُلَّ مُخْتَالٍ فَخُورٍ (23)
Kuti inu musakhumudwe chifukwa cha zinthu zabwino zimene simudazipeze kapena kunyada chifukwa cha zokoma zimene zaperekedwa kwa inu. Mulungu sakonda anthu odzikundikira
الَّذِينَ يَبْخَلُونَ وَيَأْمُرُونَ النَّاسَ بِالْبُخْلِ ۗ وَمَن يَتَوَلَّ فَإِنَّ اللَّهَ هُوَ الْغَنِيُّ الْحَمِيدُ (24)
Ndiponso anthu a umbombo amauza anzawo kuti nawonso azikhala a umbombo. Ngati wina abwerera m’mbuyo kuchokera ku njira ya Mulungu, ndithudi, Mulungu sasowa chilichonse ndipo ndi wolemekezeka
لَقَدْ أَرْسَلْنَا رُسُلَنَا بِالْبَيِّنَاتِ وَأَنزَلْنَا مَعَهُمُ الْكِتَابَ وَالْمِيزَانَ لِيَقُومَ النَّاسُ بِالْقِسْطِ ۖ وَأَنزَلْنَا الْحَدِيدَ فِيهِ بَأْسٌ شَدِيدٌ وَمَنَافِعُ لِلنَّاسِ وَلِيَعْلَمَ اللَّهُ مَن يَنصُرُهُ وَرُسُلَهُ بِالْغَيْبِ ۚ إِنَّ اللَّهَ قَوِيٌّ عَزِيزٌ (25)
Ndithudi tidatumiza kale Atumwi athu ndi zizindikiro zooneka ndipo tidatumiza pamodzi ndi iwo Buku ndi muyeso kuti anthu akhoza kukhala ndi makhalidwe abwino. Ndipo Ife tidapanga chitsulo chimene m’kati mwake muli mphamvu ndi zinthu zambiri zabwino kwa anthu. Kuti Mulungu akhoza kuyesa iwo amene amamuthandiza Iye ndi Mtumwi wake mwamseri. Ndithudi Mulungu ndi wolimba ndi wamphamvu
وَلَقَدْ أَرْسَلْنَا نُوحًا وَإِبْرَاهِيمَ وَجَعَلْنَا فِي ذُرِّيَّتِهِمَا النُّبُوَّةَ وَالْكِتَابَ ۖ فَمِنْهُم مُّهْتَدٍ ۖ وَكَثِيرٌ مِّنْهُمْ فَاسِقُونَ (26)
Ndithudi Ife tidatumiza Nowa ndi Abrahamu ndipo tidapereka kwa ana awo mphatso ya Utumwi ndi Buku ndipo ena pakati pawo ndi otsogozedwa bwino koma ambiri ndi ophwanya malamulo
ثُمَّ قَفَّيْنَا عَلَىٰ آثَارِهِم بِرُسُلِنَا وَقَفَّيْنَا بِعِيسَى ابْنِ مَرْيَمَ وَآتَيْنَاهُ الْإِنجِيلَ وَجَعَلْنَا فِي قُلُوبِ الَّذِينَ اتَّبَعُوهُ رَأْفَةً وَرَحْمَةً وَرَهْبَانِيَّةً ابْتَدَعُوهَا مَا كَتَبْنَاهَا عَلَيْهِمْ إِلَّا ابْتِغَاءَ رِضْوَانِ اللَّهِ فَمَا رَعَوْهَا حَقَّ رِعَايَتِهَا ۖ فَآتَيْنَا الَّذِينَ آمَنُوا مِنْهُمْ أَجْرَهُمْ ۖ وَكَثِيرٌ مِّنْهُمْ فَاسِقُونَ (27)
Ndipo tidawapanga Atumwi athu kuti atsatire m’mapazi mwawo; Ndipo tidatumiza Yesu, mwana wa Maria, pambuyo pake ndipo tidamupatsa Uthenga wabwino. Ndipo tidaika m’mitima mwa iwo amene adali kumutsatira iye kukoma mtima ndi chisoni. Ukakhala unsembe iwo adapeka okha, chifukwa Ife sitidawalamulire kuti akhazikitse kupatula kuti azifunafuna chisangalalo cha Mulungu koma iwo sadazilabadire ayi. Kotero tidawapatsa mphotho iwo amene adakhulupirira koma ambiri a iwo ndi oswa malamulo
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا اتَّقُوا اللَّهَ وَآمِنُوا بِرَسُولِهِ يُؤْتِكُمْ كِفْلَيْنِ مِن رَّحْمَتِهِ وَيَجْعَل لَّكُمْ نُورًا تَمْشُونَ بِهِ وَيَغْفِرْ لَكُمْ ۚ وَاللَّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (28)
oh inu anthu okhulupirira! Samalani udindo wanu kwa Mulungu ndipo mukhulupilire mwa Mtumwi wake. Iye adzakupatsani magawo awiri a chisomo chake ndikukonzerani muuni umene muzidzayenda nawo ndi kukukhululukirani machimo anu. Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha
لِّئَلَّا يَعْلَمَ أَهْلُ الْكِتَابِ أَلَّا يَقْدِرُونَ عَلَىٰ شَيْءٍ مِّن فَضْلِ اللَّهِ ۙ وَأَنَّ الْفَضْلَ بِيَدِ اللَّهِ يُؤْتِيهِ مَن يَشَاءُ ۚ وَاللَّهُ ذُو الْفَضْلِ الْعَظِيمِ (29)
Kuti anthu a m’Buku adziwe kuti iwo alibe mphamvu ina iliyonse pa chisomo cha Mulungu ndipo kuti chisomo chake chili m’manja mwake mokha ndipo amachipereka kwa aliyense amene Iye wamufuna. Mulungu ndiye Mwini mphatso zosatha
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس