Quran with Chichewa translation - Surah Al-Mujadilah ayat 22 - المُجَادلة - Page - Juz 28
﴿لَّا تَجِدُ قَوۡمٗا يُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِ يُوَآدُّونَ مَنۡ حَآدَّ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ وَلَوۡ كَانُوٓاْ ءَابَآءَهُمۡ أَوۡ أَبۡنَآءَهُمۡ أَوۡ إِخۡوَٰنَهُمۡ أَوۡ عَشِيرَتَهُمۡۚ أُوْلَٰٓئِكَ كَتَبَ فِي قُلُوبِهِمُ ٱلۡإِيمَٰنَ وَأَيَّدَهُم بِرُوحٖ مِّنۡهُۖ وَيُدۡخِلُهُمۡ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَاۚ رَضِيَ ٱللَّهُ عَنۡهُمۡ وَرَضُواْ عَنۡهُۚ أُوْلَٰٓئِكَ حِزۡبُ ٱللَّهِۚ أَلَآ إِنَّ حِزۡبَ ٱللَّهِ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ ﴾
[المُجَادلة: 22]
﴿لا تجد قوما يؤمنون بالله واليوم الآخر يوادون من حاد الله ورسوله﴾ [المُجَادلة: 22]
Khaled Ibrahim Betala “Supeza anthu okhulupirira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro akukonda amene akutsutsana ndi Allah ndi Mthenga Wake, ngakhale atakhala atate awo, ana awo abale awo ndi akumtundu wawo; kwa iwo (Allah) wazika chikhulupiliro (champhamvu) m’mitima mwawo, ndipo wawalimbikitsa ndi mphamvu zochokera kwa Iye. Ndipo adzawalowetsa m’minda yomwe pansi pake pakuyenda mitsinje; adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Allah adzakondwera nawo ndipo (iwonso) adzakondwera Naye. Iwowa ndi chipani cha Allah. Dziwani kuti chipani cha Allah ndichopambana |