قَدْ سَمِعَ اللَّهُ قَوْلَ الَّتِي تُجَادِلُكَ فِي زَوْجِهَا وَتَشْتَكِي إِلَى اللَّهِ وَاللَّهُ يَسْمَعُ تَحَاوُرَكُمَا ۚ إِنَّ اللَّهَ سَمِيعٌ بَصِيرٌ (1) Ndithudi Mulungu wamva mau a mkazi amene ali kutsutsana ndi iwe pa nkhani ya mwamuna wake ndipo iye wapereka madandaulo ake kwa Mulungu. Ndipo Mulungu wamva kukangana kwanu chifukwa Iye amamva ndiponso amaona chili chonse |
الَّذِينَ يُظَاهِرُونَ مِنكُم مِّن نِّسَائِهِم مَّا هُنَّ أُمَّهَاتِهِمْ ۖ إِنْ أُمَّهَاتُهُمْ إِلَّا اللَّائِي وَلَدْنَهُمْ ۚ وَإِنَّهُمْ لَيَقُولُونَ مُنكَرًا مِّنَ الْقَوْلِ وَزُورًا ۚ وَإِنَّ اللَّهَ لَعَفُوٌّ غَفُورٌ (2) Iwo amene ali pakati panu ndipo amasudzula akazi awo ponena kuti: “Iwe uli ngati msana wa Amai anga.” Iwo sangakhale Amai awo ai. Palibe amene angakhale amayi awo, kupatula okhawo amene anawabara. Ndithudi iwo amalankhula mau oipa ndi bodza. Ndithudi Mulungu amakhululukira nthawi zonse |
وَالَّذِينَ يُظَاهِرُونَ مِن نِّسَائِهِمْ ثُمَّ يَعُودُونَ لِمَا قَالُوا فَتَحْرِيرُ رَقَبَةٍ مِّن قَبْلِ أَن يَتَمَاسَّا ۚ ذَٰلِكُمْ تُوعَظُونَ بِهِ ۚ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرٌ (3) Ndipo iwo amene amasudzula akazi ponena kuti amaoneka ngati kumbuyo kwa amayi awo kenaka afuna kuti akhululukidwe pa zomwe adanena ayenera kumasula kapolo asanabwererane. Limeneli ndi lamulo limene mwalamulidwa kuti mulimvere ndipo Mulungu amadziwa chilichonse chimene mumachita |
فَمَن لَّمْ يَجِدْ فَصِيَامُ شَهْرَيْنِ مُتَتَابِعَيْنِ مِن قَبْلِ أَن يَتَمَاسَّا ۖ فَمَن لَّمْ يَسْتَطِعْ فَإِطْعَامُ سِتِّينَ مِسْكِينًا ۚ ذَٰلِكَ لِتُؤْمِنُوا بِاللَّهِ وَرَسُولِهِ ۚ وَتِلْكَ حُدُودُ اللَّهِ ۗ وَلِلْكَافِرِينَ عَذَابٌ أَلِيمٌ (4) Ndipo ngati wina sangathe kutero, ayenera kusala chakudya miyezi iwiri mosadukiza asanabwererane. Koma ngati sangathe kutero, ayenera kudyetsa anthu osauka makumi asanu ndi limodzi; ndi cholinga chakuti muonetse chikhulupiriro mwa Mulungu ndi Mtumwi wake. Amenewa ndiwo malamulo amene adakhazikitsidwa ndi Mulungu. Ndipo kwa anthu osakhulupilira kuli chilango chowawa |
إِنَّ الَّذِينَ يُحَادُّونَ اللَّهَ وَرَسُولَهُ كُبِتُوا كَمَا كُبِتَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۚ وَقَدْ أَنزَلْنَا آيَاتٍ بَيِّنَاتٍ ۚ وَلِلْكَافِرِينَ عَذَابٌ مُّهِينٌ (5) Ndithudi onse amene amatsutsa Mulungu ndi Mtumwi wakeadzatsitsidwakwambirimongamomweadatsitsidwira iwo amene adalipo kale. Ndipo Ife tatumiza zizindikiro zooneka. Ndipo anthu onse osakhulupirira adzalandira chilango chochititsa manyazi |
يَوْمَ يَبْعَثُهُمُ اللَّهُ جَمِيعًا فَيُنَبِّئُهُم بِمَا عَمِلُوا ۚ أَحْصَاهُ اللَّهُ وَنَسُوهُ ۚ وَاللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ شَهِيدٌ (6) Patsiku limene Mulungu adzawaukitsa onse kwa akufa ndi kuwauza ntchito zawo zonse zimene adachita. Mulungu anasunga zimene iwo adaiwala. Ndipo Mulungu ndi mboni pazinthu zonse |
أَلَمْ تَرَ أَنَّ اللَّهَ يَعْلَمُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۖ مَا يَكُونُ مِن نَّجْوَىٰ ثَلَاثَةٍ إِلَّا هُوَ رَابِعُهُمْ وَلَا خَمْسَةٍ إِلَّا هُوَ سَادِسُهُمْ وَلَا أَدْنَىٰ مِن ذَٰلِكَ وَلَا أَكْثَرَ إِلَّا هُوَ مَعَهُمْ أَيْنَ مَا كَانُوا ۖ ثُمَّ يُنَبِّئُهُم بِمَا عَمِلُوا يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۚ إِنَّ اللَّهَ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (7) Kodi iwe siudaone kuti Mulungu amadziwa zonse zimene zili mlengalenga ndi chilichonse chimene chili padziko lapansi? Palibe nkhani za chinsinsi pakati pa anthu atatu zimene Iye sakhala wachinayi, kapena pakati pa anthu asanu pamene Iye sakhala wa chisanu ndi chimodzi, kapena pakati pa anthu ochepa kapena ochuluka, koma Iye amakhala pakati pawo. Kulikonse kumene iwo angakhale pomaliza Iye adzawauza zonse zimene adachita patsiku lachiweruzo. Ndithudi Mulungu amadziwa chilichonse |
أَلَمْ تَرَ إِلَى الَّذِينَ نُهُوا عَنِ النَّجْوَىٰ ثُمَّ يَعُودُونَ لِمَا نُهُوا عَنْهُ وَيَتَنَاجَوْنَ بِالْإِثْمِ وَالْعُدْوَانِ وَمَعْصِيَتِ الرَّسُولِ وَإِذَا جَاءُوكَ حَيَّوْكَ بِمَا لَمْ يُحَيِّكَ بِهِ اللَّهُ وَيَقُولُونَ فِي أَنفُسِهِمْ لَوْلَا يُعَذِّبُنَا اللَّهُ بِمَا نَقُولُ ۚ حَسْبُهُمْ جَهَنَّمُ يَصْلَوْنَهَا ۖ فَبِئْسَ الْمَصِيرُ (8) Kodi iwe siudawaone amene adaletsedwa kuchita misonkhano ya mseri komabe amayambanso kuchita misonkhano ya chinsinsi imene adaletsedwa kuti asamachite? Iwo amachita misonkhano pakati pawo ndi cholinga choukira ndi kusamvera Mtumwi wa Mulungu. Koma iwo akamadza kwa iwe, iwo amakulonjera iwe osati monga mmene Mulungu amakulonjerera ayi koma mwachinyengo. Ndipo iwo amati kwa wina ndi mnzake: “Kodi bwanji Mulungu satilanga pa zimene timanena?” Gahena ndi yokwana kwa iwo, ndipo adzapsa m’malawi ake. Ndipo kumeneko ndi konyansa kwambiri |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِذَا تَنَاجَيْتُمْ فَلَا تَتَنَاجَوْا بِالْإِثْمِ وَالْعُدْوَانِ وَمَعْصِيَتِ الرَّسُولِ وَتَنَاجَوْا بِالْبِرِّ وَالتَّقْوَىٰ ۖ وَاتَّقُوا اللَّهَ الَّذِي إِلَيْهِ تُحْشَرُونَ (9) oh inu anthu okhulupirira! Pamene inu muchita misonkhano yanu yamseri musalankhule zinthu zoipa, zoukira ndi zosamvera Mtumwi koma muzilankhula zinthu zachilungamo ndi zamvano. Ndipo muopeni Mulungu chifukwa ndi kumene nonse mudzabwerera |
إِنَّمَا النَّجْوَىٰ مِنَ الشَّيْطَانِ لِيَحْزُنَ الَّذِينَ آمَنُوا وَلَيْسَ بِضَارِّهِمْ شَيْئًا إِلَّا بِإِذْنِ اللَّهِ ۚ وَعَلَى اللَّهِ فَلْيَتَوَكَّلِ الْمُؤْمِنُونَ (10) Misonkhano yamseri imachokera kwa Satana amene amafuna kusokoneza anthu okhulupirira. Koma Iye sangawalakwitse ayi kupatula ndi chilolezo cha Mulungu ndipo mwa Mulungu ndi momwe anthu okhulupirira ayenera kuika chikhulupiriro chawo |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِذَا قِيلَ لَكُمْ تَفَسَّحُوا فِي الْمَجَالِسِ فَافْسَحُوا يَفْسَحِ اللَّهُ لَكُمْ ۖ وَإِذَا قِيلَ انشُزُوا فَانشُزُوا يَرْفَعِ اللَّهُ الَّذِينَ آمَنُوا مِنكُمْ وَالَّذِينَ أُوتُوا الْعِلْمَ دَرَجَاتٍ ۚ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرٌ (11) Oh inu anthu okhulupirira! Ngati muuzidwa kukonza malo m’misonkhano yanu, konzani malo okwanira. Ndipo Mulungu adzakukonzerani inu malo okwanira kwambiri. Ndipo mukauzidwa kuti mudzuke, dzukani. Mulungu adzakweza mu maudindo ena a inu amene mukhulupirira ndi iwo amene apatsidwa nzeru. Ndipo Mulungu amadziwa ntchito zanu zonse |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِذَا نَاجَيْتُمُ الرَّسُولَ فَقَدِّمُوا بَيْنَ يَدَيْ نَجْوَاكُمْ صَدَقَةً ۚ ذَٰلِكَ خَيْرٌ لَّكُمْ وَأَطْهَرُ ۚ فَإِن لَّمْ تَجِدُوا فَإِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (12) oh inu anthu okhulupirira! Ngati mufuna kukumana ndi Mtumwi mwamseri, perekani chaulere chanu musanayambe kukambirana naye. Zimenezo zidzakhala zabwino kwa inu ndiponso dongosolo. Koma ngati inu mulibe chopereka, Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisonichosatha |
أَأَشْفَقْتُمْ أَن تُقَدِّمُوا بَيْنَ يَدَيْ نَجْوَاكُمْ صَدَقَاتٍ ۚ فَإِذْ لَمْ تَفْعَلُوا وَتَابَ اللَّهُ عَلَيْكُمْ فَأَقِيمُوا الصَّلَاةَ وَآتُوا الزَّكَاةَ وَأَطِيعُوا اللَّهَ وَرَسُولَهُ ۚ وَاللَّهُ خَبِيرٌ بِمَا تَعْمَلُونَ (13) Kodiinumulikuchitamanthakupereka chaulere chanu musanakumane naye? Ngati nditero, musachite mantha chifukwa Mulungu wakukhululukirani. Motero pitirizani kupemphera nthawi zonse, perekani msonkho wothandiza osauka, ndipo mverani Mulungu ndi Mtumwi wake. Ndithudi Mulungu amadziwa ntchito zanu zonse |
۞ أَلَمْ تَرَ إِلَى الَّذِينَ تَوَلَّوْا قَوْمًا غَضِبَ اللَّهُ عَلَيْهِم مَّا هُم مِّنكُمْ وَلَا مِنْهُمْ وَيَحْلِفُونَ عَلَى الْكَذِبِ وَهُمْ يَعْلَمُونَ (14) Kodi iwe suwaona amene amapalana ubwenzi ndi anthu amene adalandira mkwiyo wa Mulungu? Iwo si a m’gulu lako kapena a mgulu lawo, ndipo iwo amalumbira zabodza pamene ali kudziwa |
أَعَدَّ اللَّهُ لَهُمْ عَذَابًا شَدِيدًا ۖ إِنَّهُمْ سَاءَ مَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (15) Mulungu wawakonzera chilango chowawa. Ndithudi zoipa ndizo anali kuchita |
اتَّخَذُوا أَيْمَانَهُمْ جُنَّةً فَصَدُّوا عَن سَبِيلِ اللَّهِ فَلَهُمْ عَذَابٌ مُّهِينٌ (16) Iwo apanga malonjezo awo kukhala chishango. Kotero iwo amatchinjiriza anthu ku njira ya Mulungu ndipo iwo adzalandira chilango chochititsa manyazi |
لَّن تُغْنِيَ عَنْهُمْ أَمْوَالُهُمْ وَلَا أَوْلَادُهُم مِّنَ اللَّهِ شَيْئًا ۚ أُولَٰئِكَ أَصْحَابُ النَّارِ ۖ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (17) Chuma kapena ana awo sizidzawathandiza ku mkwiyo wa Mulungu. Iwo adzapita kumoto kumene adzakhaleko mpaka kalekale |
يَوْمَ يَبْعَثُهُمُ اللَّهُ جَمِيعًا فَيَحْلِفُونَ لَهُ كَمَا يَحْلِفُونَ لَكُمْ ۖ وَيَحْسَبُونَ أَنَّهُمْ عَلَىٰ شَيْءٍ ۚ أَلَا إِنَّهُمْ هُمُ الْكَاذِبُونَ (18) Patsiku limene Mulungu adzawadzutsa onse, iwo adzalumbira pamaso pake monga momwe alumbirira kwa inu. Ndipo iwo amaganiza kuti ali ndi mtsamiro. Ndithudi iwo ndi abodza |
اسْتَحْوَذَ عَلَيْهِمُ الشَّيْطَانُ فَأَنسَاهُمْ ذِكْرَ اللَّهِ ۚ أُولَٰئِكَ حِزْبُ الشَّيْطَانِ ۚ أَلَا إِنَّ حِزْبَ الشَّيْطَانِ هُمُ الْخَاسِرُونَ (19) Satana ndiye ali kuwalamulira. Ndipo wawachititsa iwo kuti aiwale kukumbukira Mulungu. Iwo ali m’gulu la Satana. Ndithudi gulu la Satana lidzakhala lolephera |
إِنَّ الَّذِينَ يُحَادُّونَ اللَّهَ وَرَسُولَهُ أُولَٰئِكَ فِي الْأَذَلِّينَ (20) Iwo amene amatsutsa Mulungu ndi Mtumwi wake adzakhala pakati pa anthu amene adzanyozedwa zedi |
كَتَبَ اللَّهُ لَأَغْلِبَنَّ أَنَا وَرُسُلِي ۚ إِنَّ اللَّهَ قَوِيٌّ عَزِيزٌ (21) Mulungu walamulira kuti: Ndithudi! Ine pamodzi ndi Atumwi anga tidzapambana. Ndithudi Mulungu ndi wamphamvu zonse |
لَّا تَجِدُ قَوْمًا يُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ يُوَادُّونَ مَنْ حَادَّ اللَّهَ وَرَسُولَهُ وَلَوْ كَانُوا آبَاءَهُمْ أَوْ أَبْنَاءَهُمْ أَوْ إِخْوَانَهُمْ أَوْ عَشِيرَتَهُمْ ۚ أُولَٰئِكَ كَتَبَ فِي قُلُوبِهِمُ الْإِيمَانَ وَأَيَّدَهُم بِرُوحٍ مِّنْهُ ۖ وَيُدْخِلُهُمْ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا ۚ رَضِيَ اللَّهُ عَنْهُمْ وَرَضُوا عَنْهُ ۚ أُولَٰئِكَ حِزْبُ اللَّهِ ۚ أَلَا إِنَّ حِزْبَ اللَّهِ هُمُ الْمُفْلِحُونَ (22) Iwe sudzapeza anthu amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza ali kuchita chibwenzi ndi iwo amene amatsutsa Mulungu ndi Mtumwi wake ngakhale kuti atakhala abambo wawo, kapena ana awo kapena abale awo kapena anansi awo. Kwa awa, Iye wakhazikitsa chikhulupiriro m’mitima mwawo, ndipo wawalimbikitsa ndi ulangizi, wochokera kwa Iye. Ndipo Iye adzawalandira m’minda ya Paradiso, imene pansi pake pamayenda mitsinje kuti akhale komweko mpaka kalekale. Mulungu wasangalala nawo ndipo nawonso asangalala ndi Iye. Iwo ndi anthu a gulu la Mulungu. Ndithudi ndi anthu a Mulungu amene adzapambana |