Quran with Chichewa translation - Surah Al-An‘am ayat 152 - الأنعَام - Page - Juz 8
﴿وَلَا تَقۡرَبُواْ مَالَ ٱلۡيَتِيمِ إِلَّا بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُ حَتَّىٰ يَبۡلُغَ أَشُدَّهُۥۚ وَأَوۡفُواْ ٱلۡكَيۡلَ وَٱلۡمِيزَانَ بِٱلۡقِسۡطِۖ لَا نُكَلِّفُ نَفۡسًا إِلَّا وُسۡعَهَاۖ وَإِذَا قُلۡتُمۡ فَٱعۡدِلُواْ وَلَوۡ كَانَ ذَا قُرۡبَىٰۖ وَبِعَهۡدِ ٱللَّهِ أَوۡفُواْۚ ذَٰلِكُمۡ وَصَّىٰكُم بِهِۦ لَعَلَّكُمۡ تَذَكَّرُونَ ﴾
[الأنعَام: 152]
﴿ولا تقربوا مال اليتيم إلا بالتي هي أحسن حتى يبلغ أشده وأوفوا﴾ [الأنعَام: 152]
Khaled Ibrahim Betala ““Ndipo musachiyandikire chuma cha mwana wamasiye, koma m’njira yabwino (monga kuchichulukitsa ndi malonda) mpaka afike pansinkhu wokwanira. Ndipo kwaniritsani mwachilungamo miyeso ya mbale ndi masikelo; sitikakamiza munthu koma chimene angathe; ndipo pamene mukunena, (popereka umboni), nenani mwachilungamo ngakhale (umboniwo) uli wokhudza achibale. Ndipo kwaniritsani lonjezo la Allah. Izi ndi zomwe akukulangizani kuti mukumbukire.” |