الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ وَجَعَلَ الظُّلُمَاتِ وَالنُّورَ ۖ ثُمَّ الَّذِينَ كَفَرُوا بِرَبِّهِمْ يَعْدِلُونَ (1) Kuyamikidwa ndi kwa Mulungu amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi kukhazikitsa mdima ndi kuwala, komabe anthu osakhulupirira amakhazikitsa milungu ina kuti ndi yolingana ndi Ambuye wawo |
هُوَ الَّذِي خَلَقَكُم مِّن طِينٍ ثُمَّ قَضَىٰ أَجَلًا ۖ وَأَجَلٌ مُّسَمًّى عِندَهُ ۖ ثُمَّ أَنتُمْ تَمْتَرُونَ (2) Iye ndiye amene adakulengani inu kuchokera ku dothi ndipo Iye adakhazikitsa nthawi. Ndipo Iye adakhazikitsanso nthawi ina, komabe inu mumakaika |
وَهُوَ اللَّهُ فِي السَّمَاوَاتِ وَفِي الْأَرْضِ ۖ يَعْلَمُ سِرَّكُمْ وَجَهْرَكُمْ وَيَعْلَمُ مَا تَكْسِبُونَ (3) Iye ndi Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi. Iye amadziwa zonse zimene mumabisa ndi zonse zimene mumaulula. Ndipo amadziwa zimene mumachita |
وَمَا تَأْتِيهِم مِّنْ آيَةٍ مِّنْ آيَاتِ رَبِّهِمْ إِلَّا كَانُوا عَنْهَا مُعْرِضِينَ (4) Ndipo chizindikiro sichidza kwa iwo kuchokera ku zizindikiro za Ambuye wawo, chimene iwo amachivomereza |
فَقَدْ كَذَّبُوا بِالْحَقِّ لَمَّا جَاءَهُمْ ۖ فَسَوْفَ يَأْتِيهِمْ أَنبَاءُ مَا كَانُوا بِهِ يَسْتَهْزِئُونَ (5) Ndithudi iwo adakana choonadi pamene chidadza kwa iwo; koma kudzadza kwa iwo nkhani za zimene adali kuchita chipongwe |
أَلَمْ يَرَوْا كَمْ أَهْلَكْنَا مِن قَبْلِهِم مِّن قَرْنٍ مَّكَّنَّاهُمْ فِي الْأَرْضِ مَا لَمْ نُمَكِّن لَّكُمْ وَأَرْسَلْنَا السَّمَاءَ عَلَيْهِم مِّدْرَارًا وَجَعَلْنَا الْأَنْهَارَ تَجْرِي مِن تَحْتِهِمْ فَأَهْلَكْنَاهُم بِذُنُوبِهِمْ وَأَنشَأْنَا مِن بَعْدِهِمْ قَرْنًا آخَرِينَ (6) Kodi iwo sadaone kuti kodi ndi mibadwo ingati, iwo asanabadwe, imene Ife tidawononga imene tidakhazikitsa pa dziko kukhala ya mphamvu kwambiri kuposa inu? Ndipo timawatumizira mvula yochuluka kuchokera kumwamba ndi kuipanga mitsinje yamadzi kuyenda pansi pawo. Komabe tidawawononga chifukwa cha machimo awo ndipo tidalenganso, pambuyo pa iwo, mibadwo ina |
وَلَوْ نَزَّلْنَا عَلَيْكَ كِتَابًا فِي قِرْطَاسٍ فَلَمَسُوهُ بِأَيْدِيهِمْ لَقَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا إِنْ هَٰذَا إِلَّا سِحْرٌ مُّبِينٌ (7) Ngakhale Ife tikadakutumizira iwe uthenga wolembedwa kale papepala kuti alikhudze ndi manja awo, anthu osakhulupirira akadanena kuti: “Ichi si china ayi koma matsenga enieni.” |
وَقَالُوا لَوْلَا أُنزِلَ عَلَيْهِ مَلَكٌ ۖ وَلَوْ أَنزَلْنَا مَلَكًا لَّقُضِيَ الْأَمْرُ ثُمَّ لَا يُنظَرُونَ (8) Iwo adati: Kodi ndi chifukwa chiyani mngelo sadatumizidwe kwa iye? Ife tikadatumiza mngelo, nkhani ikanaweruzidwa nthawi yomweyo, ndipo sakadapatsidwa mpata |
وَلَوْ جَعَلْنَاهُ مَلَكًا لَّجَعَلْنَاهُ رَجُلًا وَلَلَبَسْنَا عَلَيْهِم مَّا يَلْبِسُونَ (9) Ndipo ngati Ife tikadamupanga iye kukhala mngelo, ndithudi Ife tikadamupanga iye kuti azioneka ngati munthu ndipo tikadawasokoneza ndi zimene iwo adasokonezeka nazo kale |
وَلَقَدِ اسْتُهْزِئَ بِرُسُلٍ مِّن قَبْلِكَ فَحَاقَ بِالَّذِينَ سَخِرُوا مِنْهُم مَّا كَانُوا بِهِ يَسْتَهْزِئُونَ (10) Ndipo, ndithudi, Atumwi ena adasekedwa iwe usadadze, koma amene anali kuwaseka anazungulilidwa ndi zinthu zomwe iwo anali kuseka |
قُلْ سِيرُوا فِي الْأَرْضِ ثُمَّ انظُرُوا كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الْمُكَذِّبِينَ (11) Nena: “Yendani pa dziko lapansi ndipo muone mapeto a anthu amene anakana choonadi.” |
قُل لِّمَن مَّا فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ قُل لِّلَّهِ ۚ كَتَبَ عَلَىٰ نَفْسِهِ الرَّحْمَةَ ۚ لَيَجْمَعَنَّكُمْ إِلَىٰ يَوْمِ الْقِيَامَةِ لَا رَيْبَ فِيهِ ۚ الَّذِينَ خَسِرُوا أَنفُسَهُمْ فَهُمْ لَا يُؤْمِنُونَ (12) Nena: “Kodi mwini wa chilichonse chimene chili kumwamba ndi dziko lapansi ndani?” Nena: “Mwini wake ndi Mulungu” ndipo Iye adadzilamula yekha kuti azionetsa chifundo. Ndipo, ndithudi, Iye adzakusonkhanitsani nonse pa tsiku la kuuka kwa akufa, tsiku lopanda chikaiko. Iwo amene asochera sadzakhulupirira |
۞ وَلَهُ مَا سَكَنَ فِي اللَّيْلِ وَالنَّهَارِ ۚ وَهُوَ السَّمِيعُ الْعَلِيمُ (13) Ndipo zake ndi zonse zimene zimapezeka usiku ndi usana ndipo Iye ndi Wakumva ndi Wozindikira |
قُلْ أَغَيْرَ اللَّهِ أَتَّخِذُ وَلِيًّا فَاطِرِ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَهُوَ يُطْعِمُ وَلَا يُطْعَمُ ۗ قُلْ إِنِّي أُمِرْتُ أَنْ أَكُونَ أَوَّلَ مَنْ أَسْلَمَ ۖ وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ الْمُشْرِكِينَ (14) Nena: “Kodi ine nditenge wina aliyense osati Mulungu kuti akhale Mtetezi wanga, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi? Iye ndiye amene amadyetsa pamene Iye sadyetsedwa.” Nena: “Ndithudi ine ndalamulidwa kukhala woyamba wa anthu ogonjera kwa Mulungu.” Iwe usadzakhale mmodzi wa iwo amene amapembedza mafano |
قُلْ إِنِّي أَخَافُ إِنْ عَصَيْتُ رَبِّي عَذَابَ يَوْمٍ عَظِيمٍ (15) Nena: “Ine ndikuopa, ngati nditanyoza Ambuye wanga, chilango cha tsiku lalikulu.” |
مَّن يُصْرَفْ عَنْهُ يَوْمَئِذٍ فَقَدْ رَحِمَهُ ۚ وَذَٰلِكَ الْفَوْزُ الْمُبِينُ (16) Aliyense amene adzapulumutsidwa ku mazunzo a tsiku limeneli adzakhala atalandira chifundo cha Mulungu. Kumeneko ndiko kudzakhala kupambana kwenikweni koonekeratu |
وَإِن يَمْسَسْكَ اللَّهُ بِضُرٍّ فَلَا كَاشِفَ لَهُ إِلَّا هُوَ ۖ وَإِن يَمْسَسْكَ بِخَيْرٍ فَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (17) Ndipo ngati Mulungu akupatsa mavuto, palibe wina amene angachotse mavutowo koma Iye yekha; ndipo ngati Iye akupatsa zinthu zabwino, Iye ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse |
وَهُوَ الْقَاهِرُ فَوْقَ عِبَادِهِ ۚ وَهُوَ الْحَكِيمُ الْخَبِيرُ (18) Iye ali ndi mphamvu pa akapolo ake ndipo Iye ndiye Wanzeru ndi Wodziwa zonse |
قُلْ أَيُّ شَيْءٍ أَكْبَرُ شَهَادَةً ۖ قُلِ اللَّهُ ۖ شَهِيدٌ بَيْنِي وَبَيْنَكُمْ ۚ وَأُوحِيَ إِلَيَّ هَٰذَا الْقُرْآنُ لِأُنذِرَكُم بِهِ وَمَن بَلَغَ ۚ أَئِنَّكُمْ لَتَشْهَدُونَ أَنَّ مَعَ اللَّهِ آلِهَةً أُخْرَىٰ ۚ قُل لَّا أَشْهَدُ ۚ قُلْ إِنَّمَا هُوَ إِلَٰهٌ وَاحِدٌ وَإِنَّنِي بَرِيءٌ مِّمَّا تُشْرِكُونَ (19) Nena: “Kodi ndi chiani chili chachikulu mu umboni?” Nena: “Mulungu ndiye mboni pakati pa ine ndi inu. Buku la Korani lavumbulutsidwa kwa ine kuti ndikuchenjezeni inu ndi ena onse amene angalandire chivumbulutsochi. Kodi inu mungachitire umboni kuti pali milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni?” Nena: “Ine sindingaikire umboni pa nkhani yotere.” Nena: “Iye ndi Mulungu mmodzi yekha. Ndipo, ndithudi, ine ndili kutali ndi milungu imene inu muli kupembedza powonjezera pa Iye.” |
الَّذِينَ آتَيْنَاهُمُ الْكِتَابَ يَعْرِفُونَهُ كَمَا يَعْرِفُونَ أَبْنَاءَهُمُ ۘ الَّذِينَ خَسِرُوا أَنفُسَهُمْ فَهُمْ لَا يُؤْمِنُونَ (20) Kwa iwo amene tidawapatsa Buku amamudziwa Iye mongamomweamadziwiraanaawo. Komaiwoameneataya mizimu yawo sadzakhulupirira |
وَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّنِ افْتَرَىٰ عَلَى اللَّهِ كَذِبًا أَوْ كَذَّبَ بِآيَاتِهِ ۗ إِنَّهُ لَا يُفْلِحُ الظَّالِمُونَ (21) Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu kapena amakana chivumbulutso chake? Ndithudi anthu ochita zoipa sadzapambana ayi |
وَيَوْمَ نَحْشُرُهُمْ جَمِيعًا ثُمَّ نَقُولُ لِلَّذِينَ أَشْرَكُوا أَيْنَ شُرَكَاؤُكُمُ الَّذِينَ كُنتُمْ تَزْعُمُونَ (22) Ndipo patsiku limene tidzawasonkhanitsa onse pamodzi, Ife tidzati kwa anthu opembedza mafano: “Kodi ali kuti mafano anu aja munkawadalira?” |
ثُمَّ لَمْ تَكُن فِتْنَتُهُمْ إِلَّا أَن قَالُوا وَاللَّهِ رَبِّنَا مَا كُنَّا مُشْرِكِينَ (23) Iwo sadzawiringula china chili chonse koma adzati: “Tilumbira pali Mulungu, Ambuye wathu, kuti ife sitidali kupembedza mafano pambali pa Mulungu.” |
انظُرْ كَيْفَ كَذَبُوا عَلَىٰ أَنفُسِهِمْ ۚ وَضَلَّ عَنْهُم مَّا كَانُوا يَفْتَرُونَ (24) Taona mmene iwo ali kudzinamiza okha! Koma bodza limene anali kupeka lidzawathawira |
وَمِنْهُم مَّن يَسْتَمِعُ إِلَيْكَ ۖ وَجَعَلْنَا عَلَىٰ قُلُوبِهِمْ أَكِنَّةً أَن يَفْقَهُوهُ وَفِي آذَانِهِمْ وَقْرًا ۚ وَإِن يَرَوْا كُلَّ آيَةٍ لَّا يُؤْمِنُوا بِهَا ۚ حَتَّىٰ إِذَا جَاءُوكَ يُجَادِلُونَكَ يَقُولُ الَّذِينَ كَفَرُوا إِنْ هَٰذَا إِلَّا أَسَاطِيرُ الْأَوَّلِينَ (25) Ndipo ena a iwo amamvetsera kwa iwe koma Ife taika tchingo m’mitima mwawo kuti asazindikire ndipo m’makutu mwawo ndi mogontha ndipo iwo akaona chizindikiro chilichonse, sadzachikhulupirira ndipo amadza kwa iwe kudzatsutsana nawe, ndipo anthu osakhulupirira amati: “Ichi sichina chilichonse koma nkhani zopeka za anthu a kale kwambiri.” |
وَهُمْ يَنْهَوْنَ عَنْهُ وَيَنْأَوْنَ عَنْهُ ۖ وَإِن يُهْلِكُونَ إِلَّا أَنفُسَهُمْ وَمَا يَشْعُرُونَ (26) Ndipo iwo amaletsa anthu kumvetsera ndipo iwo amadzitalikitsa okha kwa Iye. Koma iwo sali kuwononga wina aliyense koma akudziononga okha. Koma iwo sazindikira |
وَلَوْ تَرَىٰ إِذْ وُقِفُوا عَلَى النَّارِ فَقَالُوا يَا لَيْتَنَا نُرَدُّ وَلَا نُكَذِّبَ بِآيَاتِ رَبِّنَا وَنَكُونَ مِنَ الْمُؤْمِنِينَ (27) Koma iwe ukadawaona pamene iwo adzaimitsidwe moyandikira moto! Iwo adzati: “Zikadakhala kuti tinabwezedwa! Ife sitikadakana chivumbulutso cha Ambuye wathu ndipo tikadakakhala anthu okhulupirira.” |
بَلْ بَدَا لَهُم مَّا كَانُوا يُخْفُونَ مِن قَبْلُ ۖ وَلَوْ رُدُّوا لَعَادُوا لِمَا نُهُوا عَنْهُ وَإِنَّهُمْ لَكَاذِبُونَ (28) Koma zonse zimene adali kuzibisa kale zidzaonekera poyera kwa iwo. Komabe akadabwezedwa, iwo akadakabwerera ku zinthu zimene adaletsedwa. Ndithudi iwo ndi anthu a bodza |
وَقَالُوا إِنْ هِيَ إِلَّا حَيَاتُنَا الدُّنْيَا وَمَا نَحْنُ بِمَبْعُوثِينَ (29) Iwo adanenetsa kuti: “Kulibenso moyo wina uliwonse kupatula moyo wathu wadziko lapansi ndiponso ife sitidzaukitsidwa kwa akufa.” |
وَلَوْ تَرَىٰ إِذْ وُقِفُوا عَلَىٰ رَبِّهِمْ ۚ قَالَ أَلَيْسَ هَٰذَا بِالْحَقِّ ۚ قَالُوا بَلَىٰ وَرَبِّنَا ۚ قَالَ فَذُوقُوا الْعَذَابَ بِمَا كُنتُمْ تَكْفُرُونَ (30) Ndipo iwe ukadawaona pamene ali kusonkhanitsidwa kuima pamaso pa Ambuye wawo! Iye adzati: “Kodi izi sizoona?” Iwo adzayankha: “Ndi zoona pali Ambuye wathu.” Ndipo Iye adzati: “Motero lawani chilango chifukwa inu simunali okhulupilira.” |
قَدْ خَسِرَ الَّذِينَ كَذَّبُوا بِلِقَاءِ اللَّهِ ۖ حَتَّىٰ إِذَا جَاءَتْهُمُ السَّاعَةُ بَغْتَةً قَالُوا يَا حَسْرَتَنَا عَلَىٰ مَا فَرَّطْنَا فِيهَا وَهُمْ يَحْمِلُونَ أَوْزَارَهُمْ عَلَىٰ ظُهُورِهِمْ ۚ أَلَا سَاءَ مَا يَزِرُونَ (31) Ndithudi iwo ndi olephera kwambiri amene amakana kuti adzakumana ndi Ambuye wawo mpaka pamene ola loopsa lidza pa iwo mwadzidzidzi ndipo iwo adzafuula kuti: “Kalanga ife tidali kunyalanyaza kwambiri!” Iwo adzanyamula katundu wawo pa misana yawo ndipo zoipa kwambirizimeneadzasenza |
وَمَا الْحَيَاةُ الدُّنْيَا إِلَّا لَعِبٌ وَلَهْوٌ ۖ وَلَلدَّارُ الْآخِرَةُ خَيْرٌ لِّلَّذِينَ يَتَّقُونَ ۗ أَفَلَا تَعْقِلُونَ (32) Ndipomoyowapadzikolino lapansi siuli kanthu konse koma masewera ndi nthabwala. Koma yabwino kwambiri ndi nyumba m’moyo umene uli nkudza kwa amene amaopa. Kodi simungazindikire |
قَدْ نَعْلَمُ إِنَّهُ لَيَحْزُنُكَ الَّذِي يَقُولُونَ ۖ فَإِنَّهُمْ لَا يُكَذِّبُونَكَ وَلَٰكِنَّ الظَّالِمِينَ بِآيَاتِ اللَّهِ يَجْحَدُونَ (33) Ife tili kudziwa kuti zonse zimene ali kunena zili kukukhumudwitsa. Sindiwe amene iwo ali kukana koma ndi chivumbulutso cha Mulungu chimene anthu ochita zoipa ali kukana |
وَلَقَدْ كُذِّبَتْ رُسُلٌ مِّن قَبْلِكَ فَصَبَرُوا عَلَىٰ مَا كُذِّبُوا وَأُوذُوا حَتَّىٰ أَتَاهُمْ نَصْرُنَا ۚ وَلَا مُبَدِّلَ لِكَلِمَاتِ اللَّهِ ۚ وَلَقَدْ جَاءَكَ مِن نَّبَإِ الْمُرْسَلِينَ (34) Ndithudi Atumwi ena adakanidwa iwe usanadze koma iwo adapilira pa zimene adali kuwanena ndipo anazunzidwa mpaka pamene thandizo lathu lidadza kwa iwo ndipo palibe amene angasinthe chilamulo cha Mulungu. Ndithudi iwe udamva nkhani zaAtumwi |
وَإِن كَانَ كَبُرَ عَلَيْكَ إِعْرَاضُهُمْ فَإِنِ اسْتَطَعْتَ أَن تَبْتَغِيَ نَفَقًا فِي الْأَرْضِ أَوْ سُلَّمًا فِي السَّمَاءِ فَتَأْتِيَهُم بِآيَةٍ ۚ وَلَوْ شَاءَ اللَّهُ لَجَمَعَهُمْ عَلَى الْهُدَىٰ ۚ فَلَا تَكُونَنَّ مِنَ الْجَاهِلِينَ (35) Ngati uona kuti kukana kwawo kwanyanya ndipo kuti sungathe kupirira, peza ngati ungathe, njira yapansi pa nthaka kapena makwerero oti ukwere kumwamba, kuti ukhoza kuwabweretsera chizindikiro. Ngati Mulungu akadafuna, Iye akadawasonkhanitsa onse ku chilangizo choona ndipo iwe usakhale mmodzi wa mbuli |
۞ إِنَّمَا يَسْتَجِيبُ الَّذِينَ يَسْمَعُونَ ۘ وَالْمَوْتَىٰ يَبْعَثُهُمُ اللَّهُ ثُمَّ إِلَيْهِ يُرْجَعُونَ (36) Ndi okhawo amene amamva, amene adzapindula koma anthu akufa Mulungu adzawadzutsa kwa akufa ndipo kwa Iye adzabwerera |
وَقَالُوا لَوْلَا نُزِّلَ عَلَيْهِ آيَةٌ مِّن رَّبِّهِ ۚ قُلْ إِنَّ اللَّهَ قَادِرٌ عَلَىٰ أَن يُنَزِّلَ آيَةً وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (37) Iwo amafunsa: “Kodi ndi chifukwa chiyani chizindikiro sichinadze kwa iye kuchokera kwa Ambuye wake?” Nena: “Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu zotumiza chizindikiro koma ambiri a iwo sazindikira.” |
وَمَا مِن دَابَّةٍ فِي الْأَرْضِ وَلَا طَائِرٍ يَطِيرُ بِجَنَاحَيْهِ إِلَّا أُمَمٌ أَمْثَالُكُم ۚ مَّا فَرَّطْنَا فِي الْكِتَابِ مِن شَيْءٍ ۚ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّهِمْ يُحْشَرُونَ (38) Palibe chinthu cha moyo padziko lapansi kapena mbalame imene imauluka ndi mapiko ake awiri imene ndi zosiyana ndi inu. Ife sitidasiye china chilichonse m’Buku ndipo kwa Ambuye wawo iwo adzasonkhanitsidwa |
وَالَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا صُمٌّ وَبُكْمٌ فِي الظُّلُمَاتِ ۗ مَن يَشَإِ اللَّهُ يُضْلِلْهُ وَمَن يَشَأْ يَجْعَلْهُ عَلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (39) Koma iwo amene amakana zizindikiro zathu, ndi agonthi m’khutu ndi abububu mu mdima. Mulungu amasocheza aliyense amene Iye wamufuna ndipo amatsogolera, kunjira yoyenera, aliyense amene Iye wamufuna |
قُلْ أَرَأَيْتَكُمْ إِنْ أَتَاكُمْ عَذَابُ اللَّهِ أَوْ أَتَتْكُمُ السَّاعَةُ أَغَيْرَ اللَّهِ تَدْعُونَ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (40) Nena: “Ndiuzeni, ngati chilango cha Mulungu chitadza pa inu kapena ola loopsa lidza pa inu, kodi inu mudzapempha wina amene sali Mulungu kuti akuthandizeni inu? Yankhani ngati mukunena zoona.” |
بَلْ إِيَّاهُ تَدْعُونَ فَيَكْشِفُ مَا تَدْعُونَ إِلَيْهِ إِن شَاءَ وَتَنسَوْنَ مَا تُشْرِكُونَ (41) Iyayi! Ndi kwa Iye yekha kumene inu mumapempha ndipo ngati Iye atafuna akhoza kukuchotserani zovuta zanu, ndipo inu pa nthawi imeneyi mudzaiwala mafano anu |
وَلَقَدْ أَرْسَلْنَا إِلَىٰ أُمَمٍ مِّن قَبْلِكَ فَأَخَذْنَاهُم بِالْبَأْسَاءِ وَالضَّرَّاءِ لَعَلَّهُمْ يَتَضَرَّعُونَ (42) Ndithudi Ife tidatumiza, iwe usanadze, Atumwi ku mitundu ina. Ndipo tidawagwetsera umphawi, matenda ndi matsoka ochuluka kuti akhoza kukhulupilira modzichepetsa |
فَلَوْلَا إِذْ جَاءَهُم بَأْسُنَا تَضَرَّعُوا وَلَٰكِن قَسَتْ قُلُوبُهُمْ وَزَيَّنَ لَهُمُ الشَّيْطَانُ مَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (43) Nanga ndi chifukwa chiyani iwo sadadzichepetse pamene mazunzo athu adadza pa iwo? Koma mitima yawo inalimba ndipo Satana adawakongoletsera zochita zawo zoipa zimene adali kuchita |
فَلَمَّا نَسُوا مَا ذُكِّرُوا بِهِ فَتَحْنَا عَلَيْهِمْ أَبْوَابَ كُلِّ شَيْءٍ حَتَّىٰ إِذَا فَرِحُوا بِمَا أُوتُوا أَخَذْنَاهُم بَغْتَةً فَإِذَا هُم مُّبْلِسُونَ (44) Ndipo pamene iwo adaiwala zimene adachenjezedwa, Ife tidawatsegulira makomo a zinthu zonse zabwino mpaka pamene adasangalala ndi zimene adapatsidwa, mwadzidzidzi Ife tidawalanga ndipo ah! Iwo adalowa m’chionongeko wokhumudwa ndi a chisoni |
فَقُطِعَ دَابِرُ الْقَوْمِ الَّذِينَ ظَلَمُوا ۚ وَالْحَمْدُ لِلَّهِ رَبِّ الْعَالَمِينَ (45) Motero maziko a anthu ochimwa adaonongedwa. Ndipo kutamandidwa konse kukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengezedwa zonse |
قُلْ أَرَأَيْتُمْ إِنْ أَخَذَ اللَّهُ سَمْعَكُمْ وَأَبْصَارَكُمْ وَخَتَمَ عَلَىٰ قُلُوبِكُم مَّنْ إِلَٰهٌ غَيْرُ اللَّهِ يَأْتِيكُم بِهِ ۗ انظُرْ كَيْفَ نُصَرِّفُ الْآيَاتِ ثُمَّ هُمْ يَصْدِفُونَ (46) Nena: “Tandiuzani! Ngati Mulungu akadakulandani kumva kwanu, kuona kwanu ndi kutseka mitima yanu, kodi pali mulungu wina, woonjezera pa Mulungu weniweni, amene angakubwezereni zimenezi?” Taonani mmene tifotokozera chivumbulutso chathu ndi mmene iwo sakhulupilira |
قُلْ أَرَأَيْتَكُمْ إِنْ أَتَاكُمْ عَذَابُ اللَّهِ بَغْتَةً أَوْ جَهْرَةً هَلْ يُهْلَكُ إِلَّا الْقَوْمُ الظَّالِمُونَ (47) Nena: “Ndiuzeni, ngati chilango cha Mulungu chitadza mwadzidzidzi kapena moonekera, kodi ndani angaonongeke kupatula anthu ochita zoipa?” |
وَمَا نُرْسِلُ الْمُرْسَلِينَ إِلَّا مُبَشِّرِينَ وَمُنذِرِينَ ۖ فَمَنْ آمَنَ وَأَصْلَحَ فَلَا خَوْفٌ عَلَيْهِمْ وَلَا هُمْ يَحْزَنُونَ (48) Ndipo Ife sititumiza Aneneri koma kuti azikawauza anthu nkhani yabwino ndi kuwachenjeza. Motero aliyense amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, iye sadzakhala ndi nkhawa kapena kudandaula |
وَالَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا يَمَسُّهُمُ الْعَذَابُ بِمَا كَانُوا يَفْسُقُونَ (49) Koma iwo amene akana chivumbulutso chathu, chilango chidzawapeza chifukwa cha kusakhulupilira kwawo |
قُل لَّا أَقُولُ لَكُمْ عِندِي خَزَائِنُ اللَّهِ وَلَا أَعْلَمُ الْغَيْبَ وَلَا أَقُولُ لَكُمْ إِنِّي مَلَكٌ ۖ إِنْ أَتَّبِعُ إِلَّا مَا يُوحَىٰ إِلَيَّ ۚ قُلْ هَلْ يَسْتَوِي الْأَعْمَىٰ وَالْبَصِيرُ ۚ أَفَلَا تَتَفَكَّرُونَ (50) Nena: “Ine sindili kukuuzani kuti ndili ndi chuma cha Mulungu kapena kuti ndimadziwa zinthu zobisika kapena kuti ine ndine mngelo. Ine sinditsatira china chilichonse kupatula zokhazo zimene zavumbulutsidwa kwa ine.” Nena: “Kodi munthu wakhungu ndi munthu openya angafanane? Kodi inu simungaganize?” |
وَأَنذِرْ بِهِ الَّذِينَ يَخَافُونَ أَن يُحْشَرُوا إِلَىٰ رَبِّهِمْ ۙ لَيْسَ لَهُم مِّن دُونِهِ وَلِيٌّ وَلَا شَفِيعٌ لَّعَلَّهُمْ يَتَّقُونَ (51) Ndipo achenjeze iwo amene amaopa kuti adzasonkhanitsidwa kupita kwa Ambuye wawo, amene alibe wowasamalira kapena mkhalapakati woonjezera pa Mulungu, kuti akhoza kumalewa zoipa |
وَلَا تَطْرُدِ الَّذِينَ يَدْعُونَ رَبَّهُم بِالْغَدَاةِ وَالْعَشِيِّ يُرِيدُونَ وَجْهَهُ ۖ مَا عَلَيْكَ مِنْ حِسَابِهِم مِّن شَيْءٍ وَمَا مِنْ حِسَابِكَ عَلَيْهِم مِّن شَيْءٍ فَتَطْرُدَهُمْ فَتَكُونَ مِنَ الظَّالِمِينَ (52) Ndipo usawathamangitse iwo amene amapembedza Ambuye wawo m’mawa ndi madzulo pofuna chisangalalo chake. Iwe siudzaimbidwa mlandu pa zochita zawo ndipo nawonso sadzaimbidwa mlandu pa zochita zako ndipo ngati iwe uwathamangitsa udzakhala mugulu la anthu opanda chilungamo |
وَكَذَٰلِكَ فَتَنَّا بَعْضَهُم بِبَعْضٍ لِّيَقُولُوا أَهَٰؤُلَاءِ مَنَّ اللَّهُ عَلَيْهِم مِّن بَيْنِنَا ۗ أَلَيْسَ اللَّهُ بِأَعْلَمَ بِالشَّاكِرِينَ (53) Motero ife tinawayesa ena a iwo kupyolera mwa anzawo kuti akhoza kunena, “Kodi awa ndiwo amene Mulungu wawadalitsa pakati pathu?” Kodi Mulungu sazindikira anthu othokoza |
وَإِذَا جَاءَكَ الَّذِينَ يُؤْمِنُونَ بِآيَاتِنَا فَقُلْ سَلَامٌ عَلَيْكُمْ ۖ كَتَبَ رَبُّكُمْ عَلَىٰ نَفْسِهِ الرَّحْمَةَ ۖ أَنَّهُ مَنْ عَمِلَ مِنكُمْ سُوءًا بِجَهَالَةٍ ثُمَّ تَابَ مِن بَعْدِهِ وَأَصْلَحَ فَأَنَّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (54) Ngati atadza kwa iwe anthu amene amakhulupirira chivumbulutso chathu. Nena, “Mtendere ukhale pa inu.” Ambuye wanu adadzilamulira yekha kuti azionetsa chisoni kuti ngati wina wa inu achita choipa chifukwa chosadziwa ndipo alapa pambuyo pake ndipo achita ntchito zabwino, ndithudi Iye ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha |
وَكَذَٰلِكَ نُفَصِّلُ الْآيَاتِ وَلِتَسْتَبِينَ سَبِيلُ الْمُجْرِمِينَ (55) Motero Ife timafotokoza chivulumbutso chathu poyera kuti njira ya anthu ochita zoipa ionekere poyera |
قُلْ إِنِّي نُهِيتُ أَنْ أَعْبُدَ الَّذِينَ تَدْعُونَ مِن دُونِ اللَّهِ ۚ قُل لَّا أَتَّبِعُ أَهْوَاءَكُمْ ۙ قَدْ ضَلَلْتُ إِذًا وَمَا أَنَا مِنَ الْمُهْتَدِينَ (56) Nena, “Ine ndaletsedwa kupembedza milungu imene inumumaipembedzapowonjezerapa Mulungu.” Nena,“Ine sindidzatsatira zilakolako zanu zachabe. Ngati nditatero ndiye kuti ndasochera ndipo ine sindikhala mugulu la anthu otsogozedwa bwino.” |
قُلْ إِنِّي عَلَىٰ بَيِّنَةٍ مِّن رَّبِّي وَكَذَّبْتُم بِهِ ۚ مَا عِندِي مَا تَسْتَعْجِلُونَ بِهِ ۚ إِنِ الْحُكْمُ إِلَّا لِلَّهِ ۖ يَقُصُّ الْحَقَّ ۖ وَهُوَ خَيْرُ الْفَاصِلِينَ (57) Nena, “Ine ndalandira umboni wokwana kuchokera kwa Ambuye wanga komabe inu muli kuukana. Ine ndilibe mphamvu yobweretsa msangamsanga chilango chimene mufuna. Chiweruzo chili m’manja mwa Mulungu yekha, Iye amanena zoona ndipo ndi yekhayo amene ali wabwino poweruza.” |
قُل لَّوْ أَنَّ عِندِي مَا تَسْتَعْجِلُونَ بِهِ لَقُضِيَ الْأَمْرُ بَيْنِي وَبَيْنَكُمْ ۗ وَاللَّهُ أَعْلَمُ بِالظَّالِمِينَ (58) Nena, “Ine ndikadakhala nacho chimene mufuna mwamsanga msanga, mkangano wa pakati pa inu ndi ine ukadaweruzidwa kalekale koma Mulungu amadziwa anthu onse ochita zoipa.” |
۞ وَعِندَهُ مَفَاتِحُ الْغَيْبِ لَا يَعْلَمُهَا إِلَّا هُوَ ۚ وَيَعْلَمُ مَا فِي الْبَرِّ وَالْبَحْرِ ۚ وَمَا تَسْقُطُ مِن وَرَقَةٍ إِلَّا يَعْلَمُهَا وَلَا حَبَّةٍ فِي ظُلُمَاتِ الْأَرْضِ وَلَا رَطْبٍ وَلَا يَابِسٍ إِلَّا فِي كِتَابٍ مُّبِينٍ (59) Iye ali ndi makiyi a zinthu zonse zobisika, palibe wina amene azidziwa koma Iye yekha. Iye amadziwa zonse zimene zili m’nthaka ndiponso m’nyanja; ndipo lisadagwe tsamba Iye amalidziwa. Palibe mbewu mu mdima wa nthaka kapena china chilichonse cha chiwisi kapena chouma koma zonsezo zidalembedwa mu Buku looneka bwino |
وَهُوَ الَّذِي يَتَوَفَّاكُم بِاللَّيْلِ وَيَعْلَمُ مَا جَرَحْتُم بِالنَّهَارِ ثُمَّ يَبْعَثُكُمْ فِيهِ لِيُقْضَىٰ أَجَلٌ مُّسَمًّى ۖ ثُمَّ إِلَيْهِ مَرْجِعُكُمْ ثُمَّ يُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (60) Iye ndiye amene amachotsa mizimu yanu nthawi yausiku ndipo amadziwa zonse zimene mwachita masana ndipo amakudzutsani kuti mukwaniritse nthawi imene idaperekedwa pa moyo wanu ndipo pambuyo pake nonse mudzabwerera kwa Iye. Ndipo Iye adzakuuzani zonse zimene mumachita |
وَهُوَ الْقَاهِرُ فَوْقَ عِبَادِهِ ۖ وَيُرْسِلُ عَلَيْكُمْ حَفَظَةً حَتَّىٰ إِذَا جَاءَ أَحَدَكُمُ الْمَوْتُ تَوَفَّتْهُ رُسُلُنَا وَهُمْ لَا يُفَرِّطُونَ (61) Iye ndi wamphamvu pa akapolo ake ndipo amatumiza atetezi amene amakuyang’anirani inu mpaka pamene mmodzi wa inu imufikira imfa; Atumiki athu amachotsa moyo wake ndipo iwo sanyoza zimene alamulidwa |
ثُمَّ رُدُّوا إِلَى اللَّهِ مَوْلَاهُمُ الْحَقِّ ۚ أَلَا لَهُ الْحُكْمُ وَهُوَ أَسْرَعُ الْحَاسِبِينَ (62) Ndipo iwo amabwerera kwa Mulungu, Ambuye wawo woona. Ndithudi Iye ndiye muweruzi ndipo Iye ndi wachangu powerengera zochita zanu |
قُلْ مَن يُنَجِّيكُم مِّن ظُلُمَاتِ الْبَرِّ وَالْبَحْرِ تَدْعُونَهُ تَضَرُّعًا وَخُفْيَةً لَّئِنْ أَنجَانَا مِنْ هَٰذِهِ لَنَكُونَنَّ مِنَ الشَّاكِرِينَ (63) Nena, “Kodi ndani amakupulumutsani m’mavuto a pa mtunda ndi a pa nyanja ndi pamene inu mumamupempha Iye modzichepetsa ndi mwamseri, ponena kuti: ‘Ngati Iye atipulumutsa ife pa mavuto awa, ndithudi, ife tidzakhala othokoza.” |
قُلِ اللَّهُ يُنَجِّيكُم مِّنْهَا وَمِن كُلِّ كَرْبٍ ثُمَّ أَنتُمْ تُشْرِكُونَ (64) Nena, “Mulungu amakupulumutsani inu ku zovuta izi ndi kumavuto ena onse, komabe inu mumapembedzabe mafano mowonjezera pa Iye.” |
قُلْ هُوَ الْقَادِرُ عَلَىٰ أَن يَبْعَثَ عَلَيْكُمْ عَذَابًا مِّن فَوْقِكُمْ أَوْ مِن تَحْتِ أَرْجُلِكُمْ أَوْ يَلْبِسَكُمْ شِيَعًا وَيُذِيقَ بَعْضَكُم بَأْسَ بَعْضٍ ۗ انظُرْ كَيْفَ نُصَرِّفُ الْآيَاتِ لَعَلَّهُمْ يَفْقَهُونَ (65) Nena, “Iye ali ndi mphamvu yotumiza chilango chake pa inu kuchokerapamutupanukapenapansipamapazianukapena kukugawani inu kukhala m’magulu a anthu osagwirizana ndi kukulawitsani mazunzo ochokera kwa anzanu. Taonani mmene timaonetsera poyera chivumbulutso chathu kuti akhale ozindikira.” |
وَكَذَّبَ بِهِ قَوْمُكَ وَهُوَ الْحَقُّ ۚ قُل لَّسْتُ عَلَيْكُم بِوَكِيلٍ (66) Koma anthu ako alikana ili ngakhale lili choonadi chenicheni. Nena: “Ine sindine Msungi wanu ayi.” |
لِّكُلِّ نَبَإٍ مُّسْتَقَرٌّ ۚ وَسَوْفَ تَعْلَمُونَ (67) Nkhani iliyonse ili ndi nthawi yake ndipo posachedwapa mudzazindikira |
وَإِذَا رَأَيْتَ الَّذِينَ يَخُوضُونَ فِي آيَاتِنَا فَأَعْرِضْ عَنْهُمْ حَتَّىٰ يَخُوضُوا فِي حَدِيثٍ غَيْرِهِ ۚ وَإِمَّا يُنسِيَنَّكَ الشَّيْطَانُ فَلَا تَقْعُدْ بَعْدَ الذِّكْرَىٰ مَعَ الْقَوْمِ الظَّالِمِينَ (68) Ndipo pamene iwe uwaona iwo amene amanyoza chivumbulutso chathu, usakhale nawo pamodzi mpaka pokhapokha akamba nkhani ina. Ngati satana akuiwalitsa, ndipo pambuyo pake ukumbukira usakhale mgulu la anthu ochita zoipa |
وَمَا عَلَى الَّذِينَ يَتَّقُونَ مِنْ حِسَابِهِم مِّن شَيْءٍ وَلَٰكِن ذِكْرَىٰ لَعَلَّهُمْ يَتَّقُونَ (69) Iwo amene amaopa Mulungu alibe udindo pa iwo koma kungowakumbutsa kuti apewe kunyoza |
وَذَرِ الَّذِينَ اتَّخَذُوا دِينَهُمْ لَعِبًا وَلَهْوًا وَغَرَّتْهُمُ الْحَيَاةُ الدُّنْيَا ۚ وَذَكِّرْ بِهِ أَن تُبْسَلَ نَفْسٌ بِمَا كَسَبَتْ لَيْسَ لَهَا مِن دُونِ اللَّهِ وَلِيٌّ وَلَا شَفِيعٌ وَإِن تَعْدِلْ كُلَّ عَدْلٍ لَّا يُؤْخَذْ مِنْهَا ۗ أُولَٰئِكَ الَّذِينَ أُبْسِلُوا بِمَا كَسَبُوا ۖ لَهُمْ شَرَابٌ مِّنْ حَمِيمٍ وَعَذَابٌ أَلِيمٌ بِمَا كَانُوا يَكْفُرُونَ (70) Apewe iwo amene amasandutsa chipembedzo chawo kukhala masewera kapena nthabwala ndipo asokonezeka ndi zokoma za moyo wa dziko lapansi. Koma achenjeze ndi ilo kuti ungadzaonongeke mzimu wawo chifukwa cha zimene udachita pamene siudzakhala ndi wousamalira kapena kuwuteteza kupatula Mulungu, ndipo ngakhale iwo apereka chuma chopepesera, sichidzalandiridwa konse. Otere ndiwo amene aonongedwa chifukwa cha zimene anachita. Iwo adzalandira zakumwa zowira ndi chilango chowawa chifukwa cha zinthu zimene sadakhulupirire |
قُلْ أَنَدْعُو مِن دُونِ اللَّهِ مَا لَا يَنفَعُنَا وَلَا يَضُرُّنَا وَنُرَدُّ عَلَىٰ أَعْقَابِنَا بَعْدَ إِذْ هَدَانَا اللَّهُ كَالَّذِي اسْتَهْوَتْهُ الشَّيَاطِينُ فِي الْأَرْضِ حَيْرَانَ لَهُ أَصْحَابٌ يَدْعُونَهُ إِلَى الْهُدَى ائْتِنَا ۗ قُلْ إِنَّ هُدَى اللَّهِ هُوَ الْهُدَىٰ ۖ وَأُمِرْنَا لِنُسْلِمَ لِرَبِّ الْعَالَمِينَ (71) Nena, “Kodi ife tizipembedza ena powonjezera pa Mulungu amene sangathe kutithandiza kapena kutiwononga ndipo kodi ife tibwerere m’mbuyo pamene Mulungu watitsogolera? Monga ngati munthu amene alodzedwa ndi Satana, kumangoyenda uku ndi uku ngakhale kuti abwenzi ake ali kumuitana kuti atsatire njira yoyenera, ponena: Bwerani kuno?” Nena, “Ndithudi utsogoleri wa Mulungu ndiwo utsogoleri weniweni ndipo Ife talamulidwa kugonjera Mulungu Ambuye wa zolengedwa zonse.” |
وَأَنْ أَقِيمُوا الصَّلَاةَ وَاتَّقُوهُ ۚ وَهُوَ الَّذِي إِلَيْهِ تُحْشَرُونَ (72) Ndi kuti muzipemphera moyenera, kumvera Mulungu ndi kumuopa Iye ndipo ndi kwa Iye kumene nonse mudzasonkhanitsidwa |
وَهُوَ الَّذِي خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ بِالْحَقِّ ۖ وَيَوْمَ يَقُولُ كُن فَيَكُونُ ۚ قَوْلُهُ الْحَقُّ ۚ وَلَهُ الْمُلْكُ يَوْمَ يُنفَخُ فِي الصُّورِ ۚ عَالِمُ الْغَيْبِ وَالشَّهَادَةِ ۚ وَهُوَ الْحَكِيمُ الْخَبِيرُ (73) Iye ndiye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi ndipo patsikuli Iye adzati: “Khala” ndipo chidzakhala. Liwu lake ndi loonadi. Wake udzakhala Ufumu pa tsiku limene lipenga lidzaombedwa. Iye amadziwa zonse zosaoneka ndi zooneka. Iye ndi wanzeru ndi wodziwa zinthu zonse |
۞ وَإِذْ قَالَ إِبْرَاهِيمُ لِأَبِيهِ آزَرَ أَتَتَّخِذُ أَصْنَامًا آلِهَةً ۖ إِنِّي أَرَاكَ وَقَوْمَكَ فِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (74) Ndi pamene Abrahamu adati kwa abambo ake a Uzar: “Kodi inu muzipembedza mafano ngati milungu yanu? Ndithudi ine ndili kuona kuti inu pamodzi ndi anthu anu mwasochera moonekera.” |
وَكَذَٰلِكَ نُرِي إِبْرَاهِيمَ مَلَكُوتَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَلِيَكُونَ مِنَ الْمُوقِنِينَ (75) Motero tidamuonetsa Abrahamu Ufumu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi kuti akhale mmodzi wa wokhulupirira kweniweni |
فَلَمَّا جَنَّ عَلَيْهِ اللَّيْلُ رَأَىٰ كَوْكَبًا ۖ قَالَ هَٰذَا رَبِّي ۖ فَلَمَّا أَفَلَ قَالَ لَا أُحِبُّ الْآفِلِينَ (76) Ndipo pamene usiku udamukuta ndi mdima, iye adaona nyenyezi. Iye adati: “Iyo ndiyo Ambuye wanga.” Koma pamene iyo idalowa, iye adati: “Ine sindikonda zimene zimalowa.” |
فَلَمَّا رَأَى الْقَمَرَ بَازِغًا قَالَ هَٰذَا رَبِّي ۖ فَلَمَّا أَفَلَ قَالَ لَئِن لَّمْ يَهْدِنِي رَبِّي لَأَكُونَنَّ مِنَ الْقَوْمِ الضَّالِّينَ (77) Ndipo pamene iye adaona mwezi uli kutuluka, iye adati: “Uwo ndiwo Ambuye wanga.” Koma pamene iwo unalowa, Iye adati: “Ngati Ambuye wanga sanditsogolera ine, ndithudi, ine ndidzakhala m’gulu la anthu osochera.” |
فَلَمَّا رَأَى الشَّمْسَ بَازِغَةً قَالَ هَٰذَا رَبِّي هَٰذَا أَكْبَرُ ۖ فَلَمَّا أَفَلَتْ قَالَ يَا قَوْمِ إِنِّي بَرِيءٌ مِّمَّا تُشْرِكُونَ (78) Ndipo pamene adaona dzuwa lili kutuluka, iye adati: “Ili ndilo Ambuye wanga. Ndipo ilo ndi lalikulu koposa.” Koma pamene ilo lidalowa, iye adati: “oh inu anthu anga! Ine ndatalikirana ndi zimene inu mukusakaniza popembedza Mulungu.” |
إِنِّي وَجَّهْتُ وَجْهِيَ لِلَّذِي فَطَرَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ حَنِيفًا ۖ وَمَا أَنَا مِنَ الْمُشْرِكِينَ (79) Ndithudi ine ndayang’anitsa nkhope yanga kwa Iye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Ine sindine mmodzi wa iwo opembedza mafano |
وَحَاجَّهُ قَوْمُهُ ۚ قَالَ أَتُحَاجُّونِّي فِي اللَّهِ وَقَدْ هَدَانِ ۚ وَلَا أَخَافُ مَا تُشْرِكُونَ بِهِ إِلَّا أَن يَشَاءَ رَبِّي شَيْئًا ۗ وَسِعَ رَبِّي كُلَّ شَيْءٍ عِلْمًا ۗ أَفَلَا تَتَذَكَّرُونَ (80) Anthu ake adatsutsana naye ndipo iye adati: “Kodi inu mukutsutsana ndi ine za Mulungu pamene Iye wanditsogolera? Ndipo ine sindiopa mafano anu kupatula ngati Ambuye wanga atafuna chilichonse. Ambuye wanga amadziwa bwino chilichonse. Kodi inu simungakumbukire |
وَكَيْفَ أَخَافُ مَا أَشْرَكْتُمْ وَلَا تَخَافُونَ أَنَّكُمْ أَشْرَكْتُم بِاللَّهِ مَا لَمْ يُنَزِّلْ بِهِ عَلَيْكُمْ سُلْطَانًا ۚ فَأَيُّ الْفَرِيقَيْنِ أَحَقُّ بِالْأَمْنِ ۖ إِن كُنتُمْ تَعْلَمُونَ (81) Ndipo kodi ine ndingaope bwanji milungu yanu yabodza pamene inuyo mulibe mantha pomapembedza mafano amene Mulungu sadakupatseniumboniwake? Kodindaniwamaguluawiriwa amene afuna chitetezo ngati inu mumadziwa?” |
الَّذِينَ آمَنُوا وَلَمْ يَلْبِسُوا إِيمَانَهُم بِظُلْمٍ أُولَٰئِكَ لَهُمُ الْأَمْنُ وَهُم مُّهْتَدُونَ (82) Ndiwo amene ali okhulupirira ndipo sasakaniza chikhulupiriro chawo pochita ntchito zoipa, kwa iwo kuli mtendere ndipo ndi otsogozedwa |
وَتِلْكَ حُجَّتُنَا آتَيْنَاهَا إِبْرَاهِيمَ عَلَىٰ قَوْمِهِ ۚ نَرْفَعُ دَرَجَاتٍ مَّن نَّشَاءُ ۗ إِنَّ رَبَّكَ حَكِيمٌ عَلِيمٌ (83) Chimenechi chinali chizindikiro chathu chimene tidamupatsa Abrahamu kuti agonjetsere anthu ake. Ife timakweza wina aliyense amene tamufuna. Ndithudi Ambuye wako ndi wanzeru ndi wodziwa zinthu zonse |
وَوَهَبْنَا لَهُ إِسْحَاقَ وَيَعْقُوبَ ۚ كُلًّا هَدَيْنَا ۚ وَنُوحًا هَدَيْنَا مِن قَبْلُ ۖ وَمِن ذُرِّيَّتِهِ دَاوُودَ وَسُلَيْمَانَ وَأَيُّوبَ وَيُوسُفَ وَمُوسَىٰ وَهَارُونَ ۚ وَكَذَٰلِكَ نَجْزِي الْمُحْسِنِينَ (84) Ndipo tidamupatsa iye Isake ndi Yakobo, aliyense tidamutsogolera ndipo iye asanadze, tidatsogolera Nowa ndipo pakati pa adzukulu wake Davide, Solomoni, Yobu, Yosefe, Mose ndi Aroni. Motero ndi mmene timalipirira anthu ochita abwino |
وَزَكَرِيَّا وَيَحْيَىٰ وَعِيسَىٰ وَإِلْيَاسَ ۖ كُلٌّ مِّنَ الصَّالِحِينَ (85) Ndi Zakariya, Yohane, Yesu, ndi Eliya, aliyense adali wangwiro |
وَإِسْمَاعِيلَ وَالْيَسَعَ وَيُونُسَ وَلُوطًا ۚ وَكُلًّا فَضَّلْنَا عَلَى الْعَالَمِينَ (86) Ndi Ishimayeli, Elisa, Yona ndi Loti, onsewa tidawalemekeza pakati pa zolengedwa zonse |
وَمِنْ آبَائِهِمْ وَذُرِّيَّاتِهِمْ وَإِخْوَانِهِمْ ۖ وَاجْتَبَيْنَاهُمْ وَهَدَيْنَاهُمْ إِلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (87) Ndiponso makolo awo, ana awo, ndi abale awo Ife tidawasankha ndi kuwatsogolera ku njira yoyenera |
ذَٰلِكَ هُدَى اللَّهِ يَهْدِي بِهِ مَن يَشَاءُ مِنْ عِبَادِهِ ۚ وَلَوْ أَشْرَكُوا لَحَبِطَ عَنْهُم مَّا كَانُوا يَعْمَلُونَ (88) Ichi ndi chilangizo cha Mulungu chimene amalangiza nacho aliyense amene wamufuna wa akapolo ake. Koma iwo akadatumikira milungu ina yoonjezera pa Mulungu m’modzi, ntchito zawo zonse zikadakhala zopanda phindu |
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ آتَيْنَاهُمُ الْكِتَابَ وَالْحُكْمَ وَالنُّبُوَّةَ ۚ فَإِن يَكْفُرْ بِهَا هَٰؤُلَاءِ فَقَدْ وَكَّلْنَا بِهَا قَوْمًا لَّيْسُوا بِهَا بِكَافِرِينَ (89) Awa ndi amene tidawapatsa Buku, chiweruzo ndi Utumwi. Koma ngati awa sakhulupirira mwa ilo, ndithudi Ife tawapatsa iwo amene akhulupilira mwa ilo |
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ هَدَى اللَّهُ ۖ فَبِهُدَاهُمُ اقْتَدِهْ ۗ قُل لَّا أَسْأَلُكُمْ عَلَيْهِ أَجْرًا ۖ إِنْ هُوَ إِلَّا ذِكْرَىٰ لِلْعَالَمِينَ (90) Amenewa ndi anthu amene Mulungu adawatsogolera. Choncho tsatira chilangizo chawo. Nena, “Ine sindili kufuna malipiro chifukwa cha ntchito iyi ayi. Ili ndi chenjezo kwa zolengedwa zonse.” |
وَمَا قَدَرُوا اللَّهَ حَقَّ قَدْرِهِ إِذْ قَالُوا مَا أَنزَلَ اللَّهُ عَلَىٰ بَشَرٍ مِّن شَيْءٍ ۗ قُلْ مَنْ أَنزَلَ الْكِتَابَ الَّذِي جَاءَ بِهِ مُوسَىٰ نُورًا وَهُدًى لِّلنَّاسِ ۖ تَجْعَلُونَهُ قَرَاطِيسَ تُبْدُونَهَا وَتُخْفُونَ كَثِيرًا ۖ وَعُلِّمْتُم مَّا لَمْ تَعْلَمُوا أَنتُمْ وَلَا آبَاؤُكُمْ ۖ قُلِ اللَّهُ ۖ ثُمَّ ذَرْهُمْ فِي خَوْضِهِمْ يَلْعَبُونَ (91) Iwo sadapereke ulemu woyenera Mulungu pamene adati: “Mulungu sadavumbulutse china chilichonse kwa munthu.” Nena, “Kodi ndani yemwe adavumbulutsa Buku limene Mose anabwera nalo, muuni ndi chilangizo kwa anthu onse; amene mwalemba pa mipukutu ya mapepala, kuulula zina ndi kubisa zambiri? Ndipo mudaphunzitsidwa zimene inu ndiponso makolo anu sadazidziwe ndi kale lomwe.” Nena: “Ndi Mulungu.” Ndipo asiye okha kuti abadzisangalatsa ndi nkhani zopusa |
وَهَٰذَا كِتَابٌ أَنزَلْنَاهُ مُبَارَكٌ مُّصَدِّقُ الَّذِي بَيْنَ يَدَيْهِ وَلِتُنذِرَ أُمَّ الْقُرَىٰ وَمَنْ حَوْلَهَا ۚ وَالَّذِينَ يُؤْمِنُونَ بِالْآخِرَةِ يُؤْمِنُونَ بِهِ ۖ وَهُمْ عَلَىٰ صَلَاتِهِمْ يُحَافِظُونَ (92) Ndipo ili ndi Buku lodalitsika limene tavumbulutsa, kuchitira umboni zimene zinadza ilo lisadadze kuti uchenjeze Mzinda wa Makka ndi iwo amene amakhala mouzungulira. Iwo amene ali ndi chikhulupiriro mu zamoyo umene uli nkudza amakhulupirira ilo ndipo amasamala kwambiri m’mapemphero awo |
وَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّنِ افْتَرَىٰ عَلَى اللَّهِ كَذِبًا أَوْ قَالَ أُوحِيَ إِلَيَّ وَلَمْ يُوحَ إِلَيْهِ شَيْءٌ وَمَن قَالَ سَأُنزِلُ مِثْلَ مَا أَنزَلَ اللَّهُ ۗ وَلَوْ تَرَىٰ إِذِ الظَّالِمُونَ فِي غَمَرَاتِ الْمَوْتِ وَالْمَلَائِكَةُ بَاسِطُو أَيْدِيهِمْ أَخْرِجُوا أَنفُسَكُمُ ۖ الْيَوْمَ تُجْزَوْنَ عَذَابَ الْهُونِ بِمَا كُنتُمْ تَقُولُونَ عَلَى اللَّهِ غَيْرَ الْحَقِّ وَكُنتُمْ عَنْ آيَاتِهِ تَسْتَكْبِرُونَ (93) Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa iye amene amapeka bodza lonamizira Mulungu kapena amati: “Ine ndalandira chibvumbulutso pamene sichidavumbulutsidwe kwa iye chilichonse?” Kapena munthu amene amati: “Ine ndikhoza kuvumbulutsa zinthu zofanana ndi zimene Mulungu wavumbulutsa?” Ndipo iwe ukadangoona anthu ochimwa pamene ali kufa ndi pamene angelo ali kutambasula manja awo akuti: “Perekani mizimu yanu. Inu mudzalipidwa mphotho yochititsa manyazi lero chifukwa cha zimene munali kunena zabodza zokhudza Mulungu. Ndiponso inu munali kukana chivumbulutso chake mwa mwano.” |
وَلَقَدْ جِئْتُمُونَا فُرَادَىٰ كَمَا خَلَقْنَاكُمْ أَوَّلَ مَرَّةٍ وَتَرَكْتُم مَّا خَوَّلْنَاكُمْ وَرَاءَ ظُهُورِكُمْ ۖ وَمَا نَرَىٰ مَعَكُمْ شُفَعَاءَكُمُ الَّذِينَ زَعَمْتُمْ أَنَّهُمْ فِيكُمْ شُرَكَاءُ ۚ لَقَد تَّقَطَّعَ بَيْنَكُمْ وَضَلَّ عَنكُم مَّا كُنتُمْ تَزْعُمُونَ (94) “Ndipo, ndithudi, mwadza kwa Ife, nokha, monga momwe tidakulengerani inu poyamba. Inu mwasiya zonse zimene tidakupatsani kumbuyo kwanu. Ndiponso Ife sitili kuona pamodzi ndi inu zimene mumazipembedza, zija mumati ndi zofanana ndi Mulungu. Tsopano ubale wonse umene umakugwirizitsani waduka ndipo zonse zimene mumaziganizira kuti zingakuthandizeni zakuthawirani.” |
۞ إِنَّ اللَّهَ فَالِقُ الْحَبِّ وَالنَّوَىٰ ۖ يُخْرِجُ الْحَيَّ مِنَ الْمَيِّتِ وَمُخْرِجُ الْمَيِّتِ مِنَ الْحَيِّ ۚ ذَٰلِكُمُ اللَّهُ ۖ فَأَنَّىٰ تُؤْفَكُونَ (95) Ndithudi! Ndi Mulungu amene amasiyanitsa mbewu ndi khoko lake kuti imere. Iye amatulutsa chamoyo kuchokera mu chakufa ndipo ndiye amatulutsa chakufa kuchokera ku chamoyo. Ameneyo ndiye Mulungu, nanga ndi chifukwa chiyani mukusokera kusiya choonadi |
فَالِقُ الْإِصْبَاحِ وَجَعَلَ اللَّيْلَ سَكَنًا وَالشَّمْسَ وَالْقَمَرَ حُسْبَانًا ۚ ذَٰلِكَ تَقْدِيرُ الْعَزِيزِ الْعَلِيمِ (96) Iye amadzetsa kuwala kwa m’mawa. Ndipo Iye waika usiku kuti ikhale nthawi yopumula, dzuwa ndi mwezi kuti zikhale zothandiza kuwerengera; umenewo ndiwo muyeso wa Mwini mphamvu zonse ndi wodziwa chilichonse |
وَهُوَ الَّذِي جَعَلَ لَكُمُ النُّجُومَ لِتَهْتَدُوا بِهَا فِي ظُلُمَاتِ الْبَرِّ وَالْبَحْرِ ۗ قَدْ فَصَّلْنَا الْآيَاتِ لِقَوْمٍ يَعْلَمُونَ (97) Iye ndiye amene adakulengerani nyenyezi kuti zizikutsogolerani mu mdima wa pa mtunda ndi pa nyanja. Ife tafotokoza chivumbulutso kwa anthu odziwa kwambiri |
وَهُوَ الَّذِي أَنشَأَكُم مِّن نَّفْسٍ وَاحِدَةٍ فَمُسْتَقَرٌّ وَمُسْتَوْدَعٌ ۗ قَدْ فَصَّلْنَا الْآيَاتِ لِقَوْمٍ يَفْقَهُونَ (98) Iye ndiye amene adakulengani inu kuchokera kwa munthu mmodzi ndipo adakupatsani malo okhalamo ndi osungidwa. Ife ndithudi tafotokoza chivumbulutso chathu kwa anthu omvetsa |
وَهُوَ الَّذِي أَنزَلَ مِنَ السَّمَاءِ مَاءً فَأَخْرَجْنَا بِهِ نَبَاتَ كُلِّ شَيْءٍ فَأَخْرَجْنَا مِنْهُ خَضِرًا نُّخْرِجُ مِنْهُ حَبًّا مُّتَرَاكِبًا وَمِنَ النَّخْلِ مِن طَلْعِهَا قِنْوَانٌ دَانِيَةٌ وَجَنَّاتٍ مِّنْ أَعْنَابٍ وَالزَّيْتُونَ وَالرُّمَّانَ مُشْتَبِهًا وَغَيْرَ مُتَشَابِهٍ ۗ انظُرُوا إِلَىٰ ثَمَرِهِ إِذَا أَثْمَرَ وَيَنْعِهِ ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكُمْ لَآيَاتٍ لِّقَوْمٍ يُؤْمِنُونَ (99) Iye ndiye amene amatumiza mvula kuchokera kumwamba ndipo ndi iyo, Ife timameretsa mbewu zosiyana siyana ndipo kuchokera ku izo timatulutsa mphesi za ziwisi zimene zimabereka mbeu mothinana. Ndipo kuchokera ku mitengo ya tende kumadza zipatso za tende zotsika pansi, minda ya mphesa ndi mitengo ya mafuta ya azitona, chimanga cha chizungu, zipatso zofanana koma zosiyanasiyana. Taonani zipatso zake pamene zili kubereka, kukhwima ndi kumapsya. Ndithudi! Mu izi muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira |
وَجَعَلُوا لِلَّهِ شُرَكَاءَ الْجِنَّ وَخَلَقَهُمْ ۖ وَخَرَقُوا لَهُ بَنِينَ وَبَنَاتٍ بِغَيْرِ عِلْمٍ ۚ سُبْحَانَهُ وَتَعَالَىٰ عَمَّا يَصِفُونَ (100) Komabe iwo amasankha majini kukhala milungu kuonjezera pa Mulungu weniweni ngakhale kuti Iye ndiye amene anawalenga ndipo amamunamizira Mulungu kuti ali ndi ana amuna ndi akazi. Ulemerero ukhale kwa Iye! Alemekezeke Iye koposa zonse zimene akunena |
بَدِيعُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ أَنَّىٰ يَكُونُ لَهُ وَلَدٌ وَلَمْ تَكُن لَّهُ صَاحِبَةٌ ۖ وَخَلَقَ كُلَّ شَيْءٍ ۖ وَهُوَ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (101) Iye ndi Namalenga wa kumwamba ndi dziko lapansi. Kodi Iye angakhale ndi ana bwanji pamene Iye alibe mkazi? Iye adalenga zinthu zonse ndipo amadziwa chilichonse |
ذَٰلِكُمُ اللَّهُ رَبُّكُمْ ۖ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۖ خَالِقُ كُلِّ شَيْءٍ فَاعْبُدُوهُ ۚ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ وَكِيلٌ (102) Ameneyo ndiye Mulungu, Ambuye wanu. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha, Namalenga wa zinthu zonse. Motero mpembedzeni Iye yekha. Iye ndiye wosamalira zinthu zonse |
لَّا تُدْرِكُهُ الْأَبْصَارُ وَهُوَ يُدْرِكُ الْأَبْصَارَ ۖ وَهُوَ اللَّطِيفُ الْخَبِيرُ (103) Palibe amene angamuone Iye koma Iye amaona chili chonse. Iye ndiye wachifundo ndipo amadziwa zonse |
قَدْ جَاءَكُم بَصَائِرُ مِن رَّبِّكُمْ ۖ فَمَنْ أَبْصَرَ فَلِنَفْسِهِ ۖ وَمَنْ عَمِيَ فَعَلَيْهَا ۚ وَمَا أَنَا عَلَيْكُم بِحَفِيظٍ (104) Ndithudi zizindikiro zonse zadza kwa inu kuchokera kwa Ambuye wanu ndipo aliyense amene aona zidzampindulira iye koma aliyense amene ali wakhungu adzalephera yekha ndipo ine sindine wokuyang’anirani |
وَكَذَٰلِكَ نُصَرِّفُ الْآيَاتِ وَلِيَقُولُوا دَرَسْتَ وَلِنُبَيِّنَهُ لِقَوْمٍ يَعْلَمُونَ (105) Motero Ife timafotokoza chivumbulutso chathu, kuti iwo anene kuti: “Iwe waphunzira” ndi kuti tifotokoze momveka kwa anthu ozindikira |
اتَّبِعْ مَا أُوحِيَ إِلَيْكَ مِن رَّبِّكَ ۖ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۖ وَأَعْرِضْ عَنِ الْمُشْرِكِينَ (106) Choncho tsatira zonse zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha ndipo alewe anthu osakhulupirira |
وَلَوْ شَاءَ اللَّهُ مَا أَشْرَكُوا ۗ وَمَا جَعَلْنَاكَ عَلَيْهِمْ حَفِيظًا ۖ وَمَا أَنتَ عَلَيْهِم بِوَكِيلٍ (107) Ngati Mulungu akadafuna, iwo sakanapembedza mafano. Ndipo Ife sitikadakusankha iwe kukhala owayang’anira ayi ndiponso iwe sindiwe wowasamalira wawo |
وَلَا تَسُبُّوا الَّذِينَ يَدْعُونَ مِن دُونِ اللَّهِ فَيَسُبُّوا اللَّهَ عَدْوًا بِغَيْرِ عِلْمٍ ۗ كَذَٰلِكَ زَيَّنَّا لِكُلِّ أُمَّةٍ عَمَلَهُمْ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّهِم مَّرْجِعُهُمْ فَيُنَبِّئُهُم بِمَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (108) Ndipo musatukwane iwo amene amapembedza mafano poonjezera pa Mulungu weniweni kuti mwina iwo angathe kutukwana Mulungu molakwa ndi mwa umbuli. Motero tazipanga zochita zawo kukhala zosangalatsa ndipo ndi kwa Ambuye wawo kumene onse adzabwerera ndipo Iye adzawauza iwo zonse zimene anali kuchita |
وَأَقْسَمُوا بِاللَّهِ جَهْدَ أَيْمَانِهِمْ لَئِن جَاءَتْهُمْ آيَةٌ لَّيُؤْمِنُنَّ بِهَا ۚ قُلْ إِنَّمَا الْآيَاتُ عِندَ اللَّهِ ۖ وَمَا يُشْعِرُكُمْ أَنَّهَا إِذَا جَاءَتْ لَا يُؤْمِنُونَ (109) Ndipo iwo amalumbira pali Mulungu motsindika kuti ngati chizindikiro chitaperekedwa kwa iwo, iwo adzachikhulupirira. Nena, “Ndithudi zizindikiro zonse zili ndi Mulungu ndipo kodi inu mungadziwe bwanji ngati chidza kwa iwo kuti iwo sadzachikhulupirira?” |
وَنُقَلِّبُ أَفْئِدَتَهُمْ وَأَبْصَارَهُمْ كَمَا لَمْ يُؤْمِنُوا بِهِ أَوَّلَ مَرَّةٍ وَنَذَرُهُمْ فِي طُغْيَانِهِمْ يَعْمَهُونَ (110) Ndipo Ife tidzatembenuza mitima yawo ndi maso awo monga mmene adakana kukhulupirira nthawi yoyamba ndipo Ife tidzawasiya mukusochera kwawo akusowa chochita |
۞ وَلَوْ أَنَّنَا نَزَّلْنَا إِلَيْهِمُ الْمَلَائِكَةَ وَكَلَّمَهُمُ الْمَوْتَىٰ وَحَشَرْنَا عَلَيْهِمْ كُلَّ شَيْءٍ قُبُلًا مَّا كَانُوا لِيُؤْمِنُوا إِلَّا أَن يَشَاءَ اللَّهُ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ يَجْهَلُونَ (111) Ngakhale Ife tikadawatumizira iwo angelo ndi kupangaanthuakufakutialankhulenawondikusonkhanitsa zinthu zonse pamaso pawo, iwo sakadakhulupirirabe pokhapokha ngati Mulungu afuna koma ambiri a iwo ndi anthu osadziwa |
وَكَذَٰلِكَ جَعَلْنَا لِكُلِّ نَبِيٍّ عَدُوًّا شَيَاطِينَ الْإِنسِ وَالْجِنِّ يُوحِي بَعْضُهُمْ إِلَىٰ بَعْضٍ زُخْرُفَ الْقَوْلِ غُرُورًا ۚ وَلَوْ شَاءَ رَبُّكَ مَا فَعَلُوهُ ۖ فَذَرْهُمْ وَمَا يَفْتَرُونَ (112) Kotero Ife tidakhazikitsa mdani kwa Mtumwi aliyense. A satana amene ali pakati pa anthu ndi majini, amene amauzana wina ndi mnzake mawu okoma ndiponso a chinyengo. Koma Ambuye wako akadafuna, iwo sakadachita zotero ayi motero asiyeni okha ndi zimene akupeka |
وَلِتَصْغَىٰ إِلَيْهِ أَفْئِدَةُ الَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ بِالْآخِرَةِ وَلِيَرْضَوْهُ وَلِيَقْتَرِفُوا مَا هُم مُّقْتَرِفُونَ (113) Kuti mitima ya anthu amene sakhulupirira m’moyo umene uli nkudza ipendekere kuzolankhula zawo ndipo kuti azitsatira zimene apeka okha ndi kumasangalala kuti mwina akhoza kuchita zimene ali nkuchita |
أَفَغَيْرَ اللَّهِ أَبْتَغِي حَكَمًا وَهُوَ الَّذِي أَنزَلَ إِلَيْكُمُ الْكِتَابَ مُفَصَّلًا ۚ وَالَّذِينَ آتَيْنَاهُمُ الْكِتَابَ يَعْلَمُونَ أَنَّهُ مُنَزَّلٌ مِّن رَّبِّكَ بِالْحَقِّ ۖ فَلَا تَكُونَنَّ مِنَ الْمُمْتَرِينَ (114) “Kodi ine ndifune wina woweruza oposa Mulungu pamene ndiye amene adavumbulutsa Korani kwa inu ndi malamulo ofotokozedwa bwino?” Iwo amene tidawapatsa Mau athu amadziwa kuti lidavumbulutsidwa kuchokera kwa Ambuye wako mwa choonadi. Motero usakhale mmodzi wa anthu okaika |
وَتَمَّتْ كَلِمَتُ رَبِّكَ صِدْقًا وَعَدْلًا ۚ لَّا مُبَدِّلَ لِكَلِمَاتِهِ ۚ وَهُوَ السَّمِيعُ الْعَلِيمُ (115) Ndipo Mau a Ambuye wako akwaniritsidwa moona ndi mwachilungamo. Palibe wina amene angasinthe Mau ake. Iye amamva ndipo ndi wozindikira chili chonse |
وَإِن تُطِعْ أَكْثَرَ مَن فِي الْأَرْضِ يُضِلُّوكَ عَن سَبِيلِ اللَّهِ ۚ إِن يَتَّبِعُونَ إِلَّا الظَّنَّ وَإِنْ هُمْ إِلَّا يَخْرُصُونَ (116) Ndipo ngati iwe umvera zonena za anthu ambiri apa dziko lapansi iwo adzakusocheza ku njira ya Mulungu. Iwo satsatira chilichonse koma nkhani zongoganiza chabe ndipo sachita china chilichonse koma kunama |
إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعْلَمُ مَن يَضِلُّ عَن سَبِيلِهِ ۖ وَهُوَ أَعْلَمُ بِالْمُهْتَدِينَ (117) Ndithudi Ambuye wako! Ndiye amene amadziwa anthu onse amene amasochera ku njira yake ndiponso Iye amadziwa iwo amene atsogozedwa bwino bwino |
فَكُلُوا مِمَّا ذُكِرَ اسْمُ اللَّهِ عَلَيْهِ إِن كُنتُم بِآيَاتِهِ مُؤْمِنِينَ (118) Motero idyani nyama yokhayo imene yaphedwa m’dzina la Mulungu ngati inu mukhulupiriradi mu chivumbulutso chake |
وَمَا لَكُمْ أَلَّا تَأْكُلُوا مِمَّا ذُكِرَ اسْمُ اللَّهِ عَلَيْهِ وَقَدْ فَصَّلَ لَكُم مَّا حَرَّمَ عَلَيْكُمْ إِلَّا مَا اضْطُرِرْتُمْ إِلَيْهِ ۗ وَإِنَّ كَثِيرًا لَّيُضِلُّونَ بِأَهْوَائِهِم بِغَيْرِ عِلْمٍ ۗ إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعْلَمُ بِالْمُعْتَدِينَ (119) Kodi inu simungadye bwanji nyama imene yaphedwa m’dzina la Mulungu pamene Iye adaulula poyera zimene adakuletsani pokhapokha ngati mwasimidwa? Ndithudi ambiri amasochera potsatira zilako lako zawo mwa umbuli. Ndithudi Ambuye wako amadziwa onse oswa malamulo |
وَذَرُوا ظَاهِرَ الْإِثْمِ وَبَاطِنَهُ ۚ إِنَّ الَّذِينَ يَكْسِبُونَ الْإِثْمَ سَيُجْزَوْنَ بِمَا كَانُوا يَقْتَرِفُونَ (120) Pewa machimo oonekera kapena obisika. Ndithudi iwo amene amachita zoipa adzalangidwa chifukwa cha zoipa zawo |
وَلَا تَأْكُلُوا مِمَّا لَمْ يُذْكَرِ اسْمُ اللَّهِ عَلَيْهِ وَإِنَّهُ لَفِسْقٌ ۗ وَإِنَّ الشَّيَاطِينَ لَيُوحُونَ إِلَىٰ أَوْلِيَائِهِمْ لِيُجَادِلُوكُمْ ۖ وَإِنْ أَطَعْتُمُوهُمْ إِنَّكُمْ لَمُشْرِكُونَ (121) Musadye nyama iliyonse imene sidaphedwe m’dzina la Mulungu chifukwa kutero ndi kulakwa. Ndithudi a Satana amaphunzitsa anthu awo kuti azikangana ndi inu ndipo ngati inu muwamvera, ndithudi, nanunso mudzakhala opembedza mafano |
أَوَمَن كَانَ مَيْتًا فَأَحْيَيْنَاهُ وَجَعَلْنَا لَهُ نُورًا يَمْشِي بِهِ فِي النَّاسِ كَمَن مَّثَلُهُ فِي الظُّلُمَاتِ لَيْسَ بِخَارِجٍ مِّنْهَا ۚ كَذَٰلِكَ زُيِّنَ لِلْكَافِرِينَ مَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (122) Kodi munthu amene adafa, ndipo tamuukitsa kwa akufa ndipo wapatsidwa kuwala kumene kukhoza kumutsogolera pakati pa anthu, angafanizidwe ndi iye amene ali kusochera mumdima umene sadzatulukamo? Chomwecho zimakongoletsedwa kwa anthu osakhulupirira zimene adali kuchita |
وَكَذَٰلِكَ جَعَلْنَا فِي كُلِّ قَرْيَةٍ أَكَابِرَ مُجْرِمِيهَا لِيَمْكُرُوا فِيهَا ۖ وَمَا يَمْكُرُونَ إِلَّا بِأَنفُسِهِمْ وَمَا يَشْعُرُونَ (123) Motero Ife tidakhazikitsa mu Mzinda uliwonse atsogoleri a anthu olakwa kwambiri amene amakonza njira zoswera malamulo m’kati mwa Mzindawo. Koma iwo amakonza njira zoti zibweretse chiwonongeko pa iwo eni ndipo iwo sadziwa |
وَإِذَا جَاءَتْهُمْ آيَةٌ قَالُوا لَن نُّؤْمِنَ حَتَّىٰ نُؤْتَىٰ مِثْلَ مَا أُوتِيَ رُسُلُ اللَّهِ ۘ اللَّهُ أَعْلَمُ حَيْثُ يَجْعَلُ رِسَالَتَهُ ۗ سَيُصِيبُ الَّذِينَ أَجْرَمُوا صَغَارٌ عِندَ اللَّهِ وَعَذَابٌ شَدِيدٌ بِمَا كَانُوا يَمْكُرُونَ (124) Ndipo pamene zizindikiro ziwafikira iwo amati: “Ife sitidzakhulupirira mu ichi pokhapokha ngati tipatsidwa chimene Atumwi a Mulungu adapatsidwa.” Mulungu amadziwa bwino ndani amene akhoza kumupatsa uthenga wake. Kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi kochokera kwa Mulungu ndiponso chilango chowawa chidzadza pa anthu oipa chifukwa cha zimene anali kuchita |
فَمَن يُرِدِ اللَّهُ أَن يَهْدِيَهُ يَشْرَحْ صَدْرَهُ لِلْإِسْلَامِ ۖ وَمَن يُرِدْ أَن يُضِلَّهُ يَجْعَلْ صَدْرَهُ ضَيِّقًا حَرَجًا كَأَنَّمَا يَصَّعَّدُ فِي السَّمَاءِ ۚ كَذَٰلِكَ يَجْعَلُ اللَّهُ الرِّجْسَ عَلَى الَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ (125) Ndipo aliyense amene Mulungu afuna kumutsogolera, Iye amatsegula mtima wake kuti akhale Msilamu ndipo aliyense amene Iye afuna kumusocheretsa, Iye amachititsa mtima wake kukhala opapatizika ndi ovutika ngati kuti akukwera kumwamba. Mmenemo ndi mmene Mulungu amaikira mkwiyo pa anthu osakhulupirira |
وَهَٰذَا صِرَاطُ رَبِّكَ مُسْتَقِيمًا ۗ قَدْ فَصَّلْنَا الْآيَاتِ لِقَوْمٍ يَذَّكَّرُونَ (126) Iyi ndi njira ya Ambuye wako, yoyenera. Ife tafotokoza chivumbulutso kwa anthu oganizira |
۞ لَهُمْ دَارُ السَّلَامِ عِندَ رَبِّهِمْ ۖ وَهُوَ وَلِيُّهُم بِمَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (127) Kwa iwo kudzakhala nyumba ya mtendere imene ili ndi Ambuye wawo. Iye adzakhala Mtetezi wawo chifukwa cha zimene anali kuchita |
وَيَوْمَ يَحْشُرُهُمْ جَمِيعًا يَا مَعْشَرَ الْجِنِّ قَدِ اسْتَكْثَرْتُم مِّنَ الْإِنسِ ۖ وَقَالَ أَوْلِيَاؤُهُم مِّنَ الْإِنسِ رَبَّنَا اسْتَمْتَعَ بَعْضُنَا بِبَعْضٍ وَبَلَغْنَا أَجَلَنَا الَّذِي أَجَّلْتَ لَنَا ۚ قَالَ النَّارُ مَثْوَاكُمْ خَالِدِينَ فِيهَا إِلَّا مَا شَاءَ اللَّهُ ۗ إِنَّ رَبَّكَ حَكِيمٌ عَلِيمٌ (128) Ndipo patsiku limene adzawasonkhanitsa onse, ndi kuti: “oh inu gulu la majini! Inu mudali kusokeletsa anthu mu unyinji wawo.” Ndipo anzawo ochokera m’gulu la anthu adzati: “Ambuye ife tidapindula kuchokera kwa wina ndi mnzake, koma tsopano tafika pa mapeto ya nthawi yathu imene mudatikhazikitsira ife.” Mulungu adzati: “Kumoto ndiko kumalo kwanu ndipo kumeneko mukakhala mpaka kalekale kufikira pamene Mulungu adzafuna.” Ndithudi Ambuye wako ndi Wanzeru ndi Wozindikira |
وَكَذَٰلِكَ نُوَلِّي بَعْضَ الظَّالِمِينَ بَعْضًا بِمَا كَانُوا يَكْسِبُونَ (129) Ndipo motero ndi mmene timapangira anthu olakwa kuthandizana wina ndi mzake chifukwa cha zimene anali kuchita |
يَا مَعْشَرَ الْجِنِّ وَالْإِنسِ أَلَمْ يَأْتِكُمْ رُسُلٌ مِّنكُمْ يَقُصُّونَ عَلَيْكُمْ آيَاتِي وَيُنذِرُونَكُمْ لِقَاءَ يَوْمِكُمْ هَٰذَا ۚ قَالُوا شَهِدْنَا عَلَىٰ أَنفُسِنَا ۖ وَغَرَّتْهُمُ الْحَيَاةُ الدُّنْيَا وَشَهِدُوا عَلَىٰ أَنفُسِهِمْ أَنَّهُمْ كَانُوا كَافِرِينَ (130) Inu gulu la majini ndi anthu! “Kodi sikudadze kwa inu Atumwi a mtundu wanu amene adali kukuuzani za zizindikiro zanga ndi kuchenjeza za kukumana kwa tsiku lanuli?” Iwo adzayankha, “Ife tidzichitira umboni wodzitsutsa tokha.” Ndi moyo wa dziko lino lapansi umene udawanyenga. Ndipo iwo adzadzichitira umboni okha kuti iwo adali osakhulupirira |
ذَٰلِكَ أَن لَّمْ يَكُن رَّبُّكَ مُهْلِكَ الْقُرَىٰ بِظُلْمٍ وَأَهْلُهَا غَافِلُونَ (131) Ichi ndi chifukwa chakuti Ambuye wako samaononga Mizinda chifukwa cha zochita zawo, pamene anthu ake sadali kudziwa |
وَلِكُلٍّ دَرَجَاتٌ مِّمَّا عَمِلُوا ۚ وَمَا رَبُّكَ بِغَافِلٍ عَمَّا يَعْمَلُونَ (132) Kwa aliyense kudzaperekedwa gawo molingana ndi zimene adachita. Sikuti Ambuye wako sadziwa zimene iwo achita |
وَرَبُّكَ الْغَنِيُّ ذُو الرَّحْمَةِ ۚ إِن يَشَأْ يُذْهِبْكُمْ وَيَسْتَخْلِفْ مِن بَعْدِكُم مَّا يَشَاءُ كَمَا أَنشَأَكُم مِّن ذُرِّيَّةِ قَوْمٍ آخَرِينَ (133) Ambuye wako ndi wolemera ndiponso ndi wachisoni ndipo ngati Iye afuna, akhoza kukuonongani ndi kuika m’malo mwanu ena amene Iye wafuna monga momwe Iye adakulengerani inu kuchokera ku mbeu ya anthu ena |
إِنَّ مَا تُوعَدُونَ لَآتٍ ۖ وَمَا أَنتُم بِمُعْجِزِينَ (134) Ndithudi chimene inu mukulonjezedwa chidzachitika ndipo inu simungachizembe ayi |
قُلْ يَا قَوْمِ اعْمَلُوا عَلَىٰ مَكَانَتِكُمْ إِنِّي عَامِلٌ ۖ فَسَوْفَ تَعْلَمُونَ مَن تَكُونُ لَهُ عَاقِبَةُ الدَّارِ ۗ إِنَّهُ لَا يُفْلِحُ الظَّالِمُونَ (135) Nena, “oh anthu anga! Chitani chimene mungachite, ndithudi, nanenso ndili kuchita chimene ndimachita ndipo inu mudzadziwa kuti ndani wa ife amene adzakhala ndi mapeto abwino m’moyo umene uli nkudza. Ndithudi anthu olakwa sadzapambana.” |
وَجَعَلُوا لِلَّهِ مِمَّا ذَرَأَ مِنَ الْحَرْثِ وَالْأَنْعَامِ نَصِيبًا فَقَالُوا هَٰذَا لِلَّهِ بِزَعْمِهِمْ وَهَٰذَا لِشُرَكَائِنَا ۖ فَمَا كَانَ لِشُرَكَائِهِمْ فَلَا يَصِلُ إِلَى اللَّهِ ۖ وَمَا كَانَ لِلَّهِ فَهُوَ يَصِلُ إِلَىٰ شُرَكَائِهِمْ ۗ سَاءَ مَا يَحْكُمُونَ (136) Ndipo iwo amaika pa mbali gawo la mbewu ndi gawo la ziweto kuti ndi za Mulungu ndipo amati: “Izi ndi za Mulungu pamene izi ndi za mafano athu.” Koma gawo limene amati ndi la mafano awo silifika kwa Mulungu ayi pamene gawo la Mulungu limafika lonse kwa mafano awo! Chiweruzo chawo ndi choipa kwambiri |
وَكَذَٰلِكَ زَيَّنَ لِكَثِيرٍ مِّنَ الْمُشْرِكِينَ قَتْلَ أَوْلَادِهِمْ شُرَكَاؤُهُمْ لِيُرْدُوهُمْ وَلِيَلْبِسُوا عَلَيْهِمْ دِينَهُمْ ۖ وَلَوْ شَاءَ اللَّهُ مَا فَعَلُوهُ ۖ فَذَرْهُمْ وَمَا يَفْتَرُونَ (137) Motero kwa anthu opembedza mafano, mafano awo adapangitsa kupha ana awo kukhala chinthu chokondweretsa ndi cholinga chakuti awawononge iwo ndi kuwasokonezera chipembedzo chawo. Koma ngati Mulungu akadafuna, iwo sakadachita choncho. Motero asiyeni okha ndi zimene akupeka |
وَقَالُوا هَٰذِهِ أَنْعَامٌ وَحَرْثٌ حِجْرٌ لَّا يَطْعَمُهَا إِلَّا مَن نَّشَاءُ بِزَعْمِهِمْ وَأَنْعَامٌ حُرِّمَتْ ظُهُورُهَا وَأَنْعَامٌ لَّا يَذْكُرُونَ اسْمَ اللَّهِ عَلَيْهَا افْتِرَاءً عَلَيْهِ ۚ سَيَجْزِيهِم بِمَا كَانُوا يَفْتَرُونَ (138) Potsatira zofuna zawo, iwo amati: “Nyama izi ndiponso mbewu izi ndi zoletsedwa ndipo palibe munthu amene adye kupatula okhawo amene tawaloleza.” Ndipo pali nyama zina zimene amaletsa anthu kuti asakwere kapena kugwira ntchito, ndi zina zimene satchulapo dzina la Mulungu komwe ndi kumunamizira Iye. Mulungu adzawalipira chifukwa cha mabodza awo amene amapeka |
وَقَالُوا مَا فِي بُطُونِ هَٰذِهِ الْأَنْعَامِ خَالِصَةٌ لِّذُكُورِنَا وَمُحَرَّمٌ عَلَىٰ أَزْوَاجِنَا ۖ وَإِن يَكُن مَّيْتَةً فَهُمْ فِيهِ شُرَكَاءُ ۚ سَيَجْزِيهِمْ وَصْفَهُمْ ۚ إِنَّهُ حَكِيمٌ عَلِيمٌ (139) Ndipo iwo amati: “Zam’kati zanyamazi ndi zololedwa kudyedwa ndi anthu athu amuna okha ndipo ndi zoletsedwa kwa anthu a akazi koma ngati izo zibadwa zakufa onse amagawana. Mulungu adzawalanga chifukwa cha zonse zimene amamunamizira Iye. Ndithudi Iye ndi Wanzeru ndi Wodziwa.” |
قَدْ خَسِرَ الَّذِينَ قَتَلُوا أَوْلَادَهُمْ سَفَهًا بِغَيْرِ عِلْمٍ وَحَرَّمُوا مَا رَزَقَهُمُ اللَّهُ افْتِرَاءً عَلَى اللَّهِ ۚ قَدْ ضَلُّوا وَمَا كَانُوا مُهْتَدِينَ (140) Ndithudi olephera ndi amene, adapha ana awo mwaumbuli ndipo adaletsa zinthu zimene Mulungu adawapatsa iwo ndi kupeka bodza lokhudza Mulungu. Ndithudi iwo asokera ndipo siotsogozedwa |
۞ وَهُوَ الَّذِي أَنشَأَ جَنَّاتٍ مَّعْرُوشَاتٍ وَغَيْرَ مَعْرُوشَاتٍ وَالنَّخْلَ وَالزَّرْعَ مُخْتَلِفًا أُكُلُهُ وَالزَّيْتُونَ وَالرُّمَّانَ مُتَشَابِهًا وَغَيْرَ مُتَشَابِهٍ ۚ كُلُوا مِن ثَمَرِهِ إِذَا أَثْمَرَ وَآتُوا حَقَّهُ يَوْمَ حَصَادِهِ ۖ وَلَا تُسْرِفُوا ۚ إِنَّهُ لَا يُحِبُّ الْمُسْرِفِينَ (141) Iye ndiye amene amapanga minda ya mbewu za mitundumitundu; zoyanga ndi zosayanga, mitengo ya tende ndi mbeu zosiyanasiyana kukoma kwake, azitona ndi chimanga cha chizungu zofanana ndi zosiyana. Idyani zipatso zake pamene zibereka ndipo perekani chaulere chake nthawi yake. Koma musawononge ayi. Ndithudi Mulungu sakonda anthu owononga |
وَمِنَ الْأَنْعَامِ حَمُولَةً وَفَرْشًا ۚ كُلُوا مِمَّا رَزَقَكُمُ اللَّهُ وَلَا تَتَّبِعُوا خُطُوَاتِ الشَّيْطَانِ ۚ إِنَّهُ لَكُمْ عَدُوٌّ مُّبِينٌ (142) Ndipo pakati pa nyama, pali zina zonyamula katundu ndi zina zosanyamula katundu. Idyani zimene Mulungu wakupatsani ndipo musatsatire mapazi a Satana ayi. Ndithudi iye ndi mdani wooneka |
ثَمَانِيَةَ أَزْوَاجٍ ۖ مِّنَ الضَّأْنِ اثْنَيْنِ وَمِنَ الْمَعْزِ اثْنَيْنِ ۗ قُلْ آلذَّكَرَيْنِ حَرَّمَ أَمِ الْأُنثَيَيْنِ أَمَّا اشْتَمَلَتْ عَلَيْهِ أَرْحَامُ الْأُنثَيَيْنِ ۖ نَبِّئُونِي بِعِلْمٍ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (143) Tengani ng’ombe zisanu ndi zitatu, ndi nkhosa ziwiri, ndi mbuzi ziwiri. Nena, “Kodi Iye adaletsa zazimuna ziwiri kapena zazikazi ziwiri kapena ana amene ali m’mimba? Ndiyankheni mozindikira ngati mukunena zoona.” |
وَمِنَ الْإِبِلِ اثْنَيْنِ وَمِنَ الْبَقَرِ اثْنَيْنِ ۗ قُلْ آلذَّكَرَيْنِ حَرَّمَ أَمِ الْأُنثَيَيْنِ أَمَّا اشْتَمَلَتْ عَلَيْهِ أَرْحَامُ الْأُنثَيَيْنِ ۖ أَمْ كُنتُمْ شُهَدَاءَ إِذْ وَصَّاكُمُ اللَّهُ بِهَٰذَا ۚ فَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّنِ افْتَرَىٰ عَلَى اللَّهِ كَذِبًا لِّيُضِلَّ النَّاسَ بِغَيْرِ عِلْمٍ ۗ إِنَّ اللَّهَ لَا يَهْدِي الْقَوْمَ الظَّالِمِينَ (144) Ndipo kuchokera ku ngamira, ziwiri ndi ng’ombe ziwiri. Nena, “Kodi Iye adaletsa zazimuna ziwiri kapena zazikazi ziwiri kapena ana amene ali m’mimba mwawo? Kodi mudalipo pamene Mulungu adakupatsani malamulo awa? Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu ndi kusocheretsa anthu popanda kuzindikira? Ndithudi Mulungu satsogolera anthu ochita zoipa.” |
قُل لَّا أَجِدُ فِي مَا أُوحِيَ إِلَيَّ مُحَرَّمًا عَلَىٰ طَاعِمٍ يَطْعَمُهُ إِلَّا أَن يَكُونَ مَيْتَةً أَوْ دَمًا مَّسْفُوحًا أَوْ لَحْمَ خِنزِيرٍ فَإِنَّهُ رِجْسٌ أَوْ فِسْقًا أُهِلَّ لِغَيْرِ اللَّهِ بِهِ ۚ فَمَنِ اضْطُرَّ غَيْرَ بَاغٍ وَلَا عَادٍ فَإِنَّ رَبَّكَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (145) Nena, “Ine sindipeza china chilichonse mu zimene zavumbulutsidwa kwa ine choletsa aliyense kudya chakudya china chilichonse kupatula nyama yofa yokha kapena liwende kapena nyama ya nkhumba, chifukwa zimenezo ndi zauve ndi zodetsedwa kapena nyama ina iliyonse imene yaphedwa osati mu dzina la Mulungu. Koma aliyense amene waumirizidwa kudya chilichonse cha izi, osati mokondweretsedwa kapena ndi cholinga chofuna kuswa malamulo, ndithudi, Ambuye wako ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha.” |
وَعَلَى الَّذِينَ هَادُوا حَرَّمْنَا كُلَّ ذِي ظُفُرٍ ۖ وَمِنَ الْبَقَرِ وَالْغَنَمِ حَرَّمْنَا عَلَيْهِمْ شُحُومَهُمَا إِلَّا مَا حَمَلَتْ ظُهُورُهُمَا أَوِ الْحَوَايَا أَوْ مَا اخْتَلَطَ بِعَظْمٍ ۚ ذَٰلِكَ جَزَيْنَاهُم بِبَغْيِهِمْ ۖ وَإِنَّا لَصَادِقُونَ (146) Ife tidawaletsa Ayuda kudya nyama zonse zosabsyukula ndipo tinawaletsa mafuta a ng’ombe ndi a nkhosa kupatula amene ali pa msana ndi m’matumbo kapena amene adasakanizika ndi mafupa. Motero tidawapatsa chilango chifukwa cha kulakwa kwawo. Ndithudi Ife tili kunena zoonadi |
فَإِن كَذَّبُوكَ فَقُل رَّبُّكُمْ ذُو رَحْمَةٍ وَاسِعَةٍ وَلَا يُرَدُّ بَأْسُهُ عَنِ الْقَوْمِ الْمُجْرِمِينَ (147) Ngati iwo akukunamizani, nena, “Ambuye wanu ndi Mwini chifundo chosatha koma mkwiyo wake siungachotsedwe pa anthu ochita zoipa.” |
سَيَقُولُ الَّذِينَ أَشْرَكُوا لَوْ شَاءَ اللَّهُ مَا أَشْرَكْنَا وَلَا آبَاؤُنَا وَلَا حَرَّمْنَا مِن شَيْءٍ ۚ كَذَٰلِكَ كَذَّبَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ حَتَّىٰ ذَاقُوا بَأْسَنَا ۗ قُلْ هَلْ عِندَكُم مِّنْ عِلْمٍ فَتُخْرِجُوهُ لَنَا ۖ إِن تَتَّبِعُونَ إِلَّا الظَّنَّ وَإِنْ أَنتُمْ إِلَّا تَخْرُصُونَ (148) Anthu opembedza mafano adzati: “Mulungu akadafuna, ife kapena makolo athu, sitikadatumikira milungu ina yoonjezera pa Iye ndipo ife sitikadaletsa china chilichonse.” Mmenemu ndi mmene anthu amene adalipo kale adanamira mpaka pamene analawa mkwiyo wathu. Nena, “Kodi inu muli ndi umboni uliwonse umene mungatisonyeze Ife?” Ndithudi inu simutsatira china koma zinthu zongoganiza ndiponso simuchita china chilichonse koma bodza basi |
قُلْ فَلِلَّهِ الْحُجَّةُ الْبَالِغَةُ ۖ فَلَوْ شَاءَ لَهَدَاكُمْ أَجْمَعِينَ (149) Nena, “Ndi Mulungu yekha amene ali ndi umboni weniweni ndipo Iye akadafuna akadakutsogolerani nonse.” |
قُلْ هَلُمَّ شُهَدَاءَكُمُ الَّذِينَ يَشْهَدُونَ أَنَّ اللَّهَ حَرَّمَ هَٰذَا ۖ فَإِن شَهِدُوا فَلَا تَشْهَدْ مَعَهُمْ ۚ وَلَا تَتَّبِعْ أَهْوَاءَ الَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا وَالَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ بِالْآخِرَةِ وَهُم بِرَبِّهِمْ يَعْدِلُونَ (150) Nena, “Bweretsani mboni zanu zonse zimene zikhoza kuchitira umboni kuti Mulungu adakuletsani izi. Ngati iwo apereka umboni, iwe usapereke umboni wako. Ndipo usatsatire zilakolako za iwo amene amati chivumbulutso chathu ndi chabodza, amene sakhulupirira za m’moyo umene uli nkudza ndipo amapanga milungu ina kukhala yofanana ndi Ambuye wawo.” |
۞ قُلْ تَعَالَوْا أَتْلُ مَا حَرَّمَ رَبُّكُمْ عَلَيْكُمْ ۖ أَلَّا تُشْرِكُوا بِهِ شَيْئًا ۖ وَبِالْوَالِدَيْنِ إِحْسَانًا ۖ وَلَا تَقْتُلُوا أَوْلَادَكُم مِّنْ إِمْلَاقٍ ۖ نَّحْنُ نَرْزُقُكُمْ وَإِيَّاهُمْ ۖ وَلَا تَقْرَبُوا الْفَوَاحِشَ مَا ظَهَرَ مِنْهَا وَمَا بَطَنَ ۖ وَلَا تَقْتُلُوا النَّفْسَ الَّتِي حَرَّمَ اللَّهُ إِلَّا بِالْحَقِّ ۚ ذَٰلِكُمْ وَصَّاكُم بِهِ لَعَلَّكُمْ تَعْقِلُونَ (151) Nena, “Bwerani! Ine ndikuwerengerani zimene Ambuye wanu wakulamulani inu kuti musachite. Musapembedze milungu ina yowonjezera pa Iye; Muzionetsa chifundo kwa makolo anu; musaphe ana anu chifukwa chaumphawi, Ife timakudyetsani inu pamodzi ndi iwo; musayandikire zinthu zoipa zimene zili zoonekera kapena zili zobisika ndipo musaphe munthu amene Mulungu waletsa pokhapokha ngati pali chifukwa choyenera.” Ichi wakulamulani inu kuti muzindikire |
وَلَا تَقْرَبُوا مَالَ الْيَتِيمِ إِلَّا بِالَّتِي هِيَ أَحْسَنُ حَتَّىٰ يَبْلُغَ أَشُدَّهُ ۖ وَأَوْفُوا الْكَيْلَ وَالْمِيزَانَ بِالْقِسْطِ ۖ لَا نُكَلِّفُ نَفْسًا إِلَّا وُسْعَهَا ۖ وَإِذَا قُلْتُمْ فَاعْدِلُوا وَلَوْ كَانَ ذَا قُرْبَىٰ ۖ وَبِعَهْدِ اللَّهِ أَوْفُوا ۚ ذَٰلِكُمْ وَصَّاكُم بِهِ لَعَلَّكُمْ تَذَكَّرُونَ (152) “Ndipo musayandikire chuma cha ana a masiye kupatula m’njira yabwino yowakonzera tsogolo lawo mpaka pamene iwo akula msinkhu. Kwaniritsani muyeso woyenera ndipo muyese mwachilungamo. Ife sitinyamulitsa munthu wina aliyense katundu wolemera amene iye sangathe kunyamula. Ndipo mukamalankhula, muzilankhula mwachilungamo ngakhale kuti nkhanizo zikhudza abale anu ndipo kwaniritsani malonjezo a Mulungu. Ichi wakulamurani inu kuti mudzikumbukira.” |
وَأَنَّ هَٰذَا صِرَاطِي مُسْتَقِيمًا فَاتَّبِعُوهُ ۖ وَلَا تَتَّبِعُوا السُّبُلَ فَتَفَرَّقَ بِكُمْ عَن سَبِيلِهِ ۚ ذَٰلِكُمْ وَصَّاكُم بِهِ لَعَلَّكُمْ تَتَّقُونَ (153) Ndithu iyi ndi njira yanga yoyenera motero itsatireni ndipo musatsatire njira zina zake chifukwa izo zidzakusocheretsani inu ku njira yake. Ichi Iye wakulamulani kuti mukhale angwiro |
ثُمَّ آتَيْنَا مُوسَى الْكِتَابَ تَمَامًا عَلَى الَّذِي أَحْسَنَ وَتَفْصِيلًا لِّكُلِّ شَيْءٍ وَهُدًى وَرَحْمَةً لَّعَلَّهُم بِلِقَاءِ رَبِّهِمْ يُؤْمِنُونَ (154) Ndipo Ife tidamupatsa Mose Buku, kumaliza ubwino wathu kwa aliyense wochita zabwino ndiponso lofotokoza chinthu chilichonse, ulangizi ndi chisomo kuti akhulupirire mukukumana kwawo ndi Ambuye wawo |
وَهَٰذَا كِتَابٌ أَنزَلْنَاهُ مُبَارَكٌ فَاتَّبِعُوهُ وَاتَّقُوا لَعَلَّكُمْ تُرْحَمُونَ (155) Ili ndi Buku lodalitsika limene talivumbulutsa, motero opani Mulungu kuti mulandire chisomo |
أَن تَقُولُوا إِنَّمَا أُنزِلَ الْكِتَابُ عَلَىٰ طَائِفَتَيْنِ مِن قَبْلِنَا وَإِن كُنَّا عَن دِرَاسَتِهِمْ لَغَافِلِينَ (156) Kuti inu musadzanene kuti: “Buku lidangovumbulutsidwa ku magulu awiri pambuyo pathu, ndipo ife sitidadziwe zimene adali kuwerenga.” |
أَوْ تَقُولُوا لَوْ أَنَّا أُنزِلَ عَلَيْنَا الْكِتَابُ لَكُنَّا أَهْدَىٰ مِنْهُمْ ۚ فَقَدْ جَاءَكُم بَيِّنَةٌ مِّن رَّبِّكُمْ وَهُدًى وَرَحْمَةٌ ۚ فَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّن كَذَّبَ بِآيَاتِ اللَّهِ وَصَدَفَ عَنْهَا ۗ سَنَجْزِي الَّذِينَ يَصْدِفُونَ عَنْ آيَاتِنَا سُوءَ الْعَذَابِ بِمَا كَانُوا يَصْدِفُونَ (157) Kapena mukhoza kudzanena kuti: “Buku la Mulungu likanavumbulutsidwa kwa ife, ndithudi, tikadalangizidwa bwino kuposa iwo.” Ndithudi chizindikiro chosakaikitsa chadza tsopano kuchokera kwa a Ambuye wanu; chilangizo ndi madalitso. Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene akana chivumbulutso cha Mulungu ndipo safuna kuchitsatira? Ife tidzawalipira onse amene amakana zizindikiro zathu ndi chilango chowawa chifukwa chokana kwawo |
هَلْ يَنظُرُونَ إِلَّا أَن تَأْتِيَهُمُ الْمَلَائِكَةُ أَوْ يَأْتِيَ رَبُّكَ أَوْ يَأْتِيَ بَعْضُ آيَاتِ رَبِّكَ ۗ يَوْمَ يَأْتِي بَعْضُ آيَاتِ رَبِّكَ لَا يَنفَعُ نَفْسًا إِيمَانُهَا لَمْ تَكُنْ آمَنَتْ مِن قَبْلُ أَوْ كَسَبَتْ فِي إِيمَانِهَا خَيْرًا ۗ قُلِ انتَظِرُوا إِنَّا مُنتَظِرُونَ (158) Kodi iwo ali kudikira wina kupatula angelo kuti adze kwa iwo kapena kuti Ambuye wako adze kapena zina mwa zizindikiro za Ambuye wako zidze? Tsiku limene zina mwa zizindikiro za Ambuye wako zidzadza, chikhulupiriro sichidzathandiza mzimu umene unalibe chikhulupiriro kale kapena umene siudagwiritse ntchito bwino chikhulupiriro. Nena, “Dikirani! Nafenso tili kudikira.” |
إِنَّ الَّذِينَ فَرَّقُوا دِينَهُمْ وَكَانُوا شِيَعًا لَّسْتَ مِنْهُمْ فِي شَيْءٍ ۚ إِنَّمَا أَمْرُهُمْ إِلَى اللَّهِ ثُمَّ يُنَبِّئُهُم بِمَا كَانُوا يَفْعَلُونَ (159) Ndithudi iwo amene apatukana m’chipembedzo ndi kupanga mipingo yosiyanasiyana, iwe sizikukhudza zimenezo. Nkhani yawo adzathetsa ndi Mulungu ndipo Iye adzawauza zomwe amachita |
مَن جَاءَ بِالْحَسَنَةِ فَلَهُ عَشْرُ أَمْثَالِهَا ۖ وَمَن جَاءَ بِالسَّيِّئَةِ فَلَا يُجْزَىٰ إِلَّا مِثْلَهَا وَهُمْ لَا يُظْلَمُونَ (160) Aliyense amene amachita ntchito yabwino adzalipidwa magawo khumi olingana ndi iyo ndipo aliyense amene amachita zoipa adzalandira choipa chomwecho ndipo iwo sadzaponderezedwa ayi |
قُلْ إِنَّنِي هَدَانِي رَبِّي إِلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ دِينًا قِيَمًا مِّلَّةَ إِبْرَاهِيمَ حَنِيفًا ۚ وَمَا كَانَ مِنَ الْمُشْرِكِينَ (161) Nena, “Ndithudi Ambuye wanga wanditsogolera ine ku njira yoyenera, ku chipembedzo changwiro, chikhulupiriro cha Abrahamu wangwiro chifukwa Abrahamu sadali mmodzi wa anthu opembedza mafano.” |
قُلْ إِنَّ صَلَاتِي وَنُسُكِي وَمَحْيَايَ وَمَمَاتِي لِلَّهِ رَبِّ الْعَالَمِينَ (162) Nena, “Ndithudi mapemphero anga, nsembe yanga, moyo wanga ndi imfa yanga zonse zili m’manja mwa Mulungu Ambuye wazolengedwa zonse.” |
لَا شَرِيكَ لَهُ ۖ وَبِذَٰلِكَ أُمِرْتُ وَأَنَا أَوَّلُ الْمُسْلِمِينَ (163) Iye alibe wothandizana naye. Pa izi ine ndalamulidwa ndipo ine ndine woyamba wa iwo ogonjera malamulo a Mulungu |
قُلْ أَغَيْرَ اللَّهِ أَبْغِي رَبًّا وَهُوَ رَبُّ كُلِّ شَيْءٍ ۚ وَلَا تَكْسِبُ كُلُّ نَفْسٍ إِلَّا عَلَيْهَا ۚ وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٌ وِزْرَ أُخْرَىٰ ۚ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّكُم مَّرْجِعُكُمْ فَيُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمْ فِيهِ تَخْتَلِفُونَ (164) Nena, “Kodi ine ndifune Ambuye wina osati Mulungu pamene Iye ndi Ambuye wa zinthu zonse? Munthu aliyense adzakolola zipatso za ntchito yake ndipo palibe mzimu umene udzanyamula katundu wa wina wake. Pomaliza nonse mudzabwerera kwa Ambuye wanu; ndipo Iye adzakuuzani zomwe munali kutsutsana.” |
وَهُوَ الَّذِي جَعَلَكُمْ خَلَائِفَ الْأَرْضِ وَرَفَعَ بَعْضَكُمْ فَوْقَ بَعْضٍ دَرَجَاتٍ لِّيَبْلُوَكُمْ فِي مَا آتَاكُمْ ۗ إِنَّ رَبَّكَ سَرِيعُ الْعِقَابِ وَإِنَّهُ لَغَفُورٌ رَّحِيمٌ (165) Ndipo ndiye amene anakulengani kukhala mibadwo yodza pambuyo pa mibadwo yina, kulowa m’malo mwa uzake padziko lapansi. Ndipo anakukwezani m’maudindo, ena kuposa anzawo kuti akhoza kukuyesani ndi zimene wakupatsani. Ndithudi Ambuye wanu ndi wachangu polanga koma ndithudi Iye amakhululuka, Mwini chisoni chosatha |