Quran with Chichewa translation - Surah Al-An‘am ayat 99 - الأنعَام - Page - Juz 7
﴿وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَأَخۡرَجۡنَا بِهِۦ نَبَاتَ كُلِّ شَيۡءٖ فَأَخۡرَجۡنَا مِنۡهُ خَضِرٗا نُّخۡرِجُ مِنۡهُ حَبّٗا مُّتَرَاكِبٗا وَمِنَ ٱلنَّخۡلِ مِن طَلۡعِهَا قِنۡوَانٞ دَانِيَةٞ وَجَنَّٰتٖ مِّنۡ أَعۡنَابٖ وَٱلزَّيۡتُونَ وَٱلرُّمَّانَ مُشۡتَبِهٗا وَغَيۡرَ مُتَشَٰبِهٍۗ ٱنظُرُوٓاْ إِلَىٰ ثَمَرِهِۦٓ إِذَآ أَثۡمَرَ وَيَنۡعِهِۦٓۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكُمۡ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ ﴾
[الأنعَام: 99]
﴿وهو الذي أنـزل من السماء ماء فأخرجنا به نبات كل شيء فأخرجنا﴾ [الأنعَام: 99]
Khaled Ibrahim Betala “Iye ndi Yemwe amavumbwitsa mvula kuchokera kumwamba. Ndi madzi a mvulayo timameretsa mmera wa chinthu chilichonse. Ndipo m’menemo tikuphukitsa masamba obiriwira, tikutulutsa mmenemo njere zosanjikana; ndiponso m’kanjedza m’mikoko mwake mumatuluka maphava ogoweka (ndizipatso). Ndipo amakumeretserani minda ya mphesa, mzitona ndi makomamanga, ofanana ndi osafanana. Tapenyani zipatso zake pamene zikupatsa ndi kupsa kwake. Ndithu m’zimenezo muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira |