Quran with Chichewa translation - Surah Al-A‘raf ayat 142 - الأعرَاف - Page - Juz 9
﴿۞ وَوَٰعَدۡنَا مُوسَىٰ ثَلَٰثِينَ لَيۡلَةٗ وَأَتۡمَمۡنَٰهَا بِعَشۡرٖ فَتَمَّ مِيقَٰتُ رَبِّهِۦٓ أَرۡبَعِينَ لَيۡلَةٗۚ وَقَالَ مُوسَىٰ لِأَخِيهِ هَٰرُونَ ٱخۡلُفۡنِي فِي قَوۡمِي وَأَصۡلِحۡ وَلَا تَتَّبِعۡ سَبِيلَ ٱلۡمُفۡسِدِينَ ﴾
[الأعرَاف: 142]
﴿وواعدنا موسى ثلاثين ليلة وأتممناها بعشر فتم ميقات ربه أربعين ليلة وقال﴾ [الأعرَاف: 142]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo tidamlonjeza Mûsa masiku makumi atatu (kuti achite mapemphero kuti kenako timpatse Taurat). Ndipo tidawakwaniritsa ndi masiku khumi; chomwecho lidakwanira pangano la Mbuye wake (lopita kukampatsa Tauratiyo) m’masiku makumi anayi. Ndipo Mûsa adati kwa m’bale wake Harun: “Lowa m’malo mwanga pa (kuwatsogolera) anthu angawa. Ndipo konza; usatsate njira ya oononga.” |