×

Ndipo pamene Mose adabwera panthawi ndi malo osankhidwa ndi Ife, Ambuye wake 7:143 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah Al-A‘raf ⮕ (7:143) ayat 143 in Chichewa

7:143 Surah Al-A‘raf ayat 143 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah Al-A‘raf ayat 143 - الأعرَاف - Page - Juz 9

﴿وَلَمَّا جَآءَ مُوسَىٰ لِمِيقَٰتِنَا وَكَلَّمَهُۥ رَبُّهُۥ قَالَ رَبِّ أَرِنِيٓ أَنظُرۡ إِلَيۡكَۚ قَالَ لَن تَرَىٰنِي وَلَٰكِنِ ٱنظُرۡ إِلَى ٱلۡجَبَلِ فَإِنِ ٱسۡتَقَرَّ مَكَانَهُۥ فَسَوۡفَ تَرَىٰنِيۚ فَلَمَّا تَجَلَّىٰ رَبُّهُۥ لِلۡجَبَلِ جَعَلَهُۥ دَكّٗا وَخَرَّ مُوسَىٰ صَعِقٗاۚ فَلَمَّآ أَفَاقَ قَالَ سُبۡحَٰنَكَ تُبۡتُ إِلَيۡكَ وَأَنَا۠ أَوَّلُ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ﴾
[الأعرَاف: 143]

Ndipo pamene Mose adabwera panthawi ndi malo osankhidwa ndi Ife, Ambuye wake adalankhula naye ndipo iye adati: “Oh Ambuye wanga! Dzionetseni inu kwa ine kuti ndikuoneni.” Mulungu adati: “Iwe siudzandiona Ine ayi. Koma uone kuphiri ndipo ngati ilo lingakhalebe chikhalire ndiye kuti ukhoza kundiona Ine.” Ndipo pamene Ambuye wake anadzionetsera pa phiri, phiri lidaphwanyika ndi kusanduka fumbi lokhalokha ndipo Mose adagwa pansi ndipo adakomoka koma pamene anatsitsimuka iye adati: “Ulemerero ukhale kwa Inu. Ine ndalapa kwa Inu ndipo ine ndine woyamba wa anthu okhulupirira.”

❮ Previous Next ❯

ترجمة: ولما جاء موسى لميقاتنا وكلمه ربه قال رب أرني أنظر إليك قال, باللغة نيانجا

﴿ولما جاء موسى لميقاتنا وكلمه ربه قال رب أرني أنظر إليك قال﴾ [الأعرَاف: 143]

Khaled Ibrahim Betala
“Pamene Mûsa adafika kumalo achipangano Chathucho, ndipo Mbuye wake namulankhula, (Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Dzionetseni kwa ine kuti ndikuoneni.” Allah adati: “Sungathe kundiona; koma yang’ana phirilo (lomwe lili patsogolo pako). Ngati likhazikika pamalo pake (popanda kusweka), ukhoza kundiona.” Choncho Mbuye wake pamene adadzionetsa kwa phirilo, adalichita kukhala loswekasweka ndipo Mussa adagwa ndi kukomoka. Pamene adatsitsimuka adati: “(Ha! Ndikutsimikizadi kuti) Inu ndinu Wolemekezeka. Ndalapa kwa Inu, ndipo ndine woyamba mwa okhulupirira (izi).”
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek