Quran with Chichewa translation - Surah Al-Anfal ayat 42 - الأنفَال - Page - Juz 10
﴿إِذۡ أَنتُم بِٱلۡعُدۡوَةِ ٱلدُّنۡيَا وَهُم بِٱلۡعُدۡوَةِ ٱلۡقُصۡوَىٰ وَٱلرَّكۡبُ أَسۡفَلَ مِنكُمۡۚ وَلَوۡ تَوَاعَدتُّمۡ لَٱخۡتَلَفۡتُمۡ فِي ٱلۡمِيعَٰدِ وَلَٰكِن لِّيَقۡضِيَ ٱللَّهُ أَمۡرٗا كَانَ مَفۡعُولٗا لِّيَهۡلِكَ مَنۡ هَلَكَ عَنۢ بَيِّنَةٖ وَيَحۡيَىٰ مَنۡ حَيَّ عَنۢ بَيِّنَةٖۗ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَسَمِيعٌ عَلِيمٌ ﴾
[الأنفَال: 42]
﴿إذ أنتم بالعدوة الدنيا وهم بالعدوة القصوى والركب أسفل منكم ولو تواعدتم﴾ [الأنفَال: 42]
Khaled Ibrahim Betala “(Kumbukirani) pamene mudali mbali ya chigwa yoyandikira (mzinda wa Madina) pomwe iwo (ankhondo a Chikuraishi) adali mbali ya kutali ya tsidya lina (la chigwacho) pomwe aulendo amalonda adali cha kumunsi kwanu. Ngati mukadapangana nthawi yokumanirana (kuti mukumane nthawi yakutiyakuti), mukadasiyana posunga chipangano (chifukwa cha kuopa kuchuluka kwa adani anuwo). Koma (mwakumana mosayembekezera ndi ankhondo a adaniwo) kuti Allah akwaniritse chinthu chomwe nchofunika kuti chichitike, kuti awonongeke amene waonongeka (posankha kusakhulupirira) ndi umboni woonekera (umene adaukana kuutsata), ndi kuti akhale ndi moyo amene wakhala ndi moyo (amene watsata njira ya Chisilamu) ndi umboninso woonekera. Ndithudi Allah Ngwakumva zonse, Ngodziwa kwambiri |