يَسْأَلُونَكَ عَنِ الْأَنفَالِ ۖ قُلِ الْأَنفَالُ لِلَّهِ وَالرَّسُولِ ۖ فَاتَّقُوا اللَّهَ وَأَصْلِحُوا ذَاتَ بَيْنِكُمْ ۖ وَأَطِيعُوا اللَّهَ وَرَسُولَهُ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ (1) Iwo akukufunsa iwe za katundu amene mumapeza mukamenya nkhondo. Nena: “Mwini wake wa katundu uyu ndi Mulungu ndi Mtumwi. Motero muopeni Mulungu ndipo yanjanani pakati panu ndipo mverani Mulungu ndi Mtumwi wake ngati inu ndinu okhulupirira.” |
إِنَّمَا الْمُؤْمِنُونَ الَّذِينَ إِذَا ذُكِرَ اللَّهُ وَجِلَتْ قُلُوبُهُمْ وَإِذَا تُلِيَتْ عَلَيْهِمْ آيَاتُهُ زَادَتْهُمْ إِيمَانًا وَعَلَىٰ رَبِّهِمْ يَتَوَكَّلُونَ (2) Okhulupirira enieni ndi okhawo, amene ngati dzina la Mulungu litchulidwa, amachita mantha m’mitima mwawo ndipo pamene mavesi ake awerengedwa kwa iwo, iwo amaonjezera chikhulupiriro chawo ndipo amaika chikhulupiriro chawo mwa Ambuye wawo |
الَّذِينَ يُقِيمُونَ الصَّلَاةَ وَمِمَّا رَزَقْنَاهُمْ يُنفِقُونَ (3) Amene amapitiriza mapemphero ndipo amapereka mwaulere gawo lina la zinthu zimene tawapatsa |
أُولَٰئِكَ هُمُ الْمُؤْمِنُونَ حَقًّا ۚ لَّهُمْ دَرَجَاتٌ عِندَ رَبِّهِمْ وَمَغْفِرَةٌ وَرِزْقٌ كَرِيمٌ (4) Iwo ndiwo amene ali okhulupirira enieni. Kwa iwo kuli maudindo olemekezeka amene ali ndi Ambuye wawo ndiponso chikhululukiro ndi mphotho yolemekezeka |
كَمَا أَخْرَجَكَ رَبُّكَ مِن بَيْتِكَ بِالْحَقِّ وَإِنَّ فَرِيقًا مِّنَ الْمُؤْمِنِينَ لَكَارِهُونَ (5) Monga momwe Ambuye wako adakutulutsa m’nyumba yako ndi choonadi ndipo, ndithudi, gulu lina la okhulupirira sadakondwe ndi icho |
يُجَادِلُونَكَ فِي الْحَقِّ بَعْدَمَا تَبَيَّنَ كَأَنَّمَا يُسَاقُونَ إِلَى الْمَوْتِ وَهُمْ يَنظُرُونَ (6) Kutsutsana ndi iwe pa choonadi chimene chinadza ngati kuti iwo anali kuperekedwa ku imfa pamene iwo anali kuona |
وَإِذْ يَعِدُكُمُ اللَّهُ إِحْدَى الطَّائِفَتَيْنِ أَنَّهَا لَكُمْ وَتَوَدُّونَ أَنَّ غَيْرَ ذَاتِ الشَّوْكَةِ تَكُونُ لَكُمْ وَيُرِيدُ اللَّهُ أَن يُحِقَّ الْحَقَّ بِكَلِمَاتِهِ وَيَقْطَعَ دَابِرَ الْكَافِرِينَ (7) Ndi pamene Mulungu adalonjeza gulu lina pakati pa magulu awiri, ilo ndi lanu ndipo inu mudakonda kuti mukhale ndi gulu lija lopanda zida koma Mulungu adafuna kukwaniritsa chilungamo ndi mawu ake ndi kudula maziko ya anthu osakhulupirira |
لِيُحِقَّ الْحَقَّ وَيُبْطِلَ الْبَاطِلَ وَلَوْ كَرِهَ الْمُجْرِمُونَ (8) Kuti choonadi chikhoza kupambana ndi kuthetsa bodza ngakhale kuti anthu osakhulupirira anali kudana nazo |
إِذْ تَسْتَغِيثُونَ رَبَّكُمْ فَاسْتَجَابَ لَكُمْ أَنِّي مُمِدُّكُم بِأَلْفٍ مِّنَ الْمَلَائِكَةِ مُرْدِفِينَ (9) Ndi pamene inu mudapempha thandizo la Ambuye wanu ndipo Iye adakuyankhani: “Ine ndikuthandizani ndi angelo chikwi chimodzi m’magulumagulu otsatana.” |
وَمَا جَعَلَهُ اللَّهُ إِلَّا بُشْرَىٰ وَلِتَطْمَئِنَّ بِهِ قُلُوبُكُمْ ۚ وَمَا النَّصْرُ إِلَّا مِنْ عِندِ اللَّهِ ۚ إِنَّ اللَّهَ عَزِيزٌ حَكِيمٌ (10) Mulungu anafuna kukusangalatsani chabe kuti mitima yanu ikhazikike. Ndipo palibe kupambana kupatula kochokera kwa Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi Wamphamvu ndi Wanzeru |
إِذْ يُغَشِّيكُمُ النُّعَاسَ أَمَنَةً مِّنْهُ وَيُنَزِّلُ عَلَيْكُم مِّنَ السَّمَاءِ مَاءً لِّيُطَهِّرَكُم بِهِ وَيُذْهِبَ عَنكُمْ رِجْزَ الشَّيْطَانِ وَلِيَرْبِطَ عَلَىٰ قُلُوبِكُمْ وَيُثَبِّتَ بِهِ الْأَقْدَامَ (11) Pamene adakubweretsani inu tulo ngati mtendere kuchokera kwa Iye ndipo adakutumizirani mvula kuchokera kumwamba kuti ikutsukeni ndi kukuyeretsani ku uve wa Satana ndi kulimbikitsa mitima yanu ndi mapazi anu |
إِذْ يُوحِي رَبُّكَ إِلَى الْمَلَائِكَةِ أَنِّي مَعَكُمْ فَثَبِّتُوا الَّذِينَ آمَنُوا ۚ سَأُلْقِي فِي قُلُوبِ الَّذِينَ كَفَرُوا الرُّعْبَ فَاضْرِبُوا فَوْقَ الْأَعْنَاقِ وَاضْرِبُوا مِنْهُمْ كُلَّ بَنَانٍ (12) Pamene Mulungu ananena ndi angelo kuti: Ndithudi Ine ndili ndi inu ndipo limbikitsani anthu amene akhulupirira. Ine ndidzakhazikitsa mantha m’mitima ya anthu osakhulupirira, motero amenyeni m’makosi mwawo ndipo konkhonthani zala zawo za kumanja ndi za kumapazi |
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ شَاقُّوا اللَّهَ وَرَسُولَهُ ۚ وَمَن يُشَاقِقِ اللَّهَ وَرَسُولَهُ فَإِنَّ اللَّهَ شَدِيدُ الْعِقَابِ (13) Ichi ndi chifukwa chakuti iwo sanamvere Mulungu ndi Mtumwiwake. Ndipoaliyenseamenesamvera Mulungundi Mtumwi wake, ndithudi, Mulungu ndi wolanga kwambiri |
ذَٰلِكُمْ فَذُوقُوهُ وَأَنَّ لِلْكَافِرِينَ عَذَابَ النَّارِ (14) Ichi ndi chilango motero chilaweni ndipo, ndithudi, anthu osakhulupirira chawo ndi chilango chakumoto |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِذَا لَقِيتُمُ الَّذِينَ كَفَرُوا زَحْفًا فَلَا تُوَلُّوهُمُ الْأَدْبَارَ (15) oh inu anthu okhulupirira! Pamene mukumana ndi magulu a nkhondo a anthu osakhulupirira musathawe |
وَمَن يُوَلِّهِمْ يَوْمَئِذٍ دُبُرَهُ إِلَّا مُتَحَرِّفًا لِّقِتَالٍ أَوْ مُتَحَيِّزًا إِلَىٰ فِئَةٍ فَقَدْ بَاءَ بِغَضَبٍ مِّنَ اللَّهِ وَمَأْوَاهُ جَهَنَّمُ ۖ وَبِئْسَ الْمَصِيرُ (16) Ndipo aliyense amene adzathawe patsiku limeneli kupatula ngati kuli kukonzekera nkhondo kapena kubwerera ku gulu lake, iye adzaputa mkwiyo wa Mulungu. Ndipo Gahena idzakhala mudzi wake ndipo malowa ndi oipa kukhalako |
فَلَمْ تَقْتُلُوهُمْ وَلَٰكِنَّ اللَّهَ قَتَلَهُمْ ۚ وَمَا رَمَيْتَ إِذْ رَمَيْتَ وَلَٰكِنَّ اللَّهَ رَمَىٰ ۚ وَلِيُبْلِيَ الْمُؤْمِنِينَ مِنْهُ بَلَاءً حَسَنًا ۚ إِنَّ اللَّهَ سَمِيعٌ عَلِيمٌ (17) Inu simunawaphe ai koma Mulungu ndiye amene anawapha. Iwe siudaponye pamene udaponya koma Mulungu ndi amene adaponya kuti akhoza kuyesa okhulupirira ndi mayesero oyenera ochokera kwa Iye. Ndithudi Mulungu ndi wakumva ndi wodziwa chili chonse |
ذَٰلِكُمْ وَأَنَّ اللَّهَ مُوهِنُ كَيْدِ الْكَافِرِينَ (18) Ichi, ndipo ndithudi, Mulungu amafoketsa ziwembu za anthu osakhulupirira |
إِن تَسْتَفْتِحُوا فَقَدْ جَاءَكُمُ الْفَتْحُ ۖ وَإِن تَنتَهُوا فَهُوَ خَيْرٌ لَّكُمْ ۖ وَإِن تَعُودُوا نَعُدْ وَلَن تُغْنِيَ عَنكُمْ فِئَتُكُمْ شَيْئًا وَلَوْ كَثُرَتْ وَأَنَّ اللَّهَ مَعَ الْمُؤْمِنِينَ (19) Ngati inu mufunsa chiweruzo, tsopano chiweruzo chadza kwa inu ndipo ngati inu musiya kuchita zoipa zidzakhala bwino kwa inu ndipo ngati inu mubwerera, Ifenso tidzabwerera ndipo magulu anu a nkhondo, ngakhale kuti ndi ochuluka, sadzakuthandizani china chilichonse ndipo, ndithudi, Mulungu ali kumbali ya anthu okhulupirira |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا أَطِيعُوا اللَّهَ وَرَسُولَهُ وَلَا تَوَلَّوْا عَنْهُ وَأَنتُمْ تَسْمَعُونَ (20) Oh inu anthu okhulupirira! Mverani Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo musamutaye ayi pamene inu muli kumva |
وَلَا تَكُونُوا كَالَّذِينَ قَالُوا سَمِعْنَا وَهُمْ لَا يَسْمَعُونَ (21) Ndipo musakhale ngati iwo amene amati: “Tamva”; pamene iwo sanamve |
۞ إِنَّ شَرَّ الدَّوَابِّ عِندَ اللَّهِ الصُّمُّ الْبُكْمُ الَّذِينَ لَا يَعْقِلُونَ (22) Ndithudi! Zolengedwa za moyo zimene zili zoipa kwambiri pamaso pa Mulungu ndizo zimene zili zosamva, zosalankhula ndi izo zimene sizizindikira |
وَلَوْ عَلِمَ اللَّهُ فِيهِمْ خَيْرًا لَّأَسْمَعَهُمْ ۖ وَلَوْ أَسْمَعَهُمْ لَتَوَلَّوا وَّهُم مُّعْرِضُونَ (23) Ngakhale Mulungu akadadziwa ubwino umene uli mwa iwo, ndithudi, Iye akadawapanga kumva koma ngakhale Iye akadawapanga kuti azimva, iwo akadabwerera m’mbuyo ndi kukana choonadi |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا اسْتَجِيبُوا لِلَّهِ وَلِلرَّسُولِ إِذَا دَعَاكُمْ لِمَا يُحْيِيكُمْ ۖ وَاعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ يَحُولُ بَيْنَ الْمَرْءِ وَقَلْبِهِ وَأَنَّهُ إِلَيْهِ تُحْشَرُونَ (24) oh inu anthu okhulupirira! Yankhani Mulungu ndi Mtumwi wake pamene akukuitanani ku chimene chikupatsani inu moyo ndipo dziwani kuti Mulungu amaima pakati pa munthu ndi mtima wake. Ndipo, ndithudi, nonse mudzasonkhanitsidwa kudza kwa Iye |
وَاتَّقُوا فِتْنَةً لَّا تُصِيبَنَّ الَّذِينَ ظَلَمُوا مِنكُمْ خَاصَّةً ۖ وَاعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ شَدِيدُ الْعِقَابِ (25) Ndipo opani mayesero amene sabwera kwa anthu oipa okha koma kwa inu nonse ndipo dziwani kuti Mulungu ndi wokhwimitsa chilango chake |
وَاذْكُرُوا إِذْ أَنتُمْ قَلِيلٌ مُّسْتَضْعَفُونَ فِي الْأَرْضِ تَخَافُونَ أَن يَتَخَطَّفَكُمُ النَّاسُ فَآوَاكُمْ وَأَيَّدَكُم بِنَصْرِهِ وَرَزَقَكُم مِّنَ الطَّيِّبَاتِ لَعَلَّكُمْ تَشْكُرُونَ (26) Ndipo kumbukirani pamene inu mudali ochepa ndipo mumaganizidwa kuti munali opanda mphamvu m’dziko ndipo mudali kuopa kuti mwina anthu akulandani. Koma Iye adakupatsani malo otetezedwa okhala ndi kukulimbikitsani ndi chithandizo chake ndipo adakupatsani zinthu zabwino kuti muzimuyamika |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَخُونُوا اللَّهَ وَالرَّسُولَ وَتَخُونُوا أَمَانَاتِكُمْ وَأَنتُمْ تَعْلَمُونَ (27) oh inu anthu okhulupirira! Musamunyenge Mulungu ndi Mtumwi ndipo musachite chinyengo pamene muli nkudziwa pophwanya malonjezo anu |
وَاعْلَمُوا أَنَّمَا أَمْوَالُكُمْ وَأَوْلَادُكُمْ فِتْنَةٌ وَأَنَّ اللَّهَ عِندَهُ أَجْرٌ عَظِيمٌ (28) Ndipo dziwani kuti chuma chanu ndi ana anu ndi mayesero ndipo kuti, ndithudi, kwa Mulungu kuli mphotho yaikulu |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِن تَتَّقُوا اللَّهَ يَجْعَل لَّكُمْ فُرْقَانًا وَيُكَفِّرْ عَنكُمْ سَيِّئَاتِكُمْ وَيَغْفِرْ لَكُمْ ۗ وَاللَّهُ ذُو الْفَضْلِ الْعَظِيمِ (29) Oh inu anthu okhulupirira! Ngati inu mumvera ndi kuopa Mulungu, Iye adzakupatsani nzeru zodziwira chabwino ndi choipa ndipo adzakukhululukirani machimo anu ndipo Mulungu ndiye Mwini chuma chochuluka |
وَإِذْ يَمْكُرُ بِكَ الَّذِينَ كَفَرُوا لِيُثْبِتُوكَ أَوْ يَقْتُلُوكَ أَوْ يُخْرِجُوكَ ۚ وَيَمْكُرُونَ وَيَمْكُرُ اللَّهُ ۖ وَاللَّهُ خَيْرُ الْمَاكِرِينَ (30) Ndi mmene anthu osakhulupirira adakupangira chiwembu choti akugwire kuti ukhale mndende kapena kukupha kapena kukuchotsa m’dziko lako. Iwo amachita chiwembu koma Mulungu, nayenso amakonza chiwembu chake, ndipo Mulungu ndi wopambana pokonza chiwembu |
وَإِذَا تُتْلَىٰ عَلَيْهِمْ آيَاتُنَا قَالُوا قَدْ سَمِعْنَا لَوْ نَشَاءُ لَقُلْنَا مِثْلَ هَٰذَا ۙ إِنْ هَٰذَا إِلَّا أَسَاطِيرُ الْأَوَّلِينَ (31) Ndipo pamene chivumbulutso chathu chilakatulidwa kwa iwo, iwo amati: “Ife tamva kale ndipo ngati ife tikanafuna, tikhoza kunena cholingana nacho. Izi si zina koma nkhani zopanda pake za anthu akale.” |
وَإِذْ قَالُوا اللَّهُمَّ إِن كَانَ هَٰذَا هُوَ الْحَقَّ مِنْ عِندِكَ فَأَمْطِرْ عَلَيْنَا حِجَارَةً مِّنَ السَّمَاءِ أَوِ ائْتِنَا بِعَذَابٍ أَلِيمٍ (32) Ndi pamene iwo adanena kuti, “oh Ambuye! Ngati ichi ndi chivumbulutso choonadi chochokera kwa Inu, gwetsani pamwamba pathu miyala kuchokera kumwamba kapena tipatseni chilango chowawa.” |
وَمَا كَانَ اللَّهُ لِيُعَذِّبَهُمْ وَأَنتَ فِيهِمْ ۚ وَمَا كَانَ اللَّهُ مُعَذِّبَهُمْ وَهُمْ يَسْتَغْفِرُونَ (33) Ndipo Mulungu sakadawalanga iwo pamene iwe unali pakati pawo ndipo Iye sadzawalanga pamene iwo ali kupempha chikhululukiro chake |
وَمَا لَهُمْ أَلَّا يُعَذِّبَهُمُ اللَّهُ وَهُمْ يَصُدُّونَ عَنِ الْمَسْجِدِ الْحَرَامِ وَمَا كَانُوا أَوْلِيَاءَهُ ۚ إِنْ أَوْلِيَاؤُهُ إِلَّا الْمُتَّقُونَ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (34) Kodi Mulungu asawalange iwo pamene iwo akhala ali kuletsa ena kuti alowe mu Mzikiti Wolemekezeka ngakhale kuti iwo alibe udindo woteteza Mzikitiwo? Palibe outeteza kupatula okhawo amene amaopa Mulungu, koma ambiri a iwo sadziwa |
وَمَا كَانَ صَلَاتُهُمْ عِندَ الْبَيْتِ إِلَّا مُكَاءً وَتَصْدِيَةً ۚ فَذُوقُوا الْعَذَابَ بِمَا كُنتُمْ تَكْفُرُونَ (35) Mapemphero awo mu Mzikiti wolemekezeka sadali china chili chonse koma miluzu ndi kuomba m’manja basi, motero lawani chilango chifukwa inu simunali kukhulupirira |
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا يُنفِقُونَ أَمْوَالَهُمْ لِيَصُدُّوا عَن سَبِيلِ اللَّهِ ۚ فَسَيُنفِقُونَهَا ثُمَّ تَكُونُ عَلَيْهِمْ حَسْرَةً ثُمَّ يُغْلَبُونَ ۗ وَالَّذِينَ كَفَرُوا إِلَىٰ جَهَنَّمَ يُحْشَرُونَ (36) Ndithudi iwo amene sakhulupirira, amaononga chuma chawo ndi cholinga choletsa anthu kutsatira njira ya Mulungu. Motero iwo adzapitirira kumwaza chuma chawo; koma pomaliza iwo adzanong’oneza bombono. Ndipo adzagonjetsedwa. Ndipo iwo amene sakhulupirira adzasonkhanitsidwaku Gahena |
لِيَمِيزَ اللَّهُ الْخَبِيثَ مِنَ الطَّيِّبِ وَيَجْعَلَ الْخَبِيثَ بَعْضَهُ عَلَىٰ بَعْضٍ فَيَرْكُمَهُ جَمِيعًا فَيَجْعَلَهُ فِي جَهَنَّمَ ۚ أُولَٰئِكَ هُمُ الْخَاسِرُونَ (37) Kuti Mulunguasiyanitse pakati pa anthu oipa ndi abwino ndi kuwaika anthu oipa wina pamwamba pa mnzake, ndipo adzawaunjika onse pamodzi ndi kuwaponya ku Gahena. Awa! Ndiwo amene ali olephera |
قُل لِّلَّذِينَ كَفَرُوا إِن يَنتَهُوا يُغْفَرْ لَهُم مَّا قَدْ سَلَفَ وَإِن يَعُودُوا فَقَدْ مَضَتْ سُنَّتُ الْأَوَّلِينَ (38) Nena kwa anthu osakhulupirira kuti ngati iwo asintha njira yawo, zochimwa zawo zonse zakale zidzakhululukidwa. Koma ngati iwo apitirirabe kuchimwa, zitsanzo za anthu akale, amene Mulungu adawaononga, zikhale phunziro lawo |
وَقَاتِلُوهُمْ حَتَّىٰ لَا تَكُونَ فِتْنَةٌ وَيَكُونَ الدِّينُ كُلُّهُ لِلَّهِ ۚ فَإِنِ انتَهَوْا فَإِنَّ اللَّهَ بِمَا يَعْمَلُونَ بَصِيرٌ (39) Menyanani nawo mpaka pamene kusakhulupirira ndi kupembedza mafano kutha ndipo chipembedzo cha Mulungu chikhazikitsidwa ponseponse koma ngati iwo asiya, ndithudi Mulungu akuona zochita zawo zonse |
وَإِن تَوَلَّوْا فَاعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ مَوْلَاكُمْ ۚ نِعْمَ الْمَوْلَىٰ وَنِعْمَ النَّصِيرُ (40) Koma ngati iwo sakumvera, dziwa kuti Mulungu ndi Mtetezi wako. Iye ndi Mtetezi wabwino ndi Mthandizi wabwino |
۞ وَاعْلَمُوا أَنَّمَا غَنِمْتُم مِّن شَيْءٍ فَأَنَّ لِلَّهِ خُمُسَهُ وَلِلرَّسُولِ وَلِذِي الْقُرْبَىٰ وَالْيَتَامَىٰ وَالْمَسَاكِينِ وَابْنِ السَّبِيلِ إِن كُنتُمْ آمَنتُم بِاللَّهِ وَمَا أَنزَلْنَا عَلَىٰ عَبْدِنَا يَوْمَ الْفُرْقَانِ يَوْمَ الْتَقَى الْجَمْعَانِ ۗ وَاللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (41) Ndipo dziwani kuti pa katundu yense amene mupeza pa nkhondo, ndithudi gawo limodzi pa magawo asanu ndi la Mulungu ndi Mtumwi ndi abale ake ndi ana a masiye, anthu osauka ndi a paulendo, ngati inu mukhulupirira mwa Mulungu ndi m’chivumbulutso chathu chimene tidatumiza kwa kapolo wathu ndi tsiku lamayeso, tsiku limene magulu awiri a nkhondo adakumana. Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu pa chilichonse |
إِذْ أَنتُم بِالْعُدْوَةِ الدُّنْيَا وَهُم بِالْعُدْوَةِ الْقُصْوَىٰ وَالرَّكْبُ أَسْفَلَ مِنكُمْ ۚ وَلَوْ تَوَاعَدتُّمْ لَاخْتَلَفْتُمْ فِي الْمِيعَادِ ۙ وَلَٰكِن لِّيَقْضِيَ اللَّهُ أَمْرًا كَانَ مَفْعُولًا لِّيَهْلِكَ مَنْ هَلَكَ عَن بَيِّنَةٍ وَيَحْيَىٰ مَنْ حَيَّ عَن بَيِّنَةٍ ۗ وَإِنَّ اللَّهَ لَسَمِيعٌ عَلِيمٌ (42) Ndi pamene inu mudali tsidya lino la dambo ndi pamene anthu osakhulupirira adali tsidya ilo ndi magareta mmunsi mwanu. Ngakhale inu mukadagwirizana za malo okumana, inu mukadalephera kukwaniritsa chipanganocho koma Mulungu adafunitsitsa kuti akwaniritse zonse zimene adalamulira kuti aliyense amene adalembedwa kuti adzaonongeka, aonongeke pamene atalandira malangizo ooneka ndipo kuti iwo amene adalembedwa kuti asafe akhale ndi moyo atalandira malangizo ooneka. Ndithudi Mulungu ndi wakumva ndi wodziwa |
إِذْ يُرِيكَهُمُ اللَّهُ فِي مَنَامِكَ قَلِيلًا ۖ وَلَوْ أَرَاكَهُمْ كَثِيرًا لَّفَشِلْتُمْ وَلَتَنَازَعْتُمْ فِي الْأَمْرِ وَلَٰكِنَّ اللَّهَ سَلَّمَ ۗ إِنَّهُ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (43) Pamene Mulungu adakuonetsam’malotoakongatigululaling’ono.Akadakhala kuti adakuonetsa iwe kuti ndi gulu lalikulu, ndithudi iwe ukadagwa mphwayi ndipo ukadavutika popereka malamulo. Koma Mulungu adakupulumutsa. Ndithudi Iye amadziwa zinthu zonse zimene zili m’maganizo mwanu |
وَإِذْ يُرِيكُمُوهُمْ إِذِ الْتَقَيْتُمْ فِي أَعْيُنِكُمْ قَلِيلًا وَيُقَلِّلُكُمْ فِي أَعْيُنِهِمْ لِيَقْضِيَ اللَّهُ أَمْرًا كَانَ مَفْعُولًا ۗ وَإِلَى اللَّهِ تُرْجَعُ الْأُمُورُ (44) Ndipamenemudakumananawo,Mulunguadakuonetsani ngati ochepa m’maso mwanu ndipo anakuonetsani iwo inu ngati ochepa m’maso mwawo kuti Mulungu akwaniritse lamulo lake, limene anakhazikitsa kale, ndipo ndi kwa Mulungu kumene zinthu zonse zimabwerera |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِذَا لَقِيتُمْ فِئَةً فَاثْبُتُوا وَاذْكُرُوا اللَّهَ كَثِيرًا لَّعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ (45) oh inu anthu okhulupirira! Ngati mukumana ndi gulu la nkhondo limbikani ndipo kumbukirani dzina la Mulungu kwambiri kuti mupambane |
وَأَطِيعُوا اللَّهَ وَرَسُولَهُ وَلَا تَنَازَعُوا فَتَفْشَلُوا وَتَذْهَبَ رِيحُكُمْ ۖ وَاصْبِرُوا ۚ إِنَّ اللَّهَ مَعَ الصَّابِرِينَ (46) Ndipo mverani Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo musatsutsane wina ndi mnzake chifukwa mudzakhumudwa ndi kuchita ulesi, ndipo pirirani. Ndithudi Mulungu ali pamodzi ndi anthu opirira |
وَلَا تَكُونُوا كَالَّذِينَ خَرَجُوا مِن دِيَارِهِم بَطَرًا وَرِئَاءَ النَّاسِ وَيَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ اللَّهِ ۚ وَاللَّهُ بِمَا يَعْمَلُونَ مُحِيطٌ (47) Ndipo musakhale ngati iwo amene amachoka m’nyumba mwawo modzitukumula ndi kudzionetsera kwa anthu ndi kuwaletsa anthu kutsatira njira ya Mulungu, ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene iwo amachita |
وَإِذْ زَيَّنَ لَهُمُ الشَّيْطَانُ أَعْمَالَهُمْ وَقَالَ لَا غَالِبَ لَكُمُ الْيَوْمَ مِنَ النَّاسِ وَإِنِّي جَارٌ لَّكُمْ ۖ فَلَمَّا تَرَاءَتِ الْفِئَتَانِ نَكَصَ عَلَىٰ عَقِبَيْهِ وَقَالَ إِنِّي بَرِيءٌ مِّنكُمْ إِنِّي أَرَىٰ مَا لَا تَرَوْنَ إِنِّي أَخَافُ اللَّهَ ۚ وَاللَّهُ شَدِيدُ الْعِقَابِ (48) Ndi pamene Satana adakometsa ntchito zawo zopusa nati, “Palibe munthu wina aliyense amene adzakugonjetsani inu lero, ndithudi ine ndidzakhala pafupi kukuthandizani inu.” Koma pamene magulu awiri a nkhondo adakumana, iye adathawa ndipo anati: “Ndithudi ine ndilibe nanu ntchito. Ndithudi ine ndaona zimene inu simungathe kuziona. Ndithudi ine ndiopa Mulungu chifukwa chilango chake ndi choopsya.” |
إِذْ يَقُولُ الْمُنَافِقُونَ وَالَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٌ غَرَّ هَٰؤُلَاءِ دِينُهُمْ ۗ وَمَن يَتَوَكَّلْ عَلَى اللَّهِ فَإِنَّ اللَّهَ عَزِيزٌ حَكِيمٌ (49) Pamene anthu a chinyengo pamodzi ndi anthu amene m’mitima mwawo mudali matenda adati: “Anthu awa ali kunyengedwa ndi chipembedzo chawo.” Koma aliyense amene aika chikhulupiriro chake mwa Mulungu, ndithudi, Mulungu ndi Wamphamvu ndi Wanzeru |
وَلَوْ تَرَىٰ إِذْ يَتَوَفَّى الَّذِينَ كَفَرُوا ۙ الْمَلَائِكَةُ يَضْرِبُونَ وُجُوهَهُمْ وَأَدْبَارَهُمْ وَذُوقُوا عَذَابَ الْحَرِيقِ (50) Iwe ukadawaona angelo pamene amachotsa mizimu ya anthu osakhulupirira! Iwo amamenya pa nkhope ndi pa misana yawo nati: “Lawani ululu wa moto wa ku Gahena.” |
ذَٰلِكَ بِمَا قَدَّمَتْ أَيْدِيكُمْ وَأَنَّ اللَّهَ لَيْسَ بِظَلَّامٍ لِّلْعَبِيدِ (51) “Ichi ndi chifukwa cha zimene manja anu adatsogoza. Ndipo ndithudi, Mulungu sapondereza akapolo ake.” |
كَدَأْبِ آلِ فِرْعَوْنَ ۙ وَالَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۚ كَفَرُوا بِآيَاتِ اللَّهِ فَأَخَذَهُمُ اللَّهُ بِذُنُوبِهِمْ ۗ إِنَّ اللَّهَ قَوِيٌّ شَدِيدُ الْعِقَابِ (52) Monga anthu a Farao ndi iwo amene adalipo kale, iwo adakana zizindikiro za Mulungu, ndipo Mulungu adawalanga chifukwa cha kulakwa kwawo. Ndithudi Mulungu ndi wamphamvu ndipo amakhwimitsa chilango |
ذَٰلِكَ بِأَنَّ اللَّهَ لَمْ يَكُ مُغَيِّرًا نِّعْمَةً أَنْعَمَهَا عَلَىٰ قَوْمٍ حَتَّىٰ يُغَيِّرُوا مَا بِأَنفُسِهِمْ ۙ وَأَنَّ اللَّهَ سَمِيعٌ عَلِيمٌ (53) Ichi ndi chifukwa chakuti Mulungu sasintha madalitso amene amapereka kwa anthu mpaka pamene iwo asintha makhalidwe awo, ndipo ndithudi, Mulungu ndi wakumva ndi wodziwa |
كَدَأْبِ آلِ فِرْعَوْنَ ۙ وَالَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۚ كَذَّبُوا بِآيَاتِ رَبِّهِمْ فَأَهْلَكْنَاهُم بِذُنُوبِهِمْ وَأَغْرَقْنَا آلَ فِرْعَوْنَ ۚ وَكُلٌّ كَانُوا ظَالِمِينَ (54) Monga anthu a Farawo ndi iwo amene adalipo kale, iwo sadakhulupirire uthenga wa Ambuye wawo kotero Ife tidawaononga chifukwa cha zolakwa zawo ndipo Ife tidamiza anthu a Farawo chifukwa onse adali osalungama |
إِنَّ شَرَّ الدَّوَابِّ عِندَ اللَّهِ الَّذِينَ كَفَرُوا فَهُمْ لَا يُؤْمِنُونَ (55) Ndithudi zolengedwa za moyo zimene ndi zoipitsitsa pamaso pa Mulungu ndi anthu osakhulupirira ndipo iwo sadzakhulupirira |
الَّذِينَ عَاهَدتَّ مِنْهُمْ ثُمَّ يَنقُضُونَ عَهْدَهُمْ فِي كُلِّ مَرَّةٍ وَهُمْ لَا يَتَّقُونَ (56) Iwo ndiwo amene iwe umapanga nawo mapangano koma iwo amaphwanya mapangano awo nthawi zonse ndipo iwo saopa Mulungu |
فَإِمَّا تَثْقَفَنَّهُمْ فِي الْحَرْبِ فَشَرِّدْ بِهِم مَّنْ خَلْفَهُمْ لَعَلَّهُمْ يَذَّكَّرُونَ (57) Ngati iwe uwapambana pomenyana nawo nkhondo, alange kwambiri kuti ukhoza kuthamangitsa iwo amene ali kumbuyo kwawo kuti akhoza kuphunzira |
وَإِمَّا تَخَافَنَّ مِن قَوْمٍ خِيَانَةً فَانبِذْ إِلَيْهِمْ عَلَىٰ سَوَاءٍ ۚ إِنَّ اللَّهَ لَا يُحِبُّ الْخَائِنِينَ (58) Ngati iwe uopa chinyengo chochokera kwa anthu, nawenso abwezere mwawubwino machitidwe omwewo. Ndithudi Mulungu sakonda anthu aupandu |
وَلَا يَحْسَبَنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا سَبَقُوا ۚ إِنَّهُمْ لَا يُعْجِزُونَ (59) Ndipo anthu osakhulupirira asaganize kuti akhoza kuthawa chilango. Ndithudi iwo sadzatha kudzipulumutsa |
وَأَعِدُّوا لَهُم مَّا اسْتَطَعْتُم مِّن قُوَّةٍ وَمِن رِّبَاطِ الْخَيْلِ تُرْهِبُونَ بِهِ عَدُوَّ اللَّهِ وَعَدُوَّكُمْ وَآخَرِينَ مِن دُونِهِمْ لَا تَعْلَمُونَهُمُ اللَّهُ يَعْلَمُهُمْ ۚ وَمَا تُنفِقُوا مِن شَيْءٍ فِي سَبِيلِ اللَّهِ يُوَفَّ إِلَيْكُمْ وَأَنتُمْ لَا تُظْلَمُونَ (60) Ndipo akonzekereni iwo mwamphamvu, mmene mungathere, kuopseza adani a Mulungu ndi adani anu ndiponso ena amene inu simuli kuwadziwa koma Mulungu amawadziwa. Ndipo chili chonse chimene mudzaononga mu njira ya Mulungu chidzabwezedwa kwa inu ndipo inu simudzaponderezedwa |
۞ وَإِن جَنَحُوا لِلسَّلْمِ فَاجْنَحْ لَهَا وَتَوَكَّلْ عَلَى اللَّهِ ۚ إِنَّهُ هُوَ السَّمِيعُ الْعَلِيمُ (61) Koma ngati iwo afuna kukhazikitsa mtendere, nanunso khazikitsani mtendere ndipo khulupirirani mwa Mulungu. Ndithudi Iye ndi wakumva ndi wodziwa |
وَإِن يُرِيدُوا أَن يَخْدَعُوكَ فَإِنَّ حَسْبَكَ اللَّهُ ۚ هُوَ الَّذِي أَيَّدَكَ بِنَصْرِهِ وَبِالْمُؤْمِنِينَ (62) Ndipo ngati iwo afuna kukunyenga ndithudi Mulungu ndi wokwanira kwa iwe. Iye ndiye amene adakulimbikitsa pokupatsa chithandizo chake ndi anthu okhulupirira |
وَأَلَّفَ بَيْنَ قُلُوبِهِمْ ۚ لَوْ أَنفَقْتَ مَا فِي الْأَرْضِ جَمِيعًا مَّا أَلَّفْتَ بَيْنَ قُلُوبِهِمْ وَلَٰكِنَّ اللَّهَ أَلَّفَ بَيْنَهُمْ ۚ إِنَّهُ عَزِيزٌ حَكِيمٌ (63) Ndipo Iye wayanjanitsa mitima yawo. Ngati iwe ukadawononga zinthu zonse za padziko lapansi iwe siukadatha kuyanjanitsa mitima yawo ayi koma Mulungu waiyanjanitsa. Ndithudi Iye ndi Wamphamvu ndi Wanzeru |
يَا أَيُّهَا النَّبِيُّ حَسْبُكَ اللَّهُ وَمَنِ اتَّبَعَكَ مِنَ الْمُؤْمِنِينَ (64) oh iwe Mtumwi! Mulungu ndi wokwanira kwa iwe ndi kwa anthu okhulupirira amene amakutsatira iwe |
يَا أَيُّهَا النَّبِيُّ حَرِّضِ الْمُؤْمِنِينَ عَلَى الْقِتَالِ ۚ إِن يَكُن مِّنكُمْ عِشْرُونَ صَابِرُونَ يَغْلِبُوا مِائَتَيْنِ ۚ وَإِن يَكُن مِّنكُم مِّائَةٌ يَغْلِبُوا أَلْفًا مِّنَ الَّذِينَ كَفَرُوا بِأَنَّهُمْ قَوْمٌ لَّا يَفْقَهُونَ (65) oh iwe Mtumwi! Alimbikitse anthu okhulupirira kuti amenye nkhondo. Ngati pali anthu makumi awiri opilira pakati panu, iwo adzagonjetsa anthu mazana awiri; ndipo ngati pali anthu zana limodzi, iwo adzagonjetsa anthu chikwi chimodzi cha anthu osakhulupirira chifukwa iwo ndi anthu amene sazindikira |
الْآنَ خَفَّفَ اللَّهُ عَنكُمْ وَعَلِمَ أَنَّ فِيكُمْ ضَعْفًا ۚ فَإِن يَكُن مِّنكُم مِّائَةٌ صَابِرَةٌ يَغْلِبُوا مِائَتَيْنِ ۚ وَإِن يَكُن مِّنكُمْ أَلْفٌ يَغْلِبُوا أَلْفَيْنِ بِإِذْنِ اللَّهِ ۗ وَاللَّهُ مَعَ الصَّابِرِينَ (66) Mulungu tsopano wachepetsa vuto lanu chifukwa Iye adziwa kuti pakati panu pali anthu ofoka. Motero ngati pali anthu zana limodzi opilira pakati panu iwo adzagonjetsa anthu mazana awiri, ndipo ngati pali anthu chikwi chimodzi, iwo adzagonjetsa anthu zikwi ziwiri mwachifuniro cha Mulungu. Ndipo Mulungu ali pamodzi ndi anthu opirira |
مَا كَانَ لِنَبِيٍّ أَن يَكُونَ لَهُ أَسْرَىٰ حَتَّىٰ يُثْخِنَ فِي الْأَرْضِ ۚ تُرِيدُونَ عَرَضَ الدُّنْيَا وَاللَّهُ يُرِيدُ الْآخِرَةَ ۗ وَاللَّهُ عَزِيزٌ حَكِيمٌ (67) Sikoyenera kuti Mtumwi akhale ndi akapolo a nkhondo mpaka iye atamenya nkhondo ndi kupambana m’dziko. Inu mufuna kupeza zinthu zabwino za m’dziko lino koma Mulungu akukufunirani za m’dziko limene lili nkudza. Mulungu ndi wamphamvu ndi wanzeru |
لَّوْلَا كِتَابٌ مِّنَ اللَّهِ سَبَقَ لَمَسَّكُمْ فِيمَا أَخَذْتُمْ عَذَابٌ عَظِيمٌ (68) Pakadakhala kuti padalibe lamulo lakale lochokera kwa Mulungu, inu mukadalangidwa kwambiri chifukwa cha zinthu zimene mwatenga |
فَكُلُوا مِمَّا غَنِمْتُمْ حَلَالًا طَيِّبًا ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۚ إِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (69) Ndipo idyani zinthu zabwino zololedwa zimene mwazipeza pa nkhondo ndipo opani Mulungu. Ndithudi Mulungu amakhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha |
يَا أَيُّهَا النَّبِيُّ قُل لِّمَن فِي أَيْدِيكُم مِّنَ الْأَسْرَىٰ إِن يَعْلَمِ اللَّهُ فِي قُلُوبِكُمْ خَيْرًا يُؤْتِكُمْ خَيْرًا مِّمَّا أُخِذَ مِنكُمْ وَيَغْفِرْ لَكُمْ ۗ وَاللَّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (70) o Iwe Mtumwi! Nena kwa iwo amene mwawagwira ukapolo, “Ngati Mulungu adziwa ubwino m’mitima mwanu, Iye adzakupatsani zinthu zabwino kuposa zimene mwalandidwa ndipo adzakukhululukirani machimo anu. Mulungu amakhululukira ndipo ndi Wachisoni chosatha.” |
وَإِن يُرِيدُوا خِيَانَتَكَ فَقَدْ خَانُوا اللَّهَ مِن قَبْلُ فَأَمْكَنَ مِنْهُمْ ۗ وَاللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٌ (71) Koma ngati iwo afuna kukunyenga iwe, iwo adamunyenga kale Mulungu. Motero wakupatsa iwe mphamvu kuti uwapambane iwo. Ndipo Mulungu ndi wodziwa ndi waluntha |
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا وَهَاجَرُوا وَجَاهَدُوا بِأَمْوَالِهِمْ وَأَنفُسِهِمْ فِي سَبِيلِ اللَّهِ وَالَّذِينَ آوَوا وَّنَصَرُوا أُولَٰئِكَ بَعْضُهُمْ أَوْلِيَاءُ بَعْضٍ ۚ وَالَّذِينَ آمَنُوا وَلَمْ يُهَاجِرُوا مَا لَكُم مِّن وَلَايَتِهِم مِّن شَيْءٍ حَتَّىٰ يُهَاجِرُوا ۚ وَإِنِ اسْتَنصَرُوكُمْ فِي الدِّينِ فَعَلَيْكُمُ النَّصْرُ إِلَّا عَلَىٰ قَوْمٍ بَيْنَكُمْ وَبَيْنَهُم مِّيثَاقٌ ۗ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌ (72) Ndithudi iwo amene adakhulupirira ndi kusamuka ndipoanapilirandikumenyankhondondichumachawondi iwoenim’njiraya Mulungundipondiiwoameneadawasunga ndi kuwathandiza, amenewa adzakhala a bwenzi a wina ndi mnzake. Iwo amene akhulupirira koma sadasamuke mwa njira iliyonse iwe ulibe udindo pa iwo pokhapokha ngati iwo asamuka. Koma ngati iwo afuna chithandizo cha chipembedzo ndi udindo wako kuwathandiza kupatula anthu amene ali ndi pangano logwirizana pakati pa inu ndi iwo ndipo Mulungu amaona ntchito zanu zonse |
وَالَّذِينَ كَفَرُوا بَعْضُهُمْ أَوْلِيَاءُ بَعْضٍ ۚ إِلَّا تَفْعَلُوهُ تَكُن فِتْنَةٌ فِي الْأَرْضِ وَفَسَادٌ كَبِيرٌ (73) Ndipo anthu osakhulupirira ndi abwenzi wina ndi mnzake. Ndipo ngati inu simuchita chimodzimodzi mudzakhala chisokonezo ndi kuponderezana m’dziko ndiponso chionongeko chachikulu |
وَالَّذِينَ آمَنُوا وَهَاجَرُوا وَجَاهَدُوا فِي سَبِيلِ اللَّهِ وَالَّذِينَ آوَوا وَّنَصَرُوا أُولَٰئِكَ هُمُ الْمُؤْمِنُونَ حَقًّا ۚ لَّهُم مَّغْفِرَةٌ وَرِزْقٌ كَرِيمٌ (74) Ndipo iwo amene adakhulupirira ndipo adasamuka ndipo adamenya nkhondo molimbika mu njira ya Mulungu, ndi iwo amene adawasunga ndi kuwathandiza amenewo ndiwo okhulupirira enieni ndipo iwo adzalandira chikhululukiro ndi zabwino zambiri |
وَالَّذِينَ آمَنُوا مِن بَعْدُ وَهَاجَرُوا وَجَاهَدُوا مَعَكُمْ فَأُولَٰئِكَ مِنكُمْ ۚ وَأُولُو الْأَرْحَامِ بَعْضُهُمْ أَوْلَىٰ بِبَعْضٍ فِي كِتَابِ اللَّهِ ۗ إِنَّ اللَّهَ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (75) Ndipo iwo amene adakhulupirira pambuyo pake kale ndipo adasamuka ndi kumenya nkhondo pamodzi ndi iwe, iwo ndi abale ako. Koma ubale wa magazi amodzi umakhala woganiziridwa polandira katundu malinga ndi malamulo a Mulungu amene adaperekedwa. Ndithudi Mulungu amadziwa zinthu zonse |