Quran with Chichewa translation - Surah At-Taubah ayat 111 - التوبَة - Page - Juz 11
﴿۞ إِنَّ ٱللَّهَ ٱشۡتَرَىٰ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ أَنفُسَهُمۡ وَأَمۡوَٰلَهُم بِأَنَّ لَهُمُ ٱلۡجَنَّةَۚ يُقَٰتِلُونَ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ فَيَقۡتُلُونَ وَيُقۡتَلُونَۖ وَعۡدًا عَلَيۡهِ حَقّٗا فِي ٱلتَّوۡرَىٰةِ وَٱلۡإِنجِيلِ وَٱلۡقُرۡءَانِۚ وَمَنۡ أَوۡفَىٰ بِعَهۡدِهِۦ مِنَ ٱللَّهِۚ فَٱسۡتَبۡشِرُواْ بِبَيۡعِكُمُ ٱلَّذِي بَايَعۡتُم بِهِۦۚ وَذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ ﴾
[التوبَة: 111]
﴿إن الله اشترى من المؤمنين أنفسهم وأموالهم بأن لهم الجنة يقاتلون في﴾ [التوبَة: 111]
Khaled Ibrahim Betala “Ndithu Allah wagula kwa okhulupirira moyo wawo ndi chuma chawo (kuti apereke moyo wawo ndi chuma chawo pomenya nkhondo pa njira ya Allah) kuti iwo alandire Munda wamtendere. Akumenya nkhondo pa njira ya Allah, ndipo akupha ndi kuphedwa. Ili ndi lonjezo loona lokakamizika pa Iye lomwe likupezeka m’buku la Taurati, Injili ndi Qur’an. Kodi ndani wokwaniritsa lonjezo lake kuposa Allah? Choncho kondwerani ndi kugulitsa kwanu komwe mwagulitsana Naye. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu |