Quran with Chichewa translation - Surah At-Taubah ayat 7 - التوبَة - Page - Juz 10
﴿كَيۡفَ يَكُونُ لِلۡمُشۡرِكِينَ عَهۡدٌ عِندَ ٱللَّهِ وَعِندَ رَسُولِهِۦٓ إِلَّا ٱلَّذِينَ عَٰهَدتُّمۡ عِندَ ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِۖ فَمَا ٱسۡتَقَٰمُواْ لَكُمۡ فَٱسۡتَقِيمُواْ لَهُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ يُحِبُّ ٱلۡمُتَّقِينَ ﴾
[التوبَة: 7]
﴿كيف يكون للمشركين عهد عند الله وعند رسوله إلا الذين عاهدتم عند﴾ [التوبَة: 7]
Khaled Ibrahim Betala “Chingakhalepo bwanji chipangano pakati pa Amushirikina (oswa mapangano nthawi ndi nthawi) ndi Allah ndi Mthenga Wake, kupatula okhawo amene mudapangana nawo mapangano pa Msikiti Wopatulika? (Amene adakwaniritsa mapangano awo). Ngati iwo akupitiriza kulungama (posunga mapanganowo) kwa inu, nanunso pitirizani kulungama kwa iwo. Ndithu Allah akukonda amene akumuopa |