×

Surah Al-Hujuraat in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Hujurat

Translation of the Meanings of Surah Hujurat in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Hujurat translated into Chichewa, Surah Al-Hujuraat in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Hujurat in Chichewa - نيانجا, Verses 18 - Surah Number 49 - Page 515.

بسم الله الرحمن الرحيم

يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تُقَدِّمُوا بَيْنَ يَدَيِ اللَّهِ وَرَسُولِهِ ۖ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۚ إِنَّ اللَّهَ سَمِيعٌ عَلِيمٌ (1)
Oh inu anthu okhulupirira! Musadzikweze pamaso pa Mulungu ndi pa Mthenga wake, koma opani Mulungu chifukwa Iye ndiye amene amamva ndi kudziwa chinthu china chilichonse
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَرْفَعُوا أَصْوَاتَكُمْ فَوْقَ صَوْتِ النَّبِيِّ وَلَا تَجْهَرُوا لَهُ بِالْقَوْلِ كَجَهْرِ بَعْضِكُمْ لِبَعْضٍ أَن تَحْبَطَ أَعْمَالُكُمْ وَأَنتُمْ لَا تَشْعُرُونَ (2)
Oh inu anthu okhulupirira! Musakweze mawu anu kuposa a Mtumwi ndipo musayankhule ndi mawu okweza kwa iye monga momwe mumachitira mukamayankhulana nokhanokhanu chifukwa ntchito zanu zingasanduke zopanda pake pamene inu simuli kudziwa
إِنَّ الَّذِينَ يَغُضُّونَ أَصْوَاتَهُمْ عِندَ رَسُولِ اللَّهِ أُولَٰئِكَ الَّذِينَ امْتَحَنَ اللَّهُ قُلُوبَهُمْ لِلتَّقْوَىٰ ۚ لَهُم مَّغْفِرَةٌ وَأَجْرٌ عَظِيمٌ (3)
Ndithudi iwo amene amayankhula motsitsa pamaso pa Mtumwi wa Mulungu ndiwo amene Mulungu wayesa mitima yawo kuti ndi yabwino, ndipo iwo adzalandira chikhululukiro ndi mphotho yaikulu
إِنَّ الَّذِينَ يُنَادُونَكَ مِن وَرَاءِ الْحُجُرَاتِ أَكْثَرُهُمْ لَا يَعْقِلُونَ (4)
Ndithudi iwo amene amafuulira iwe kunja kwa zipinda, onse alibe nzeru
وَلَوْ أَنَّهُمْ صَبَرُوا حَتَّىٰ تَخْرُجَ إِلَيْهِمْ لَكَانَ خَيْرًا لَّهُمْ ۚ وَاللَّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (5)
Iwo akadapirira mpaka pamene iwe udza kwa iwo, ndithudi, zikadakhala bwino ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِن جَاءَكُمْ فَاسِقٌ بِنَبَإٍ فَتَبَيَّنُوا أَن تُصِيبُوا قَوْمًا بِجَهَالَةٍ فَتُصْبِحُوا عَلَىٰ مَا فَعَلْتُمْ نَادِمِينَ (6)
oh inu anthu okhulupirira! Ngati munthu wochita zoipa adza kwa inu ndi nkhani, ifufuzeni poyamba chifukwa mwina mukhoza kupweteka anthu mosadziwa ndi kuyamba kumva chisoni pambuyo pake chifukwa cha zimene mwachita
وَاعْلَمُوا أَنَّ فِيكُمْ رَسُولَ اللَّهِ ۚ لَوْ يُطِيعُكُمْ فِي كَثِيرٍ مِّنَ الْأَمْرِ لَعَنِتُّمْ وَلَٰكِنَّ اللَّهَ حَبَّبَ إِلَيْكُمُ الْإِيمَانَ وَزَيَّنَهُ فِي قُلُوبِكُمْ وَكَرَّهَ إِلَيْكُمُ الْكُفْرَ وَالْفُسُوقَ وَالْعِصْيَانَ ۚ أُولَٰئِكَ هُمُ الرَّاشِدُونَ (7)
Ndipo dziwani kuti pakati panu pali Mtumwi wa Mulungu ndipo iye akamachita zimene Al Hujurat 553 mufuna, ndithudi, inu mukadavutika kwambiri. Koma Mulungu wakusungitsani inu chipembedzo chake ndipo wachipanga icho kukhala chokongola m’mitima mwanu, ndi kupanga kusakhulupirira kukhala chinthu choipa ndiponso kuswa malamulo ndi kusamvera. Awa ndiwo amene amatsatira njira yoyenera
فَضْلًا مِّنَ اللَّهِ وَنِعْمَةً ۚ وَاللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٌ (8)
Chisomo ndi chifundo chochokera kwa Mulungu. Ndipo Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse ndipo ndi wanzeru kwambiri
وَإِن طَائِفَتَانِ مِنَ الْمُؤْمِنِينَ اقْتَتَلُوا فَأَصْلِحُوا بَيْنَهُمَا ۖ فَإِن بَغَتْ إِحْدَاهُمَا عَلَى الْأُخْرَىٰ فَقَاتِلُوا الَّتِي تَبْغِي حَتَّىٰ تَفِيءَ إِلَىٰ أَمْرِ اللَّهِ ۚ فَإِن فَاءَتْ فَأَصْلِحُوا بَيْنَهُمَا بِالْعَدْلِ وَأَقْسِطُوا ۖ إِنَّ اللَّهَ يُحِبُّ الْمُقْسِطِينَ (9)
Ngati magulu awiri ochokera kwa anthu okhulupirira amenyana, khazikitsa mtendere pakati pawo. Koma ngati gulu lina liswa malamulo mopyola muyeso, nonse menyanani nalo gulu lotero mpaka pamene limvera lamulo la Mulungu. Ndipo ngati ilo limvera, khazikitsani mtendere pakati pawo mwachilungamo. Ndithudi Mulungu amakonda iwo amene amachita chilungamo
إِنَّمَا الْمُؤْمِنُونَ إِخْوَةٌ فَأَصْلِحُوا بَيْنَ أَخَوَيْكُمْ ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ لَعَلَّكُمْ تُرْحَمُونَ (10)
Onse okhulupirira ali pachibale. Kotero khazikitsani mtendere ndi kukhululukirana ndi abale anu ndipo opani Mulungu kuti mulandire chisomo chake
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا يَسْخَرْ قَوْمٌ مِّن قَوْمٍ عَسَىٰ أَن يَكُونُوا خَيْرًا مِّنْهُمْ وَلَا نِسَاءٌ مِّن نِّسَاءٍ عَسَىٰ أَن يَكُنَّ خَيْرًا مِّنْهُنَّ ۖ وَلَا تَلْمِزُوا أَنفُسَكُمْ وَلَا تَنَابَزُوا بِالْأَلْقَابِ ۖ بِئْسَ الِاسْمُ الْفُسُوقُ بَعْدَ الْإِيمَانِ ۚ وَمَن لَّمْ يَتُبْ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الظَّالِمُونَ (11)
oh inu anthu okhulupirira! Musalole kuti anthu ena aziseka anzawo. Mwina kungatheke kuti gulu limene lisekedwa likhoza kukhala labwino kuposa limene likuseka. Ndiponso musalole akazi kuti aseke anzawo chifukwa mwina kungatheke kuti osekedwawo akhoza kukhala abwino kuposa osekawo. Musafunirane zifukwa wina ndi mnzake kapena kuitanana ndi mayina a mchedzera. Mayina a mchedzera ndi oipa kwa amene wakhulupirira. Ndipo aliyense amene sasiya kuitana anzake ndi maina a mchedzera , ameneyo ndiye wopanda chilungamo
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا اجْتَنِبُوا كَثِيرًا مِّنَ الظَّنِّ إِنَّ بَعْضَ الظَّنِّ إِثْمٌ ۖ وَلَا تَجَسَّسُوا وَلَا يَغْتَب بَّعْضُكُم بَعْضًا ۚ أَيُحِبُّ أَحَدُكُمْ أَن يَأْكُلَ لَحْمَ أَخِيهِ مَيْتًا فَكَرِهْتُمُوهُ ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۚ إِنَّ اللَّهَ تَوَّابٌ رَّحِيمٌ (12)
oh inu anthu akhulupirira! Pewani kukaikirana chifukwa kukhala ndi chikayiko ndi tchimo. Ndipo musachite ukazitape pakati panu kapena amiseche. Kodi wina wa inu angakondwere kudya mnofu wa mnzake amene ndi wakufa? Kodi koma inu mumakana kudya.. Kotero opani Mulungu. Ndithudi Mulungu amabwezera chisoni chifukwa ndiye Mwini Chisoni Chosatha
يَا أَيُّهَا النَّاسُ إِنَّا خَلَقْنَاكُم مِّن ذَكَرٍ وَأُنثَىٰ وَجَعَلْنَاكُمْ شُعُوبًا وَقَبَائِلَ لِتَعَارَفُوا ۚ إِنَّ أَكْرَمَكُمْ عِندَ اللَّهِ أَتْقَاكُمْ ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلِيمٌ خَبِيرٌ (13)
oh anthu inu inu! Ndithudi Ife tidakulengani inu mwamuna ndi mkazi ndipo tidakupangani inu kukhala mitundu ya anthu ndi mabanja muzidziwana, Ndithudi wopambana kwambiri pakati panu ndiponso pamaso pa Mulungu ndi amene amaopa Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi wodziwa chinthu china chilichonse
۞ قَالَتِ الْأَعْرَابُ آمَنَّا ۖ قُل لَّمْ تُؤْمِنُوا وَلَٰكِن قُولُوا أَسْلَمْنَا وَلَمَّا يَدْخُلِ الْإِيمَانُ فِي قُلُوبِكُمْ ۖ وَإِن تُطِيعُوا اللَّهَ وَرَسُولَهُ لَا يَلِتْكُم مِّنْ أَعْمَالِكُمْ شَيْئًا ۚ إِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (14)
Anthu okhala m’midzi amati, “Ife timakhulupirira.” Nena, “Inu mulibe chikhulupiriro. Koma nenani kuti, “Tadzipereka kwa Mulungu chifukwa chikhulupiriro sichidakhazikike m’mitima mwanu. Ndipo ngati inu mumvera Mulungu ndi Mtumwi wake, Iye sadzachepetsa ntchito zanu, ngakhale m’pang’ono pomwe. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira nthawi zonse ndi Mwini chisoni chosatha.”
إِنَّمَا الْمُؤْمِنُونَ الَّذِينَ آمَنُوا بِاللَّهِ وَرَسُولِهِ ثُمَّ لَمْ يَرْتَابُوا وَجَاهَدُوا بِأَمْوَالِهِمْ وَأَنفُسِهِمْ فِي سَبِيلِ اللَّهِ ۚ أُولَٰئِكَ هُمُ الصَّادِقُونَ (15)
okhulupirira ndi okhawo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo sakayika ngakhale ndi pang’ono pomwe. Iwo amadzipereka kwathunthu pamodzi ndi chuma chawo m’njira ya Mulungu. Ndipo iwo ndiwo olungama
قُلْ أَتُعَلِّمُونَ اللَّهَ بِدِينِكُمْ وَاللَّهُ يَعْلَمُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۚ وَاللَّهُ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (16)
Nena, “Kodi inu mungamuphunzitse Mulungu za chipembedzo chanu? Pamene Mulungu amadziwa chilichonse chili mlengalenga ndi padziko lapansi. Ndipo Mulungundi wodziwa chilichonse
يَمُنُّونَ عَلَيْكَ أَنْ أَسْلَمُوا ۖ قُل لَّا تَمُنُّوا عَلَيَّ إِسْلَامَكُم ۖ بَلِ اللَّهُ يَمُنُّ عَلَيْكُمْ أَنْ هَدَاكُمْ لِلْإِيمَانِ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (17)
Iwo amaganiza kuti ali kukuchitira iwe chisoni pamene alowa Chisilamu. Nena, “Inu simuli kundichitira ine chisoni polowa chisilamu. Iyayi, koma ndi Mulungu amene wakuchitirani inu chisoni pokulangizani njira yoyenera ngati inu, muli anthu olungama.”
إِنَّ اللَّهَ يَعْلَمُ غَيْبَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ وَاللَّهُ بَصِيرٌ بِمَا تَعْمَلُونَ (18)
Ndithudi Mulungu amadziwa zobisika zonse zimene zili mlengalenga ndi padziko lapansi ndipo Mulungu amaona zonse zimene mumachita
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas