يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَتَّخِذُوا عَدُوِّي وَعَدُوَّكُمْ أَوْلِيَاءَ تُلْقُونَ إِلَيْهِم بِالْمَوَدَّةِ وَقَدْ كَفَرُوا بِمَا جَاءَكُم مِّنَ الْحَقِّ يُخْرِجُونَ الرَّسُولَ وَإِيَّاكُمْ ۙ أَن تُؤْمِنُوا بِاللَّهِ رَبِّكُمْ إِن كُنتُمْ خَرَجْتُمْ جِهَادًا فِي سَبِيلِي وَابْتِغَاءَ مَرْضَاتِي ۚ تُسِرُّونَ إِلَيْهِم بِالْمَوَدَّةِ وَأَنَا أَعْلَمُ بِمَا أَخْفَيْتُمْ وَمَا أَعْلَنتُمْ ۚ وَمَن يَفْعَلْهُ مِنكُمْ فَقَدْ ضَلَّ سَوَاءَ السَّبِيلِ (1) oh inu anthu amene mwakhulupirira! Musasandutse adani anga ndi adani anu kukhala abwenzi anu powaonetsa chikondi chanu pamene iwo akana choonadi chimene chadza kwa inu ndipo amupirikitsa Mtumwi pamodzi ndi inu nomwe kuchokera ku nyumba zanu, chifukwa chakuti inu mumakhulupirira mwa Mulungu Ambuye wanu. Ngati inu mwadza ndi cholinga chogwira ntchito m’njira yanga ndi kufunafuna chisangalalo changa(musachite nawo ubwenzi). Ndipo ngati inu mumaonetsa chikondi kwa iwo mwamseri, ndithudi, mukatero mwasochera. Ine ndimadziwa zonse zimene mumachita mseri |
إِن يَثْقَفُوكُمْ يَكُونُوا لَكُمْ أَعْدَاءً وَيَبْسُطُوا إِلَيْكُمْ أَيْدِيَهُمْ وَأَلْسِنَتَهُم بِالسُّوءِ وَوَدُّوا لَوْ تَكْفُرُونَ (2) Ngati iwo akupambanani, ndithudi, adzakuonetsani kuti ndi adani anu ndipo adzagwiritsa ntchito manja awo ndi malirime awo pa inu pokuchitirani zoipa. Iwo afunitsitsa kuti nanu mukhale anthu osakhulupirira |
لَن تَنفَعَكُمْ أَرْحَامُكُمْ وَلَا أَوْلَادُكُمْ ۚ يَوْمَ الْقِيَامَةِ يَفْصِلُ بَيْنَكُمْ ۚ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌ (3) Abale anu kapena ana anu sadzakhala a phindu kwa inu patsiku la chiweruzo. Iye adzaweruza pakati panu chifukwa Mulungu amaona zonse zimene mumachita |
قَدْ كَانَتْ لَكُمْ أُسْوَةٌ حَسَنَةٌ فِي إِبْرَاهِيمَ وَالَّذِينَ مَعَهُ إِذْ قَالُوا لِقَوْمِهِمْ إِنَّا بُرَآءُ مِنكُمْ وَمِمَّا تَعْبُدُونَ مِن دُونِ اللَّهِ كَفَرْنَا بِكُمْ وَبَدَا بَيْنَنَا وَبَيْنَكُمُ الْعَدَاوَةُ وَالْبَغْضَاءُ أَبَدًا حَتَّىٰ تُؤْمِنُوا بِاللَّهِ وَحْدَهُ إِلَّا قَوْلَ إِبْرَاهِيمَ لِأَبِيهِ لَأَسْتَغْفِرَنَّ لَكَ وَمَا أَمْلِكُ لَكَ مِنَ اللَّهِ مِن شَيْءٍ ۖ رَّبَّنَا عَلَيْكَ تَوَكَّلْنَا وَإِلَيْكَ أَنَبْنَا وَإِلَيْكَ الْمَصِيرُ (4) Muli chitsanzo chabwino kwa inu mwa Abrahamu ndi mwa iwo amene adali naye pamene iwo ananena kwa anthu awo kuti: “Ife sitili m’gulu lanu ndipo sitipembedza zimene inu mumapembedza pozifanizira ndi Mulungu. Ife takukanani ndipo pabuka pakati pa ife ndi inu udani ndi chidani chosatha kupatula ngati inu mukhulupirira mwa Mulungu ndi mwa Iye yekha.” Kupatula zonena za Abrahamu kwa Abambo ake kuti: “Ine ndidzapempha chikhululukiro chanu chifukwa ine ndilibe mphamvu pa chilichonse cha inu kuchokera kwa Mulungu. Ambuye wathu, mwa Inu ife takhulupirira ndi kwa Inu ndiko timapempha chikhululukiro, ndipo kwa Inu ndiko kumene tonse tidzabwerera pomaliza.” |
رَبَّنَا لَا تَجْعَلْنَا فِتْنَةً لِّلَّذِينَ كَفَرُوا وَاغْفِرْ لَنَا رَبَّنَا ۖ إِنَّكَ أَنتَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (5) “Ambuye wathu, musatisandutse ife kukhala mayesero a anthu osakhulupirira koma tikhululukireni Ambuye wathu. Ndithudi Inu ndinu Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru zonse.” |
لَقَدْ كَانَ لَكُمْ فِيهِمْ أُسْوَةٌ حَسَنَةٌ لِّمَن كَانَ يَرْجُو اللَّهَ وَالْيَوْمَ الْآخِرَ ۚ وَمَن يَتَوَلَّ فَإِنَّ اللَّهَ هُوَ الْغَنِيُّ الْحَمِيدُ (6) Ndithudi, mwa iwo mudali chitsanzo chabwino kwa inu kuti mutsatire, makamaka iwo amene amaika chikhulupiriro chawo mwa Mulungu ndi m’tsiku la chiweruzo. Ndithudi Mulungu ndi wolemera ndipo ndiye yekha amene ayenera kulemekezedwa |
۞ عَسَى اللَّهُ أَن يَجْعَلَ بَيْنَكُمْ وَبَيْنَ الَّذِينَ عَادَيْتُم مِّنْهُم مَّوَدَّةً ۚ وَاللَّهُ قَدِيرٌ ۚ وَاللَّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (7) Mwina Mulungu angakhazikitse chikondi pakati pa inu ndi iwo amene inu mumawaganizira kuti ndi adani anu. Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu pa china chilichonse ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha |
لَّا يَنْهَاكُمُ اللَّهُ عَنِ الَّذِينَ لَمْ يُقَاتِلُوكُمْ فِي الدِّينِ وَلَمْ يُخْرِجُوكُم مِّن دِيَارِكُمْ أَن تَبَرُّوهُمْ وَتُقْسِطُوا إِلَيْهِمْ ۚ إِنَّ اللَّهَ يُحِبُّ الْمُقْسِطِينَ (8) Mulungu sali kukuletsani kuti muonetse chilungamo ndi chisoni kwa iwo amene sadamenyane nanu chifukwa cha chikhulupiliro chanu ndipo sanakuthamangitseni mu nyumba zanu. Ndithudi, Mulungu amakonda iwo amene amachita zolungama |
إِنَّمَا يَنْهَاكُمُ اللَّهُ عَنِ الَّذِينَ قَاتَلُوكُمْ فِي الدِّينِ وَأَخْرَجُوكُم مِّن دِيَارِكُمْ وَظَاهَرُوا عَلَىٰ إِخْرَاجِكُمْ أَن تَوَلَّوْهُمْ ۚ وَمَن يَتَوَلَّهُمْ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الظَّالِمُونَ (9) Mulungu wakuletsani kuchita ubwenzi ndi anthu amene munamenyana nawo chifukwa cha chikhulupiriro ndipo anakuthamangitsani ku nyumba zanu kapena adathandiza anthu ena kuti amenyane ndi kukupirikitsani inu. Ndipo aliyense amene achita ubwenzi ndi anthu otere ndi ochimwa |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِذَا جَاءَكُمُ الْمُؤْمِنَاتُ مُهَاجِرَاتٍ فَامْتَحِنُوهُنَّ ۖ اللَّهُ أَعْلَمُ بِإِيمَانِهِنَّ ۖ فَإِنْ عَلِمْتُمُوهُنَّ مُؤْمِنَاتٍ فَلَا تَرْجِعُوهُنَّ إِلَى الْكُفَّارِ ۖ لَا هُنَّ حِلٌّ لَّهُمْ وَلَا هُمْ يَحِلُّونَ لَهُنَّ ۖ وَآتُوهُم مَّا أَنفَقُوا ۚ وَلَا جُنَاحَ عَلَيْكُمْ أَن تَنكِحُوهُنَّ إِذَا آتَيْتُمُوهُنَّ أُجُورَهُنَّ ۚ وَلَا تُمْسِكُوا بِعِصَمِ الْكَوَافِرِ وَاسْأَلُوا مَا أَنفَقْتُمْ وَلْيَسْأَلُوا مَا أَنفَقُوا ۚ ذَٰلِكُمْ حُكْمُ اللَّهِ ۖ يَحْكُمُ بَيْنَكُمْ ۚ وَاللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٌ (10) Oh inu anthu okhulupirira! Pamene akazi okhulupirira adza kwa inu ngati othawa mavuto, afufuzeni bwinobwino. Mulungu yekha ndiye amene adziwa bwino bwino chikhulupiriro chawo. Ngati inu mukhutitsidwa kuti ndi okhulupirira m’choonadi, musawabwezere kwa anthu osakhulupirira chifukwa iwo saloledwa kukwatiwa ndi anthu osakhulupirira monga momwe amuna osakhulupirira saloledwa kukwatira akazi okhulupirira. Koma abwezereni anthu osakhulupirira ziwongo zimene apereka. Ndipo sikulakwa ngati inu muwakwatira akazi okhulupirirawa ngati mwapereka chiwongo. Musapitilize ukwati wanu ndi akazi wosakhulupirira. Itanitsani zimene mwaononga ngati chiwongo cha ukwati ndipo aloleni osakhulupirira kuti nawonso aitanitse zimene aononga pa akazi okhulupirira amene adza kwa inu. Ili ndi lamulo la Mulungu. Iye amaweruza mwachilungamo pakati panu. Mulungu ndi wa nzeru ndi luntha |
وَإِن فَاتَكُمْ شَيْءٌ مِّنْ أَزْوَاجِكُمْ إِلَى الْكُفَّارِ فَعَاقَبْتُمْ فَآتُوا الَّذِينَ ذَهَبَتْ أَزْوَاجُهُم مِّثْلَ مَا أَنفَقُوا ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ الَّذِي أَنتُم بِهِ مُؤْمِنُونَ (11) Ndipo ngati ena, mwa akazi anu, athawa ndi kukakwatiwa ndi osakhulupirira, ndipo inu mupeza mwayi wolandira akazi wochokera kwa anthu osakhulupirira abwezereni chiwongo ndi china chilichonse chimene iwo adapereka anthu amene akazi awo awathawa. Ndipo opani Mulungu amene inu mumamukhulupirira |
يَا أَيُّهَا النَّبِيُّ إِذَا جَاءَكَ الْمُؤْمِنَاتُ يُبَايِعْنَكَ عَلَىٰ أَن لَّا يُشْرِكْنَ بِاللَّهِ شَيْئًا وَلَا يَسْرِقْنَ وَلَا يَزْنِينَ وَلَا يَقْتُلْنَ أَوْلَادَهُنَّ وَلَا يَأْتِينَ بِبُهْتَانٍ يَفْتَرِينَهُ بَيْنَ أَيْدِيهِنَّ وَأَرْجُلِهِنَّ وَلَا يَعْصِينَكَ فِي مَعْرُوفٍ ۙ فَبَايِعْهُنَّ وَاسْتَغْفِرْ لَهُنَّ اللَّهَ ۖ إِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (12) Oh iwe Mtumwi! Ngati akazi okhulupirira adza kwa iwe kudzalumbira lonjezo lakuti sadzamufanizira Mulungu ndi wina wake akamapembedza, kuti sadzaba, sadzachita chigololo, sadzapha ana awo, sadzalankhula mawu ojeda, sadzapeka nkhani zabodza ndipo kuti adzakumvera iwe pa nkhani ina iliyonse, iwe uyenera kulandira lonjezo lawo ndipo pempha kwa Mulungu kuti awakhululukire machimo awo chifukwa Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَتَوَلَّوْا قَوْمًا غَضِبَ اللَّهُ عَلَيْهِمْ قَدْ يَئِسُوا مِنَ الْآخِرَةِ كَمَا يَئِسَ الْكُفَّارُ مِنْ أَصْحَابِ الْقُبُورِ (13) Oh inu okhulupirira! Musapalane ubwenzi ndi anthu amene adalandira mkwiyo wa Mulungu. Ndithudi iwo ali ndi mantha ndi zimene zidzawachitikira m’moyo umene uli nkudza monga momwe anthu osakhulupirira amachitira mantha ndi iwo amene adaikidwa m’manda |