×

Oh inu anthu okhulupirira! Pamene akazi okhulupirira adza kwa inu ngati othawa 60:10 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah Al-Mumtahanah ⮕ (60:10) ayat 10 in Chichewa

60:10 Surah Al-Mumtahanah ayat 10 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah Al-Mumtahanah ayat 10 - المُمتَحنَة - Page - Juz 28

﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا جَآءَكُمُ ٱلۡمُؤۡمِنَٰتُ مُهَٰجِرَٰتٖ فَٱمۡتَحِنُوهُنَّۖ ٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِإِيمَٰنِهِنَّۖ فَإِنۡ عَلِمۡتُمُوهُنَّ مُؤۡمِنَٰتٖ فَلَا تَرۡجِعُوهُنَّ إِلَى ٱلۡكُفَّارِۖ لَا هُنَّ حِلّٞ لَّهُمۡ وَلَا هُمۡ يَحِلُّونَ لَهُنَّۖ وَءَاتُوهُم مَّآ أَنفَقُواْۚ وَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكُمۡ أَن تَنكِحُوهُنَّ إِذَآ ءَاتَيۡتُمُوهُنَّ أُجُورَهُنَّۚ وَلَا تُمۡسِكُواْ بِعِصَمِ ٱلۡكَوَافِرِ وَسۡـَٔلُواْ مَآ أَنفَقۡتُمۡ وَلۡيَسۡـَٔلُواْ مَآ أَنفَقُواْۚ ذَٰلِكُمۡ حُكۡمُ ٱللَّهِ يَحۡكُمُ بَيۡنَكُمۡۖ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٞ ﴾
[المُمتَحنَة: 10]

Oh inu anthu okhulupirira! Pamene akazi okhulupirira adza kwa inu ngati othawa mavuto, afufuzeni bwinobwino. Mulungu yekha ndiye amene adziwa bwino bwino chikhulupiriro chawo. Ngati inu mukhutitsidwa kuti ndi okhulupirira m’choonadi, musawabwezere kwa anthu osakhulupirira chifukwa iwo saloledwa kukwatiwa ndi anthu osakhulupirira monga momwe amuna osakhulupirira saloledwa kukwatira akazi okhulupirira. Koma abwezereni anthu osakhulupirira ziwongo zimene apereka. Ndipo sikulakwa ngati inu muwakwatira akazi okhulupirirawa ngati mwapereka chiwongo. Musapitilize ukwati wanu ndi akazi wosakhulupirira. Itanitsani zimene mwaononga ngati chiwongo cha ukwati ndipo aloleni osakhulupirira kuti nawonso aitanitse zimene aononga pa akazi okhulupirira amene adza kwa inu. Ili ndi lamulo la Mulungu. Iye amaweruza mwachilungamo pakati panu. Mulungu ndi wa nzeru ndi luntha

❮ Previous Next ❯

ترجمة: ياأيها الذين آمنوا إذا جاءكم المؤمنات مهاجرات فامتحنوهن الله أعلم بإيمانهن فإن, باللغة نيانجا

﴿ياأيها الذين آمنوا إذا جاءكم المؤمنات مهاجرات فامتحنوهن الله أعلم بإيمانهن فإن﴾ [المُمتَحنَة: 10]

Khaled Ibrahim Betala
“E inu amene mwakhulupirira! Akakudzerani okhulupirira aakazi osamuka, ayeseni mayeso (kuti mudziwe chikhulupiliro chawo); Allah ali wodziwa kwambiri za chikhulupiliro chawo; ngati mutawadziwa kuti ndiokhulupirira musawabwezere kwa osakhulupirira. Akaziwo saloledwa kukwatiwa ndi osakhulupirira, iwonso saloledwa kuwakwatira. Abwezereni chiwongo chimene adapereka amuna osakhulupirirawo. Ndipo palibe tchimo kwa inu kuwakwatira, (ngakhale adasiya amuna awo achikafiri (ku Makka) ngati muwapatsa chiwongo chawo. Musakakamire maukwati ndi akazi achikafiri (osakhulupirira amene adatsalira ku Makka). Itanitsani zimene mudapereka kwa akazi anu (achikafiriwo), naonso Akafiri aitanitse zimene adapereka (kwa akazi awo akalowa m’Chisilamu). Limeneli ndi lamulo la Allah limene akulamula pakati panu. Allah ndiwodziwa kwambiri ndiponso Ngwanzeru (poika malamulo)
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek