Quran with Chichewa translation - Surah Al-Mumtahanah ayat 4 - المُمتَحنَة - Page - Juz 28
﴿قَدۡ كَانَتۡ لَكُمۡ أُسۡوَةٌ حَسَنَةٞ فِيٓ إِبۡرَٰهِيمَ وَٱلَّذِينَ مَعَهُۥٓ إِذۡ قَالُواْ لِقَوۡمِهِمۡ إِنَّا بُرَءَٰٓؤُاْ مِنكُمۡ وَمِمَّا تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ كَفَرۡنَا بِكُمۡ وَبَدَا بَيۡنَنَا وَبَيۡنَكُمُ ٱلۡعَدَٰوَةُ وَٱلۡبَغۡضَآءُ أَبَدًا حَتَّىٰ تُؤۡمِنُواْ بِٱللَّهِ وَحۡدَهُۥٓ إِلَّا قَوۡلَ إِبۡرَٰهِيمَ لِأَبِيهِ لَأَسۡتَغۡفِرَنَّ لَكَ وَمَآ أَمۡلِكُ لَكَ مِنَ ٱللَّهِ مِن شَيۡءٖۖ رَّبَّنَا عَلَيۡكَ تَوَكَّلۡنَا وَإِلَيۡكَ أَنَبۡنَا وَإِلَيۡكَ ٱلۡمَصِيرُ ﴾
[المُمتَحنَة: 4]
﴿قد كانت لكم أسوة حسنة في إبراهيم والذين معه إذ قالوا لقومهم﴾ [المُمتَحنَة: 4]
Khaled Ibrahim Betala “Ndithu inu muli ndi chitsanzo chabwino cha (mtumiki) Ibrahim ndi amene adali naye pamene adawauza anzawo (osakhulupirira kuti): “Ndithu ife tapatukana nanu pamodzi ndi milungu yanu imene mukuipembedza kusiya Allah; takukanani, ndipo chidani ndi kusakondana zaonekera poyera pakati pa inu ndi ife mpaka muyaya, kufikira, mutakhulupirira mwa Allah mmodzi (inunso chitani chimodzimodzi, muwakane abale anu amene ali akafiri), kupatula mawu a Ibrahim pamene adamuuza tate wake (kuti): “Ndithu ndikupempherani chikhululuko. Palibe chimene ndingakutetezereni nacho kwa Allah (ngati mutamuphatikiza Allah ndi zina.”) E Mbuye wathu! Kwa Inu tatsamira. Ndipo kwa Inu tatembenukira ndiponso kobwerera nkwa Inu |