سَبَّحَ لِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۖ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (1) Chilichonse chimene chili kumwamba ndi padziko lapansi chimalemekeza Mulungu. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi wanzeru |
هُوَ الَّذِي أَخْرَجَ الَّذِينَ كَفَرُوا مِنْ أَهْلِ الْكِتَابِ مِن دِيَارِهِمْ لِأَوَّلِ الْحَشْرِ ۚ مَا ظَنَنتُمْ أَن يَخْرُجُوا ۖ وَظَنُّوا أَنَّهُم مَّانِعَتُهُمْ حُصُونُهُم مِّنَ اللَّهِ فَأَتَاهُمُ اللَّهُ مِنْ حَيْثُ لَمْ يَحْتَسِبُوا ۖ وَقَذَفَ فِي قُلُوبِهِمُ الرُّعْبَ ۚ يُخْرِبُونَ بُيُوتَهُم بِأَيْدِيهِمْ وَأَيْدِي الْمُؤْمِنِينَ فَاعْتَبِرُوا يَا أُولِي الْأَبْصَارِ (2) Ndiye amene adachotsa anthu osakhulupirira amene adali pakati pa anthu a m’Buku kuchokera ku nyumba zawo pamene adakumana poyamba. Iwe sumaganiza ndi pang’ono pomwe kuti angachoke. Ndipo iwo anali kuganiza kuti Malinga awo adzawateteza kwa Mulungu! Koma chilango cha Mulungu chidadza pa iwo kuchokera kumbali imene iwo sanali kuyembekezera. Ndipo Iye adaika mantha m’mitima mwawo kotero iwo adagwetsa nyumba ndi manja awo ndiponso manja a anthu okhulupirira. Motero chenjerani tsopano inu amene muli ndi maso |
وَلَوْلَا أَن كَتَبَ اللَّهُ عَلَيْهِمُ الْجَلَاءَ لَعَذَّبَهُمْ فِي الدُّنْيَا ۖ وَلَهُمْ فِي الْآخِرَةِ عَذَابُ النَّارِ (3) Ngati Mulungu akadapanda kuwalamulira kuti achotsedwe, ndithudi, Iye akanawalanga m’dziko lomwe lino ndipo m’moyo umene uli nkudza, ndithudi, iwo adzalandira chilango cha ku Gahena |
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ شَاقُّوا اللَّهَ وَرَسُولَهُ ۖ وَمَن يُشَاقِّ اللَّهَ فَإِنَّ اللَّهَ شَدِيدُ الْعِقَابِ (4) Chifukwa iwo adatsutsa Mulungu ndi Mtumwi mwake. Ndipo ngati wina atsutsa Mulungu ndi Mtumwi wake, ndithudi, Mulungu ali ndi chilango choopsa |
مَا قَطَعْتُم مِّن لِّينَةٍ أَوْ تَرَكْتُمُوهَا قَائِمَةً عَلَىٰ أُصُولِهَا فَبِإِذْنِ اللَّهِ وَلِيُخْزِيَ الْفَاسِقِينَ (5) Chilichonse chimene mudula cha mitengo ing’ono ing’ono ya tende kapena muisiya kuti ikhale njo pa mizu yake, mumachita ndi chilolezo cha Mulungu, ndi cholinga choti achititse manyazi anthu ochita zoipa |
وَمَا أَفَاءَ اللَّهُ عَلَىٰ رَسُولِهِ مِنْهُمْ فَمَا أَوْجَفْتُمْ عَلَيْهِ مِنْ خَيْلٍ وَلَا رِكَابٍ وَلَٰكِنَّ اللَّهَ يُسَلِّطُ رُسُلَهُ عَلَىٰ مَن يَشَاءُ ۚ وَاللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (6) Chimene Mulungu wapereka kwa Mtumwi wake ndipo walanda kuchokera kwa iwo, si ndinu amene mudapereka akabvalo kapena ngamira kwa iwo. Koma Mulungu ndiye amene amapereka mphamvu kwa Mtumwi wake kupambana aliyense amene iye wafuna ndipo Mulungu ali ndi mphamvu pa chilichonse |
مَّا أَفَاءَ اللَّهُ عَلَىٰ رَسُولِهِ مِنْ أَهْلِ الْقُرَىٰ فَلِلَّهِ وَلِلرَّسُولِ وَلِذِي الْقُرْبَىٰ وَالْيَتَامَىٰ وَالْمَسَاكِينِ وَابْنِ السَّبِيلِ كَيْ لَا يَكُونَ دُولَةً بَيْنَ الْأَغْنِيَاءِ مِنكُمْ ۚ وَمَا آتَاكُمُ الرَّسُولُ فَخُذُوهُ وَمَا نَهَاكُمْ عَنْهُ فَانتَهُوا ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۖ إِنَّ اللَّهَ شَدِيدُ الْعِقَابِ (7) Chilichonse chimene Mulungu wapereka ngati chuma chopeza pa nkhondo kwa Mtumwi wake, kuchokera kwa anthu a m’mizinda, mwini wakendi Mulungu, Mtumwiwakendiabalendiamasiye, ndi anthu osauka, ndi a paulendo ndi cholinga choti asakhale katundu wa anthu olemera amene ali pakati panu. Kotero landirani zimene Mtumwi akupatsani ndipo mulewe chimene akuletsani. Ndipo opani Mulungu. Ndithudi Mulungu amalanga molapitsa |
لِلْفُقَرَاءِ الْمُهَاجِرِينَ الَّذِينَ أُخْرِجُوا مِن دِيَارِهِمْ وَأَمْوَالِهِمْ يَبْتَغُونَ فَضْلًا مِّنَ اللَّهِ وَرِضْوَانًا وَيَنصُرُونَ اللَّهَ وَرَسُولَهُ ۚ أُولَٰئِكَ هُمُ الصَّادِقُونَ (8) Ndi wa amphawi amene adabwera ndi Mtumwi amene adapilikitsidwa m’nyumba zawo ndi katundu wawo pofunafuna chisomo chochokera kwa Mulungu ndi chisangalalo chake. Ndipo amatsatira Mulungu ndi Mtumwi wake. Amenewa, ndithudi, ndiwo olungama |
وَالَّذِينَ تَبَوَّءُوا الدَّارَ وَالْإِيمَانَ مِن قَبْلِهِمْ يُحِبُّونَ مَنْ هَاجَرَ إِلَيْهِمْ وَلَا يَجِدُونَ فِي صُدُورِهِمْ حَاجَةً مِّمَّا أُوتُوا وَيُؤْثِرُونَ عَلَىٰ أَنفُسِهِمْ وَلَوْ كَانَ بِهِمْ خَصَاصَةٌ ۚ وَمَن يُوقَ شُحَّ نَفْسِهِ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْمُفْلِحُونَ (9) Ndipo iwo ndi amene, awa asadadze, adali ndi nyumba zawo ndipo adalowa Chisilamu, ndipo adaonetsa chikondi kwa iwo amene amadza kwa iwo, ndipo samachita kaduka ndi katundu amene aperekedwa kwa iwo koma amalolera kuti iwo akhale otsiliza polandira ngakhale kuti nawonso amazifuna. Ndipo aliyense amene amadziteteza ku zilakolako zake, ndithudi, iye adzakhala opambana |
وَالَّذِينَ جَاءُوا مِن بَعْدِهِمْ يَقُولُونَ رَبَّنَا اغْفِرْ لَنَا وَلِإِخْوَانِنَا الَّذِينَ سَبَقُونَا بِالْإِيمَانِ وَلَا تَجْعَلْ فِي قُلُوبِنَا غِلًّا لِّلَّذِينَ آمَنُوا رَبَّنَا إِنَّكَ رَءُوفٌ رَّحِيمٌ (10) Ndipo iwo amene adadza pambuyo pawo adati: “Ambuye wathu, tikhululukireni ife pamodzi ndi abale athu amene adalowa Chisilamu poyambirira, ndipo musasiye m’mitima mwathu kaduka wowachitira iwo amene adakhulupirira kale. Ambuye wathu! Ndithudi inu ndinu okoma mtima, Mwini chifundo.” |
۞ أَلَمْ تَرَ إِلَى الَّذِينَ نَافَقُوا يَقُولُونَ لِإِخْوَانِهِمُ الَّذِينَ كَفَرُوا مِنْ أَهْلِ الْكِتَابِ لَئِنْ أُخْرِجْتُمْ لَنَخْرُجَنَّ مَعَكُمْ وَلَا نُطِيعُ فِيكُمْ أَحَدًا أَبَدًا وَإِن قُوتِلْتُمْ لَنَنصُرَنَّكُمْ وَاللَّهُ يَشْهَدُ إِنَّهُمْ لَكَاذِبُونَ (11) Kodi iwe sudawaone anthu a chinyengo ali kunena kwa abale awo osakhulupirira amene ali pakati pa anthu a m’Buku? (Ponena kuti): “Ngati iwo akupirikitsani inu, nafenso tidzapita nanu, ndipo sitidzamvera wina aliyense wodana ndi inu. Ngati inu muputidwa, ndithudi, ife tidzakuthandizani.” Koma Mulungu achitira umboni kuti, ndithudi, iwo ndi abodza |
لَئِنْ أُخْرِجُوا لَا يَخْرُجُونَ مَعَهُمْ وَلَئِن قُوتِلُوا لَا يَنصُرُونَهُمْ وَلَئِن نَّصَرُوهُمْ لَيُوَلُّنَّ الْأَدْبَارَ ثُمَّ لَا يُنصَرُونَ (12) Ndithudi ngati iwo apirikitsidwa, iwo sadzapita nawo ayi ndipo ngati inu muputidwa iwo sadzakuthandizani konsekonse. Ndipo ngati iwo atathandiza, iwo adzangobwerera m’mbuyo motero iwo sadzapambana ai |
لَأَنتُمْ أَشَدُّ رَهْبَةً فِي صُدُورِهِم مِّنَ اللَّهِ ۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ قَوْمٌ لَّا يَفْقَهُونَ (13) Ndithudi inu mumayambitsa mantha m’mitima mwawo kuposa Mulungu. Ichi ndi chifukwa chakuti iwo ndi anthu osazindikira |
لَا يُقَاتِلُونَكُمْ جَمِيعًا إِلَّا فِي قُرًى مُّحَصَّنَةٍ أَوْ مِن وَرَاءِ جُدُرٍ ۚ بَأْسُهُم بَيْنَهُمْ شَدِيدٌ ۚ تَحْسَبُهُمْ جَمِيعًا وَقُلُوبُهُمْ شَتَّىٰ ۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ قَوْمٌ لَّا يَعْقِلُونَ (14) Iwo sadzamenyana nawe ngati gulu limodzi ayi koma mozemba pogwiritsa ntchito Malinga ya m’mizinda kapena pobisala kuzipupa. Mtima womenya nkhondo ulipo pakati pawo moti iwe ukhoza kuganiza kuti ndi ogwirizana. Koma mitima yawo ndi yogawikana chifukwa iwo ndi anthu osadziwa chilichonse |
كَمَثَلِ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ قَرِيبًا ۖ ذَاقُوا وَبَالَ أَمْرِهِمْ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (15) Iwo ali ngati amene adadza pambuyo pawo amene adalandira dipo loipa chifukwa cha ntchito zawo ndipo iwo adzalandira chilango chowawa kwambiri |
كَمَثَلِ الشَّيْطَانِ إِذْ قَالَ لِلْإِنسَانِ اكْفُرْ فَلَمَّا كَفَرَ قَالَ إِنِّي بَرِيءٌ مِّنكَ إِنِّي أَخَافُ اللَّهَ رَبَّ الْعَالَمِينَ (16) Monga Satana pamene amamuuza munthu kuti: “Usakhulupirire mwa Mulungu.” Ndipo pamene munthu sakhulupirira mwa Mulungu, Satana amati: “Ndathana nawe tsopano chifukwa ine ndimaopa Mulungu, Ambuye wazolengedwa zonse.” |
فَكَانَ عَاقِبَتَهُمَا أَنَّهُمَا فِي النَّارِ خَالِدَيْنِ فِيهَا ۚ وَذَٰلِكَ جَزَاءُ الظَّالِمِينَ (17) Motero mapeto awo ndi akuti onsewa adzapsa ku moto kumene adzakhalako mpaka kalekale. Limenelo ndilo dipo la anthu ochita zoipa |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا اتَّقُوا اللَّهَ وَلْتَنظُرْ نَفْسٌ مَّا قَدَّمَتْ لِغَدٍ ۖ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۚ إِنَّ اللَّهَ خَبِيرٌ بِمَا تَعْمَلُونَ (18) oh inu anthu okhulupirira! opani Mulungu. Ndipo kwaniritsani udindo wanu kwa Iye. Ndipo ulekeni mzimu uliwonse uganize zimene udzalandire mawa ndipo opani Mulungu. Ndithudi Mulungu amadziwa chilichonse chimene mumachita |
وَلَا تَكُونُوا كَالَّذِينَ نَسُوا اللَّهَ فَأَنسَاهُمْ أَنفُسَهُمْ ۚ أُولَٰئِكَ هُمُ الْفَاسِقُونَ (19) Ndipo inu musakhale ngati iwo amene adaiwala Mulungu ndipo Iye adawachititsa kuti adziiwale eni ake. Amenewa ndiwo amene amaphwanya malamulo mopitiriza |
لَا يَسْتَوِي أَصْحَابُ النَّارِ وَأَصْحَابُ الْجَنَّةِ ۚ أَصْحَابُ الْجَنَّةِ هُمُ الْفَائِزُونَ (20) Anthu a ku Gahena siofanana ndi anthu a ku Paradiso. Ndi anthu a ku Paradiso amene adzakhala opambana |
لَوْ أَنزَلْنَا هَٰذَا الْقُرْآنَ عَلَىٰ جَبَلٍ لَّرَأَيْتَهُ خَاشِعًا مُّتَصَدِّعًا مِّنْ خَشْيَةِ اللَّهِ ۚ وَتِلْكَ الْأَمْثَالُ نَضْرِبُهَا لِلنَّاسِ لَعَلَّهُمْ يَتَفَكَّرُونَ (21) Ife tikadatumiza Buku la Korani ili pa phiri, ndithudi; iwe ukadaona ilo lili kudzichepetsa ndi kung’ambika chifukwa cha mantha ndi Mulungu. Zimenezi ndi zitsanzo zimene timaulula kwa anthu kuti atha kuganiza |
هُوَ اللَّهُ الَّذِي لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۖ عَالِمُ الْغَيْبِ وَالشَّهَادَةِ ۖ هُوَ الرَّحْمَٰنُ الرَّحِيمُ (22) Iye ndiye Mulungu ndipo kupatula Iye kulibe Mulungu wina amene amadziwa zinthu zonse zachinsinsi ndi zolankhula mokweza. Iye ndi Wachifundo, Mwini chisoni chosatha |
هُوَ اللَّهُ الَّذِي لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ الْمَلِكُ الْقُدُّوسُ السَّلَامُ الْمُؤْمِنُ الْمُهَيْمِنُ الْعَزِيزُ الْجَبَّارُ الْمُتَكَبِّرُ ۚ سُبْحَانَ اللَّهِ عَمَّا يُشْرِكُونَ (23) Iye ndiye Mulungu ndipo kupatula Iye kulibe Mulungu wina. Iye ndi Mwini Ufumu, Woyera, Maziko a mtendere, Mtetezi ndi Mwini ukulu. Ulemerero ukhale kwa Mulungu kuposa zimene amamusinjirira |
هُوَ اللَّهُ الْخَالِقُ الْبَارِئُ الْمُصَوِّرُ ۖ لَهُ الْأَسْمَاءُ الْحُسْنَىٰ ۚ يُسَبِّحُ لَهُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (24) Iye ndi Mulungu, Namalenga, Chiyambi ndi Mkonzi. Ake ndi mayina abwino okhaokha. Chilichonse chimene chili kumwamba ndi padziko lapansi chimamulemekeza ndi kumuyamika ndipo Iye ndi Wolemekezeka, Wamphamvu ndi Wanzeru |