Quran with Chichewa translation - Surah At-Tahrim ayat 8 - التَّحرِيم - Page - Juz 28
﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ تُوبُوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ تَوۡبَةٗ نَّصُوحًا عَسَىٰ رَبُّكُمۡ أَن يُكَفِّرَ عَنكُمۡ سَيِّـَٔاتِكُمۡ وَيُدۡخِلَكُمۡ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ يَوۡمَ لَا يُخۡزِي ٱللَّهُ ٱلنَّبِيَّ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَهُۥۖ نُورُهُمۡ يَسۡعَىٰ بَيۡنَ أَيۡدِيهِمۡ وَبِأَيۡمَٰنِهِمۡ يَقُولُونَ رَبَّنَآ أَتۡمِمۡ لَنَا نُورَنَا وَٱغۡفِرۡ لَنَآۖ إِنَّكَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ ﴾
[التَّحرِيم: 8]
﴿ياأيها الذين آمنوا توبوا إلى الله توبة نصوحا عسى ربكم أن يكفر﴾ [التَّحرِيم: 8]
Khaled Ibrahim Betala “E inu amene mwakhulupirira! Lapani kwa Allah; kulapa koona; ndithu Mbuye wanu akufafanizirani zoipa zanu ndi kukakulowetsani m’minda momwe mitsinje ikuyenda pansi pake, tsiku limene Allah sadzayalutsa mneneli ndi amene adakhulupirira pamodzi naye. Dangalira lawo lidzayenda chapatsogolo pawo ndi mbali yakumanja kwawo, uku akunena: “Mbuye wathu! Tikwanitsireni dangalira lathu (mpaka likatifikitse ku Munda wamtendere), ndiponso tikhululukireni ndithu Inu ndi Wokhoza chilichonse.” |