Quran with Chichewa translation - Surah Hud ayat 7 - هُود - Page - Juz 12
﴿وَهُوَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ فِي سِتَّةِ أَيَّامٖ وَكَانَ عَرۡشُهُۥ عَلَى ٱلۡمَآءِ لِيَبۡلُوَكُمۡ أَيُّكُمۡ أَحۡسَنُ عَمَلٗاۗ وَلَئِن قُلۡتَ إِنَّكُم مَّبۡعُوثُونَ مِنۢ بَعۡدِ ٱلۡمَوۡتِ لَيَقُولَنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا سِحۡرٞ مُّبِينٞ ﴾
[هُود: 7]
﴿وهو الذي خلق السموات والأرض في ستة أيام وكان عرشه على الماء﴾ [هُود: 7]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo Iye ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo Arsh Yake (Mpando Wake wachifumu) idali pa madzi. (Adakulengani) kuti akuyeseni mayeso, ndani mwa inu ali wochita zabwino. Koma ukanena (kwa iwo kuti): “Inu mudzaukitsidwa pambuyo pa imfa,” amene sadakhulupirire akuti: “Izi sikanthu koma ndi matsenga oonekera.” |