Quran with Chichewa translation - Surah Yusuf ayat 19 - يُوسُف - Page - Juz 12
﴿وَجَآءَتۡ سَيَّارَةٞ فَأَرۡسَلُواْ وَارِدَهُمۡ فَأَدۡلَىٰ دَلۡوَهُۥۖ قَالَ يَٰبُشۡرَىٰ هَٰذَا غُلَٰمٞۚ وَأَسَرُّوهُ بِضَٰعَةٗۚ وَٱللَّهُ عَلِيمُۢ بِمَا يَعۡمَلُونَ ﴾
[يُوسُف: 19]
﴿وجاءت سيارة فأرسلوا واردهم فأدلى دلوه قال يابشرى هذا غلام وأسروه بضاعة﴾ [يُوسُف: 19]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo aulendo adadza (pafupi ndi chitsimecho) ndipo adatuma wotunga madzi wawo, choncho iye adaponya ndowa yake (m’chitsime, ndipo akukoka ndowa ija adaona mwana) nati: “Eee, chisangalalo changa! Aka kamwana kakamuna!” Pomwepo iwo (amene adalipo pa chitsimepo) adam’bisa (kwa a paulendo anzawo) monga katundu wamalonda (yemwe adamgula). Koma Allah ankadziwa zimene adali kuchita (ndipo adanka naye ku Iguputo) |