Quran with Chichewa translation - Surah Yusuf ayat 31 - يُوسُف - Page - Juz 12
﴿فَلَمَّا سَمِعَتۡ بِمَكۡرِهِنَّ أَرۡسَلَتۡ إِلَيۡهِنَّ وَأَعۡتَدَتۡ لَهُنَّ مُتَّكَـٔٗا وَءَاتَتۡ كُلَّ وَٰحِدَةٖ مِّنۡهُنَّ سِكِّينٗا وَقَالَتِ ٱخۡرُجۡ عَلَيۡهِنَّۖ فَلَمَّا رَأَيۡنَهُۥٓ أَكۡبَرۡنَهُۥ وَقَطَّعۡنَ أَيۡدِيَهُنَّ وَقُلۡنَ حَٰشَ لِلَّهِ مَا هَٰذَا بَشَرًا إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا مَلَكٞ كَرِيمٞ ﴾
[يُوسُف: 31]
﴿فلما سمعت بمكرهن أرسلت إليهن وأعتدت لهن متكأ وآتت كل واحدة منهن﴾ [يُوسُف: 31]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo (mkazi wa nduna) pamene adamva kunyogodola kwawo, adawaitana (kuti adzaone kukongola kwa Yûsuf kuti adziwe kuti yemwe wathedwa nzeru polakalaka Yûsuf ngosayenera kudzudzulidwa). Ndipo adawakonzera phwando ndikupatsa aliyense wa iwo mpeni; kenaka adamuuza (Yûsuf): “Tuluka ndi kubwera pamaso pa iwo.” Choncho pamene (akazi aja) adamuona, adaona kuti nchinthu chachikulu zedi ndipo adadzicheka manja awo (ndi mipeni ija. Sadazindikire kuti akudzicheka chifukwa cha chidwi ndi kukongola kwa Yûsuf), ndipo adati: “Hasha Lillah! (tikudzitchinjiriza kwa Allah) uyu simunthu, uyu sichina koma ndi mngelo wolemekezeka.” |