Quran with Chichewa translation - Surah Ar-Ra‘d ayat 16 - الرَّعد - Page - Juz 13
﴿قُلۡ مَن رَّبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ قُلِ ٱللَّهُۚ قُلۡ أَفَٱتَّخَذۡتُم مِّن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءَ لَا يَمۡلِكُونَ لِأَنفُسِهِمۡ نَفۡعٗا وَلَا ضَرّٗاۚ قُلۡ هَلۡ يَسۡتَوِي ٱلۡأَعۡمَىٰ وَٱلۡبَصِيرُ أَمۡ هَلۡ تَسۡتَوِي ٱلظُّلُمَٰتُ وَٱلنُّورُۗ أَمۡ جَعَلُواْ لِلَّهِ شُرَكَآءَ خَلَقُواْ كَخَلۡقِهِۦ فَتَشَٰبَهَ ٱلۡخَلۡقُ عَلَيۡهِمۡۚ قُلِ ٱللَّهُ خَٰلِقُ كُلِّ شَيۡءٖ وَهُوَ ٱلۡوَٰحِدُ ٱلۡقَهَّٰرُ ﴾
[الرَّعد: 16]
﴿قل من رب السموات والأرض قل الله قل أفاتخذتم من دونه أولياء﴾ [الرَّعد: 16]
Khaled Ibrahim Betala “Nena: “Ndani Mbuye wa thambo ndi nthaka?” Nena: “Ndi Allah.” Nena: “Mukudzipangira milungu ina kusiya Iye, (milungu) yomwe siingadzibweretsere zabwino kapena kudzichotsera sautso?” Nena: “Kodi angakhale ofanana wakhungu ndi wopenya? Kodi kapena ungafanane mdima ndi kuunika?” Kapena ampangira anzake Allah omwe adalenga zofanana ndi zomwe Allah adalenga kotero kuti zolengedwa (zambali ziwirizo) zikufanana kwa iwo? Nena: “Allah ndiye Mlengi wa chilichonse. Ndipo Iye ndi Mmodzi Wayekha, Wopambana (ndipo chimene Iye wafuna ndi chimene chimachitika)” |