Quran with Chichewa translation - Surah Ar-Ra‘d ayat 17 - الرَّعد - Page - Juz 13
﴿أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَسَالَتۡ أَوۡدِيَةُۢ بِقَدَرِهَا فَٱحۡتَمَلَ ٱلسَّيۡلُ زَبَدٗا رَّابِيٗاۖ وَمِمَّا يُوقِدُونَ عَلَيۡهِ فِي ٱلنَّارِ ٱبۡتِغَآءَ حِلۡيَةٍ أَوۡ مَتَٰعٖ زَبَدٞ مِّثۡلُهُۥۚ كَذَٰلِكَ يَضۡرِبُ ٱللَّهُ ٱلۡحَقَّ وَٱلۡبَٰطِلَۚ فَأَمَّا ٱلزَّبَدُ فَيَذۡهَبُ جُفَآءٗۖ وَأَمَّا مَا يَنفَعُ ٱلنَّاسَ فَيَمۡكُثُ فِي ٱلۡأَرۡضِۚ كَذَٰلِكَ يَضۡرِبُ ٱللَّهُ ٱلۡأَمۡثَالَ ﴾
[الرَّعد: 17]
﴿أنـزل من السماء ماء فسالت أودية بقدرها فاحتمل السيل زبدا رابيا ومما﴾ [الرَّعد: 17]
Khaled Ibrahim Betala “Adatsitsa madzi, kuchokera ku mitambo, ndipo zigwa zidayendetsa madzi mwa mlingo wake. Ndipo msefukiro wamadzi udatenga thovu lomwe limayandama pamwamba pa madzi. Ndiponso zomwe amazisungunula pa moto chifukwa chofuna zodzikongoletseranazo kapena ziwiya (monga zagolide ndi siliva), mumakhalanso thovu chimodzimodzi. Umo ndi momwe Allah akuperekera fanizo lachoonadi ndi fanizo lachonama. Tsono thovu, limangopita monga zitakataka chabe; koma zimene zimathandiza anthu, zimakhazikika m’nthaka. Umo ndi m’mene Allah akuperekera mafanizo |