Quran with Chichewa translation - Surah Maryam ayat 21 - مَريَم - Page - Juz 16
﴿قَالَ كَذَٰلِكِ قَالَ رَبُّكِ هُوَ عَلَيَّ هَيِّنٞۖ وَلِنَجۡعَلَهُۥٓ ءَايَةٗ لِّلنَّاسِ وَرَحۡمَةٗ مِّنَّاۚ وَكَانَ أَمۡرٗا مَّقۡضِيّٗا ﴾
[مَريَم: 21]
﴿قال كذلك قال ربك هو علي هين ولنجعله آية للناس ورحمة منا﴾ [مَريَم: 21]
Khaled Ibrahim Betala “(Mngelo) adati: “Ndimomwemo.” Mbuye Wako akuti: “Zimenezi kwa Ine nzosavuta. Ndipo timchita kukhala chozizwitsa kwa anthu ndi chifundo chochokera kwa Ife. (Nchifukwa chake tachita izi;) ndipo ichi ndi chinthu chimene chidalamulidwa kale. (Chichitika monga momwe Allah adafunira).” |