كهيعص (1) Kaf ha ya ain suad |
ذِكْرُ رَحْمَتِ رَبِّكَ عَبْدَهُ زَكَرِيَّا (2) Ichi ndi chikumbutso cha chifuniro cha Ambuye wako kwa kapolo wake Zakariya |
إِذْ نَادَىٰ رَبَّهُ نِدَاءً خَفِيًّا (3) Pamene Iye adamupempha Ambuye wake motsitsa mawu |
قَالَ رَبِّ إِنِّي وَهَنَ الْعَظْمُ مِنِّي وَاشْتَعَلَ الرَّأْسُ شَيْبًا وَلَمْ أَكُن بِدُعَائِكَ رَبِّ شَقِيًّا (4) Iye adati, “oh Ambuye wanga! Mafupa anga ndi ofoka ndipo mutu wanga uli ndi imvi chifukwa cha ukalamba. Komabe, Ambuye, ine sindidapemphe kwa Inu mopanda phindu.” |
وَإِنِّي خِفْتُ الْمَوَالِيَ مِن وَرَائِي وَكَانَتِ امْرَأَتِي عَاقِرًا فَهَبْ لِي مِن لَّدُنكَ وَلِيًّا (5) “Ndithudi ine ndili ndi mantha ndi abale anga za amene adzalowe m’malo mwanga ndiponso mkazi wanga ndi chumba. Ndipatseni mwana wamwamuna.” |
يَرِثُنِي وَيَرِثُ مِنْ آلِ يَعْقُوبَ ۖ وَاجْعَلْهُ رَبِّ رَضِيًّا (6) “Amene adzalowe m’malo mwanga ndi m’malo mwa ana a Yakobo, ndipo mpangeni, Ambuye wanga, kukhala mmodzi wa wokondedwa wanu.” |
يَا زَكَرِيَّا إِنَّا نُبَشِّرُكَ بِغُلَامٍ اسْمُهُ يَحْيَىٰ لَمْ نَجْعَل لَّهُ مِن قَبْلُ سَمِيًّا (7) “Ee iwe Zakariya! Ife tili kukuuza nkhani yabwino yakuti iwe udzapatsidwa mwana wamwamuna ndipo adzatchedwa Yohane, dzina limene silidapatsidwe kwa aliyense kumbuyoku.” |
قَالَ رَبِّ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي غُلَامٌ وَكَانَتِ امْرَأَتِي عَاقِرًا وَقَدْ بَلَغْتُ مِنَ الْكِبَرِ عِتِيًّا (8) Zakariya adati, “Ambuye! Kodi ine ndingakhale ndi mwana wamwamuna bwanji, pamene mkazi wanga ndi chumba ndipo ine ndine wokalamba?” |
قَالَ كَذَٰلِكَ قَالَ رَبُّكَ هُوَ عَلَيَّ هَيِّنٌ وَقَدْ خَلَقْتُكَ مِن قَبْلُ وَلَمْ تَكُ شَيْئًا (9) Iye adati, “Chimenechi, wanena Ambuye wako! Idzakhala ntchito yopepuka kwa Ine chifukwa Ine ndidakupanga kukhala munthu pamene iwe siunali chinthu china chilichonse chodziwika.” |
قَالَ رَبِّ اجْعَل لِّي آيَةً ۚ قَالَ آيَتُكَ أَلَّا تُكَلِّمَ النَّاسَ ثَلَاثَ لَيَالٍ سَوِيًّا (10) Zakariya adati, “Ambuye, ndipatseni chizindikiro chokhudza zimene zidzachitike.” Iye adati, “Chizindikiro chako ndi chakuti siudzalankhula ndi anthu usiku utatu ngakhale ulibe chilema.” |
فَخَرَجَ عَلَىٰ قَوْمِهِ مِنَ الْمِحْرَابِ فَأَوْحَىٰ إِلَيْهِمْ أَن سَبِّحُوا بُكْرَةً وَعَشِيًّا (11) Pamene Zakariya adadza kwa anthu ake kuchokera m’kachisi, adawauza anthuwo kuti, “Lemekezani Ambuye wanu m’mawa ndi madzulo.” |
يَا يَحْيَىٰ خُذِ الْكِتَابَ بِقُوَّةٍ ۖ وَآتَيْنَاهُ الْحُكْمَ صَبِيًّا (12) “Oh Yohane! Samala mawu a Mulungu kwambiri.” Ife tidamupatsa luntha pamene adali mwana |
وَحَنَانًا مِّن لَّدُنَّا وَزَكَاةً ۖ وَكَانَ تَقِيًّا (13) Ndiponso tidamupatsa mtima wachifundo ndi woyeretsedwa ndipo adali munthu opewa zoipa |
وَبَرًّا بِوَالِدَيْهِ وَلَمْ يَكُن جَبَّارًا عَصِيًّا (14) Ndipo adali kulemekeza abambo ndi amayi ake. Iye sadali wodzikweza kapena wonyoza malamulo a Mulungu |
وَسَلَامٌ عَلَيْهِ يَوْمَ وُلِدَ وَيَوْمَ يَمُوتُ وَيَوْمَ يُبْعَثُ حَيًّا (15) Mtendere udali pa iye pa tsiku limene adabadwa ndi pa tsiku limene adafa ndipo mtendere ukhale pa iye pamene aukitsidwa kwa akufa |
وَاذْكُرْ فِي الْكِتَابِ مَرْيَمَ إِذِ انتَبَذَتْ مِنْ أَهْلِهَا مَكَانًا شَرْقِيًّا (16) Ndipo kukumbukira nkhani ya Maria m’Buku! Pamene iye adasiya anthu ake ndi kupita kumalo a payekha kumbali ya ku m’mawa |
فَاتَّخَذَتْ مِن دُونِهِمْ حِجَابًا فَأَرْسَلْنَا إِلَيْهَا رُوحَنَا فَتَمَثَّلَ لَهَا بَشَرًا سَوِيًّا (17) Ndipo iye adafunda nsalu kuti anthu asaone nkhope yake. Ife tidamutumizira iye Mzimu wathu umene udaoneka ngati munthu |
قَالَتْ إِنِّي أَعُوذُ بِالرَّحْمَٰنِ مِنكَ إِن كُنتَ تَقِيًّا (18) Maria adati, “Mwini chisoni anditeteze ine kwa iwe! Ngati iwe umaopa Ambuye, ndisiye ndekha, usandiyandikire ayi.” |
قَالَ إِنَّمَا أَنَا رَسُولُ رَبِّكِ لِأَهَبَ لَكِ غُلَامًا زَكِيًّا (19) Mngelo adati, “Ine ndine Mthenga wa Ambuye wako ndipo ndadza kudzakupatsa mwana wamwamuna woyera.” |
قَالَتْ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي غُلَامٌ وَلَمْ يَمْسَسْنِي بَشَرٌ وَلَمْ أَكُ بَغِيًّا (20) Maria adati, “Kodi ine ndidzabereka mwana bwanji pamene ine ndine wosakhudzidwa ndi mwamuna ndiponso si ndine wachiwerewere ayi?” |
قَالَ كَذَٰلِكِ قَالَ رَبُّكِ هُوَ عَلَيَّ هَيِّنٌ ۖ وَلِنَجْعَلَهُ آيَةً لِّلنَّاسِ وَرَحْمَةً مِّنَّا ۚ وَكَانَ أَمْرًا مَّقْضِيًّا (21) Mngelo adati, “Ndi momwemo” Ambuye wako wanena kuti, “Zimenezo, kwa Ine, ndi zopepuka. Tidzamupanga iye kukhala chizindikiro kwa anthu ndi madalitso ochoka kwa Ife. Limeneli ndilo lamulo limene lalamulidwa.” |
۞ فَحَمَلَتْهُ فَانتَبَذَتْ بِهِ مَكَانًا قَصِيًّا (22) Ndipo iye adakhala ndi pakati ndipo adapita kumalo akutali |
فَأَجَاءَهَا الْمَخَاضُ إِلَىٰ جِذْعِ النَّخْلَةِ قَالَتْ يَا لَيْتَنِي مِتُّ قَبْلَ هَٰذَا وَكُنتُ نَسْيًا مَّنسِيًّا (23) Ndipo ululu wa kubereka udamubwerera pamene adali patsinde pa mtengo wa tende ndipo adalira nati, “Kalanga ine, bola ndikadangofa zisanachitike izi chifukwa ndikadakhala woiwalidwa.” |
فَنَادَاهَا مِن تَحْتِهَا أَلَّا تَحْزَنِي قَدْ جَعَلَ رَبُّكِ تَحْتَكِ سَرِيًّا (24) Kudabwera mawu kuchokera pansi oti: “Usadandaule ayi. Ambuye wako wakukonzera ka mtsinje kamene kalikuyenda ku mapazi ako.” |
وَهُزِّي إِلَيْكِ بِجِذْعِ النَّخْلَةِ تُسَاقِطْ عَلَيْكِ رُطَبًا جَنِيًّا (25) “Ndipo gwedeza mtengo watendewu, iwo udzagwetsa zipatso za tende zaziwisi ndi zakupsa.” |
فَكُلِي وَاشْرَبِي وَقَرِّي عَيْنًا ۖ فَإِمَّا تَرَيِنَّ مِنَ الْبَشَرِ أَحَدًا فَقُولِي إِنِّي نَذَرْتُ لِلرَّحْمَٰنِ صَوْمًا فَلَنْ أُكَلِّمَ الْيَوْمَ إِنسِيًّا (26) “Idya ndi umwe, kotero sangalala.” Ndipo ukakumana ndi munthu wina aliyense muuze kuti, “Ine ndalumbira kwa Mwini chisoni kusala chakudya ndipo sindidzayankhula ndi munthu wina aliyense lero.” |
فَأَتَتْ بِهِ قَوْمَهَا تَحْمِلُهُ ۖ قَالُوا يَا مَرْيَمُ لَقَدْ جِئْتِ شَيْئًا فَرِيًّا (27) Ndipo iye adatenga mwana wake nanka naye kwa anthu ake amene adati kwa iye’ “Iwe Maria! Ndithudi iwe wabweretsa chinthu cha chilendo.” |
يَا أُخْتَ هَارُونَ مَا كَانَ أَبُوكِ امْرَأَ سَوْءٍ وَمَا كَانَتْ أُمُّكِ بَغِيًّا (28) “Iwe mlongo wake wa Aroni! Atate wako sanali munthu wochita zoipa ndiponso Amayi ako sadali a chiwerewere.” |
فَأَشَارَتْ إِلَيْهِ ۖ قَالُوا كَيْفَ نُكَلِّمُ مَن كَانَ فِي الْمَهْدِ صَبِيًّا (29) Maria adamuloza iye. Koma iwo adati, “Kodi ife tingayankhule ndi mwana wam’chikuta bwanji?” |
قَالَ إِنِّي عَبْدُ اللَّهِ آتَانِيَ الْكِتَابَ وَجَعَلَنِي نَبِيًّا (30) Mwanayo adati, “Ine ndine kapolo wa Mulungu. Iye wandipatsa ine Buku labwino ndipo wandisankha kukhala Mtumwi.” |
وَجَعَلَنِي مُبَارَكًا أَيْنَ مَا كُنتُ وَأَوْصَانِي بِالصَّلَاةِ وَالزَّكَاةِ مَا دُمْتُ حَيًّا (31) “Madalitso ake ali pa ine kulikonse kumene ndingapite ndipo wandilamulira kuti ndikhale wopemphera ndi kupereka chaulere kwa anthu osauka nthawi yonse ya moyo wanga.” |
وَبَرًّا بِوَالِدَتِي وَلَمْ يَجْعَلْنِي جَبَّارًا شَقِيًّا (32) “Iye wandilamula kuti ndizilemekeza amayi anga ndipo sadandipange kukhala wamwano ndi woipa.” |
وَالسَّلَامُ عَلَيَّ يَوْمَ وُلِدتُّ وَيَوْمَ أَمُوتُ وَيَوْمَ أُبْعَثُ حَيًّا (33) Ndipo mtendere ukhale kwa ine patsiku limene ndidabadwa, ndi patsiku limene ndidzafa ndiponso pa tsiku limene ndidzaukitsidwa kwa akufa |
ذَٰلِكَ عِيسَى ابْنُ مَرْيَمَ ۚ قَوْلَ الْحَقِّ الَّذِي فِيهِ يَمْتَرُونَ (34) Ameneyo ndiye Yesu, mwana wa Maria. Liwu loonadi limene iwo ali kukayika |
مَا كَانَ لِلَّهِ أَن يَتَّخِذَ مِن وَلَدٍ ۖ سُبْحَانَهُ ۚ إِذَا قَضَىٰ أَمْرًا فَإِنَّمَا يَقُولُ لَهُ كُن فَيَكُونُ (35) Sizili zoyenera kuti Mulungu akhale ndi mwana wamwamuna! Iye ayeretsedwe ku zimenezo. Ngati Iye afuna chinthu, Iye amangonena kuti, “Chikhale” ndipo chimakhaladi |
وَإِنَّ اللَّهَ رَبِّي وَرَبُّكُمْ فَاعْبُدُوهُ ۚ هَٰذَا صِرَاطٌ مُّسْتَقِيمٌ (36) Ndithudi Mulungu ndi Ambuye wanga ndiponso Ambuye wanu. Kotero mpembedzeni Iye yekha. Imeneyo ndiyo njira |
فَاخْتَلَفَ الْأَحْزَابُ مِن بَيْنِهِمْ ۖ فَوَيْلٌ لِّلَّذِينَ كَفَرُوا مِن مَّشْهَدِ يَوْمٍ عَظِيمٍ (37) Koma magulu a Akhirisitu adasemphana maganizo pakati pawo. Koma pamene tsiku loopsa lidza, tsoka kwa anthu osakhulupirira |
أَسْمِعْ بِهِمْ وَأَبْصِرْ يَوْمَ يَأْتُونَنَا ۖ لَٰكِنِ الظَّالِمُونَ الْيَوْمَ فِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (38) Kodi iwo adzaona ndi kumva momveka bwanji pa tsiku limene adzaonekera pa maso pathu! Koma anthu ochita zoipa lero ali mu chisokonezo choonekeratu |
وَأَنذِرْهُمْ يَوْمَ الْحَسْرَةِ إِذْ قُضِيَ الْأَمْرُ وَهُمْ فِي غَفْلَةٍ وَهُمْ لَا يُؤْمِنُونَ (39) Achenjeze za tsiku limene adzanong’oneza bombono, pamene malamulo athu adzakwaniritsidwa ndipo pamene iwo ali nkuiwala ndi kusakhulupirira |
إِنَّا نَحْنُ نَرِثُ الْأَرْضَ وَمَنْ عَلَيْهَا وَإِلَيْنَا يُرْجَعُونَ (40) Ndithudi Ife tidzatenga dziko lapansi ndi onse amene amakhala m’menemo. Ndi kwa Ife kumene onse adzabwezedwa |
وَاذْكُرْ فِي الْكِتَابِ إِبْرَاهِيمَ ۚ إِنَّهُ كَانَ صِدِّيقًا نَّبِيًّا (41) Ndipo kumbukira nkhani ya Abrahamu imene ili m’Buku. Iye adali Mtumwi ndi munthu wangwiro |
إِذْ قَالَ لِأَبِيهِ يَا أَبَتِ لِمَ تَعْبُدُ مَا لَا يَسْمَعُ وَلَا يُبْصِرُ وَلَا يُغْنِي عَنكَ شَيْئًا (42) Pamene iye adawauza bambo wake kuti, “Oh Abambo! Kodi inu mungalambire bwanji chinthu chimene sichingathe kumva, kuona kapena kukuthandizani pa chilichonse?” |
يَا أَبَتِ إِنِّي قَدْ جَاءَنِي مِنَ الْعِلْمِ مَا لَمْ يَأْتِكَ فَاتَّبِعْنِي أَهْدِكَ صِرَاطًا سَوِيًّا (43) “Ohabambo! Choonadichavumbulutsidwa kwa ine chimene sichinakufikireni inu. Kotero nditsatireni ine kuti ndikutsogolereni ku njira yoyenera.” |
يَا أَبَتِ لَا تَعْبُدِ الشَّيْطَانَ ۖ إِنَّ الشَّيْطَانَ كَانَ لِلرَّحْمَٰنِ عَصِيًّا (44) “oh abambo! Musamapembedze Satana. Ndithudi Satana adanyoza Ambuye wachisoni chosatha.” |
يَا أَبَتِ إِنِّي أَخَافُ أَن يَمَسَّكَ عَذَابٌ مِّنَ الرَّحْمَٰنِ فَتَكُونَ لِلشَّيْطَانِ وَلِيًّا (45) “oh abambo! Ine ndili kuopa kuti chilango cha Mulungu chidzadza pa inu ndipo mudzakhala bwenzi la Satana.” |
قَالَ أَرَاغِبٌ أَنتَ عَنْ آلِهَتِي يَا إِبْرَاهِيمُ ۖ لَئِن لَّمْ تَنتَهِ لَأَرْجُمَنَّكَ ۖ وَاهْجُرْنِي مَلِيًّا (46) Abambo ake adati, “Kodi ukudana ndi milungu yanga iwe Abrahamu? Ukapanda kusiya ndidzakuponya miyala ndipo unditalikire pa kanthawi kochepa.” |
قَالَ سَلَامٌ عَلَيْكَ ۖ سَأَسْتَغْفِرُ لَكَ رَبِّي ۖ إِنَّهُ كَانَ بِي حَفِيًّا (47) Abrahamu adati, “Mtendere ukhale kwa inu. Ine ndidzapempha Ambuye wanga kuti akukhululukireni popeza, Mulungu, kwa ine, ndi wokoma mtima.” |
وَأَعْتَزِلُكُمْ وَمَا تَدْعُونَ مِن دُونِ اللَّهِ وَأَدْعُو رَبِّي عَسَىٰ أَلَّا أَكُونَ بِدُعَاءِ رَبِّي شَقِيًّا (48) “Ine ndikuchokerani ndi zimene mumapembedza kuonjezera pa Mulungu. Ine ndidzapempha kwa Ambuye wanga ndipo ndikhulupirira kuti popembedza Ambuye wanga ndisadzakhale watsoka |
فَلَمَّا اعْتَزَلَهُمْ وَمَا يَعْبُدُونَ مِن دُونِ اللَّهِ وَهَبْنَا لَهُ إِسْحَاقَ وَيَعْقُوبَ ۖ وَكُلًّا جَعَلْنَا نَبِيًّا (49) Ndipo pamene Abrahamu adasiya anthu ake ndi mafano amene iwo anali kupembedza kuonjezera pa Mulungu, tidamupatsa Isake ndi Yakobo. Aliyense wa iwo tidamupanga kukhala Mtumwi |
وَوَهَبْنَا لَهُم مِّن رَّحْمَتِنَا وَجَعَلْنَا لَهُمْ لِسَانَ صِدْقٍ عَلِيًّا (50) Ndipo tidawapatsa onse mituka kuchokera m’chifundo chathu ndipo tidawapanga iwo kukhala otchulidwa mwaulemu |
وَاذْكُرْ فِي الْكِتَابِ مُوسَىٰ ۚ إِنَّهُ كَانَ مُخْلَصًا وَكَانَ رَسُولًا نَّبِيًّا (51) Ndipo kumbukira nkhani ya Mose imene ili m’Buku, amene adali wosankhidwa ndiponso Mtumwi ndi Mneneri |
وَنَادَيْنَاهُ مِن جَانِبِ الطُّورِ الْأَيْمَنِ وَقَرَّبْنَاهُ نَجِيًّا (52) Ife tidamuitana kuchokera kumbali ya dzanja la manja la phiri la Sinai ndipo tinamuyandikitsa kukhala pafupi ndi Ife kuti tiyankhule naye mwamseri |
وَوَهَبْنَا لَهُ مِن رَّحْمَتِنَا أَخَاهُ هَارُونَ نَبِيًّا (53) Tidamupatsa, mwachisoni chathu, m’bale wake Aroni kuti akhale Mtumwi |
وَاذْكُرْ فِي الْكِتَابِ إِسْمَاعِيلَ ۚ إِنَّهُ كَانَ صَادِقَ الْوَعْدِ وَكَانَ رَسُولًا نَّبِيًّا (54) Ndipo kumbukira nkhani ya Ishimayeli imene ili m’Buku. Iye adali wosunga pangano ndipo adali Mtumwi ndi Mneneri |
وَكَانَ يَأْمُرُ أَهْلَهُ بِالصَّلَاةِ وَالزَّكَاةِ وَكَانَ عِندَ رَبِّهِ مَرْضِيًّا (55) Iye anali kulamula anthu ake kuchita mapemphero ndi kupereka chothandiza nacho anthu osauka ndipo adali, kwa Ambuye wake, wokondedwa |
وَاذْكُرْ فِي الْكِتَابِ إِدْرِيسَ ۚ إِنَّهُ كَانَ صِدِّيقًا نَّبِيًّا (56) Ndipo kumbukira za Idrissa. Iye adali munthu wonena zoona ndi Mtumwi |
وَرَفَعْنَاهُ مَكَانًا عَلِيًّا (57) Ife tidamukweza kukhala malo a pamwamba |
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ أَنْعَمَ اللَّهُ عَلَيْهِم مِّنَ النَّبِيِّينَ مِن ذُرِّيَّةِ آدَمَ وَمِمَّنْ حَمَلْنَا مَعَ نُوحٍ وَمِن ذُرِّيَّةِ إِبْرَاهِيمَ وَإِسْرَائِيلَ وَمِمَّنْ هَدَيْنَا وَاجْتَبَيْنَا ۚ إِذَا تُتْلَىٰ عَلَيْهِمْ آيَاتُ الرَّحْمَٰنِ خَرُّوا سُجَّدًا وَبُكِيًّا ۩ (58) Awa ndi anthu amene Mulungu adawaonetsera chisomo chake. Atumwi ochokera ku m’badwo wa Adamu ndi iwo amene tidawatenga pamodzi m’chombo ndi Nowa. Ana a Abrahamu, a Israyeli ndi iwo amene Ife tawatsogolera ndi kuwasankha. Pamene zivumbulutso za Mwini chisoni chosatha zinali kulakatulidwa kwa iwo, iwo adali kugwa nkhope zawo pansi ndi kumalira |
۞ فَخَلَفَ مِن بَعْدِهِمْ خَلْفٌ أَضَاعُوا الصَّلَاةَ وَاتَّبَعُوا الشَّهَوَاتِ ۖ فَسَوْفَ يَلْقَوْنَ غَيًّا (59) Koma mibadwo ya anthu imene inadza iwo atachoka idanyoza mapemphero ndi kutsatira zilakolako zawo. Ndithudi awa adzakumana ndi mavuto |
إِلَّا مَن تَابَ وَآمَنَ وَعَمِلَ صَالِحًا فَأُولَٰئِكَ يَدْخُلُونَ الْجَنَّةَ وَلَا يُظْلَمُونَ شَيْئًا (60) Kupatula amene alapa machimo ndi kukhulupirira choonadi ndi kumachita ntchito zabwino. Iwo adzalowa ku Paradiso ndipo sadzaponderezedwa m’chilichonse |
جَنَّاتِ عَدْنٍ الَّتِي وَعَدَ الرَّحْمَٰنُ عِبَادَهُ بِالْغَيْبِ ۚ إِنَّهُ كَانَ وَعْدُهُ مَأْتِيًّا (61) Iwo adzakhala m’minda ya Edeni mpaka muyaya, imene Mwini chisoni chosatha adalonjeza akapolo ake ngakhale kuti iwo sadaione. Ndithudi lonjezo lake lidzakwaniritsidwa |
لَّا يَسْمَعُونَ فِيهَا لَغْوًا إِلَّا سَلَامًا ۖ وَلَهُمْ رِزْقُهُمْ فِيهَا بُكْرَةً وَعَشِيًّا (62) Kumeneko iwo sadzamva zinthu zopanda pake koma mawu a mtendere okha, ndipo chakudya chidzapatsidwa kwa iwo m’mawa ndi madzulo |
تِلْكَ الْجَنَّةُ الَّتِي نُورِثُ مِنْ عِبَادِنَا مَن كَانَ تَقِيًّا (63) Imeneyo ndiyo Paradiso imene tidzawapatsa akapolo athu omwe anali kuopa Mulungu |
وَمَا نَتَنَزَّلُ إِلَّا بِأَمْرِ رَبِّكَ ۖ لَهُ مَا بَيْنَ أَيْدِينَا وَمَا خَلْفَنَا وَمَا بَيْنَ ذَٰلِكَ ۚ وَمَا كَانَ رَبُّكَ نَسِيًّا (64) Ife sititsika kuchoka kumwamba pokhapokha ngati taloledwa ndi Ambuye wako. Iye ndiye mwini wa zinthu zonse zimene zili pamaso pathu, kumbuyo kwathu ndi zonse zimene zili pakati pa zimenezi. Ndipo Ambuye wako saiwala |
رَّبُّ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَمَا بَيْنَهُمَا فَاعْبُدْهُ وَاصْطَبِرْ لِعِبَادَتِهِ ۚ هَلْ تَعْلَمُ لَهُ سَمِيًّا (65) Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo. Kotero m’pembedze Iye yekha ndipo khala wopirira pamapemphero ake. Kodi ukudziwa wina amene ali ndi dzina ngati la Iye |
وَيَقُولُ الْإِنسَانُ أَإِذَا مَا مِتُّ لَسَوْفَ أُخْرَجُ حَيًّا (66) Munthu amati, “Pamene ine nditafa kodi ndidzaukitsidwa ndi kukhalanso ndi moyo?” |
أَوَلَا يَذْكُرُ الْإِنسَانُ أَنَّا خَلَقْنَاهُ مِن قَبْلُ وَلَمْ يَكُ شَيْئًا (67) Kodi munthu sakumbukira kuti tidamulenga iye pamene poyamba sadali chinthu china chilichonse |
فَوَرَبِّكَ لَنَحْشُرَنَّهُمْ وَالشَّيَاطِينَ ثُمَّ لَنُحْضِرَنَّهُمْ حَوْلَ جَهَنَّمَ جِثِيًّا (68) Motero pali Ambuye wako; ndithudi Tidzawasonkhanitsa pamodzi ndi a Satana ndipo onse tidzawabweretsa m’mphepete mwa Gahena atagwada |
ثُمَّ لَنَنزِعَنَّ مِن كُلِّ شِيعَةٍ أَيُّهُمْ أَشَدُّ عَلَى الرَّحْمَٰنِ عِتِيًّا (69) Ndipo mwachoonadi tidzachotsa mugulu lililonse onse amene adanyoza Mulungu kwambiri |
ثُمَّ لَنَحْنُ أَعْلَمُ بِالَّذِينَ هُمْ أَوْلَىٰ بِهَا صِلِيًّا (70) Ndithudi Ife tilikuwadziwa kwambiri amene ali oyenera kuotchedwa |
وَإِن مِّنكُمْ إِلَّا وَارِدُهَا ۚ كَانَ عَلَىٰ رَبِّكَ حَتْمًا مَّقْضِيًّا (71) Palibe wina wa inu amene sadzapita kumbali ya Moto. Limeneli ndilo lamulo la mphamvu la Ambuye wanu |
ثُمَّ نُنَجِّي الَّذِينَ اتَّقَوا وَّنَذَرُ الظَّالِمِينَ فِيهَا جِثِيًّا (72) Ndipo Ife tidzapulumutsa onse amene amaopa ndi kuwasiya ochita zoipa, atagwada, kuti amve ululu wake |
وَإِذَا تُتْلَىٰ عَلَيْهِمْ آيَاتُنَا بَيِّنَاتٍ قَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا لِلَّذِينَ آمَنُوا أَيُّ الْفَرِيقَيْنِ خَيْرٌ مَّقَامًا وَأَحْسَنُ نَدِيًّا (73) Pamene zivumbulutso zathu zilakatulidwa momveka kwa iwo, anthu osakhulupirira amanena kwa anthu okhulupirira kuti, “Kodi ndi gulu liti pa magulu awiriwa limene lili ndi malo abwino okhala ndi anthu apamwamba?” |
وَكَمْ أَهْلَكْنَا قَبْلَهُم مِّن قَرْنٍ هُمْ أَحْسَنُ أَثَاثًا وَرِئْيًا (74) Kodi ndi mibadwo ingati yakale imene tidaononga iwo asanadze, mibadwo imene idali ndi zinthu zabwino ndiponso zokongola |
قُلْ مَن كَانَ فِي الضَّلَالَةِ فَلْيَمْدُدْ لَهُ الرَّحْمَٰنُ مَدًّا ۚ حَتَّىٰ إِذَا رَأَوْا مَا يُوعَدُونَ إِمَّا الْعَذَابَ وَإِمَّا السَّاعَةَ فَسَيَعْلَمُونَ مَنْ هُوَ شَرٌّ مَّكَانًا وَأَضْعَفُ جُندًا (75) Nena, “Aliyense amene alakwa, Mwini chisoni chosatha adzawaonjezera nthawi, mpaka pamene adzaone zomwe adalonjezedwa. Kaya ndi chilango kapena ola lomaliza, pamenepo ndiye adzadziwa kuti ndani amene ali mwini wa malo oipa ndi gulu lankhondo lofoka.” |
وَيَزِيدُ اللَّهُ الَّذِينَ اهْتَدَوْا هُدًى ۗ وَالْبَاقِيَاتُ الصَّالِحَاتُ خَيْرٌ عِندَ رَبِّكَ ثَوَابًا وَخَيْرٌ مَّرَدًّا (76) Mulungu amapitiriza kutsogolera iwo amene atsatira njira yoyenera. Ntchito zabwino zimene zili ndi malipiro osatha zili ndi mphotho yabwino pamaso pa Ambuye wako ndiponso zotsatira zake ndi zabwino |
أَفَرَأَيْتَ الَّذِي كَفَرَ بِآيَاتِنَا وَقَالَ لَأُوتَيَنَّ مَالًا وَوَلَدًا (77) Kodi mwamuona munthu amene akana zivumbulutso zathu ndipo amanena kuti, “Ine, ndithudi, ndidzapatsidwa chuma ndi ana?” |
أَطَّلَعَ الْغَيْبَ أَمِ اتَّخَذَ عِندَ الرَّحْمَٰنِ عَهْدًا (78) Kodi iye waziona zinthu zosaoneka kapena Mwini chisoni chosatha wamupatsa lonjezo lotere |
كَلَّا ۚ سَنَكْتُبُ مَا يَقُولُ وَنَمُدُّ لَهُ مِنَ الْعَذَابِ مَدًّا (79) Osatheka! Ife tidzalemba zimene akunena ndi kuchipanga chilango chake kukhala chachitali |
وَنَرِثُهُ مَا يَقُولُ وَيَأْتِينَا فَرْدًا (80) Zonse zimene azilankhula iye zidzabwerera kwa Ife ndipo adzadza pamaso pathu yekha |
وَاتَّخَذُوا مِن دُونِ اللَّهِ آلِهَةً لِّيَكُونُوا لَهُمْ عِزًّا (81) Anthu osakhulupirira adadzisankhira milungu ina kuti iwapatse mphamvu ndi ulemerero |
كَلَّا ۚ سَيَكْفُرُونَ بِعِبَادَتِهِمْ وَيَكُونُونَ عَلَيْهِمْ ضِدًّا (82) Ayi. Koma milunguyo idzakana kupembedza kwawo ndipo idzakhala adani awo |
أَلَمْ تَرَ أَنَّا أَرْسَلْنَا الشَّيَاطِينَ عَلَى الْكَافِرِينَ تَؤُزُّهُمْ أَزًّا (83) Kodi siudaone kuti timatumiza kwa anthu osakhulupirira a Satana amene amawaonetsa zinthu zoti achimwe nazo |
فَلَا تَعْجَلْ عَلَيْهِمْ ۖ إِنَّمَا نَعُدُّ لَهُمْ عَدًّا (84) Kotero musafulumize kuwapemphera chionongeko, ndithudi, tikuwawerengera masiku awo |
يَوْمَ نَحْشُرُ الْمُتَّقِينَ إِلَى الرَّحْمَٰنِ وَفْدًا (85) Tsiku limenetidzasonkhanitsaanthuolungamam’magulu kufika pamaso pa Ambuye wachisoni kudzalandira ulemu |
وَنَسُوقُ الْمُجْرِمِينَ إِلَىٰ جَهَنَّمَ وِرْدًا (86) Ndipo tidzawakusa anthu oipa kupita ku moto wa ku Gahena ali ndi ludzu lodetsa nkhawa |
لَّا يَمْلِكُونَ الشَّفَاعَةَ إِلَّا مَنِ اتَّخَذَ عِندَ الرَّحْمَٰنِ عَهْدًا (87) Palibe amene adzakhala ndi mphamvu zodandaula kupatula yekhayo amene walandira chilolezo cha Mwini chisoni chosatha |
وَقَالُوا اتَّخَذَ الرَّحْمَٰنُ وَلَدًا (88) Iwo amati, “Mwini chisoni chosatha wabala mwana wamwamuna.” |
لَّقَدْ جِئْتُمْ شَيْئًا إِدًّا (89) Ndithudi mwanena chinthu choipitsitsa |
تَكَادُ السَّمَاوَاتُ يَتَفَطَّرْنَ مِنْهُ وَتَنشَقُّ الْأَرْضُ وَتَخِرُّ الْجِبَالُ هَدًّا (90) Pafupifupi kumwamba kumafuna kung’ambika chifukwa cha mawu amenewa ndipo nthaka imafuna kugawikana ndi mapiri kugudubuzika ndi kuonongeka |
أَن دَعَوْا لِلرَّحْمَٰنِ وَلَدًا (91) Chifukwa chonena Mwini Chisoni Chosatha ali ndi mwana wamwamuna |
وَمَا يَنبَغِي لِلرَّحْمَٰنِ أَن يَتَّخِذَ وَلَدًا (92) Si zoyenera kwa Mwini chisoni chosatha kuti akhale ndi mwana |
إِن كُلُّ مَن فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ إِلَّا آتِي الرَّحْمَٰنِ عَبْدًا (93) Palibe china chilichonse chimene chili kumwamba kapena pa dziko lapansi chimene chimabwera kwa Mwini chisoni chosatha kupatula ngati kapolo |
لَّقَدْ أَحْصَاهُمْ وَعَدَّهُمْ عَدًّا (94) Iye wasunga chiwerengero cha zolengedwa zake zonse |
وَكُلُّهُمْ آتِيهِ يَوْمَ الْقِيَامَةِ فَرْدًا (95) Ndipo onse, mmodzimmodzi, adzabwerera kwa Iye pa tsiku la kuuka kwa akufa |
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ سَيَجْعَلُ لَهُمُ الرَّحْمَٰنُ وُدًّا (96) Ndithudi amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, Mwini chisoni chosatha adzawakonda |
فَإِنَّمَا يَسَّرْنَاهُ بِلِسَانِكَ لِتُبَشِّرَ بِهِ الْمُتَّقِينَ وَتُنذِرَ بِهِ قَوْمًا لُّدًّا (97) Motero Ife tapanga iyo kukhala yosavuta ya m’chiyankhulo chako kuti upeleke nkhani yabwino kwa anthu oopa ndi kuchenjeza ndi ilo anthu otsutsa |
وَكَمْ أَهْلَكْنَا قَبْلَهُم مِّن قَرْنٍ هَلْ تُحِسُّ مِنْهُم مِّنْ أَحَدٍ أَوْ تَسْمَعُ لَهُمْ رِكْزًا (98) Kodi ndi mibadwo ingati imene Ife tidaononga kale iwo asanadze? Kodi uli kumuona mmodzi aliyense wa iwo kapena kumva manong’onong’o ochokera kwa iwo |