Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 221 - البَقَرَة - Page - Juz 2
﴿وَلَا تَنكِحُواْ ٱلۡمُشۡرِكَٰتِ حَتَّىٰ يُؤۡمِنَّۚ وَلَأَمَةٞ مُّؤۡمِنَةٌ خَيۡرٞ مِّن مُّشۡرِكَةٖ وَلَوۡ أَعۡجَبَتۡكُمۡۗ وَلَا تُنكِحُواْ ٱلۡمُشۡرِكِينَ حَتَّىٰ يُؤۡمِنُواْۚ وَلَعَبۡدٞ مُّؤۡمِنٌ خَيۡرٞ مِّن مُّشۡرِكٖ وَلَوۡ أَعۡجَبَكُمۡۗ أُوْلَٰٓئِكَ يَدۡعُونَ إِلَى ٱلنَّارِۖ وَٱللَّهُ يَدۡعُوٓاْ إِلَى ٱلۡجَنَّةِ وَٱلۡمَغۡفِرَةِ بِإِذۡنِهِۦۖ وَيُبَيِّنُ ءَايَٰتِهِۦ لِلنَّاسِ لَعَلَّهُمۡ يَتَذَكَّرُونَ ﴾
[البَقَرَة: 221]
﴿ولا تنكحوا المشركات حتى يؤمن ولأمة مؤمنة خير من مشركة ولو أعجبتكم﴾ [البَقَرَة: 221]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo musakwatire akazi opembedza mafano mpaka atakhulupirira. Ndithudi, mdzakazi wokhulupirira (Allah) ngwabwino kuposa mfulu ya chikazi yopembedza mafano, ngakhale itakukondweretsani. (Ndipo ana anu aakazi a Chisilamu) musawakwatitse kwa amuna osakhulupirira, mpaka akhulupirire. Ndipo kapolo wokhulupirira (Allah) ngwabwino kuposa mfulu yopembedza mafano, ngakhale ikukukondweretsani. Iwowo akuitanira ku Moto. Koma Allah akuitanira ku Munda wamtendere ndi ku chikhululuko mwa lamulo lake. Ndipo Iye akulongosola mwatsatanetsatane ndime za mawu ake kwa anthu, kuti athe kukumbukira |