×

Siudzakhala mlandu kwa inu ngati muonetsa chidwi choti mudzawafunsira chikwati amayi ofedwa 2:235 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah Al-Baqarah ⮕ (2:235) ayat 235 in Chichewa

2:235 Surah Al-Baqarah ayat 235 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 235 - البَقَرَة - Page - Juz 2

﴿وَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكُمۡ فِيمَا عَرَّضۡتُم بِهِۦ مِنۡ خِطۡبَةِ ٱلنِّسَآءِ أَوۡ أَكۡنَنتُمۡ فِيٓ أَنفُسِكُمۡۚ عَلِمَ ٱللَّهُ أَنَّكُمۡ سَتَذۡكُرُونَهُنَّ وَلَٰكِن لَّا تُوَاعِدُوهُنَّ سِرًّا إِلَّآ أَن تَقُولُواْ قَوۡلٗا مَّعۡرُوفٗاۚ وَلَا تَعۡزِمُواْ عُقۡدَةَ ٱلنِّكَاحِ حَتَّىٰ يَبۡلُغَ ٱلۡكِتَٰبُ أَجَلَهُۥۚ وَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ مَا فِيٓ أَنفُسِكُمۡ فَٱحۡذَرُوهُۚ وَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ غَفُورٌ حَلِيمٞ ﴾
[البَقَرَة: 235]

Siudzakhala mlandu kwa inu ngati muonetsa chidwi choti mudzawafunsira chikwati amayi ofedwa kapena kuwaganizira m’mitima mwanu. Mulungu amadziwa kuti inu mudzawakumbukira iwo. Koma inu musapereke lonjezo la ukwati mwa mseri, koma lankhulani nawo mwaulemu. Ndipo inu musawakwatire nthawi yawo yodikira isanathe. Ndipo dziwani kuti Mulungu amadziwa zimene zili m’mitima mwanu, kotero muopeni Iye ndipo dziwani kuti Mulungu ndi wokhululukira ndi wopilira

❮ Previous Next ❯

ترجمة: ولا جناح عليكم فيما عرضتم به من خطبة النساء أو أكننتم في, باللغة نيانجا

﴿ولا جناح عليكم فيما عرضتم به من خطبة النساء أو أكننتم في﴾ [البَقَرَة: 235]

Khaled Ibrahim Betala
“Ndipo sitchimo kwa inu kupereka mawu okuluwika ofunsira ukwati kwa akaziwo (pamene chiyembekezero cha edda yawo chisanathe. Ndiponso palibe uchimo) kapena kubisa mu mtima mwanu, kuwakwatira (chiyembekezo chawo chikadzatha). Allah wadziwa kuti mukhala mukuwakumbukira akaziwo. Koma musawalonjeze mobisa (kuti: “Ikatha edda ndidzakukwatira).” Koma nenani mawu abwino. Ndipo musatsimikize kumanga ukwati mpaka nyengo yolembedwayo ikwanire. Ndipo dziwani kuti Allah akudziwa zomwe zili m’mitima mwanu. Tero muopeni (Allah), dziwaninso kuti Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek