Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 259 - البَقَرَة - Page - Juz 3
﴿أَوۡ كَٱلَّذِي مَرَّ عَلَىٰ قَرۡيَةٖ وَهِيَ خَاوِيَةٌ عَلَىٰ عُرُوشِهَا قَالَ أَنَّىٰ يُحۡيِۦ هَٰذِهِ ٱللَّهُ بَعۡدَ مَوۡتِهَاۖ فَأَمَاتَهُ ٱللَّهُ مِاْئَةَ عَامٖ ثُمَّ بَعَثَهُۥۖ قَالَ كَمۡ لَبِثۡتَۖ قَالَ لَبِثۡتُ يَوۡمًا أَوۡ بَعۡضَ يَوۡمٖۖ قَالَ بَل لَّبِثۡتَ مِاْئَةَ عَامٖ فَٱنظُرۡ إِلَىٰ طَعَامِكَ وَشَرَابِكَ لَمۡ يَتَسَنَّهۡۖ وَٱنظُرۡ إِلَىٰ حِمَارِكَ وَلِنَجۡعَلَكَ ءَايَةٗ لِّلنَّاسِۖ وَٱنظُرۡ إِلَى ٱلۡعِظَامِ كَيۡفَ نُنشِزُهَا ثُمَّ نَكۡسُوهَا لَحۡمٗاۚ فَلَمَّا تَبَيَّنَ لَهُۥ قَالَ أَعۡلَمُ أَنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ ﴾
[البَقَرَة: 259]
﴿أو كالذي مر على قرية وهي خاوية على عروشها قال أنى يحيي﴾ [البَقَرَة: 259]
Khaled Ibrahim Betala “Kapena ngati fanizo la uja amene adadutsa pafupi ndi mudzi umene madenga ndi zipupa zake zidaphwasuka (udaferatu) adati: “Kodi Allah adzaukitsa chotani mudzi uwu pambuyo pakufa kwake?” Ndipo Allah adampatsa imfa kwa nthawi yokwana zaka zana limodzi , kenako adamuukitsa namufunsa: “Kodi wakhala nyengo yaitali bwanji?” Adati: “Ndakhala nthawi yatsiku limodzi, kapena theka latsiku.” (Allah) adati: “Korna wakhala zaka zana limodzi, ndipo ona chakudya chako ndi zakumwa zako, sizinaonongeke (sizinavunde). Ndipo yang’ana bulu wako (ali mafupa okhaokha oyoyoka); ndi kuti ukhale chisonyezo kwa anthu, (nchifukwa chake takuukitsa ku imfa). Ndipo yang’ana mafupa (a bulu wako) momwe tingawaukitsire, kenako nkumaaveka minofu.” Choncho pamene zidazindikirika (kwa iye, woukitsidwayo), adati: “Ndikudziwa kuti Allah Ngokhoza chilichonse.” |