Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 260 - البَقَرَة - Page - Juz 3
﴿وَإِذۡ قَالَ إِبۡرَٰهِـۧمُ رَبِّ أَرِنِي كَيۡفَ تُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰۖ قَالَ أَوَلَمۡ تُؤۡمِنۖ قَالَ بَلَىٰ وَلَٰكِن لِّيَطۡمَئِنَّ قَلۡبِيۖ قَالَ فَخُذۡ أَرۡبَعَةٗ مِّنَ ٱلطَّيۡرِ فَصُرۡهُنَّ إِلَيۡكَ ثُمَّ ٱجۡعَلۡ عَلَىٰ كُلِّ جَبَلٖ مِّنۡهُنَّ جُزۡءٗا ثُمَّ ٱدۡعُهُنَّ يَأۡتِينَكَ سَعۡيٗاۚ وَٱعۡلَمۡ أَنَّ ٱللَّهَ عَزِيزٌ حَكِيمٞ ﴾
[البَقَرَة: 260]
﴿وإذ قال إبراهيم رب أرني كيف تحي الموتى قال أو لم تؤمن﴾ [البَقَرَة: 260]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo (kumbukira) pamene Ibrahim adati: “E Mbuye wanga!, Ndionetseni mmene mudzaaukitsire akufa.” (Allah) adati: “Kodi sunakhulupirirebe?” Adati: “Iyayi, (ndikukhulupirira), koma (ndikufuna kuona zimenezo) kuti mtima wanga ukhazikike.” (Allah) adati: “Choncho katenge mbalame zinayi; uzisonkhanitse kwa iwe (mpaka uyizindikire mbalame iliyonse mmene ilili, ndipo kenako uziduledule zonsezo zidutswazidutswa ndikuzisakaniza ndi kuzigawa mzigawo zinayi). Ndipo paphiri lililonse ukaikepo gawo limodzi la zimenezo, ndipo kenako uziitane. Zikudzera zikuthamanga. Ndipo dziwa kuti Allah ndi Mwini mphamvu zoposa, Ngwanzem zakuya.” |