Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 282 - البَقَرَة - Page - Juz 3
﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا تَدَايَنتُم بِدَيۡنٍ إِلَىٰٓ أَجَلٖ مُّسَمّٗى فَٱكۡتُبُوهُۚ وَلۡيَكۡتُب بَّيۡنَكُمۡ كَاتِبُۢ بِٱلۡعَدۡلِۚ وَلَا يَأۡبَ كَاتِبٌ أَن يَكۡتُبَ كَمَا عَلَّمَهُ ٱللَّهُۚ فَلۡيَكۡتُبۡ وَلۡيُمۡلِلِ ٱلَّذِي عَلَيۡهِ ٱلۡحَقُّ وَلۡيَتَّقِ ٱللَّهَ رَبَّهُۥ وَلَا يَبۡخَسۡ مِنۡهُ شَيۡـٔٗاۚ فَإِن كَانَ ٱلَّذِي عَلَيۡهِ ٱلۡحَقُّ سَفِيهًا أَوۡ ضَعِيفًا أَوۡ لَا يَسۡتَطِيعُ أَن يُمِلَّ هُوَ فَلۡيُمۡلِلۡ وَلِيُّهُۥ بِٱلۡعَدۡلِۚ وَٱسۡتَشۡهِدُواْ شَهِيدَيۡنِ مِن رِّجَالِكُمۡۖ فَإِن لَّمۡ يَكُونَا رَجُلَيۡنِ فَرَجُلٞ وَٱمۡرَأَتَانِ مِمَّن تَرۡضَوۡنَ مِنَ ٱلشُّهَدَآءِ أَن تَضِلَّ إِحۡدَىٰهُمَا فَتُذَكِّرَ إِحۡدَىٰهُمَا ٱلۡأُخۡرَىٰۚ وَلَا يَأۡبَ ٱلشُّهَدَآءُ إِذَا مَا دُعُواْۚ وَلَا تَسۡـَٔمُوٓاْ أَن تَكۡتُبُوهُ صَغِيرًا أَوۡ كَبِيرًا إِلَىٰٓ أَجَلِهِۦۚ ذَٰلِكُمۡ أَقۡسَطُ عِندَ ٱللَّهِ وَأَقۡوَمُ لِلشَّهَٰدَةِ وَأَدۡنَىٰٓ أَلَّا تَرۡتَابُوٓاْ إِلَّآ أَن تَكُونَ تِجَٰرَةً حَاضِرَةٗ تُدِيرُونَهَا بَيۡنَكُمۡ فَلَيۡسَ عَلَيۡكُمۡ جُنَاحٌ أَلَّا تَكۡتُبُوهَاۗ وَأَشۡهِدُوٓاْ إِذَا تَبَايَعۡتُمۡۚ وَلَا يُضَآرَّ كَاتِبٞ وَلَا شَهِيدٞۚ وَإِن تَفۡعَلُواْ فَإِنَّهُۥ فُسُوقُۢ بِكُمۡۗ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَۖ وَيُعَلِّمُكُمُ ٱللَّهُۗ وَٱللَّهُ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٞ ﴾
[البَقَرَة: 282]
﴿ياأيها الذين آمنوا إذا تداينتم بدين إلى أجل مسمى فاكتبوه وليكتب بينكم﴾ [البَقَرَة: 282]
Khaled Ibrahim Betala “E inu amene mwakhulupirira! Mukamakongozana ngongole kwa nyengo yodziwika ilembeni. Ndipo mlembi pakati panu alembe mwachilungamo; ndipo mlembi asakane kulemba monga momwe Allah wamphunzitsira; choncho alembe. Ndipo alakatule (mawu olembedwawo ndi wokongolayo) yemwe ngongole ili pa iye. Nayenso aope Allah, Mbuye wake, ndipo asapungule chilichonse m’menemo (m’ngongole). Ndipo ngati wokongola ndiozelezeka kapena wofooka, kapena iye mwini sangathe kulembetsa (momveka), choncho amulembetsere myang’aniri (wakili) wake (yemwe akuyang’anira zinthu zake) mwachilungamo. Ndipo funiraponi mboni ziwiri zochokera mwa anthu anu aamuna (asilamu). Koma ngati amuna awiri palibe, choncho apezeke mwamuna mmodzi ndi akazi awiri (kuti aikire umboniwo), amene mumavomereza kukhala mboni kuti ngati mmodzi mwa iwo (akazi awiriwo) angaiwale mmodzi wawo akumbutse winayo. Ndipo mboni zisakane zikaitanidwa. Ndiponso musanyozere kulemba (ngongoleyo) yaing’ono kapena yaikulu mpaka nyengo yake. Zimenezo (kulembako) ndibwino kwa Allah, ndipo ncholungama zedi kumbali yaumboni, ndiponso nchothandiza kuti musakhale ndi chipeneko. Koma akakhala malonda omwe ali pompo omwe mukupatsana pakati panu (tsintho) sikulakwa kwa inu kusawalemba. Koma funani mboni pamene mukugulitsana. Komatu asavutitsidwe mlembi ndiponso mboni. Ngati mutachita zimenezo (zoletsedwazo) kumeneko ndiko kutuluka (m’chilamulo cha Mulungu wanu), ndipo opani Allah, Allah akukuphunzitsani. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse |