Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 283 - البَقَرَة - Page - Juz 3
﴿۞ وَإِن كُنتُمۡ عَلَىٰ سَفَرٖ وَلَمۡ تَجِدُواْ كَاتِبٗا فَرِهَٰنٞ مَّقۡبُوضَةٞۖ فَإِنۡ أَمِنَ بَعۡضُكُم بَعۡضٗا فَلۡيُؤَدِّ ٱلَّذِي ٱؤۡتُمِنَ أَمَٰنَتَهُۥ وَلۡيَتَّقِ ٱللَّهَ رَبَّهُۥۗ وَلَا تَكۡتُمُواْ ٱلشَّهَٰدَةَۚ وَمَن يَكۡتُمۡهَا فَإِنَّهُۥٓ ءَاثِمٞ قَلۡبُهُۥۗ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ عَلِيمٞ ﴾
[البَقَرَة: 283]
﴿وإن كنتم على سفر ولم تجدوا كاتبا فرهان مقبوضة فإن أمن بعضكم﴾ [البَقَرَة: 283]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo ngati muli pa ulendo, ndipo simudapeze mlembi, choncho (wokongoza) apatsidwe chikole (pinyolo) m’manja mwake. Ngati wina wasungitsa mmodzi wa inu chinthu (pomudalira wokhulupirika) choncho amene wayesedwa wokhulupirikayo abweze chinthucho kwa mwini wake, ndipo aope Allah, Mbuye wake. Ndipo musabise umboni (ngakhale uli wokuipirani). Ndipo amene abise ndiye kuti mu mtima mwake mwalowa uchimo; ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita |