Quran with Chichewa translation - Surah Al-hajj ayat 78 - الحج - Page - Juz 17
﴿وَجَٰهِدُواْ فِي ٱللَّهِ حَقَّ جِهَادِهِۦۚ هُوَ ٱجۡتَبَىٰكُمۡ وَمَا جَعَلَ عَلَيۡكُمۡ فِي ٱلدِّينِ مِنۡ حَرَجٖۚ مِّلَّةَ أَبِيكُمۡ إِبۡرَٰهِيمَۚ هُوَ سَمَّىٰكُمُ ٱلۡمُسۡلِمِينَ مِن قَبۡلُ وَفِي هَٰذَا لِيَكُونَ ٱلرَّسُولُ شَهِيدًا عَلَيۡكُمۡ وَتَكُونُواْ شُهَدَآءَ عَلَى ٱلنَّاسِۚ فَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُواْ ٱلزَّكَوٰةَ وَٱعۡتَصِمُواْ بِٱللَّهِ هُوَ مَوۡلَىٰكُمۡۖ فَنِعۡمَ ٱلۡمَوۡلَىٰ وَنِعۡمَ ٱلنَّصِيرُ ﴾
[الحج: 78]
﴿وجاهدوا في الله حق جهاده هو اجتباكم وما جعل عليكم في الدين﴾ [الحج: 78]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo menyerani chipembedzo cha Allah, kumenyera kwa choonadi; Iye ndi Amene adakusankhani (kuti mukhale mpingo wabwino;) ndipo sadaike pa inu zinthu zolemera pa chipembedzo, ndi chipembedzo cha tate wanu Ibrahim. Iye (Allah) adakutchani Asilamu kuyambira kale (m’mabuku akale) ndi mu iyi, (Qur’an) kuti Mtumiki akhale mboni pa inu, inunso kuti mukhale mboni pa anthu. Choncho pempherani Swala moyenera, perekani Zakaat ndipo gwirizanani chifukwa cha Allah. Iye ndiye Mbuye wanu, Mbuye wabwino zedi, ndi Mthandizi wabwino zedi |