Quran with Chichewa translation - Surah An-Nur ayat 33 - النور - Page - Juz 18
﴿وَلۡيَسۡتَعۡفِفِ ٱلَّذِينَ لَا يَجِدُونَ نِكَاحًا حَتَّىٰ يُغۡنِيَهُمُ ٱللَّهُ مِن فَضۡلِهِۦۗ وَٱلَّذِينَ يَبۡتَغُونَ ٱلۡكِتَٰبَ مِمَّا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُكُمۡ فَكَاتِبُوهُمۡ إِنۡ عَلِمۡتُمۡ فِيهِمۡ خَيۡرٗاۖ وَءَاتُوهُم مِّن مَّالِ ٱللَّهِ ٱلَّذِيٓ ءَاتَىٰكُمۡۚ وَلَا تُكۡرِهُواْ فَتَيَٰتِكُمۡ عَلَى ٱلۡبِغَآءِ إِنۡ أَرَدۡنَ تَحَصُّنٗا لِّتَبۡتَغُواْ عَرَضَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَمَن يُكۡرِههُّنَّ فَإِنَّ ٱللَّهَ مِنۢ بَعۡدِ إِكۡرَٰهِهِنَّ غَفُورٞ رَّحِيمٞ ﴾
[النور: 33]
﴿وليستعفف الذين لا يجدون نكاحا حتى يغنيهم الله من فضله والذين يبتغون﴾ [النور: 33]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo amene sapeza chokwatilira apewe (uve wa chiwerewere) kufikira Allah atawalemeletsa ndi zabwino Zake. Ndipo amene afuna kuti awalembere (kuti apate ufulu) mwa amene manja anu akumanja apeza, alembereni (kuti adziombole) ngati mwaona zabwino mwa iwo. Ndipo apatseni gawo la chuma cha Allah chomwe akupatsani. Musawakakamize adzakadzi anu kuchita uhule ngati akufuna kudzisunga, ncholinga choti mupeze zinthu za moyo wa dziko lapansi. Ndipo amene angawakakamize, ndithu Allah, pambuyo pokakamizidwa kwawoko, Ngokhululuka; Ngwachisoni (kwa okakamizidwawo) |