×

Mulungu ndi Muuni wa kumwamba ndi dziko lapansi. Kuunika kwake kukhoza kufaniziridwa 24:35 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah An-Nur ⮕ (24:35) ayat 35 in Chichewa

24:35 Surah An-Nur ayat 35 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah An-Nur ayat 35 - النور - Page - Juz 18

﴿۞ ٱللَّهُ نُورُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ مَثَلُ نُورِهِۦ كَمِشۡكَوٰةٖ فِيهَا مِصۡبَاحٌۖ ٱلۡمِصۡبَاحُ فِي زُجَاجَةٍۖ ٱلزُّجَاجَةُ كَأَنَّهَا كَوۡكَبٞ دُرِّيّٞ يُوقَدُ مِن شَجَرَةٖ مُّبَٰرَكَةٖ زَيۡتُونَةٖ لَّا شَرۡقِيَّةٖ وَلَا غَرۡبِيَّةٖ يَكَادُ زَيۡتُهَا يُضِيٓءُ وَلَوۡ لَمۡ تَمۡسَسۡهُ نَارٞۚ نُّورٌ عَلَىٰ نُورٖۚ يَهۡدِي ٱللَّهُ لِنُورِهِۦ مَن يَشَآءُۚ وَيَضۡرِبُ ٱللَّهُ ٱلۡأَمۡثَٰلَ لِلنَّاسِۗ وَٱللَّهُ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٞ ﴾
[النور: 35]

Mulungu ndi Muuni wa kumwamba ndi dziko lapansi. Kuunika kwake kukhoza kufaniziridwa ndi malo olowa m’chipupa amene m’kati mwake muli nyali imene ili m’galasi looneka ngati nyenyezi yowala. Iyo imayatsidwa kuchokera ku mtengo wodalitsika wa Azitona umene siuli kum’mawa kapena kumadzulo. Mafuta ake amatha kuwala ngakhale kuti palibe moto owayakitsa mafutawo. Muuni pa Muuni unzake ndipo Mulungu amatsogolera, ndi kuwala kwake, aliyense amene Iye wamufuna. Mulungu amapereka zitsanzo kwa anthu. Ndipo Mulungu amadziwa chilichonse

❮ Previous Next ❯

ترجمة: الله نور السموات والأرض مثل نوره كمشكاة فيها مصباح المصباح في زجاجة, باللغة نيانجا

﴿الله نور السموات والأرض مثل نوره كمشكاة فيها مصباح المصباح في زجاجة﴾ [النور: 35]

Khaled Ibrahim Betala
“Allah ndiye Kuunika kwa kuthambo ndi nthaka. Fanizo la kuunika Kwake (powaongolera akapolo Ake) lili ngati “Mishikati” (chibowo cha pa khoma choikapo nyali) yomwe mkati mwake mwaikidwa nyali. Nyali ili m’galasi. Ndipo galasilo lili ngati nyenyezi yowala. Nyali imeneyo imayatsidwa ndi mafuta ochokera ku mtengo wodalitsidwa wa mzitona, womwe suli mbali yakuvuma ngakhale kuzambwe; (umamenyedwa kwambiri ndi dzuwa pamene likutuluka, ndi parnene likulowa). Mafuta ake ngoyandikira kuwala okha (chifukwa champhamvu yake) ngakhale moto usanawakhudze. Kuunika pamwamba pa kuunika! Allah amamuongolera ku kuunika Kwake amene wamfuna. Allah amaponya mafanizo kwa anthu (kuti aganizire ndi kupeza phunziro), ndipo Allah Ngodziwa chilichonse
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek