Quran with Chichewa translation - Surah An-Nur ayat 55 - النور - Page - Juz 18
﴿وَعَدَ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مِنكُمۡ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَيَسۡتَخۡلِفَنَّهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ كَمَا ٱسۡتَخۡلَفَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ وَلَيُمَكِّنَنَّ لَهُمۡ دِينَهُمُ ٱلَّذِي ٱرۡتَضَىٰ لَهُمۡ وَلَيُبَدِّلَنَّهُم مِّنۢ بَعۡدِ خَوۡفِهِمۡ أَمۡنٗاۚ يَعۡبُدُونَنِي لَا يُشۡرِكُونَ بِي شَيۡـٔٗاۚ وَمَن كَفَرَ بَعۡدَ ذَٰلِكَ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡفَٰسِقُونَ ﴾
[النور: 55]
﴿وعد الله الذين آمنوا منكم وعملوا الصالحات ليستخلفنهم في الأرض كما استخلف﴾ [النور: 55]
Khaled Ibrahim Betala “Allah walonjeza mwa inu amene akhulupirira ndikuchita ntchito yabwino kuti ndithu awathandiza kukhala oyang’anira pa dziko monga momwe adawachitira amene adalipo kale kukhala oyang’anira; ndipo ndithu awalimbikitsira chipembedzo chawo chimene wawayanja nacho; ndipo awachotsera mantha awo kukhala opanda mantha.” Akhale akundilambira Ine, osandiphatikiza ndi chilichonse. Ndipo amene asiye kukhulupirira pambuyo pa zimenezi, iwo ngakuswa malamulo |