×

Si cholakwa ngati munthu wakhungu kapena wolumala kapena wodwala kapena inu eni 24:61 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah An-Nur ⮕ (24:61) ayat 61 in Chichewa

24:61 Surah An-Nur ayat 61 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah An-Nur ayat 61 - النور - Page - Juz 18

﴿لَّيۡسَ عَلَى ٱلۡأَعۡمَىٰ حَرَجٞ وَلَا عَلَى ٱلۡأَعۡرَجِ حَرَجٞ وَلَا عَلَى ٱلۡمَرِيضِ حَرَجٞ وَلَا عَلَىٰٓ أَنفُسِكُمۡ أَن تَأۡكُلُواْ مِنۢ بُيُوتِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ ءَابَآئِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ أُمَّهَٰتِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ إِخۡوَٰنِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ أَخَوَٰتِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ أَعۡمَٰمِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ عَمَّٰتِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ أَخۡوَٰلِكُمۡ أَوۡ بُيُوتِ خَٰلَٰتِكُمۡ أَوۡ مَا مَلَكۡتُم مَّفَاتِحَهُۥٓ أَوۡ صَدِيقِكُمۡۚ لَيۡسَ عَلَيۡكُمۡ جُنَاحٌ أَن تَأۡكُلُواْ جَمِيعًا أَوۡ أَشۡتَاتٗاۚ فَإِذَا دَخَلۡتُم بُيُوتٗا فَسَلِّمُواْ عَلَىٰٓ أَنفُسِكُمۡ تَحِيَّةٗ مِّنۡ عِندِ ٱللَّهِ مُبَٰرَكَةٗ طَيِّبَةٗۚ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ ٱللَّهُ لَكُمُ ٱلۡأٓيَٰتِ لَعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ ﴾
[النور: 61]

Si cholakwa ngati munthu wakhungu kapena wolumala kapena wodwala kapena inu eni ake mudya m’nyumba zanu kapena m’nyumba za atate anu kapena m’nyumba za amayi anu kapena m’nyumba za achimwene anu kapena m’nyumba za alongo anu kapena m’nyumba za achimwene a atate anu kapena alongo awo atate anu kapena m’nyumba za amalume anu kapena m’nyumba za achemwali a amayi anu kapena m’nyumba zimene makiyi ake mwasunga kapena aliyense m’nyumba za abwenzi anu. Palibe cholakwa kwa inu ngati mudya pamodzi kapena payekha payekha. Pamene mulowa m’nyumba, lonjeranani wina ndi mnzake malonje odalitsika ochokera kwa Mulungu. Kotero Mulungu ali kukufotokozerani zizindikiro kuti mukhoza kukhala ozindikira

❮ Previous Next ❯

ترجمة: ليس على الأعمى حرج ولا على الأعرج حرج ولا على المريض حرج, باللغة نيانجا

﴿ليس على الأعمى حرج ولا على الأعرج حرج ولا على المريض حرج﴾ [النور: 61]

Khaled Ibrahim Betala
“Palibe kulakwa pa akhungu (osapenya) ndiponso palibe kulakwa pa olumala; palibenso kulakwa pa odwala, ngakhalenso pa inu eni ngati muli kudya m’nyumba zanu kapena m’nyumba za atate anu, kapena m’nyumba za amayi anu, kapena m’nyumba za abale anu, kapena m’nyumba za alongo anu, kapena m’nyumba za abambo anu ang’ono kapena akulu, kapena m’nyumba za azakhali anu, kapena m’nyumba za atsibweni anu, kapena m’nyumba za amayi anu akulu kapena ang’ono, kapena m’nyumba za omwe mukuwasungira makiyi, kapena (m’nyumba za) anzanu; palibe kulakwa pa inu ngati mukudyera limodzi kapena payekhapayekha. Ndipo mukamalowa m’nyumba dziperekereni nokha salaamu. (lonjero ili) ndi malonje ochokera kwa Allah amadalitso, abwino. Umo ndi momwe Allah akukulongosolerani Ayah (ndime) Zake kuti muzindikire
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek