×

Ndi okhawo amene ali ndi chikhulupiriro, amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi 24:62 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah An-Nur ⮕ (24:62) ayat 62 in Chichewa

24:62 Surah An-Nur ayat 62 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah An-Nur ayat 62 - النور - Page - Juz 18

﴿إِنَّمَا ٱلۡمُؤۡمِنُونَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ وَإِذَا كَانُواْ مَعَهُۥ عَلَىٰٓ أَمۡرٖ جَامِعٖ لَّمۡ يَذۡهَبُواْ حَتَّىٰ يَسۡتَـٔۡذِنُوهُۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ يَسۡتَـٔۡذِنُونَكَ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ يُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦۚ فَإِذَا ٱسۡتَـٔۡذَنُوكَ لِبَعۡضِ شَأۡنِهِمۡ فَأۡذَن لِّمَن شِئۡتَ مِنۡهُمۡ وَٱسۡتَغۡفِرۡ لَهُمُ ٱللَّهَۚ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ رَّحِيمٞ ﴾
[النور: 62]

Ndi okhawo amene ali ndi chikhulupiriro, amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo amati akasonkhana pamodzi ndi iye pa zinthu zofunika sachoka mpaka pamene apempha chilolezo chake. Ndithudi anthu amene amakupempha chilolezo ndiwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi wake. Pamene akupempha iwe chilolezo choti achoke ndi cholinga chokagwira ntchito zawo, pereka chilolezo kwa aliyense amene iwe wamufuna ndipo mumupemphe Mulungu kuti awakhululukire machimo awo. Mulungu amakhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha

❮ Previous Next ❯

ترجمة: إنما المؤمنون الذين آمنوا بالله ورسوله وإذا كانوا معه على أمر جامع, باللغة نيانجا

﴿إنما المؤمنون الذين آمنوا بالله ورسوله وإذا كانوا معه على أمر جامع﴾ [النور: 62]

Khaled Ibrahim Betala
“Ndithu okhulupirira (owona) ndiamene akhulupirira mwa Allah ndi Mtumiki Wake; ndipo akakhala naye pa chinthu chokhudza onse, sachoka mpaka atampempha (Mtumiki) chilolezo. Ndithu amene akukupempha chilolezo, iwowo ndi amene akukhulupirira Allah ndi Mtumiki Wake. Choncho akakupempha chilolezo chifukwa cha zinthu zawo zina, muloleze mwa iwo amene wamfuna (ngati utaona kuti chidandaulo chake nchoona), ndipo uwapemphere chikhululuko kwa Allah; ndithu Allah Ngokhululuka kwabasi; Ngwachisoni chosatha
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek