Quran with Chichewa translation - Surah al-‘Imran ayat 112 - آل عِمران - Page - Juz 4
﴿ضُرِبَتۡ عَلَيۡهِمُ ٱلذِّلَّةُ أَيۡنَ مَا ثُقِفُوٓاْ إِلَّا بِحَبۡلٖ مِّنَ ٱللَّهِ وَحَبۡلٖ مِّنَ ٱلنَّاسِ وَبَآءُو بِغَضَبٖ مِّنَ ٱللَّهِ وَضُرِبَتۡ عَلَيۡهِمُ ٱلۡمَسۡكَنَةُۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ كَانُواْ يَكۡفُرُونَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَيَقۡتُلُونَ ٱلۡأَنۢبِيَآءَ بِغَيۡرِ حَقّٖۚ ذَٰلِكَ بِمَا عَصَواْ وَّكَانُواْ يَعۡتَدُونَ ﴾
[آل عِمران: 112]
﴿ضربت عليهم الذلة أين ما ثقفوا إلا بحبل من الله وحبل من﴾ [آل عِمران: 112]
Khaled Ibrahim Betala “Adindidwa chidindo chakunyozeka paliponse pamene angapezeke kupatula (akagwira) chingwe (cha chipembedzo) cha Allah, kapena chingwe cha anthu (pothandizidwa ndi anthu ena. Koma paokha sangakhale ndi nyonga). Abwerera ndi mkwiyo wa Allah; ndipo chidindo chaumphawi chadindidwa pa iwo. Izi nchifukwa chakuti iwo sadali kukhulupirira mawu a Allah, ndipo amapha aneneri popanda choonadi. Izi nchifukwa chakutinso adanyoza ndi kulumpha malire |