×

سورة آل عمران باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة آل عمران

ترجمة معاني سورة آل عمران باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة آل عمران مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Al Imran in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة آل عمران باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 200 - رقم السورة 3 - الصفحة 50.

بسم الله الرحمن الرحيم

الم (1)
Alif Lam Mim
اللَّهُ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ الْحَيُّ الْقَيُّومُ (2)
Mulungu! Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Wamuyaya ndi Msungi wa zinthu zonse
نَزَّلَ عَلَيْكَ الْكِتَابَ بِالْحَقِّ مُصَدِّقًا لِّمَا بَيْنَ يَدَيْهِ وَأَنزَلَ التَّوْرَاةَ وَالْإِنجِيلَ (3)
Ndiye amene wavumbulutsa kwa iwe Buku la choonadi, kutsimikiza mawu amene adaperekedwa kale. Ndipo Iye anavumbulutsa Buku la chipangano chakale ndi Buku la chipangano chatsopano
مِن قَبْلُ هُدًى لِّلنَّاسِ وَأَنزَلَ الْفُرْقَانَ ۗ إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا بِآيَاتِ اللَّهِ لَهُمْ عَذَابٌ شَدِيدٌ ۗ وَاللَّهُ عَزِيزٌ ذُو انتِقَامٍ (4)
Kale ngati ulangizi kwa anthu ndipo adatumiza muyeso. Ndithudi iwo amene amakana chivumbulutso cha Mulungu adzalangidwa kwambiri. Ndipo Mulungu ndi wamphamvu ndiponso Mwini kubwezera
إِنَّ اللَّهَ لَا يَخْفَىٰ عَلَيْهِ شَيْءٌ فِي الْأَرْضِ وَلَا فِي السَّمَاءِ (5)
Ndithudi palibe chinthu chimene chili padziko lapansi kapena kumwamba chimene chimabisika kwa Mulungu
هُوَ الَّذِي يُصَوِّرُكُمْ فِي الْأَرْحَامِ كَيْفَ يَشَاءُ ۚ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (6)
Iye ndiye amene amakukonzani pamene muli m’mimba mwa amayi anu mwa chifuniro chake. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha, Mwini mphamvu ndi Mwini nzeru
هُوَ الَّذِي أَنزَلَ عَلَيْكَ الْكِتَابَ مِنْهُ آيَاتٌ مُّحْكَمَاتٌ هُنَّ أُمُّ الْكِتَابِ وَأُخَرُ مُتَشَابِهَاتٌ ۖ فَأَمَّا الَّذِينَ فِي قُلُوبِهِمْ زَيْغٌ فَيَتَّبِعُونَ مَا تَشَابَهَ مِنْهُ ابْتِغَاءَ الْفِتْنَةِ وَابْتِغَاءَ تَأْوِيلِهِ ۗ وَمَا يَعْلَمُ تَأْوِيلَهُ إِلَّا اللَّهُ ۗ وَالرَّاسِخُونَ فِي الْعِلْمِ يَقُولُونَ آمَنَّا بِهِ كُلٌّ مِّنْ عِندِ رَبِّنَا ۗ وَمَا يَذَّكَّرُ إِلَّا أُولُو الْأَلْبَابِ (7)
Ndiye amene wavumbulutsa kwa iwe Buku. Ndipo ena mwamavesiakealindimatanthauzoozindikirika, omwendi mazikoa Buku, pameneenandiovutakuwazindikira. Ndipo iwo amene mitima yawo yadzazidwa ndi chisokonekero, iwo amatsatira mavesi amene ndi ovuta kuwazindikira ndi cholinga chofuna chisokonezo ndi kufuna kupereka matanthauzo awoawo. Koma palibe amene amadziwa matanthauzo ake kupatula Mulungu. Ndipo iwo amene ali ndi nzeru amati: “Ife timakhulupirira mwa ilo chifukwa lonse ndi lochokera kwa Ambuye wathu.” Ndipo palibe amene amalabadira kupatula okhawo amene ali ndi nzeru
رَبَّنَا لَا تُزِغْ قُلُوبَنَا بَعْدَ إِذْ هَدَيْتَنَا وَهَبْ لَنَا مِن لَّدُنكَ رَحْمَةً ۚ إِنَّكَ أَنتَ الْوَهَّابُ (8)
oh Ambuye wathu! Musalole kuti mitima yathu isokere pamene Inu mwatilangiza ndipo tipatseni chisomo chanu. Ndithudi Inu ndinu opereka moolowa manja
رَبَّنَا إِنَّكَ جَامِعُ النَّاسِ لِيَوْمٍ لَّا رَيْبَ فِيهِ ۚ إِنَّ اللَّهَ لَا يُخْلِفُ الْمِيعَادَ (9)
oh Ambuye wathu! Ndithudi Inu mudzasonkhanitsa anthu onse kudza kwa Inu pa tsiku lopanda chikaiko. Ndithudi Mulungu saphwanya lonjezo lake
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا لَن تُغْنِيَ عَنْهُمْ أَمْوَالُهُمْ وَلَا أَوْلَادُهُم مِّنَ اللَّهِ شَيْئًا ۖ وَأُولَٰئِكَ هُمْ وَقُودُ النَّارِ (10)
Ndithudi iwo amene sakhulupirira, chuma chawo ndiponso ana awo sadzatha kuwapulumutsa ku mkwiyo wa Mulungu ndipo iwo adzakhala nkhuni za ku Gahena
كَدَأْبِ آلِ فِرْعَوْنَ وَالَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۚ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا فَأَخَذَهُمُ اللَّهُ بِذُنُوبِهِمْ ۗ وَاللَّهُ شَدِيدُ الْعِقَابِ (11)
Monga anthu a Farawo ndi iwo amene adalipo kale, iwo adakana chivumbulutso chathu, motero Mulungu adawalanga chifukwa cha machimo awo. Mulungu amakhwimitsa chilango chake
قُل لِّلَّذِينَ كَفَرُوا سَتُغْلَبُونَ وَتُحْشَرُونَ إِلَىٰ جَهَنَّمَ ۚ وَبِئْسَ الْمِهَادُ (12)
Nena kwa anthu amene sakhulupirira: “Inu mudzagonjetsedwa ndi kusonkhanitsidwa kupita ku Gahena omwe ndi malo oipa kukhalako.”
قَدْ كَانَ لَكُمْ آيَةٌ فِي فِئَتَيْنِ الْتَقَتَا ۖ فِئَةٌ تُقَاتِلُ فِي سَبِيلِ اللَّهِ وَأُخْرَىٰ كَافِرَةٌ يَرَوْنَهُم مِّثْلَيْهِمْ رَأْيَ الْعَيْنِ ۚ وَاللَّهُ يُؤَيِّدُ بِنَصْرِهِ مَن يَشَاءُ ۗ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَعِبْرَةً لِّأُولِي الْأَبْصَارِ (13)
Ndithudi mudali chizindikiro kwa inu, m’magulu awiri ankhondo, amene adakumana pamalo omenyera nkhondo. Gulu lina linali kumenya nkhondo munjira ya Mulungu pamene lina linali gulu la anthu osakhulupirira. Anthu okhulupirira adaona ndi maso awo kuti anthu osakhulupirira adali ambiri kuposa iwo. Koma Mulungu amapereka mphamvu ndi chipulumutso chake kwa amene wamufuna. Ndithudi mu zimenezi muli phunziro kwa anthu ozindikira
زُيِّنَ لِلنَّاسِ حُبُّ الشَّهَوَاتِ مِنَ النِّسَاءِ وَالْبَنِينَ وَالْقَنَاطِيرِ الْمُقَنطَرَةِ مِنَ الذَّهَبِ وَالْفِضَّةِ وَالْخَيْلِ الْمُسَوَّمَةِ وَالْأَنْعَامِ وَالْحَرْثِ ۗ ذَٰلِكَ مَتَاعُ الْحَيَاةِ الدُّنْيَا ۖ وَاللَّهُ عِندَهُ حُسْنُ الْمَآبِ (14)
Zokoma kwa amuna ndi chikondi chimene ali nacho pa zinthu zimene apeza, akazi, ana, chuma cha golide ndi siliva chimene chasonkhanitsidwa, mahatchi okongola, ziweto ndipo minda yolimidwa bwino. Ichi ndi chisangalalo cha m’moyo uno koma Mulungu ali ndi zinthu zabwino
۞ قُلْ أَؤُنَبِّئُكُم بِخَيْرٍ مِّن ذَٰلِكُمْ ۚ لِلَّذِينَ اتَّقَوْا عِندَ رَبِّهِمْ جَنَّاتٌ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا وَأَزْوَاجٌ مُّطَهَّرَةٌ وَرِضْوَانٌ مِّنَ اللَّهِ ۗ وَاللَّهُ بَصِيرٌ بِالْعِبَادِ (15)
Nena: “Kodi ine ndikuuzeni zinthu zabwino kuposa izi? Kwa anthu olungama kuli minda imene ili ndi Ambuye wawo,yoyenda madzi pansi pake, imene adzakhalako mpaka kalekale ndipo adzapatsidwa akazi abwino chimene chili chisomo chochokera kwa Ambuye wawo. Mulungu ali kuwaona akapolo ake.”
الَّذِينَ يَقُولُونَ رَبَّنَا إِنَّنَا آمَنَّا فَاغْفِرْ لَنَا ذُنُوبَنَا وَقِنَا عَذَابَ النَّارِ (16)
Iwo amene amati: “Ambuye wathu! Ife timakhulupirira mwa Inu kotero tikhululukireni machimo athu ndipo titetezeni kuchilango chamoto.”
الصَّابِرِينَ وَالصَّادِقِينَ وَالْقَانِتِينَ وَالْمُنفِقِينَ وَالْمُسْتَغْفِرِينَ بِالْأَسْحَارِ (17)
Iwo amene ali opirira, a chilungamo, omvera ndi woolowa manja, ndipo iwo ndi amene amapempha chikhululukiro kwa Mulungu nthawi ya m’mawa
شَهِدَ اللَّهُ أَنَّهُ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ وَالْمَلَائِكَةُ وَأُولُو الْعِلْمِ قَائِمًا بِالْقِسْطِ ۚ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (18)
Mulungu achitira umboni kuti kulibe mulungu wina koma Iye yekha ndipo angelo ake ndi anthu ozindikira, nawo amachitira umboni, Iye amasamala zolengedwa zake mwa chilungamo. Kulibe mulungu wina koma Iye yekha, Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru
إِنَّ الدِّينَ عِندَ اللَّهِ الْإِسْلَامُ ۗ وَمَا اخْتَلَفَ الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ إِلَّا مِن بَعْدِ مَا جَاءَهُمُ الْعِلْمُ بَغْيًا بَيْنَهُمْ ۗ وَمَن يَكْفُرْ بِآيَاتِ اللَّهِ فَإِنَّ اللَّهَ سَرِيعُ الْحِسَابِ (19)
Ndithudi chipembedzo cha Mulungu ndi Chisilamu. Iwo amene adapatsidwa Buku sadagawikane pa chifukwa china chili chonse koma nsanje pamene nzeru zidadza kwa iwo. Ndipo aliyense amene akana zizindikiro za Mulungu, ndithudi, Mulungu ndi wachangu polanga
فَإِنْ حَاجُّوكَ فَقُلْ أَسْلَمْتُ وَجْهِيَ لِلَّهِ وَمَنِ اتَّبَعَنِ ۗ وَقُل لِّلَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ وَالْأُمِّيِّينَ أَأَسْلَمْتُمْ ۚ فَإِنْ أَسْلَمُوا فَقَدِ اهْتَدَوا ۖ وَّإِن تَوَلَّوْا فَإِنَّمَا عَلَيْكَ الْبَلَاغُ ۗ وَاللَّهُ بَصِيرٌ بِالْعِبَادِ (20)
Ndipo ngati iwo atsutsana nawe, nena: “Ine ndadzipereka kwa Mulungu pamodzi ndi anthu onse amene anditsatira ine.” Ndipo nena kwa iwo amene adalandira Buku kale ndi kwa iwo amene ali mbuli kuti: “Kodi inu mwadzipereka?” Ngati iwo adzipereka, iwo ndi otsogozedwa koma ngati salabadira, iwe ntchito yako ndi kupereka uthenga ndipo Mulungu amaona akapolo ake
إِنَّ الَّذِينَ يَكْفُرُونَ بِآيَاتِ اللَّهِ وَيَقْتُلُونَ النَّبِيِّينَ بِغَيْرِ حَقٍّ وَيَقْتُلُونَ الَّذِينَ يَأْمُرُونَ بِالْقِسْطِ مِنَ النَّاسِ فَبَشِّرْهُم بِعَذَابٍ أَلِيمٍ (21)
Ndithudi iwo amene sakhulupirira chivumbulutso cha Mulungu ndipo kumapha Atumwi mosayenera, ndipo amapha anthu amene amalamulira kuchita chilungamo, auzeni za chilango chowawa
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ حَبِطَتْ أَعْمَالُهُمْ فِي الدُّنْيَا وَالْآخِرَةِ وَمَا لَهُم مِّن نَّاصِرِينَ (22)
Amenewa ndiwo amene ntchito zawo zidzakhala zopanda pake m’dziko lino ndi m’dziko limene lili nkudza ndipo iwo sadzapeza owathandiza
أَلَمْ تَرَ إِلَى الَّذِينَ أُوتُوا نَصِيبًا مِّنَ الْكِتَابِ يُدْعَوْنَ إِلَىٰ كِتَابِ اللَّهِ لِيَحْكُمَ بَيْنَهُمْ ثُمَّ يَتَوَلَّىٰ فَرِيقٌ مِّنْهُمْ وَهُم مُّعْرِضُونَ (23)
Kodi siunawaone iwo amene adapatsidwa gawo la Mau a Mulungu? Iwo ali kuitanidwa kuti adzamve mawu amene ali m’Buku la Mulungu kuti aweruzane pakati pawo koma gulu lina mwa iwo limabwerera m’mbuyo ndipo limachita mwano
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ قَالُوا لَن تَمَسَّنَا النَّارُ إِلَّا أَيَّامًا مَّعْدُودَاتٍ ۖ وَغَرَّهُمْ فِي دِينِهِم مَّا كَانُوا يَفْتَرُونَ (24)
Ichi ndi chifukwa chakuti iwo amanena kuti: “Ife sitidzakhudzidwa ndi moto kupatula masiku owerengeka okha.” Ndipo chimene iwo amapeka chokhudza chipembedzo chawo, chawasokeretsa iwo
فَكَيْفَ إِذَا جَمَعْنَاهُمْ لِيَوْمٍ لَّا رَيْبَ فِيهِ وَوُفِّيَتْ كُلُّ نَفْسٍ مَّا كَسَبَتْ وَهُمْ لَا يُظْلَمُونَ (25)
Kodi zidzakhala bwanji pamene Ife tidzawasonkhanitsa pamodzi pa tsiku losakaikitsa? Ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa chimene udachita. Ndipo iwo sadzaponderezedwa
قُلِ اللَّهُمَّ مَالِكَ الْمُلْكِ تُؤْتِي الْمُلْكَ مَن تَشَاءُ وَتَنزِعُ الْمُلْكَ مِمَّن تَشَاءُ وَتُعِزُّ مَن تَشَاءُ وَتُذِلُّ مَن تَشَاءُ ۖ بِيَدِكَ الْخَيْرُ ۖ إِنَّكَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (26)
Nena: “oh Ambuye! Mwini Ufumu! Inu mumamupatsa ufumu aliyense amene mwamufuna ndipo mumalanda ufumu wa aliyense amene mwamufuna. Inu mumalemekeza aliyense amene mwamufuna ndi kumpeputsa aliyense amene mwamufuna. M’manja mwanu muli ubwino wonse. Ndithudi Inu muli ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse.”
تُولِجُ اللَّيْلَ فِي النَّهَارِ وَتُولِجُ النَّهَارَ فِي اللَّيْلِ ۖ وَتُخْرِجُ الْحَيَّ مِنَ الْمَيِّتِ وَتُخْرِجُ الْمَيِّتَ مِنَ الْحَيِّ ۖ وَتَرْزُقُ مَن تَشَاءُ بِغَيْرِ حِسَابٍ (27)
“Inu mumasanduliza usiku kuti ukhale usana ndi usana kuti ukhale usiku. Inu mumatulutsa cha moyo kuchokera ku chakufa ndi chakufa kuchokera ku chamoyo. Inu mumapereka chuma ndi chakudya moolowa manja kwa aliyense amene Inu mwamufuna.”
لَّا يَتَّخِذِ الْمُؤْمِنُونَ الْكَافِرِينَ أَوْلِيَاءَ مِن دُونِ الْمُؤْمِنِينَ ۖ وَمَن يَفْعَلْ ذَٰلِكَ فَلَيْسَ مِنَ اللَّهِ فِي شَيْءٍ إِلَّا أَن تَتَّقُوا مِنْهُمْ تُقَاةً ۗ وَيُحَذِّرُكُمُ اللَّهُ نَفْسَهُ ۗ وَإِلَى اللَّهِ الْمَصِيرُ (28)
Anthu okhulupirira asapange ubwenzi ndi anthu osakhulupirira m’malo mwa anthu okhulupirira, ndipo aliyense amene achita izi sadzathandizidwa ndi Mulungu mwanjira ili yonse kupatula ngati inu muopa choipa chochokera kwa iwo. Ndipo Mulungu ali kukuchenjezani za chilango chake ndipo pomaliza ndi kwa Mulungu kumene zonse zidzabwerera
قُلْ إِن تُخْفُوا مَا فِي صُدُورِكُمْ أَوْ تُبْدُوهُ يَعْلَمْهُ اللَّهُ ۗ وَيَعْلَمُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۗ وَاللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (29)
Nena: “Kaya mubisa zimene zili mumitima mwanu kapena muulula, zonse Mulungu akuzidziwa. Ndipo Iye amadziwa zonse zimene zili mlengalenga ndi zimene zili padziko lapansi. Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu pa zinthu zonse.”
يَوْمَ تَجِدُ كُلُّ نَفْسٍ مَّا عَمِلَتْ مِنْ خَيْرٍ مُّحْضَرًا وَمَا عَمِلَتْ مِن سُوءٍ تَوَدُّ لَوْ أَنَّ بَيْنَهَا وَبَيْنَهُ أَمَدًا بَعِيدًا ۗ وَيُحَذِّرُكُمُ اللَّهُ نَفْسَهُ ۗ وَاللَّهُ رَءُوفٌ بِالْعِبَادِ (30)
Pa tsiku limene mzimu uliwonse udzaona zabwino zonse zimene udachita zitabweretsedwa ndiponso zoipa zonse zimene udachita, iwo udzafunitsitsa kuti pakadakhala mtunda wautali pakati pa iwo ndi zoipazo. Ndipo Mulungu ali kukuchenjezani inu zachilango chake ndipo Mulungu ali ndi chisoni chambiri kwa akapolo ake
قُلْ إِن كُنتُمْ تُحِبُّونَ اللَّهَ فَاتَّبِعُونِي يُحْبِبْكُمُ اللَّهُ وَيَغْفِرْ لَكُمْ ذُنُوبَكُمْ ۗ وَاللَّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (31)
Nena: “Ngati inu, ndithudi, mukonda Mulungu, nditsatireni ine. Mulungu adzakukondani ndipo adzakukhululukirani machimo anu. Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha.”
قُلْ أَطِيعُوا اللَّهَ وَالرَّسُولَ ۖ فَإِن تَوَلَّوْا فَإِنَّ اللَّهَ لَا يُحِبُّ الْكَافِرِينَ (32)
Nena: “Mverani Mulungu ndi Mtumwi. Koma ngati simumvera Mulungu sakonda anthu osakhulupirira.”
۞ إِنَّ اللَّهَ اصْطَفَىٰ آدَمَ وَنُوحًا وَآلَ إِبْرَاهِيمَ وَآلَ عِمْرَانَ عَلَى الْعَالَمِينَ (33)
Ndithudi Mulungu adasankha Adamu, Nowa ndi banja la Abrahamu ndi banja la Imran kukhala opambana mitundu yonse ya nthawi yawo
ذُرِّيَّةً بَعْضُهَا مِن بَعْضٍ ۗ وَاللَّهُ سَمِيعٌ عَلِيمٌ (34)
Ana a wina ndi mnzake ndipo Mulungu ndi wakumva ndi wodziwa
إِذْ قَالَتِ امْرَأَتُ عِمْرَانَ رَبِّ إِنِّي نَذَرْتُ لَكَ مَا فِي بَطْنِي مُحَرَّرًا فَتَقَبَّلْ مِنِّي ۖ إِنَّكَ أَنتَ السَّمِيعُ الْعَلِيمُ (35)
Pamene mkazi wa Imran adati: “Ambuye wanga! Ine ndilonjeza kwa Inu chinthu chimene chili m’mimba mwanga kuti chidzakhale chokutumikirani Inu. Motero landirani ichi kuchokera kwa ine ngati nsembe yanga. Ndithudi Inu ndinu wakumva ndi wozindikira.”
فَلَمَّا وَضَعَتْهَا قَالَتْ رَبِّ إِنِّي وَضَعْتُهَا أُنثَىٰ وَاللَّهُ أَعْلَمُ بِمَا وَضَعَتْ وَلَيْسَ الذَّكَرُ كَالْأُنثَىٰ ۖ وَإِنِّي سَمَّيْتُهَا مَرْيَمَ وَإِنِّي أُعِيذُهَا بِكَ وَذُرِّيَّتَهَا مِنَ الشَّيْطَانِ الرَّجِيمِ (36)
Ndipo pamene iye anabereka mwana wake, iye adati: “Ambuye wanga! Ine ndabereka mwana wamkazi.” Koma Mulungu anadziwiratu chimene iye wabereka. “Ndipo mwana wamwamuna salingana ndi mwana wa mkazi, ndipo ine ndamutcha dzina la Maria ndipo ndili kumupereka iye pamodzi ndi mbewu yake kwa Inu kuti muwateteze kwa Satana wotembereredwa.”
فَتَقَبَّلَهَا رَبُّهَا بِقَبُولٍ حَسَنٍ وَأَنبَتَهَا نَبَاتًا حَسَنًا وَكَفَّلَهَا زَكَرِيَّا ۖ كُلَّمَا دَخَلَ عَلَيْهَا زَكَرِيَّا الْمِحْرَابَ وَجَدَ عِندَهَا رِزْقًا ۖ قَالَ يَا مَرْيَمُ أَنَّىٰ لَكِ هَٰذَا ۖ قَالَتْ هُوَ مِنْ عِندِ اللَّهِ ۖ إِنَّ اللَّهَ يَرْزُقُ مَن يَشَاءُ بِغَيْرِ حِسَابٍ (37)
Motero Ambuye wake adamulandira iye, ndi manja awiri. Ndipo Iye anamukuza bwino, ndipo anamupereka m’manja mwa Zakariya kuti amulere. Nthawi zonse pamene Zakariya adali kulowa ku chipinda kumene iye anali kukhala, anali kumupeza ndi chakudya. Iye adati: “oh Maria! Kodi chakudya ichi chili kuchokera kuti?” Iye adati: “Chili kuchokera kwa Mulungu. Ndithudi Mulungu amapereka chakudya mopanda malire, kwa aliyense amene wamufuna.”
هُنَالِكَ دَعَا زَكَرِيَّا رَبَّهُ ۖ قَالَ رَبِّ هَبْ لِي مِن لَّدُنكَ ذُرِّيَّةً طَيِّبَةً ۖ إِنَّكَ سَمِيعُ الدُّعَاءِ (38)
Nthawi imeneyo Zakariya adapempha kwa Ambuye wake nati: “Ambuye wanga! Ndipatseni ine kuchokera kwa Inu mwana wangwiro. Inu ndithudi mumamva pemphero.”
فَنَادَتْهُ الْمَلَائِكَةُ وَهُوَ قَائِمٌ يُصَلِّي فِي الْمِحْرَابِ أَنَّ اللَّهَ يُبَشِّرُكَ بِيَحْيَىٰ مُصَدِّقًا بِكَلِمَةٍ مِّنَ اللَّهِ وَسَيِّدًا وَحَصُورًا وَنَبِيًّا مِّنَ الصَّالِحِينَ (39)
Ndipo pamene iye adapitiriza mapemphero m’chipinda, angelo anamuitana iye nati: “Mulungu ali kukuuza nkhani yabwino ya Yohane amene adzatsimikiza Mawu ochokera kwa Mulungu. Iye adzakhala wolemekezeka ndi wodzisunga kwa akazi, Mtumwi wochokera pakati pa anthu angwiro.”
قَالَ رَبِّ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي غُلَامٌ وَقَدْ بَلَغَنِيَ الْكِبَرُ وَامْرَأَتِي عَاقِرٌ ۖ قَالَ كَذَٰلِكَ اللَّهُ يَفْعَلُ مَا يَشَاءُ (40)
Zakariya adati: “Ambuye wanga! Kodi ine ndingakhale ndi mwana wamwamuna bwanji pamene ine ndine wokalamba ndipo mkazi wanga ndi wouma?” Iye adati: “Mulungu amachita chimene Iye wafuna.”
قَالَ رَبِّ اجْعَل لِّي آيَةً ۖ قَالَ آيَتُكَ أَلَّا تُكَلِّمَ النَّاسَ ثَلَاثَةَ أَيَّامٍ إِلَّا رَمْزًا ۗ وَاذْكُر رَّبَّكَ كَثِيرًا وَسَبِّحْ بِالْعَشِيِّ وَالْإِبْكَارِ (41)
Iye adati: “Ambuye wanga! Ndionetseni chizindikiro.” Iye adati: “Chizindikiro chako ndi chakuti iwe siudzayankhula ndi anthu pa masiku atatu kupatulam’zizindikirozokhazokha. Ndipoumukumbukire kwambiri Ambuye wako ndi kumulemekeza madzulo ndi m’mawa.”
وَإِذْ قَالَتِ الْمَلَائِكَةُ يَا مَرْيَمُ إِنَّ اللَّهَ اصْطَفَاكِ وَطَهَّرَكِ وَاصْطَفَاكِ عَلَىٰ نِسَاءِ الْعَالَمِينَ (42)
Ndi pamene angelo adati: “oh Maria! Ndithudi Mulungu wakusankha ndi kukuyeretsa iwe ndipo wakusankha kukhala wapamwamba pakati pa akazi ena a zolengedwa zonse.”
يَا مَرْيَمُ اقْنُتِي لِرَبِّكِ وَاسْجُدِي وَارْكَعِي مَعَ الرَّاكِعِينَ (43)
“Oh Maria! Khala omvera Ambuye wako, gwetsa nkhope yako pansi, ndipo werama pamodzi ndi iwo amene amapembedza mowerama.”
ذَٰلِكَ مِنْ أَنبَاءِ الْغَيْبِ نُوحِيهِ إِلَيْكَ ۚ وَمَا كُنتَ لَدَيْهِمْ إِذْ يُلْقُونَ أَقْلَامَهُمْ أَيُّهُمْ يَكْفُلُ مَرْيَمَ وَمَا كُنتَ لَدَيْهِمْ إِذْ يَخْتَصِمُونَ (44)
Iyi ndi nkhani yobisika imene Ife tili kukuululira. Iwe kudalibe pamene iwo adachita mayere ndi zolembera zawo oti aone kuti kodi ndani wa iwo amene ayenera kusamala Maria ndiponso iwe kudalibe pamene iwo adali kukangana
إِذْ قَالَتِ الْمَلَائِكَةُ يَا مَرْيَمُ إِنَّ اللَّهَ يُبَشِّرُكِ بِكَلِمَةٍ مِّنْهُ اسْمُهُ الْمَسِيحُ عِيسَى ابْنُ مَرْيَمَ وَجِيهًا فِي الدُّنْيَا وَالْآخِرَةِ وَمِنَ الْمُقَرَّبِينَ (45)
Ndi pamene angelo adati: “oh Maria! Ndithudi Mulungu ali kukupatsa nkhani yabwino ya Mawu ochokera kwa Iye amene dzina lake ndi Messiya, Yesu mwana wa Maria, wolemekezeka m’dziko lino ndi m’dziko limene lili nkudza ndipo adzakhala m’gulu la anthu okhala pafupi ndi Mulungu.”
وَيُكَلِّمُ النَّاسَ فِي الْمَهْدِ وَكَهْلًا وَمِنَ الصَّالِحِينَ (46)
“Iye adzayankhula kwa anthu ali m’chikuta ndi atakula msinkhu ndipo adzakhala mugulu la anthu angwiro.”
قَالَتْ رَبِّ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي وَلَدٌ وَلَمْ يَمْسَسْنِي بَشَرٌ ۖ قَالَ كَذَٰلِكِ اللَّهُ يَخْلُقُ مَا يَشَاءُ ۚ إِذَا قَضَىٰ أَمْرًا فَإِنَّمَا يَقُولُ لَهُ كُن فَيَكُونُ (47)
Iye adati: “oh Ambuye wanga! Kodi ine ndingabereke mwana bwanji pamene sindidakhudzidwe ndi mwamuna?” Iye adati: “Zidzakhala choncho, chifukwa Mulungu amalenga chimene afuna. Ndipo pamene afuna chinthu, Iye amangonena kwa icho, ‘Khala’ ndipo chimakhala.”
وَيُعَلِّمُهُ الْكِتَابَ وَالْحِكْمَةَ وَالتَّوْرَاةَ وَالْإِنجِيلَ (48)
Ndipo Iye adzamuphunzitsa kulemba ndi luntha, Torah ndi Utenga wabwino
وَرَسُولًا إِلَىٰ بَنِي إِسْرَائِيلَ أَنِّي قَدْ جِئْتُكُم بِآيَةٍ مِّن رَّبِّكُمْ ۖ أَنِّي أَخْلُقُ لَكُم مِّنَ الطِّينِ كَهَيْئَةِ الطَّيْرِ فَأَنفُخُ فِيهِ فَيَكُونُ طَيْرًا بِإِذْنِ اللَّهِ ۖ وَأُبْرِئُ الْأَكْمَهَ وَالْأَبْرَصَ وَأُحْيِي الْمَوْتَىٰ بِإِذْنِ اللَّهِ ۖ وَأُنَبِّئُكُم بِمَا تَأْكُلُونَ وَمَا تَدَّخِرُونَ فِي بُيُوتِكُمْ ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَةً لَّكُمْ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ (49)
Ndipo adzamupanga iye kukhala Mtumwi wa ana a Israyeli nati: “Ine ndadza kwa inu ndi chizindikiro chochokera kwa Ambuye wanu ndipo kuchokera ku dothi ndidzakuumbirani chinthu chofanana ndi mbalame ndipo ine ndidzaipumira mpweya ndipo ndi chilolezo cha Mulungu idzakhala mbalame ya moyo. Ndi chilolezo cha Mulungu, ine ndidzachiza anthu a khungu, akhate ndi kuukitsa anthu akufa. Ine ndidzakuuzani zimene muzidya ndi zimene musunga m’nyumba mwanu. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa inu ngati muli okhulupirira.”
وَمُصَدِّقًا لِّمَا بَيْنَ يَدَيَّ مِنَ التَّوْرَاةِ وَلِأُحِلَّ لَكُم بَعْضَ الَّذِي حُرِّمَ عَلَيْكُمْ ۚ وَجِئْتُكُم بِآيَةٍ مِّن رَّبِّكُمْ فَاتَّقُوا اللَّهَ وَأَطِيعُونِ (50)
“Ndipo ine ndadzatsimikiza zimene zidalipo pambuyo panga ndi kukulolezani inu kuchita zina mwa zinthu zimene mudaletsedwa ndipo ine ndadza ndi chizindikiro chochokera kwa Ambuye wanu. Motero opani Mulungu ndipo mundimvere ine.”
إِنَّ اللَّهَ رَبِّي وَرَبُّكُمْ فَاعْبُدُوهُ ۗ هَٰذَا صِرَاطٌ مُّسْتَقِيمٌ (51)
“Ndithudi! Mulungu ndi Ambuye wanga ndi Ambuye wanu; ‘Motero m’pembedzeni Iye yekha.’ Imeneyi ndiyo njira yoyenera.”
۞ فَلَمَّا أَحَسَّ عِيسَىٰ مِنْهُمُ الْكُفْرَ قَالَ مَنْ أَنصَارِي إِلَى اللَّهِ ۖ قَالَ الْحَوَارِيُّونَ نَحْنُ أَنصَارُ اللَّهِ آمَنَّا بِاللَّهِ وَاشْهَدْ بِأَنَّا مُسْلِمُونَ (52)
Ndipo pamene Yesu adaona kuti iwo adalibe chikhulupiriro, iye adati: “Kodi ndani adzandithandiza ine mu ntchito ya Mulungu?” Ophunzira ake adati: Ife ndife othandiza mu ntchito ya Mulungu, Ife takhulupirira mwa Mulungu ndipo chitirani umboni kuti ife ndife Asilamu
رَبَّنَا آمَنَّا بِمَا أَنزَلْتَ وَاتَّبَعْنَا الرَّسُولَ فَاكْتُبْنَا مَعَ الشَّاهِدِينَ (53)
“Ambuyewathu!Ifetakhulupirirazimenemwavumbulutsa ndipo titsatira Mtumwi wanu motero tiikeni ife m’gulu la mboni zanu.”
وَمَكَرُوا وَمَكَرَ اللَّهُ ۖ وَاللَّهُ خَيْرُ الْمَاكِرِينَ (54)
Ndipo iwo adachita chiwembu koma Mulungu adakonza chiwembu chake. Ndipo Mulungu ndi wodziwa kwambiri pokonza chiwembu
إِذْ قَالَ اللَّهُ يَا عِيسَىٰ إِنِّي مُتَوَفِّيكَ وَرَافِعُكَ إِلَيَّ وَمُطَهِّرُكَ مِنَ الَّذِينَ كَفَرُوا وَجَاعِلُ الَّذِينَ اتَّبَعُوكَ فَوْقَ الَّذِينَ كَفَرُوا إِلَىٰ يَوْمِ الْقِيَامَةِ ۖ ثُمَّ إِلَيَّ مَرْجِعُكُمْ فَأَحْكُمُ بَيْنَكُمْ فِيمَا كُنتُمْ فِيهِ تَخْتَلِفُونَ (55)
Ndi Pamene Mulungu adati: “Oh iwe Yesu! Ine ndidzakutenga kudza kwa Ine ndipo ndidzakuyeretsa kwa anthu osakhulupirira ndipo ndidzawapanga onse amene amakutsatira iwe kukhala apamwamba pa iwo amene sakhulupirira mpaka pa tsiku la kuuka kwa akufa. Ndipo inu mudzabwerera kwa Ine ndipo Ine ndidzaweruza pa zimene mudali kutsutsana
فَأَمَّا الَّذِينَ كَفَرُوا فَأُعَذِّبُهُمْ عَذَابًا شَدِيدًا فِي الدُّنْيَا وَالْآخِرَةِ وَمَا لَهُم مِّن نَّاصِرِينَ (56)
Akakhala iwo amene sakhulupirira, Ine ndidzawalanga ndi chilango chowawa m’dziko lino ndi m’dziko limene lili nkudza ndipo sadzapeza wina wowathandiza
وَأَمَّا الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ فَيُوَفِّيهِمْ أُجُورَهُمْ ۗ وَاللَّهُ لَا يُحِبُّ الظَّالِمِينَ (57)
Akakhala iwo amene ndi okhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, Mulungu adzawalipira mphotho yawo yokwanira. Ndipo Mulungu sakonda anthu ochita zoipa
ذَٰلِكَ نَتْلُوهُ عَلَيْكَ مِنَ الْآيَاتِ وَالذِّكْرِ الْحَكِيمِ (58)
Ichi chimene tiri kulakatula kwa iwe ndi Mavesi ndi Chikumbutso cha nzeru.”
إِنَّ مَثَلَ عِيسَىٰ عِندَ اللَّهِ كَمَثَلِ آدَمَ ۖ خَلَقَهُ مِن تُرَابٍ ثُمَّ قَالَ لَهُ كُن فَيَكُونُ (59)
Ndithudi kulingana kwa Yesu pamaso pa Mulungu ndi chimodzimodzi ndi Adamu. Iye anamulenga kuchokera ku dothi ndipo adati kwa iye: “Khala” ndipo adakhala
الْحَقُّ مِن رَّبِّكَ فَلَا تَكُن مِّنَ الْمُمْتَرِينَ (60)
Ichi ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wako, motero usakhale mmodzi wa anthu okaika
فَمَنْ حَاجَّكَ فِيهِ مِن بَعْدِ مَا جَاءَكَ مِنَ الْعِلْمِ فَقُلْ تَعَالَوْا نَدْعُ أَبْنَاءَنَا وَأَبْنَاءَكُمْ وَنِسَاءَنَا وَنِسَاءَكُمْ وَأَنفُسَنَا وَأَنفُسَكُمْ ثُمَّ نَبْتَهِلْ فَنَجْعَل لَّعْنَتَ اللَّهِ عَلَى الْكَاذِبِينَ (61)
Ndipo iye amene atsutsana nawe pankhani za Yesu utalandira nzeru izi muuze kuti: “Bwerani kuti taitane ana athu ndi ana anu, akazi athu ndi akazi anu, ife ndi inu ndipo tipemphe modzichepetsa kuti matemberero a Mulungu akhale pa anthu amene ali nkunama.”
إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ الْقَصَصُ الْحَقُّ ۚ وَمَا مِنْ إِلَٰهٍ إِلَّا اللَّهُ ۚ وَإِنَّ اللَّهَ لَهُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (62)
Ndithudi iyi ndi nkhani yoona, ndipo kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha. Ndipo ndithudi, Mulungu ndi Wamphamvu ndi Wanzeru
فَإِن تَوَلَّوْا فَإِنَّ اللَّهَ عَلِيمٌ بِالْمُفْسِدِينَ (63)
Ngati iwo sakumvera, ndithudi, Mulungu anadziwa anthu ochita zoipa
قُلْ يَا أَهْلَ الْكِتَابِ تَعَالَوْا إِلَىٰ كَلِمَةٍ سَوَاءٍ بَيْنَنَا وَبَيْنَكُمْ أَلَّا نَعْبُدَ إِلَّا اللَّهَ وَلَا نُشْرِكَ بِهِ شَيْئًا وَلَا يَتَّخِذَ بَعْضُنَا بَعْضًا أَرْبَابًا مِّن دُونِ اللَّهِ ۚ فَإِن تَوَلَّوْا فَقُولُوا اشْهَدُوا بِأَنَّا مُسْلِمُونَ (64)
Nena: “oh inu anthu a m’Buku! Bwerani ku Mau amene ndi oona pakati pa inu ndi ife, kuti tisapembedze wina aliyense koma Mulungu mmodzi ndipo tisamuphatikize ndi china chili chonse ndipo pasakhale wina pakati pathu amene adzasankha ena ngati ambuye powonjezera pa Mulungu. Ndipo ngati iwo akana, nena: “Inu chitirani umboni kuti Ife ndife Asilamu.”
يَا أَهْلَ الْكِتَابِ لِمَ تُحَاجُّونَ فِي إِبْرَاهِيمَ وَمَا أُنزِلَتِ التَّوْرَاةُ وَالْإِنجِيلُ إِلَّا مِن بَعْدِهِ ۚ أَفَلَا تَعْقِلُونَ (65)
“oh inu anthu a m’Buku! Kodi ndi chifukwa chiyani mukutsutsana za Abrahamu, pamene Buku la Chipangano chakale ndi Chipangano Chatsopano linali lisanavumbulutsidwe panthawi yake? Kodimulibenzeru
هَا أَنتُمْ هَٰؤُلَاءِ حَاجَجْتُمْ فِيمَا لَكُم بِهِ عِلْمٌ فَلِمَ تُحَاجُّونَ فِيمَا لَيْسَ لَكُم بِهِ عِلْمٌ ۚ وَاللَّهُ يَعْلَمُ وَأَنتُمْ لَا تَعْلَمُونَ (66)
Kodiinundinuamenemumatsutsana pa nkhani zimene mumazidziwa? Nanga ndi chifukwa chiyani mukutsutsana pa zinthu zimene simudziwa? Ndi Mulungu amene amadziwa ndipo inu simuzidziwa
مَا كَانَ إِبْرَاهِيمُ يَهُودِيًّا وَلَا نَصْرَانِيًّا وَلَٰكِن كَانَ حَنِيفًا مُّسْلِمًا وَمَا كَانَ مِنَ الْمُشْرِكِينَ (67)
Abrahamu sadali Myuda kapena Mkhirisitu. Iye adali munthu wangwiro amene adadzipereka kwathunthu kwa Mulungu. Iye sadali opembedza mafano ayi
إِنَّ أَوْلَى النَّاسِ بِإِبْرَاهِيمَ لَلَّذِينَ اتَّبَعُوهُ وَهَٰذَا النَّبِيُّ وَالَّذِينَ آمَنُوا ۗ وَاللَّهُ وَلِيُّ الْمُؤْمِنِينَ (68)
Ndithudi pakati pa anthu amene ali kufupi ndi Abrahamu, pali iwo amene adamutsatira iye ndi Mtumwi uyu ndi iwo amene akhulupirira. Ndipo Mulungu amasamalira anthu okhulupirira
وَدَّت طَّائِفَةٌ مِّنْ أَهْلِ الْكِتَابِ لَوْ يُضِلُّونَكُمْ وَمَا يُضِلُّونَ إِلَّا أَنفُسَهُمْ وَمَا يَشْعُرُونَ (69)
Ena mwa anthu amene amakhulupirira Buku amafuna kukusocheretsa iwe. Komatu iwo sangasocheretse wina aliyense koma iwo eni, ndipo iwo sazindikira
يَا أَهْلَ الْكِتَابِ لِمَ تَكْفُرُونَ بِآيَاتِ اللَّهِ وَأَنتُمْ تَشْهَدُونَ (70)
oh inu anthu a m’Buku! Bwanji mumakana zizindikiro za Mulungu pamene inu mumachita umboni
يَا أَهْلَ الْكِتَابِ لِمَ تَلْبِسُونَ الْحَقَّ بِالْبَاطِلِ وَتَكْتُمُونَ الْحَقَّ وَأَنتُمْ تَعْلَمُونَ (71)
Oh inu anthu a m’Buku! Bwanji mumasakaniza choonadi ndi bodza ndipo mumabisa choonadi pamene inu muli kudziwa
وَقَالَت طَّائِفَةٌ مِّنْ أَهْلِ الْكِتَابِ آمِنُوا بِالَّذِي أُنزِلَ عَلَى الَّذِينَ آمَنُوا وَجْهَ النَّهَارِ وَاكْفُرُوا آخِرَهُ لَعَلَّهُمْ يَرْجِعُونَ (72)
Ndipo ena mwa anthu a m’Buku amati: Khulupirirani mu zimene zavumbulutsidwa kwa anthu okhulupirira m’mawa ndipo muzikane madzulo ake kuti iwo akhoza kubwerera m’mbuyo
وَلَا تُؤْمِنُوا إِلَّا لِمَن تَبِعَ دِينَكُمْ قُلْ إِنَّ الْهُدَىٰ هُدَى اللَّهِ أَن يُؤْتَىٰ أَحَدٌ مِّثْلَ مَا أُوتِيتُمْ أَوْ يُحَاجُّوكُمْ عِندَ رَبِّكُمْ ۗ قُلْ إِنَّ الْفَضْلَ بِيَدِ اللَّهِ يُؤْتِيهِ مَن يَشَاءُ ۗ وَاللَّهُ وَاسِعٌ عَلِيمٌ (73)
Ndipo musakhulupilire wina aliyense kupatula amene atsatira chipembedzo chanu. Nena: “Ndithudi! Chilangizo choonadi ndi chilangizo cha Mulungu” ndipo musakhulupirire kuti wina wake adzapatsidwa chinthu cholingana ndi chimene chapatsidwa kwa inu. Kapena iye adzatsutsana nanu pamaso pa Ambuye wanu. Nena: “Ndithudi zonse zili m’manja mwa Mulungu. Iye amazipereka kwa aliyense amene Iye wamufuna. Ndipo Mulungu ali ndi chili chonse chimene zolengedwa zake zimafuna, Mwini kudziwa chilichonse.”
يَخْتَصُّ بِرَحْمَتِهِ مَن يَشَاءُ ۗ وَاللَّهُ ذُو الْفَضْلِ الْعَظِيمِ (74)
Iye amaonetsa chifundo chake kwa aliyense amene Iye wamufuna ndipo Mulungu ndiye mwini zinthu zochuluka
۞ وَمِنْ أَهْلِ الْكِتَابِ مَنْ إِن تَأْمَنْهُ بِقِنطَارٍ يُؤَدِّهِ إِلَيْكَ وَمِنْهُم مَّنْ إِن تَأْمَنْهُ بِدِينَارٍ لَّا يُؤَدِّهِ إِلَيْكَ إِلَّا مَا دُمْتَ عَلَيْهِ قَائِمًا ۗ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ قَالُوا لَيْسَ عَلَيْنَا فِي الْأُمِّيِّينَ سَبِيلٌ وَيَقُولُونَ عَلَى اللَّهِ الْكَذِبَ وَهُمْ يَعْلَمُونَ (75)
Pakati pa anthu a m’Buku, alipo wina amene ngati ungamusungitse mulu wa chuma iye adzakubwezera chonse osachotsapo koma pakati pawo alipo wina amene ngati iwe umusungitsa ndalama imodzi ya siliva, sadzakubwezera pokhapokha utalimbikira kuitanitsa. Chifukwa iwo amati: “Ife tilibe njira yonenedwa pachifukwa cha anthu opanda nzeru.” Kotero amanena zinthu zabodza zokhudza Mulungu pamene iwo akudziwa
بَلَىٰ مَنْ أَوْفَىٰ بِعَهْدِهِ وَاتَّقَىٰ فَإِنَّ اللَّهَ يُحِبُّ الْمُتَّقِينَ (76)
Inde, aliyense amene amakwaniritsa lonjezo lake ndi kuopa Mulungu kwambiri, ndithudi Mulungu amakonda iwo amene amamuopa Iye
إِنَّ الَّذِينَ يَشْتَرُونَ بِعَهْدِ اللَّهِ وَأَيْمَانِهِمْ ثَمَنًا قَلِيلًا أُولَٰئِكَ لَا خَلَاقَ لَهُمْ فِي الْآخِرَةِ وَلَا يُكَلِّمُهُمُ اللَّهُ وَلَا يَنظُرُ إِلَيْهِمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ وَلَا يُزَكِّيهِمْ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (77)
Ndithudi, onse amene amagula phindu lochepa pa mtengo wa lonjezo la Mulungu, ndi malonjezo awo, iwo sadzakhala ndi gawo m’moyo umene uli nkudza. Mulungu sadzalankhula nawo kapena kuwayang’ana patsiku louka kwa akufa. Iye sadzawayeretsa ndipo iwo adzalandira chilango chowawa
وَإِنَّ مِنْهُمْ لَفَرِيقًا يَلْوُونَ أَلْسِنَتَهُم بِالْكِتَابِ لِتَحْسَبُوهُ مِنَ الْكِتَابِ وَمَا هُوَ مِنَ الْكِتَابِ وَيَقُولُونَ هُوَ مِنْ عِندِ اللَّهِ وَمَا هُوَ مِنْ عِندِ اللَّهِ وَيَقُولُونَ عَلَى اللَّهِ الْكَذِبَ وَهُمْ يَعْلَمُونَ (78)
Ndipo, ndithudi, pakati pawo pali iwo amene amatembenuza tanthauzo la Buku ndi malirime awo pamene akuwerenga ndi cholinga chakuti iwe uziganiza kuti zonse zimene ali kunena ndi zochokera m’Buku pamene sichoncho ayi, ndipo iwo amati: “Mawu awa ndi ochokera kwa Mulungu” pamene sadachokere kwa Mulungu ndipo iwo amanena zabodza zokhudza Mulungu pamene iwo akudziwa kuti limenelo ndi bodza
مَا كَانَ لِبَشَرٍ أَن يُؤْتِيَهُ اللَّهُ الْكِتَابَ وَالْحُكْمَ وَالنُّبُوَّةَ ثُمَّ يَقُولَ لِلنَّاسِ كُونُوا عِبَادًا لِّي مِن دُونِ اللَّهِ وَلَٰكِن كُونُوا رَبَّانِيِّينَ بِمَا كُنتُمْ تُعَلِّمُونَ الْكِتَابَ وَبِمَا كُنتُمْ تَدْرُسُونَ (79)
Sizili kwa munthu amene Mulungu adamupatsa Buku lake, nzeru ndi kuzindikira malamulo a chipembedzo kuti anene kwa anthu kuti: “Ndipembedzeni ine m’malo mwa Mulungu.” Koma iye akhoza kunena kuti: “Khalani anthu ophunzira chipembedzo amene amachita zimene adziwa ndi kuuza anzawo chifukwa inu muli kuphunzitsa Buku ndipo inu muli kuliphunzira ilo.”
وَلَا يَأْمُرَكُمْ أَن تَتَّخِذُوا الْمَلَائِكَةَ وَالنَّبِيِّينَ أَرْبَابًا ۗ أَيَأْمُرُكُم بِالْكُفْرِ بَعْدَ إِذْ أَنتُم مُّسْلِمُونَ (80)
Ndipo iye sangakulamuleni kuti musandutse Angelo ndi Atumwi ngati milungu yanu ayi. Kodi iye akhoza kukulamulirani inu kuti mukhale anthu osakhulupirira pamene inu mwadzipereka kale kwa Mulungu
وَإِذْ أَخَذَ اللَّهُ مِيثَاقَ النَّبِيِّينَ لَمَا آتَيْتُكُم مِّن كِتَابٍ وَحِكْمَةٍ ثُمَّ جَاءَكُمْ رَسُولٌ مُّصَدِّقٌ لِّمَا مَعَكُمْ لَتُؤْمِنُنَّ بِهِ وَلَتَنصُرُنَّهُ ۚ قَالَ أَأَقْرَرْتُمْ وَأَخَذْتُمْ عَلَىٰ ذَٰلِكُمْ إِصْرِي ۖ قَالُوا أَقْرَرْنَا ۚ قَالَ فَاشْهَدُوا وَأَنَا مَعَكُم مِّنَ الشَّاهِدِينَ (81)
Ndi pamene Mulungu analandira chipangano cha Atumwi ponena: “Tsatirani chimene ndidakupatsani kuchokera m’Buku ndi luntha.” Ndipo Mtumwi adadza kudzatsimikiza zimene muli nazo. Inu muyenera kumukhulupirira ndi kumuthandiza iye. Ndipo Mulungu adati: “Kodi mwatsimikiza ndi kuvomera udindo umene ndakhazikitsa pa inu?” Iwo adati: “Ife tavomera.” Iye adati: “Choncho chitirani umboni ndipo Ine ndiri ndi inu pochitira umboni.”
فَمَن تَوَلَّىٰ بَعْدَ ذَٰلِكَ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْفَاسِقُونَ (82)
Ndipo iwo amene angabwerere pambuyo pakumva izi ndi wolakwa
أَفَغَيْرَ دِينِ اللَّهِ يَبْغُونَ وَلَهُ أَسْلَمَ مَن فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ طَوْعًا وَكَرْهًا وَإِلَيْهِ يُرْجَعُونَ (83)
Kodi iwo ali kufuna chipembedzo chosiyana ndi chipembedzo cha Mulungu pamene zonse zimene zili kumwamba ndi padziko lapansi zagonjera kwa Iye monyinyirika kapena mosanyinyirika? Ndipo ndi kwa Iye kumene onse adzabwerera
قُلْ آمَنَّا بِاللَّهِ وَمَا أُنزِلَ عَلَيْنَا وَمَا أُنزِلَ عَلَىٰ إِبْرَاهِيمَ وَإِسْمَاعِيلَ وَإِسْحَاقَ وَيَعْقُوبَ وَالْأَسْبَاطِ وَمَا أُوتِيَ مُوسَىٰ وَعِيسَىٰ وَالنَّبِيُّونَ مِن رَّبِّهِمْ لَا نُفَرِّقُ بَيْنَ أَحَدٍ مِّنْهُمْ وَنَحْنُ لَهُ مُسْلِمُونَ (84)
Nena: “Ife timakhulupirira mwa Mulungu ndi zimene zavumbulutsidwa kwa ife ndi zimene zinavumbulutsidwa kwa Abrahamu ndi Ishimayeli, kwa Isake ndi Yakobo, ndi kwa ana a Yakobo; ndi zimene anapatsidwa Mose, Yesu ndi kwa Atumwi kuchokera kwa Ambuye wawo. Ife sitisiyanitsa pakati pawo ayi ndipo ndi kwa Iye kumene tadzipereka.”
وَمَن يَبْتَغِ غَيْرَ الْإِسْلَامِ دِينًا فَلَن يُقْبَلَ مِنْهُ وَهُوَ فِي الْآخِرَةِ مِنَ الْخَاسِرِينَ (85)
Ndipo aliyense amene afuna chipembedzo china osati chipembezo cha Chisilamu, sichidzaloledwa kwa iye ndipo m’dziko limene lili nkudza iye adzakhala mmodzi wa anthu otayika
كَيْفَ يَهْدِي اللَّهُ قَوْمًا كَفَرُوا بَعْدَ إِيمَانِهِمْ وَشَهِدُوا أَنَّ الرَّسُولَ حَقٌّ وَجَاءَهُمُ الْبَيِّنَاتُ ۚ وَاللَّهُ لَا يَهْدِي الْقَوْمَ الظَّالِمِينَ (86)
Kodi Mulungu adzatsogolera bwanji anthu amene anakana pambuyo pokhulupilira pamene iwo anachitira umboni woti Mtumwi ndi woona ndiponso zizindikiro zooneka zitadza kwa iwo? Ndithudi Mulungu satsogolera anthu ochita zoipa
أُولَٰئِكَ جَزَاؤُهُمْ أَنَّ عَلَيْهِمْ لَعْنَةَ اللَّهِ وَالْمَلَائِكَةِ وَالنَّاسِ أَجْمَعِينَ (87)
Iwo malipiro awo, ndithudi, ndi matemberero ochokera kwa Mulungu, angelo ndi anthu onse
خَالِدِينَ فِيهَا لَا يُخَفَّفُ عَنْهُمُ الْعَذَابُ وَلَا هُمْ يُنظَرُونَ (88)
Iwo adzakhala m’menemo mpaka kalekale. Chilango chawo sichidzachepetsedwa ayi kapena kuchedwetsedwa
إِلَّا الَّذِينَ تَابُوا مِن بَعْدِ ذَٰلِكَ وَأَصْلَحُوا فَإِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (89)
Kupatula okhawo amene pambuyo pake alapa machimo awo ndi kuchita nchito zabwino. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا بَعْدَ إِيمَانِهِمْ ثُمَّ ازْدَادُوا كُفْرًا لَّن تُقْبَلَ تَوْبَتُهُمْ وَأُولَٰئِكَ هُمُ الضَّالُّونَ (90)
Ndithudi iwo amene adakana atayamba akhulupirira ndipo anapitiliza kusakhulupilira kwawo, kulapa kwawo sikudzavomerezeka. Ndipo iwo ndi osochera
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا وَمَاتُوا وَهُمْ كُفَّارٌ فَلَن يُقْبَلَ مِنْ أَحَدِهِم مِّلْءُ الْأَرْضِ ذَهَبًا وَلَوِ افْتَدَىٰ بِهِ ۗ أُولَٰئِكَ لَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ وَمَا لَهُم مِّن نَّاصِرِينَ (91)
Ndithudi iwo amene sanakhulupirire, ndipo akufa ali osakhulupirira, machimo awo sadzakhululukidwa ngakhale atapereka golide wodzadza dziko lonse lapansi ngati chodziombolera. Kwa otero, chilango chowawa chili kuwadikira ndipo iwo sadzapeza aliyense owathandiza
لَن تَنَالُوا الْبِرَّ حَتَّىٰ تُنفِقُوا مِمَّا تُحِبُّونَ ۚ وَمَا تُنفِقُوا مِن شَيْءٍ فَإِنَّ اللَّهَ بِهِ عَلِيمٌ (92)
Inu simudzapeza ubwino mpaka mutapereka zimene mumazikonda kwambiri ndipo zopereka zonse zimene mupereka, ndithudi Mulungu amazidziwa bwino
۞ كُلُّ الطَّعَامِ كَانَ حِلًّا لِّبَنِي إِسْرَائِيلَ إِلَّا مَا حَرَّمَ إِسْرَائِيلُ عَلَىٰ نَفْسِهِ مِن قَبْلِ أَن تُنَزَّلَ التَّوْرَاةُ ۗ قُلْ فَأْتُوا بِالتَّوْرَاةِ فَاتْلُوهَا إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (93)
Chakudya chonse chidali chololedwa kwa ana Israyeli kupatula zimene Israyeli adadziletsa yekha Buku la Chipangano chakale lisanavumbulutsidwe. Nena: “Bweretsani Buku la Chipangano chakale ndipo liwerengeni ngati zimene munena ndi zoona.”
فَمَنِ افْتَرَىٰ عَلَى اللَّهِ الْكَذِبَ مِن بَعْدِ ذَٰلِكَ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الظَّالِمُونَ (94)
Ndipo zitachitika izi, aliyense amene ampekera bodza Mulungu, otere ndi osakhulupilira
قُلْ صَدَقَ اللَّهُ ۗ فَاتَّبِعُوا مِلَّةَ إِبْرَاهِيمَ حَنِيفًا وَمَا كَانَ مِنَ الْمُشْرِكِينَ (95)
Nena: “Mulungu wanena choonadi motero tsatirani chipembedzo cha Abrahamu wangwiro ndipo iye sadali mmodzi wa anthu opembeza mafano.”
إِنَّ أَوَّلَ بَيْتٍ وُضِعَ لِلنَّاسِ لَلَّذِي بِبَكَّةَ مُبَارَكًا وَهُدًى لِّلْعَالَمِينَ (96)
Ndithudi Nyumba yoyamba kuti anthu azipembedzeramo ndi ija imene idali ku Mecca, yodzadza ndi madalitso, ndi malangizo kwa anthu a mitundu yonse
فِيهِ آيَاتٌ بَيِّنَاتٌ مَّقَامُ إِبْرَاهِيمَ ۖ وَمَن دَخَلَهُ كَانَ آمِنًا ۗ وَلِلَّهِ عَلَى النَّاسِ حِجُّ الْبَيْتِ مَنِ اسْتَطَاعَ إِلَيْهِ سَبِيلًا ۚ وَمَن كَفَرَ فَإِنَّ اللَّهَ غَنِيٌّ عَنِ الْعَالَمِينَ (97)
M’menemo muli zizindikiro zooneka, malo a Abrahamu ndipo aliyense amene alowamo ndi otetezedwa. Kupita ku Hajji ndi udindo umene anthu ayenera kukwaniritsa kwa Mulungu makamaka iwo amene ali ndi chuma. Ndipo aliyense amene sakhulupirira, Mulungu safuna chithandizo cha zolengedwa zake
قُلْ يَا أَهْلَ الْكِتَابِ لِمَ تَكْفُرُونَ بِآيَاتِ اللَّهِ وَاللَّهُ شَهِيدٌ عَلَىٰ مَا تَعْمَلُونَ (98)
Nena: “Inu anthu a m’Buku! Kodi bwanji mumakana chivumbulutso cha Mulungu pamene Mulungu amaona yekha zochita zanu zonse?”
قُلْ يَا أَهْلَ الْكِتَابِ لِمَ تَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ اللَّهِ مَنْ آمَنَ تَبْغُونَهَا عِوَجًا وَأَنتُمْ شُهَدَاءُ ۗ وَمَا اللَّهُ بِغَافِلٍ عَمَّا تَعْمَلُونَ (99)
Nena: “Inu anthu a m’Buku. Kodi bwanji mumatsekereza anthu amene akhulupirira kutsatira njira ya Mulungu ndipo mumafuna kusokoneza pamene inu mudziwa kuti ndi yoyenera? Ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita.”
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِن تُطِيعُوا فَرِيقًا مِّنَ الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ يَرُدُّوكُم بَعْدَ إِيمَانِكُمْ كَافِرِينَ (100)
Oh Inu anthu okhulupirira! Ngati inu mumvera anthu amene anapatsidwa Buku kale iwo adzakubwezerani kukhala osakhulupirira pamene munali okhulupirira
وَكَيْفَ تَكْفُرُونَ وَأَنتُمْ تُتْلَىٰ عَلَيْكُمْ آيَاتُ اللَّهِ وَفِيكُمْ رَسُولُهُ ۗ وَمَن يَعْتَصِم بِاللَّهِ فَقَدْ هُدِيَ إِلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (101)
Kodi simungakhulupirire bwanji pamene mau a Mulungu ali kulakatulidwa kwa inu ndipo Mtumwi wake ali pakati panu? Ndipo aliyense amene akakamira Mulungu, ndithudi iye watsogozedwa m’njira yoyenera
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا اتَّقُوا اللَّهَ حَقَّ تُقَاتِهِ وَلَا تَمُوتُنَّ إِلَّا وَأَنتُم مُّسْلِمُونَ (102)
oh inu anthu okhulupirira! Muopeni Mulungu monga momwe ayenera kuopedwera. Musafe pokha pokha muli Asilamu
وَاعْتَصِمُوا بِحَبْلِ اللَّهِ جَمِيعًا وَلَا تَفَرَّقُوا ۚ وَاذْكُرُوا نِعْمَتَ اللَّهِ عَلَيْكُمْ إِذْ كُنتُمْ أَعْدَاءً فَأَلَّفَ بَيْنَ قُلُوبِكُمْ فَأَصْبَحْتُم بِنِعْمَتِهِ إِخْوَانًا وَكُنتُمْ عَلَىٰ شَفَا حُفْرَةٍ مِّنَ النَّارِ فَأَنقَذَكُم مِّنْهَا ۗ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ اللَّهُ لَكُمْ آيَاتِهِ لَعَلَّكُمْ تَهْتَدُونَ (103)
Ndipo gwiritsani nonsenu, chingwe cha Mulungu ndipo musagawikane. Kumbukirani zokoma zimene Mulungu wakuchitirani chifukwa mudali mdani wa wina ndi mnzake ndipo Iye adayanjanitsa mitima yanu, ndipo chifukwa cha chisomo chake, muli achibale; ndipo inu mudali m’mphepete mwadzenje la moto koma Iye adakupulumutsani ku motowo. Motero Mulungu ali kufotokoza momveka zizindikiro zake kwa inu, kuti mukhale otsogozedwa
وَلْتَكُن مِّنكُمْ أُمَّةٌ يَدْعُونَ إِلَى الْخَيْرِ وَيَأْمُرُونَ بِالْمَعْرُوفِ وَيَنْهَوْنَ عَنِ الْمُنكَرِ ۚ وَأُولَٰئِكَ هُمُ الْمُفْلِحُونَ (104)
Pakati panu payenera kukhala gulu la anthu limene liziitanira ndi kumalamulira zabwino ndi kuletsa zinthu zoipa. Ndipo ndi iwo amene ali opambana
وَلَا تَكُونُوا كَالَّذِينَ تَفَرَّقُوا وَاخْتَلَفُوا مِن بَعْدِ مَا جَاءَهُمُ الْبَيِّنَاتُ ۚ وَأُولَٰئِكَ لَهُمْ عَذَابٌ عَظِيمٌ (105)
Ndipo musakhalengatiiwoameneanagawanikanandikusemphana maganizo pambuyo pakuti zizindikiro zooneka zidabwera kwa iwo. Ndi chifukwa cha iwo kuli chilango chowawa
يَوْمَ تَبْيَضُّ وُجُوهٌ وَتَسْوَدُّ وُجُوهٌ ۚ فَأَمَّا الَّذِينَ اسْوَدَّتْ وُجُوهُهُمْ أَكَفَرْتُم بَعْدَ إِيمَانِكُمْ فَذُوقُوا الْعَذَابَ بِمَا كُنتُمْ تَكْفُرُونَ (106)
Patsiku limene nkhope zina zidzakhala zowala ndi za chimwemwe pamene zina zidzakhala za kuda.Anthu amene adzakhala ndi nkhope zakuda adzafunsidwa kuti: “Kodi inu mudakana chikhulupiriro mutachivomera poyamba? Motero lawani chilango, chifukwa chokana kukhulupilira.”
وَأَمَّا الَّذِينَ ابْيَضَّتْ وُجُوهُهُمْ فَفِي رَحْمَةِ اللَّهِ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (107)
Iwo amene nkhope zawo zidzakhala zowala, adzakhala, mpaka kalekale, m’chisomo cha Mulungu
تِلْكَ آيَاتُ اللَّهِ نَتْلُوهَا عَلَيْكَ بِالْحَقِّ ۗ وَمَا اللَّهُ يُرِيدُ ظُلْمًا لِّلْعَالَمِينَ (108)
Awa ndi Mau a Mulungu. Ife tili kuwalakatula kwa iwe mwachoonadi ndipo Mulungu safuna kupondereza zolengedwa zake
وَلِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۚ وَإِلَى اللَّهِ تُرْجَعُ الْأُمُورُ (109)
Zake ndi zinthu zonse zimene zili kumwamba ndi padziko lapansi. Ndipo kwa Iye zinthu zonse zidzabwerera
كُنتُمْ خَيْرَ أُمَّةٍ أُخْرِجَتْ لِلنَّاسِ تَأْمُرُونَ بِالْمَعْرُوفِ وَتَنْهَوْنَ عَنِ الْمُنكَرِ وَتُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ ۗ وَلَوْ آمَنَ أَهْلُ الْكِتَابِ لَكَانَ خَيْرًا لَّهُم ۚ مِّنْهُمُ الْمُؤْمِنُونَ وَأَكْثَرُهُمُ الْفَاسِقُونَ (110)
Inu ndinu anthu abwino amene adalengedwera mtundu wa anthu, inu mumalamulira kuchita zabwino ndi kuletsa zoipa ndipo mumakhulupilira mwa Mulungu. Ndipo anthu a m’Buku akadakhulupilira, zikadawakhalira bwino. Pakati pawo pali ena amene ali ndi chikhulupiliro, koma ambiri a iwo ndi ochita zoipa
لَن يَضُرُّوكُمْ إِلَّا أَذًى ۖ وَإِن يُقَاتِلُوكُمْ يُوَلُّوكُمُ الْأَدْبَارَ ثُمَّ لَا يُنصَرُونَ (111)
Iwo sangakupwetekeni ayi, kupatula kukuvutitsani kokha ndipo ngati iwo amenyana nanu iwo adzakuonetsani misana yawo ndipo sadzathandizidwa
ضُرِبَتْ عَلَيْهِمُ الذِّلَّةُ أَيْنَ مَا ثُقِفُوا إِلَّا بِحَبْلٍ مِّنَ اللَّهِ وَحَبْلٍ مِّنَ النَّاسِ وَبَاءُوا بِغَضَبٍ مِّنَ اللَّهِ وَضُرِبَتْ عَلَيْهِمُ الْمَسْكَنَةُ ۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ كَانُوا يَكْفُرُونَ بِآيَاتِ اللَّهِ وَيَقْتُلُونَ الْأَنبِيَاءَ بِغَيْرِ حَقٍّ ۚ ذَٰلِكَ بِمَا عَصَوا وَّكَانُوا يَعْتَدُونَ (112)
Iwo adzanyozedwa kulikonse kumene adzapezeke kupatula ngati atetezedwa ndi Mulungu ndi anthu. Mkwiyo wa Mulungu ukuyenera pa iwo. Ndipo manyazi adzakhazikitsidwa pa iwo. Ichi ndi chifukwa chakuti iwo sadakhulupirire chivumbulutso cha Mulungu ndipo anapha Atumwi popanda chifukwa. Ichi ndi chifukwa chakuti adaswa malamulo mopyola muyeso
۞ لَيْسُوا سَوَاءً ۗ مِّنْ أَهْلِ الْكِتَابِ أُمَّةٌ قَائِمَةٌ يَتْلُونَ آيَاتِ اللَّهِ آنَاءَ اللَّيْلِ وَهُمْ يَسْجُدُونَ (113)
Onse sali chimodzimodzi. Gulu lina la anthu a m’Buku ndi anthu angwiro,iwo amawerenga Mawu a Mulungu nthawi ya usiku ndi kumagunditsa nkhope pansi
يُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ وَيَأْمُرُونَ بِالْمَعْرُوفِ وَيَنْهَوْنَ عَنِ الْمُنكَرِ وَيُسَارِعُونَ فِي الْخَيْرَاتِ وَأُولَٰئِكَ مِنَ الصَّالِحِينَ (114)
Iwo amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku la chimaliziro, amalamulira zolungama ndi kuletsa zoipa ndipo amakhala ndi changu pochita ntchito zabwino,ndipo iwo ali pamodzi ndi anthu olungama
وَمَا يَفْعَلُوا مِنْ خَيْرٍ فَلَن يُكْفَرُوهُ ۗ وَاللَّهُ عَلِيمٌ بِالْمُتَّقِينَ (115)
Ndipo chabwino chilichonse chimene achita, palibe chimene chidzakanidwa chifukwa Mulungu amadziwa anthu olungama
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا لَن تُغْنِيَ عَنْهُمْ أَمْوَالُهُمْ وَلَا أَوْلَادُهُم مِّنَ اللَّهِ شَيْئًا ۖ وَأُولَٰئِكَ أَصْحَابُ النَّارِ ۚ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (116)
Ndithudi iwo amene amakana kukhulupirira, chuma chawo ndi ana awo sadzawathandiza ngakhale ndi pang’ono pomwe polimbana ndi Mulungu. Iwo ndiwo eni ake a ku Gahena ndipo adzakhala komweko mpaka kalekale
مَثَلُ مَا يُنفِقُونَ فِي هَٰذِهِ الْحَيَاةِ الدُّنْيَا كَمَثَلِ رِيحٍ فِيهَا صِرٌّ أَصَابَتْ حَرْثَ قَوْمٍ ظَلَمُوا أَنفُسَهُمْ فَأَهْلَكَتْهُ ۚ وَمَا ظَلَمَهُمُ اللَّهُ وَلَٰكِنْ أَنفُسَهُمْ يَظْلِمُونَ (117)
Fanizo la zimene amapereka mu umoyo wa m’dziko lino zili ngati mphepo ya chisanu imene imagwa m’minda ya anthu ochita zoipa ndi kuiononga. Mulungu sadawalakwire ayi koma iwo adadzilakwira okha
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَتَّخِذُوا بِطَانَةً مِّن دُونِكُمْ لَا يَأْلُونَكُمْ خَبَالًا وَدُّوا مَا عَنِتُّمْ قَدْ بَدَتِ الْبَغْضَاءُ مِنْ أَفْوَاهِهِمْ وَمَا تُخْفِي صُدُورُهُمْ أَكْبَرُ ۚ قَدْ بَيَّنَّا لَكُمُ الْآيَاتِ ۖ إِن كُنتُمْ تَعْقِلُونَ (118)
Oh inu anthu okhulupirira! Musapalane ubwenzi ndi anthu ena kupatula anthu a chipembedzo chanu. Iwo sadzasiya kukuchitirani zoipa chifukwa iwo afuna kukuonongani. Chidani chawo ndi chooneka chifukwa cha zimene amanena koma zimene zimabisala m’mitima mwawo ndi zoopsya. Ndithudi ife taonetsa zizindikiro zathu poyera kwa inu ngati muli ndi nzeru
هَا أَنتُمْ أُولَاءِ تُحِبُّونَهُمْ وَلَا يُحِبُّونَكُمْ وَتُؤْمِنُونَ بِالْكِتَابِ كُلِّهِ وَإِذَا لَقُوكُمْ قَالُوا آمَنَّا وَإِذَا خَلَوْا عَضُّوا عَلَيْكُمُ الْأَنَامِلَ مِنَ الْغَيْظِ ۚ قُلْ مُوتُوا بِغَيْظِكُمْ ۗ إِنَّ اللَّهَ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (119)
Iyayi! Ndinu amene muli kuwakonda iwo koma iwo sakukondani inu ayi ngakhale inu mumakhulupirira mu Mabuku onse. Pamene akumana nanu iwo amati: “Nafenso ndife okhulupirira.” Koma akakhala paokha, amaluma nsonga za zala zawo mokwiya. Nena: “Ifani ndi mkwiyo wanu! Ndithu Mulungu amadziwa zimene zili m’mitima mwanu.”
إِن تَمْسَسْكُمْ حَسَنَةٌ تَسُؤْهُمْ وَإِن تُصِبْكُمْ سَيِّئَةٌ يَفْرَحُوا بِهَا ۖ وَإِن تَصْبِرُوا وَتَتَّقُوا لَا يَضُرُّكُمْ كَيْدُهُمْ شَيْئًا ۗ إِنَّ اللَّهَ بِمَا يَعْمَلُونَ مُحِيطٌ (120)
Ngati inu mupeza bwino, iwo amadandaula, koma ngati zovuta zikugwerani, iwo amasangalala. Koma ngati inu mupirira ndi kudziteteza kumachimo, ziwembu zawo sizidzakuonongani ayi. Ndithudi Mulungu amadziwa zochita zawo zonse
وَإِذْ غَدَوْتَ مِنْ أَهْلِكَ تُبَوِّئُ الْمُؤْمِنِينَ مَقَاعِدَ لِلْقِتَالِ ۗ وَاللَّهُ سَمِيعٌ عَلِيمٌ (121)
Ndi pamene iwe udasiya abale ako m’mawa kukayika anthu okhulupirira ku malo omenyera nkhondo. Mulungu ndi wakumva ndi wodziwa
إِذْ هَمَّت طَّائِفَتَانِ مِنكُمْ أَن تَفْشَلَا وَاللَّهُ وَلِيُّهُمَا ۗ وَعَلَى اللَّهِ فَلْيَتَوَكَّلِ الْمُؤْمِنُونَ (122)
Pamene magulu anu awiri adali ndi mantha koma Mulungu adali Mtetezi wawo. Ndipo mwa Mulungu anthu okhulupirira ayenera kuika chikhulupiliro chawo
وَلَقَدْ نَصَرَكُمُ اللَّهُ بِبَدْرٍ وَأَنتُمْ أَذِلَّةٌ ۖ فَاتَّقُوا اللَّهَ لَعَلَّكُمْ تَشْكُرُونَ (123)
Mulungu adakupambanitsani pa nkhondo ya ku Badr pamene inu mudali ofoka. Choncho opani Mulungu kwambiri kuti mukhale othokoza
إِذْ تَقُولُ لِلْمُؤْمِنِينَ أَلَن يَكْفِيَكُمْ أَن يُمِدَّكُمْ رَبُّكُم بِثَلَاثَةِ آلَافٍ مِّنَ الْمَلَائِكَةِ مُنزَلِينَ (124)
Pamene iwe udanena kwa anthu okhulupirira: “Kodi simunakhutitsidwe pamene Ambuye anakuthandizani ndi angelo zikwi zitatu amene adatsitsidwa kuchokera kumwamba kuti akuthandizeni?”
بَلَىٰ ۚ إِن تَصْبِرُوا وَتَتَّقُوا وَيَأْتُوكُم مِّن فَوْرِهِمْ هَٰذَا يُمْدِدْكُمْ رَبُّكُم بِخَمْسَةِ آلَافٍ مِّنَ الْمَلَائِكَةِ مُسَوِّمِينَ (125)
“Inde, ngati inu mupirira ndi kukhala angwiro ndipo pamene mdani adza mofulumira kwa inu, Ambuye wanu adzakuthandizani ndi angelo zikwi zisanu a zizindikiro.”
وَمَا جَعَلَهُ اللَّهُ إِلَّا بُشْرَىٰ لَكُمْ وَلِتَطْمَئِنَّ قُلُوبُكُم بِهِ ۗ وَمَا النَّصْرُ إِلَّا مِنْ عِندِ اللَّهِ الْعَزِيزِ الْحَكِيمِ (126)
Mulungu adakonza ichi kuti chikhale nkhani yabwino kwa inu kuti mitima yanu ikhazikike. Kupambana sikuchokera kwa wina aliyense koma Mulungu, Mwini mphamvu ndi Mwini nzeru zonse
لِيَقْطَعَ طَرَفًا مِّنَ الَّذِينَ كَفَرُوا أَوْ يَكْبِتَهُمْ فَيَنقَلِبُوا خَائِبِينَ (127)
Kuti Iye akhoza kumwaza gulu la anthu osakhulupirira kapena kuwanyoza kuti akhoza kumwazikana
لَيْسَ لَكَ مِنَ الْأَمْرِ شَيْءٌ أَوْ يَتُوبَ عَلَيْهِمْ أَوْ يُعَذِّبَهُمْ فَإِنَّهُمْ ظَالِمُونَ (128)
Iwe ulibe lamulo lililonse munkhani iyi. Kaya Iye adzawakhululukira kapena kuwalanga, ndithudi iwo ndi anthu ochita zoipa
وَلِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۚ يَغْفِرُ لِمَن يَشَاءُ وَيُعَذِّبُ مَن يَشَاءُ ۚ وَاللَّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (129)
Zake za Mulungu ndi zinthu zonse zimene zili kumwamba ndi padziko lapansi. Iye amakhululukira aliyense amene wamufuna ndi kulanga aliyense amene wamufuna. Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَأْكُلُوا الرِّبَا أَضْعَافًا مُّضَاعَفَةً ۖ وَاتَّقُوا اللَّهَ لَعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ (130)
Oh inu anthu okhulupirira! Musadye ndalama za katapila musachulukitse ndalama motero, ndipo opani Mulungu kuti inu mupambane
وَاتَّقُوا النَّارَ الَّتِي أُعِدَّتْ لِلْكَافِرِينَ (131)
Ndipo opani Moto wa ku Gahena, umene wakonzedwera anthu osakhulupirira
وَأَطِيعُوا اللَّهَ وَالرَّسُولَ لَعَلَّكُمْ تُرْحَمُونَ (132)
Ndipo mverani Mulungu ndi Mtumwi wake kuti mupeze chifundo chake
۞ وَسَارِعُوا إِلَىٰ مَغْفِرَةٍ مِّن رَّبِّكُمْ وَجَنَّةٍ عَرْضُهَا السَّمَاوَاتُ وَالْأَرْضُ أُعِدَّتْ لِلْمُتَّقِينَ (133)
Ndipo fulumirani kukapeza chikhululukiro cha Ambuye wanu ndi Paradiso imene kutambasuka kwake kuli ngati kumwamba ndi dziko lapansi, yokonzedwera anthu oopa Mulungu
الَّذِينَ يُنفِقُونَ فِي السَّرَّاءِ وَالضَّرَّاءِ وَالْكَاظِمِينَ الْغَيْظَ وَالْعَافِينَ عَنِ النَّاسِ ۗ وَاللَّهُ يُحِبُّ الْمُحْسِنِينَ (134)
Amene amapereka mu mtendere kapena m’mavuto, ndipo amaleza mtima akakwiya ndipo amakhululukira anthu. Ndithudi Mulungu amakonda anthu ochita zabwino
وَالَّذِينَ إِذَا فَعَلُوا فَاحِشَةً أَوْ ظَلَمُوا أَنفُسَهُمْ ذَكَرُوا اللَّهَ فَاسْتَغْفَرُوا لِذُنُوبِهِمْ وَمَن يَغْفِرُ الذُّنُوبَ إِلَّا اللَّهُ وَلَمْ يُصِرُّوا عَلَىٰ مَا فَعَلُوا وَهُمْ يَعْلَمُونَ (135)
Ndi iwo amene, ngatiachitachigololokapenaalakwiramizimuyawo, amakumbukira Mulungu ndi kupempha chikhululukiro cha machimo awo, ndipo palibe wina amene angakhululukire machimo kupatula Mulungu, ndipo sapitiliza kuchita zoipa pamene iwo ali nkudziwa
أُولَٰئِكَ جَزَاؤُهُم مَّغْفِرَةٌ مِّن رَّبِّهِمْ وَجَنَّاتٌ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا ۚ وَنِعْمَ أَجْرُ الْعَامِلِينَ (136)
Kwa otere, malipiro awo ndi chikhululukiro chochokera kwa Ambuye wawo ndi minda yothiriridwa ndi mitsinje yoyenda pansi pake kumene iwo adzakhalako mpaka kalekale. Dipo la bwino kwa iwo amene amachita ntchito zabwino
قَدْ خَلَتْ مِن قَبْلِكُمْ سُنَنٌ فَسِيرُوا فِي الْأَرْضِ فَانظُرُوا كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الْمُكَذِّبِينَ (137)
Anthu akale nawo anaona mavuto otere. Motero inu yendani padziko lapansi ndipo muone chimene chidawachitikira anthu osakhulupirira
هَٰذَا بَيَانٌ لِّلنَّاسِ وَهُدًى وَمَوْعِظَةٌ لِّلْمُتَّقِينَ (138)
Awa ndi mawu omveka kwa anthu, chilangizo ndi chenjezo kwa iwo amene amalewa zoipa
وَلَا تَهِنُوا وَلَا تَحْزَنُوا وَأَنتُمُ الْأَعْلَوْنَ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ (139)
Motero musagwe ulesi kapena kudandaula, inu mudzapambana, ngati ndinu okhulupirira
إِن يَمْسَسْكُمْ قَرْحٌ فَقَدْ مَسَّ الْقَوْمَ قَرْحٌ مِّثْلُهُ ۚ وَتِلْكَ الْأَيَّامُ نُدَاوِلُهَا بَيْنَ النَّاسِ وَلِيَعْلَمَ اللَّهُ الَّذِينَ آمَنُوا وَيَتَّخِذَ مِنكُمْ شُهَدَاءَ ۗ وَاللَّهُ لَا يُحِبُّ الظَّالِمِينَ (140)
Ngati inu muvulala, zindikirani kuti ena nawo adavulala. Ndipo masiku sakoma onse ndipo Ife timapereka kwa anthu mwakasintha sintha kuti Mulungu ayese iwo amene akhulupirira ndipo kuti akhoza kupha ena kuchokera ku magulu anu. Ndipo Mulungu sakonda iwo amene amachita zoipa
وَلِيُمَحِّصَ اللَّهُ الَّذِينَ آمَنُوا وَيَمْحَقَ الْكَافِرِينَ (141)
Ndi kuti Mulungu ayeretse anthu okhulupirira ndi kuononga anthu osakhulupirira
أَمْ حَسِبْتُمْ أَن تَدْخُلُوا الْجَنَّةَ وَلَمَّا يَعْلَمِ اللَّهُ الَّذِينَ جَاهَدُوا مِنكُمْ وَيَعْلَمَ الصَّابِرِينَ (142)
Kodi inu mumaganiza kuti mukalowa ku Paradiso Mulungu asanadziwe anthu amene anamenya nkhondo m’njira ya Mulungu ndikuwadziwa amene anapirira
وَلَقَدْ كُنتُمْ تَمَنَّوْنَ الْمَوْتَ مِن قَبْلِ أَن تَلْقَوْهُ فَقَدْ رَأَيْتُمُوهُ وَأَنتُمْ تَنظُرُونَ (143)
Inu, ndithudi, munali kufuna imfa musadakumane nayo. Ndipo tsopano mwaiona mmene imakhalira ndi maso anu
وَمَا مُحَمَّدٌ إِلَّا رَسُولٌ قَدْ خَلَتْ مِن قَبْلِهِ الرُّسُلُ ۚ أَفَإِن مَّاتَ أَوْ قُتِلَ انقَلَبْتُمْ عَلَىٰ أَعْقَابِكُمْ ۚ وَمَن يَنقَلِبْ عَلَىٰ عَقِبَيْهِ فَلَن يَضُرَّ اللَّهَ شَيْئًا ۗ وَسَيَجْزِي اللَّهُ الشَّاكِرِينَ (144)
Muhammad siwina aliyense koma Mtumwi ndipo, ndithudi, Atumwi ena adalipo kale iye asanadze. Ngati iye akufa kapena aphedwa, kodi inu mudzabwerera m’mbuyo? Yense amene abwerera m’mbuyo sadzachita chilichonse chopweteka Mulungu ndipo Mulungu adzalipira anthu oyamika
وَمَا كَانَ لِنَفْسٍ أَن تَمُوتَ إِلَّا بِإِذْنِ اللَّهِ كِتَابًا مُّؤَجَّلًا ۗ وَمَن يُرِدْ ثَوَابَ الدُّنْيَا نُؤْتِهِ مِنْهَا وَمَن يُرِدْ ثَوَابَ الْآخِرَةِ نُؤْتِهِ مِنْهَا ۚ وَسَنَجْزِي الشَّاكِرِينَ (145)
Ndipo palibe amene amafa kupatula ndi chilolezo cha Mulungu ndi pa nthawi yokhazikitsidwa kale. Ndipo iye amene afuna malipiro a m’dziko lino, Ife tidzamupatsa ndipo iye amene afuna malipiro a m’moyo umene uli nkudza Ife tidzamupatsa. Ndipo Ife tidzalipira anthu othokoza
وَكَأَيِّن مِّن نَّبِيٍّ قَاتَلَ مَعَهُ رِبِّيُّونَ كَثِيرٌ فَمَا وَهَنُوا لِمَا أَصَابَهُمْ فِي سَبِيلِ اللَّهِ وَمَا ضَعُفُوا وَمَا اسْتَكَانُوا ۗ وَاللَّهُ يُحِبُّ الصَّابِرِينَ (146)
Ndi Atumwi ambiri amene adamenya nkhondo ndipo pamodzi ndi iye panali anthu ambiri odziwa chipembedzo. Koma iwo sadataye mtima chifukwa cha zimene zidagwa pa iwo m’njira ya Mulungu kapena kufoka ayi kapena kudzinyoza. Ndipo Mulungu amakonda anthu opirira
وَمَا كَانَ قَوْلَهُمْ إِلَّا أَن قَالُوا رَبَّنَا اغْفِرْ لَنَا ذُنُوبَنَا وَإِسْرَافَنَا فِي أَمْرِنَا وَثَبِّتْ أَقْدَامَنَا وَانصُرْنَا عَلَى الْقَوْمِ الْكَافِرِينَ (147)
Ndipo iwo sadanene china koma kuti: “oh Ambuye! Tikhululukireni machimo athu ndi kuswa malamulo kwathu. Limbikitsani mapazi athu ndipo tipambanitseni kwa anthu osakhulupirira.”
فَآتَاهُمُ اللَّهُ ثَوَابَ الدُّنْيَا وَحُسْنَ ثَوَابِ الْآخِرَةِ ۗ وَاللَّهُ يُحِبُّ الْمُحْسِنِينَ (148)
Motero Mulungu adawapatsa mphotho ya m’moyo uno ndi mphotho yolemekezeka ya m’moyo umene uli nkudza. Mulungu amakonda anthu olungama
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِن تُطِيعُوا الَّذِينَ كَفَرُوا يَرُدُّوكُمْ عَلَىٰ أَعْقَابِكُمْ فَتَنقَلِبُوا خَاسِرِينَ (149)
Oh inu anthu okhulupirira! Ngati inu mumvera anthu osakhulupilira iwo adzakupangani kukhala osakhulupirira ndipo mudzabwerera ngati otaika
بَلِ اللَّهُ مَوْلَاكُمْ ۖ وَهُوَ خَيْرُ النَّاصِرِينَ (150)
Iyayi, Mulungu ndiye Mtetezi wanu, ndipo Iye ndiye wothandiza kupambana wina aliyense
سَنُلْقِي فِي قُلُوبِ الَّذِينَ كَفَرُوا الرُّعْبَ بِمَا أَشْرَكُوا بِاللَّهِ مَا لَمْ يُنَزِّلْ بِهِ سُلْطَانًا ۖ وَمَأْوَاهُمُ النَّارُ ۚ وَبِئْسَ مَثْوَى الظَّالِمِينَ (151)
Ife tidzaika mantha m’mitima ya anthu osakhulupirira chifukwa amatumikira milungu ina yowojezera pa Mulungu imene iwo sadalandire chilolezo choti azitumikira. Moto udzakhala mudzi wawo. Ndithu onyansa kwambiri ndi malo amene anthu ochita zoipa akakhalako
وَلَقَدْ صَدَقَكُمُ اللَّهُ وَعْدَهُ إِذْ تَحُسُّونَهُم بِإِذْنِهِ ۖ حَتَّىٰ إِذَا فَشِلْتُمْ وَتَنَازَعْتُمْ فِي الْأَمْرِ وَعَصَيْتُم مِّن بَعْدِ مَا أَرَاكُم مَّا تُحِبُّونَ ۚ مِنكُم مَّن يُرِيدُ الدُّنْيَا وَمِنكُم مَّن يُرِيدُ الْآخِرَةَ ۚ ثُمَّ صَرَفَكُمْ عَنْهُمْ لِيَبْتَلِيَكُمْ ۖ وَلَقَدْ عَفَا عَنكُمْ ۗ وَاللَّهُ ذُو فَضْلٍ عَلَى الْمُؤْمِنِينَ (152)
Ndipo Mulungu, ndithudi, adakwaniritsa lonjezo lake kwa inu pamene inu munali kuwapha ndi chilolezo chake mpaka pamene munafooka ndipo mudayamba kukangana ndipo simunamvere Iye atakulangizani chimene mukonda. Pakati panu pali iwo amene amafuna moyo wa m’mdziko lapansi ndi ena amene afuna moyo umene uli nkudza. Ndipo Iye adakonza kuti muthawe kuti Iye akhoza kukuyesani. Koma, ndithudi, Iye adakukhululukirani inu ndipo Mulungu amaonetsa chifundo kwa anthu okhulupirira
۞ إِذْ تُصْعِدُونَ وَلَا تَلْوُونَ عَلَىٰ أَحَدٍ وَالرَّسُولُ يَدْعُوكُمْ فِي أُخْرَاكُمْ فَأَثَابَكُمْ غَمًّا بِغَمٍّ لِّكَيْلَا تَحْزَنُوا عَلَىٰ مَا فَاتَكُمْ وَلَا مَا أَصَابَكُمْ ۗ وَاللَّهُ خَبِيرٌ بِمَا تَعْمَلُونَ (153)
Pamene inu mudathawa osaona kumbali kwa wina aliyense ndipo Mtumwi adali m’mbuyo mwanu kukuitanani. Pamenepo Mulungu anakupatsani vuto powonjezera pa vuto lina ngati kubwezera ndi cholinga chokuphunzitsani inu kuti musamve chisoni pa zimene simunazipeze kapena zimene zinadza kwa inu. Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita
ثُمَّ أَنزَلَ عَلَيْكُم مِّن بَعْدِ الْغَمِّ أَمَنَةً نُّعَاسًا يَغْشَىٰ طَائِفَةً مِّنكُمْ ۖ وَطَائِفَةٌ قَدْ أَهَمَّتْهُمْ أَنفُسُهُمْ يَظُنُّونَ بِاللَّهِ غَيْرَ الْحَقِّ ظَنَّ الْجَاهِلِيَّةِ ۖ يَقُولُونَ هَل لَّنَا مِنَ الْأَمْرِ مِن شَيْءٍ ۗ قُلْ إِنَّ الْأَمْرَ كُلَّهُ لِلَّهِ ۗ يُخْفُونَ فِي أَنفُسِهِم مَّا لَا يُبْدُونَ لَكَ ۖ يَقُولُونَ لَوْ كَانَ لَنَا مِنَ الْأَمْرِ شَيْءٌ مَّا قُتِلْنَا هَاهُنَا ۗ قُل لَّوْ كُنتُمْ فِي بُيُوتِكُمْ لَبَرَزَ الَّذِينَ كُتِبَ عَلَيْهِمُ الْقَتْلُ إِلَىٰ مَضَاجِعِهِمْ ۖ وَلِيَبْتَلِيَ اللَّهُ مَا فِي صُدُورِكُمْ وَلِيُمَحِّصَ مَا فِي قُلُوبِكُمْ ۗ وَاللَّهُ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (154)
Ndipo chitantha chisoni, adakutsitsirani mtendere kuti udze pa inu. Ndipo tulo tidagwira ena a inu pamene ena adangogona kumavutika m’maganizo, chifukwa cha zilakolako zawo, kuganiza mosalungama ndikukhala ndi maganizo a umbuli okhudza Mulungu. Iwo adafunsa: “Kodi ife tili ndi chonena pankhani iyi?” Nena: “Zonse zili m’manja mwa Mulungu.” Iwo amabisa m’mitima mwawo zinthu zimene safuna kuulula kwa iwe. Iwo amanena kuti: “Tikadakhala kuti tidaloledwa kunenapo maganizo athu pankhaniyi, ife sitikanaphedwa pano.” Nena: “Ngakhale inu mukadakhala kunyumba zanu ndithudi ena amene adalembedwa kuti aphedwe akadapita ku malo kumene akadakaphedwa.” Ndipo Mulungu adachita zimenezi kuti ayese zimene zili m’mitima mwanu ndi kuyeretsa zimene zili m’mitima mwanu ndipo ndithudi Mulungu akudziwa zimene zili m’mitima
إِنَّ الَّذِينَ تَوَلَّوْا مِنكُمْ يَوْمَ الْتَقَى الْجَمْعَانِ إِنَّمَا اسْتَزَلَّهُمُ الشَّيْطَانُ بِبَعْضِ مَا كَسَبُوا ۖ وَلَقَدْ عَفَا اللَّهُ عَنْهُمْ ۗ إِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ حَلِيمٌ (155)
Ena a inu amene mudathawa patsiku limene anthu a magulu awiri ankhondo adakumana, ndi Satana amene adawapangitsa kuti athawe zimene adachita. Zoonadi Mulungu adawakhululukira. Ndithudi Mulungu ndi okhululukira ndi wopilira kwambiri
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَكُونُوا كَالَّذِينَ كَفَرُوا وَقَالُوا لِإِخْوَانِهِمْ إِذَا ضَرَبُوا فِي الْأَرْضِ أَوْ كَانُوا غُزًّى لَّوْ كَانُوا عِندَنَا مَا مَاتُوا وَمَا قُتِلُوا لِيَجْعَلَ اللَّهُ ذَٰلِكَ حَسْرَةً فِي قُلُوبِهِمْ ۗ وَاللَّهُ يُحْيِي وَيُمِيتُ ۗ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌ (156)
oh inu anthu okhulupirira! Musakhale ngati osakhulupirira amene amanena kwa abale awo pamene ayenda padziko kapena apita kunkhondo: “Akadakhala kuti adali ndi ife kuno, iwo sakadafa ayi kapena sakadaphedwa.” Mulungu amatero kuti iwo adzakumbukire mawu awo. Ndi Mulunguameneamaperekamoyondiimfa. Ndipo Mulungu amaona ntchito zonse zimene mumachita
وَلَئِن قُتِلْتُمْ فِي سَبِيلِ اللَّهِ أَوْ مُتُّمْ لَمَغْفِرَةٌ مِّنَ اللَّهِ وَرَحْمَةٌ خَيْرٌ مِّمَّا يَجْمَعُونَ (157)
Ndipo ngati inu muphedwa kapena mukufa mnjira ya Mulungu, chikhululukiro ndi chifundo chochokera kwa Mulungu ndi chabwino kuposa chuma chimene akusonkhanitsa
وَلَئِن مُّتُّمْ أَوْ قُتِلْتُمْ لَإِلَى اللَّهِ تُحْشَرُونَ (158)
Ngati inu muphedwa kapena mufa, ndithudi ndi kwa Mulungu kumene nonse mudzasonkhanitsidwa
فَبِمَا رَحْمَةٍ مِّنَ اللَّهِ لِنتَ لَهُمْ ۖ وَلَوْ كُنتَ فَظًّا غَلِيظَ الْقَلْبِ لَانفَضُّوا مِنْ حَوْلِكَ ۖ فَاعْفُ عَنْهُمْ وَاسْتَغْفِرْ لَهُمْ وَشَاوِرْهُمْ فِي الْأَمْرِ ۖ فَإِذَا عَزَمْتَ فَتَوَكَّلْ عَلَى اللَّهِ ۚ إِنَّ اللَّهَ يُحِبُّ الْمُتَوَكِّلِينَ (159)
Ndi chifundo cha Mulungu iwe udakhala nawo mwa ufulu. Ndipo iwe ukadakhala wa nkhanza kapena owuma mtima, ndithudi onse akadakuthawira. Motero akhululukire ndipo pempha kuti awakhululukire ndipo kambirana nawo. Ndipo ukatsimikiza, ika chikhulupiriro chako mwa Mulungu. Ndithudi Mulungu amakonda iwo amene amaika chikhulupiliriro chawo mwa Iye
إِن يَنصُرْكُمُ اللَّهُ فَلَا غَالِبَ لَكُمْ ۖ وَإِن يَخْذُلْكُمْ فَمَن ذَا الَّذِي يَنصُرُكُم مِّن بَعْدِهِ ۗ وَعَلَى اللَّهِ فَلْيَتَوَكَّلِ الْمُؤْمِنُونَ (160)
Ngati Mulungu akuthandizani inu, palibe amene angakugonjetseni ndipo ngati Iye atakutayani, kodi ndani amene angakuthandizeni inu kupatula Iye yekha? Ndipo mwa Mulungu onse okhulupirira ayenera kuika chikhulupiriro chawo
وَمَا كَانَ لِنَبِيٍّ أَن يَغُلَّ ۚ وَمَن يَغْلُلْ يَأْتِ بِمَا غَلَّ يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۚ ثُمَّ تُوَفَّىٰ كُلُّ نَفْسٍ مَّا كَسَبَتْ وَهُمْ لَا يُظْلَمُونَ (161)
Ndikosaloledwa kuti Mtumwi wina aliyense atenge katundu wopeza munkhondo mopanda kulamulidwa ndipo aliyense amene anyenga omutsatira ake pa nkhani ya chuma chopeza ku nkhondo, adzanyamula patsiku louka kwa akufa zimene iye anatenga mopanda chilolezo. Ndipo munthu aliyense adzalipidwa molingana ndi zochita zake ndipo iwo sadzaponderezedwa ai
أَفَمَنِ اتَّبَعَ رِضْوَانَ اللَّهِ كَمَن بَاءَ بِسَخَطٍ مِّنَ اللَّهِ وَمَأْوَاهُ جَهَنَّمُ ۚ وَبِئْسَ الْمَصِيرُ (162)
Kodi munthu amene atsata zokondweretsa Mulungu angafanizidwe ndi munthu amene walandira mkwiyo wa Mulungu? Gahena idzakhala mudzi wake ndipo malo omwe adzakhalako ndi onyansa
هُمْ دَرَجَاتٌ عِندَ اللَّهِ ۗ وَاللَّهُ بَصِيرٌ بِمَا يَعْمَلُونَ (163)
Iwo ali m’magulu osiyana siyana pamaso pa Mulungu. Ndipo Mulungu ali kuona chili chonse chimene amachita
لَقَدْ مَنَّ اللَّهُ عَلَى الْمُؤْمِنِينَ إِذْ بَعَثَ فِيهِمْ رَسُولًا مِّنْ أَنفُسِهِمْ يَتْلُو عَلَيْهِمْ آيَاتِهِ وَيُزَكِّيهِمْ وَيُعَلِّمُهُمُ الْكِتَابَ وَالْحِكْمَةَ وَإِن كَانُوا مِن قَبْلُ لَفِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (164)
Ndithudi Mulungu anaika chisomo chake pa anthu okhulupirira pamene anatumiza pakati pawo Mtumwi wochokera pakati pawo kudzawawerengera chivumbulutso chake ndi kuwayeretsa ndi kuwaphunzitsa Buku ndi luntha; angakhale kuti iwo kale adali anthu osochera moonetsera
أَوَلَمَّا أَصَابَتْكُم مُّصِيبَةٌ قَدْ أَصَبْتُم مِّثْلَيْهَا قُلْتُمْ أَنَّىٰ هَٰذَا ۖ قُلْ هُوَ مِنْ عِندِ أَنفُسِكُمْ ۗ إِنَّ اللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (165)
Pamene mavuto adza pa inu ngakhale kuti inu mudapha anthu kwambiri, inu mudati: “Kodi zichokera kuti izi?” Nena: “Zimenezi zichokera kwa inu nomwe. Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse.”
وَمَا أَصَابَكُمْ يَوْمَ الْتَقَى الْجَمْعَانِ فَبِإِذْنِ اللَّهِ وَلِيَعْلَمَ الْمُؤْمِنِينَ (166)
Kugonjetsedwa kwanu, panthawi imene magulu awiri adakumana, kudalamulidwa ndi Mulungu ndi cholinga chakuti akhoza kuyesa anthu okhulupirira
وَلِيَعْلَمَ الَّذِينَ نَافَقُوا ۚ وَقِيلَ لَهُمْ تَعَالَوْا قَاتِلُوا فِي سَبِيلِ اللَّهِ أَوِ ادْفَعُوا ۖ قَالُوا لَوْ نَعْلَمُ قِتَالًا لَّاتَّبَعْنَاكُمْ ۗ هُمْ لِلْكُفْرِ يَوْمَئِذٍ أَقْرَبُ مِنْهُمْ لِلْإِيمَانِ ۚ يَقُولُونَ بِأَفْوَاهِهِم مَّا لَيْسَ فِي قُلُوبِهِمْ ۗ وَاللَّهُ أَعْلَمُ بِمَا يَكْتُمُونَ (167)
Ndipo kuti ayese anthu achinyengo ndipo iwo auzidwa kuti: “Bwerani kuti mumenye nkhondo mu njira ya Mulungu kapena kuti mudziteteze inu nokha.” Iwo adati: “Ngati ife tikadadziwa kuti kukhala nkhondo, ndithudi Ife tikadapita nanu.” Patsiku limeneli kusakhulupirira kwawo kudawayandikira kuposa chikhulupiriro. Iwo anali kunena ndi milomo yawo zinthu zomwe sizinali m’mitima yawo. Ndipo Mulungu amadziwa zimene iwo anali kubisa
الَّذِينَ قَالُوا لِإِخْوَانِهِمْ وَقَعَدُوا لَوْ أَطَاعُونَا مَا قُتِلُوا ۗ قُلْ فَادْرَءُوا عَنْ أَنفُسِكُمُ الْمَوْتَ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (168)
Iwondiameneadanenazaabaleawoameneanafapamene iwo anakhala osapita ku nkhondo: Iwo akadatimvera ife, sakadaphedwa ayi. Nena: “Dzichotsereni imfa imene ili pakati panu ngati zimene munena ndi zoona.”
وَلَا تَحْسَبَنَّ الَّذِينَ قُتِلُوا فِي سَبِيلِ اللَّهِ أَمْوَاتًا ۚ بَلْ أَحْيَاءٌ عِندَ رَبِّهِمْ يُرْزَقُونَ (169)
Inu musaganize kuti amene adaphedwa m’njira ya Mulungu adafa ayi. Iyayi, koma iwo ali ndi moyo ndipo amasamalidwa ndi Ambuye wawo ndipo ali ndi gawo lawo
فَرِحِينَ بِمَا آتَاهُمُ اللَّهُ مِن فَضْلِهِ وَيَسْتَبْشِرُونَ بِالَّذِينَ لَمْ يَلْحَقُوا بِهِم مِّنْ خَلْفِهِمْ أَلَّا خَوْفٌ عَلَيْهِمْ وَلَا هُمْ يَحْزَنُونَ (170)
Iwo amasangalala chifukwa cha zimene Mulungu wawapatsa mwa chisomo chake ndi chifukwa cha iwo amene sadalowe mgulu lawo ndipo anatsala m’mbuyo, ndipo iwo sadzakhala ndi mantha kapena kumva chisoni
۞ يَسْتَبْشِرُونَ بِنِعْمَةٍ مِّنَ اللَّهِ وَفَضْلٍ وَأَنَّ اللَّهَ لَا يُضِيعُ أَجْرَ الْمُؤْمِنِينَ (171)
Iwo amasangalala ndi chisomo ndi chuma chochokera kwa Mulungu ndipo kuti Mulungu sadzaononga malipiro a okhulupirira
الَّذِينَ اسْتَجَابُوا لِلَّهِ وَالرَّسُولِ مِن بَعْدِ مَا أَصَابَهُمُ الْقَرْحُ ۚ لِلَّذِينَ أَحْسَنُوا مِنْهُمْ وَاتَّقَوْا أَجْرٌ عَظِيمٌ (172)
Iwo amene adavomera kuitana kwa Mulungu ndi Mtumwi pamene atavulala ndi iwo amene amachita ntchito zabwino ndi kuopa Mulungu, adzalandira mphotho ya mtengo wapatali
الَّذِينَ قَالَ لَهُمُ النَّاسُ إِنَّ النَّاسَ قَدْ جَمَعُوا لَكُمْ فَاخْشَوْهُمْ فَزَادَهُمْ إِيمَانًا وَقَالُوا حَسْبُنَا اللَّهُ وَنِعْمَ الْوَكِيلُ (173)
Iwo amene anthu adati kwa iwo: “Ndithudi anthu asonkhanitsidwa kuti alimbane nanu, motero chitani mantha.” Koma izi zidangoonjezera chikhulupiriro chawo ndipo iwo adati: “Chithandizo cha Mulungu ndi chokwanira kwa ife chifukwa Iye ndiye Mtetezi wabwino.”
فَانقَلَبُوا بِنِعْمَةٍ مِّنَ اللَّهِ وَفَضْلٍ لَّمْ يَمْسَسْهُمْ سُوءٌ وَاتَّبَعُوا رِضْوَانَ اللَّهِ ۗ وَاللَّهُ ذُو فَضْلٍ عَظِيمٍ (174)
Ndipo iwo adabwerera ndi chisomo ndi zokoma zake za Mulungu. Ndipo padalibe choipa chimene chidawagwera iwo. Ndipo iwo adatsatira zomukondweretsa Mulungu. Ndipo Mulungu ndiye Mwini wa zokoma zazikulu zosatha
إِنَّمَا ذَٰلِكُمُ الشَّيْطَانُ يُخَوِّفُ أَوْلِيَاءَهُ فَلَا تَخَافُوهُمْ وَخَافُونِ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ (175)
Ndi Satana amene amakupangitsani kuti inu muziopa omutsatira ake. Musawaope iwo koma ndiopeni Ine ngati inu ndinu okhulupirira
وَلَا يَحْزُنكَ الَّذِينَ يُسَارِعُونَ فِي الْكُفْرِ ۚ إِنَّهُمْ لَن يَضُرُّوا اللَّهَ شَيْئًا ۗ يُرِيدُ اللَّهُ أَلَّا يَجْعَلَ لَهُمْ حَظًّا فِي الْآخِرَةِ ۖ وَلَهُمْ عَذَابٌ عَظِيمٌ (176)
Ndipo asakukhumudwitseni anthu amene amachita changu posakhulupirira. Ndithudi iwo sangachite chili chonse chomupweteka Mulungu. Ndi cholinga cha Mulungu kuti iwo asadzapatsidwe gawo lina lililonse m’moyo umene uli nkudza. Iwo ali ndi chilango chachikulu
إِنَّ الَّذِينَ اشْتَرَوُا الْكُفْرَ بِالْإِيمَانِ لَن يَضُرُّوا اللَّهَ شَيْئًا وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (177)
Ndithudi iwo amene amasinthitsa chikhulupiriro chawo posankha kusakhulupirira sadzachita china chili chonse chopweteka Mulungu ayi. Ndipo chilango chowawa chidzakhala pa iwo
وَلَا يَحْسَبَنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا أَنَّمَا نُمْلِي لَهُمْ خَيْرٌ لِّأَنفُسِهِمْ ۚ إِنَّمَا نُمْلِي لَهُمْ لِيَزْدَادُوا إِثْمًا ۚ وَلَهُمْ عَذَابٌ مُّهِينٌ (178)
Ndipo anthu osakhulupirira asaganize kuti Ife tili kuchedwetsa chilango chawo ndi cholinga chabwino kwa iwo. Ife tili kuchichedwetsa ndi cholinga chakuti apitilize kulakwa. Chilango chochititsa manyazi chili kuwayembekezera
مَّا كَانَ اللَّهُ لِيَذَرَ الْمُؤْمِنِينَ عَلَىٰ مَا أَنتُمْ عَلَيْهِ حَتَّىٰ يَمِيزَ الْخَبِيثَ مِنَ الطَّيِّبِ ۗ وَمَا كَانَ اللَّهُ لِيُطْلِعَكُمْ عَلَى الْغَيْبِ وَلَٰكِنَّ اللَّهَ يَجْتَبِي مِن رُّسُلِهِ مَن يَشَاءُ ۖ فَآمِنُوا بِاللَّهِ وَرُسُلِهِ ۚ وَإِن تُؤْمِنُوا وَتَتَّقُوا فَلَكُمْ أَجْرٌ عَظِيمٌ (179)
Mulungu sadzawasiya anthu okhulupirira m’mavuto amene muli nawo tsopano mpaka pamene Iye asiyanitsa oipa pakati pa abwino. Ndipo Mulungu sadzakuululilani zinthu zobisika, koma Mulungu amasankha Atumwi ake amene Iye wawafuna. Kotero khulupirirani mwa Mulungu ndi Atumwi ake. Ndipo ngati inu mukhulupirira ndi kuopa Mulungu, mudzakhala ndi malipiro akulu
وَلَا يَحْسَبَنَّ الَّذِينَ يَبْخَلُونَ بِمَا آتَاهُمُ اللَّهُ مِن فَضْلِهِ هُوَ خَيْرًا لَّهُم ۖ بَلْ هُوَ شَرٌّ لَّهُمْ ۖ سَيُطَوَّقُونَ مَا بَخِلُوا بِهِ يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۗ وَلِلَّهِ مِيرَاثُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۗ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرٌ (180)
Ndipo anthu oumira, amene safuna kupereka gawo lina limene Mulungu wawapatsa kuchokera ku chuma chake, asaganize kuti ali kuchita zabwino. Iyayi, zidzawavuta. Zinthu zimene amabisa zidzamangidwa m’makosi mwawo patsiku louka kwa akufa. Mulungu ndiye mwini wa chilichonse chimene chili mlengalenga ndi padziko lapansi ndipo Mulungu amadziwa chilichonse chimene mumachita
لَّقَدْ سَمِعَ اللَّهُ قَوْلَ الَّذِينَ قَالُوا إِنَّ اللَّهَ فَقِيرٌ وَنَحْنُ أَغْنِيَاءُ ۘ سَنَكْتُبُ مَا قَالُوا وَقَتْلَهُمُ الْأَنبِيَاءَ بِغَيْرِ حَقٍّ وَنَقُولُ ذُوقُوا عَذَابَ الْحَرِيقِ (181)
Ndithudi Mulungu wamva mawu a iwo amene adati: “Ndithudi Mulungu ndi osauka koma ife ndife olemera.” Ife tidzalemba zomwe amanena ndi kupha kwawo kwa Atumwi opanda chifukwa ndipo Ife tidzanena kuti: “Lawani chilango chanu cha moto wowotcha.”
ذَٰلِكَ بِمَا قَدَّمَتْ أَيْدِيكُمْ وَأَنَّ اللَّهَ لَيْسَ بِظَلَّامٍ لِّلْعَبِيدِ (182)
Ichi ndi chifukwa cha zimene manja anu adatsogoza. Ndipo ndithudi Mulungu sapondereza akapolo ake
الَّذِينَ قَالُوا إِنَّ اللَّهَ عَهِدَ إِلَيْنَا أَلَّا نُؤْمِنَ لِرَسُولٍ حَتَّىٰ يَأْتِيَنَا بِقُرْبَانٍ تَأْكُلُهُ النَّارُ ۗ قُلْ قَدْ جَاءَكُمْ رُسُلٌ مِّن قَبْلِي بِالْبَيِّنَاتِ وَبِالَّذِي قُلْتُمْ فَلِمَ قَتَلْتُمُوهُمْ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (183)
Iwo amene adati: “Ndithudi Mulungu adavomera lonjezo lathu loti tisakhulupirire mwa Mtumwi wina aliyense pokhapokha ngati iye atibweretsera nsembe yomwe idzawotchedwa ndi moto wochokera kumwamba.” Nena: “Ndithudi! Kudadza kwa inuAtumwi ena ine ndisanadze ndi zizindikiro zooneka ndi zina za zimene mwanenazi. Kodi ndi chifukwa chiyani mudawapha awa ngati zimene muli kunena ndi zoona?”
فَإِن كَذَّبُوكَ فَقَدْ كُذِّبَ رُسُلٌ مِّن قَبْلِكَ جَاءُوا بِالْبَيِّنَاتِ وَالزُّبُرِ وَالْكِتَابِ الْمُنِيرِ (184)
Ngati iwo akukana iwe, Atumwi ena adakanidwanso iwe usanadze, amene adabweretsa zizindikiro zooneka, Mau a Mulungu ndi Buku loonetsa chilangizo
كُلُّ نَفْسٍ ذَائِقَةُ الْمَوْتِ ۗ وَإِنَّمَا تُوَفَّوْنَ أُجُورَكُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۖ فَمَن زُحْزِحَ عَنِ النَّارِ وَأُدْخِلَ الْجَنَّةَ فَقَدْ فَازَ ۗ وَمَا الْحَيَاةُ الدُّنْيَا إِلَّا مَتَاعُ الْغُرُورِ (185)
Mzimu uliwonse udzalawa imfa. Inu mudzalandira malipiro anu patsiku la kuuka kwa akufa. Ndipo aliyense amene adzapulumutsidwa ku moto ndi kulowa ku Paradiso, ndithudi, iye adzakhala opambana. Moyo wa padziko lapansi si wina uliwonse koma ka mtendere ka nthawi kochepa
۞ لَتُبْلَوُنَّ فِي أَمْوَالِكُمْ وَأَنفُسِكُمْ وَلَتَسْمَعُنَّ مِنَ الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ مِن قَبْلِكُمْ وَمِنَ الَّذِينَ أَشْرَكُوا أَذًى كَثِيرًا ۚ وَإِن تَصْبِرُوا وَتَتَّقُوا فَإِنَّ ذَٰلِكَ مِنْ عَزْمِ الْأُمُورِ (186)
Ndithudi inu mudzayesedwa mu chuma chanu ndi inu eni, ake ndipo inu mudzamva zonyansa zambiri kuchokera kwa anthu amene adapatsidwa Buku inu musadadze ndi kuchokera kwa iwo amene amafanizira Mulungu ndi zinthu zina. Koma ngati mupirira ndi kumuopa Mulungu, ndithudi, zimenezo ndizo zofunikira kuchita
وَإِذْ أَخَذَ اللَّهُ مِيثَاقَ الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ لَتُبَيِّنُنَّهُ لِلنَّاسِ وَلَا تَكْتُمُونَهُ فَنَبَذُوهُ وَرَاءَ ظُهُورِهِمْ وَاشْتَرَوْا بِهِ ثَمَنًا قَلِيلًا ۖ فَبِئْسَ مَا يَشْتَرُونَ (187)
Ndi pamene Mulungu adachita chipangano ndi iwo amene analandira Buku kale, kuti: “Alalikire Mau kwa anthu a mitundu yonse mosabisa ayi.” Koma iwo adaponya Mau a Mulungu kumbuyo kwawo ndi kugula zinthu zopanda pake. Ndithudi zoipa zokha ndizo zimene iwo adagula
لَا تَحْسَبَنَّ الَّذِينَ يَفْرَحُونَ بِمَا أَتَوا وَّيُحِبُّونَ أَن يُحْمَدُوا بِمَا لَمْ يَفْعَلُوا فَلَا تَحْسَبَنَّهُم بِمَفَازَةٍ مِّنَ الْعَذَابِ ۖ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (188)
Musaganize kuti iwo amene amasangalala ndi zimene achita ndiponso iwo amene amafuna kuyamikidwa pa zinthu zimene iwo sanachite, kuti adzathawa chilango chathu, ndipo chilango chowawa chiri kuwadikira
وَلِلَّهِ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۗ وَاللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (189)
Mwini Ufumu wa kumwamba ndi wa padziko lapansi ndi Mulungu. Mulungu ali ndi mphamvu pa zinthu zonse
إِنَّ فِي خَلْقِ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَاخْتِلَافِ اللَّيْلِ وَالنَّهَارِ لَآيَاتٍ لِّأُولِي الْأَلْبَابِ (190)
Ndithudi! Muchilengedwe chakumwamba ndi dziko lapansi ndi m’kasinthidwe ka usiku ndi usana, ndithudi muli zizindikiro kwa anthu anzeru
الَّذِينَ يَذْكُرُونَ اللَّهَ قِيَامًا وَقُعُودًا وَعَلَىٰ جُنُوبِهِمْ وَيَتَفَكَّرُونَ فِي خَلْقِ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ رَبَّنَا مَا خَلَقْتَ هَٰذَا بَاطِلًا سُبْحَانَكَ فَقِنَا عَذَابَ النَّارِ (191)
Iwo amene amakumbukira Mulungu ataimirira, atakhala pansi ndi pamene agona cham’mbali ndipo amaganiza m’zachilengedwe chakumwamba ndi dziko lapansi; namati: “Ambuye wathu! Inu simudalenge izi wopanda cholinga ayi. Ulemerero ukhale kwa Inu! Tipulumutseni ife ku mazunzo a ku moto.”
رَبَّنَا إِنَّكَ مَن تُدْخِلِ النَّارَ فَقَدْ أَخْزَيْتَهُ ۖ وَمَا لِلظَّالِمِينَ مِنْ أَنصَارٍ (192)
“Ambuye wathu! Ndithudi yense amene Inu mudzamuponya ku Moto, ndithudi, wotero adzachititsidwa manyazi ndipo anthu ochita zoipa sadzapeza owathandiza.”
رَّبَّنَا إِنَّنَا سَمِعْنَا مُنَادِيًا يُنَادِي لِلْإِيمَانِ أَنْ آمِنُوا بِرَبِّكُمْ فَآمَنَّا ۚ رَبَّنَا فَاغْفِرْ لَنَا ذُنُوبَنَا وَكَفِّرْ عَنَّا سَيِّئَاتِنَا وَتَوَفَّنَا مَعَ الْأَبْرَارِ (193)
“Ambuye wathu! Ndithudi ife tamva kuitana kwa iye amene ali kuwaitana anthu kuti adze ku chipembedzo choonadi.” Iye adati: “Khulupirirani mwa Ambuye wanu ndipo ife takhulupirira. Ambuye wathu tikhululukireni ife machimo athu ndipo chotsani kwa ife ntchito zathu zoipa ndipo tipangeni kuti tife pamodzi ndi anthu olungama.”
رَبَّنَا وَآتِنَا مَا وَعَدتَّنَا عَلَىٰ رُسُلِكَ وَلَا تُخْزِنَا يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۗ إِنَّكَ لَا تُخْلِفُ الْمِيعَادَ (194)
“Ambuye wathu! Tipatseni ife zimene mudatilonjeza kudzera mwa Atumwi anu ndipo musadzatichititse manyazi ife pa tsiku la kuuka kwa akufa chifukwa Inu simuphwanya lonjezo.”
فَاسْتَجَابَ لَهُمْ رَبُّهُمْ أَنِّي لَا أُضِيعُ عَمَلَ عَامِلٍ مِّنكُم مِّن ذَكَرٍ أَوْ أُنثَىٰ ۖ بَعْضُكُم مِّن بَعْضٍ ۖ فَالَّذِينَ هَاجَرُوا وَأُخْرِجُوا مِن دِيَارِهِمْ وَأُوذُوا فِي سَبِيلِي وَقَاتَلُوا وَقُتِلُوا لَأُكَفِّرَنَّ عَنْهُمْ سَيِّئَاتِهِمْ وَلَأُدْخِلَنَّهُمْ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ ثَوَابًا مِّنْ عِندِ اللَّهِ ۗ وَاللَّهُ عِندَهُ حُسْنُ الثَّوَابِ (195)
Motero Ambuye wawo adavomera pemphero lawo nati: “Ine sindidzaononga mphoto ya ntchito za munthu wa mwamuna kapena wa mkazi amene ali pakati panu.” Inu ndinu amodzi. Iwo amene adasamuka m’nyumba zawo ndi kupirikitsidwa kuchoka mu izo ndi kuzunzidwa mu njira yanga ndi iwo amene adamenya nkhondo ndi kuphedwa mnjira yanga, ndithudi, Ine ndidzawakhululukira machimo awo ndipo ndidzawalowetsa ku minda yothiriridwa ndi madzi a m’mitsinje yoyenda pansi pake, mphatso yochokera kwa Mulungu. Ndipo kwa Mulungu ndiye kumene kuli malipiro abwino
لَا يَغُرَّنَّكَ تَقَلُّبُ الَّذِينَ كَفَرُوا فِي الْبِلَادِ (196)
Inu musanyengedwe ndi makhalidwe a anthu osakhulupirira pa dziko lonse lapansi
مَتَاعٌ قَلِيلٌ ثُمَّ مَأْوَاهُمْ جَهَنَّمُ ۚ وَبِئْسَ الْمِهَادُ (197)
Kupeza bwino kwawo ndi kwa kanthawi kochepa ndipo Gahena ndiyo idzakhala mudzi wawo, malo onyansa kukhalamo
لَٰكِنِ الَّذِينَ اتَّقَوْا رَبَّهُمْ لَهُمْ جَنَّاتٌ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا نُزُلًا مِّنْ عِندِ اللَّهِ ۗ وَمَا عِندَ اللَّهِ خَيْرٌ لِّلْأَبْرَارِ (198)
Koma iwo amene amaopa Mulungu, kuli minda yothiriridwa ndi madzi woyenda pansi pake kumene adzakhalako mpaka kalekale, chisangalalo chochokera kwa Ambuye wawo. Ndithudi chimene chili ndi Mulungu ndi chabwino kwa anthu olungama
وَإِنَّ مِنْ أَهْلِ الْكِتَابِ لَمَن يُؤْمِنُ بِاللَّهِ وَمَا أُنزِلَ إِلَيْكُمْ وَمَا أُنزِلَ إِلَيْهِمْ خَاشِعِينَ لِلَّهِ لَا يَشْتَرُونَ بِآيَاتِ اللَّهِ ثَمَنًا قَلِيلًا ۗ أُولَٰئِكَ لَهُمْ أَجْرُهُمْ عِندَ رَبِّهِمْ ۗ إِنَّ اللَّهَ سَرِيعُ الْحِسَابِ (199)
Ndipo, ndithudi, alipo anthu ena pakati pa anthu a m’Buku amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi zimene zavumbulutsidwa kwa inu ndi kwa iwo ndipo amadzichepetsa pamaso pa Mulungu. Ndipo iwo sagulitsa chivumbulutso chake pamtengo wochepa ndipo malipiro awo ali kwa Ambuye wawo. Ndithudi Mulungu ndi wachangu powerengera
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا اصْبِرُوا وَصَابِرُوا وَرَابِطُوا وَاتَّقُوا اللَّهَ لَعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ (200)
oh inu anthu okhulupirira! Pilirani ndipo khalani opirira kwambiri ndipo tetezani dziko lanu poika Asirikari pamalo okhazikika pamene adani anu akhoza kudzera, ndipo muope Mulungu kuti mukhoza kukhala opambana
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس