Quran with Chichewa translation - Surah al-‘Imran ayat 156 - آل عِمران - Page - Juz 4
﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَكُونُواْ كَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَقَالُواْ لِإِخۡوَٰنِهِمۡ إِذَا ضَرَبُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ أَوۡ كَانُواْ غُزّٗى لَّوۡ كَانُواْ عِندَنَا مَا مَاتُواْ وَمَا قُتِلُواْ لِيَجۡعَلَ ٱللَّهُ ذَٰلِكَ حَسۡرَةٗ فِي قُلُوبِهِمۡۗ وَٱللَّهُ يُحۡيِۦ وَيُمِيتُۗ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٞ ﴾
[آل عِمران: 156]
﴿ياأيها الذين آمنوا لا تكونوا كالذين كفروا وقالوا لإخوانهم إذا ضربوا في﴾ [آل عِمران: 156]
Khaled Ibrahim Betala “E inu amene mwakhulupirira! Musakhale ngati amene sadakhulupirire, nanena za anzawo pamene akuyenda pa dziko kapena pomwe akumenyana nkhondo (ndikufera konko): “Akadakhala ndi ife sakadafa, ndiponso sakadaphedwa.” Allah (adawathira maganizo amenewa) kuti azipange zimenezo kukhala zodandaulitsa m’mitima mwawo. Komatu Allah ndi amene amapereka moyo ndi imfa. Ndipo Allah akuona zonse zomwe mukuchita |