Quran with Chichewa translation - Surah An-Nisa’ ayat 127 - النِّسَاء - Page - Juz 5
﴿وَيَسۡتَفۡتُونَكَ فِي ٱلنِّسَآءِۖ قُلِ ٱللَّهُ يُفۡتِيكُمۡ فِيهِنَّ وَمَا يُتۡلَىٰ عَلَيۡكُمۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ فِي يَتَٰمَى ٱلنِّسَآءِ ٱلَّٰتِي لَا تُؤۡتُونَهُنَّ مَا كُتِبَ لَهُنَّ وَتَرۡغَبُونَ أَن تَنكِحُوهُنَّ وَٱلۡمُسۡتَضۡعَفِينَ مِنَ ٱلۡوِلۡدَٰنِ وَأَن تَقُومُواْ لِلۡيَتَٰمَىٰ بِٱلۡقِسۡطِۚ وَمَا تَفۡعَلُواْ مِنۡ خَيۡرٖ فَإِنَّ ٱللَّهَ كَانَ بِهِۦ عَلِيمٗا ﴾
[النِّسَاء: 127]
﴿ويستفتونك في النساء قل الله يفتيكم فيهن وما يتلى عليكم في الكتاب﴾ [النِّسَاء: 127]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo akukufunsa zomwe zikukhudza azimayi nena: “Allah akukuuzani nkhani za iwo ndi zomwe zikuwerengedwa kwa inu m’buku (ili) za akazi amasiye omwe simukuwapatsa (chiwongo chawo) chomwe chidalamulidwa kwa iwo, komabe mukufuna kuwakwatira, ndi za ana omwe ali ofooka ndi oponderezedwa; ndipo (akukuuzani) kuti limbikirani kuwayang’anira ana amasiye mwachilungamo. Ndipo chabwino chilichonse chimene muchita, Allah akuchidziwa |