×

Ndipo ngati wina wa inu alibe mwayi woti nkukwatira mkazi wokhulupirira amene 4:25 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah An-Nisa’ ⮕ (4:25) ayat 25 in Chichewa

4:25 Surah An-Nisa’ ayat 25 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah An-Nisa’ ayat 25 - النِّسَاء - Page - Juz 5

﴿وَمَن لَّمۡ يَسۡتَطِعۡ مِنكُمۡ طَوۡلًا أَن يَنكِحَ ٱلۡمُحۡصَنَٰتِ ٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ فَمِن مَّا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُكُم مِّن فَتَيَٰتِكُمُ ٱلۡمُؤۡمِنَٰتِۚ وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِإِيمَٰنِكُمۚ بَعۡضُكُم مِّنۢ بَعۡضٖۚ فَٱنكِحُوهُنَّ بِإِذۡنِ أَهۡلِهِنَّ وَءَاتُوهُنَّ أُجُورَهُنَّ بِٱلۡمَعۡرُوفِ مُحۡصَنَٰتٍ غَيۡرَ مُسَٰفِحَٰتٖ وَلَا مُتَّخِذَٰتِ أَخۡدَانٖۚ فَإِذَآ أُحۡصِنَّ فَإِنۡ أَتَيۡنَ بِفَٰحِشَةٖ فَعَلَيۡهِنَّ نِصۡفُ مَا عَلَى ٱلۡمُحۡصَنَٰتِ مِنَ ٱلۡعَذَابِۚ ذَٰلِكَ لِمَنۡ خَشِيَ ٱلۡعَنَتَ مِنكُمۡۚ وَأَن تَصۡبِرُواْ خَيۡرٞ لَّكُمۡۗ وَٱللَّهُ غَفُورٞ رَّحِيمٞ ﴾
[النِّسَاء: 25]

Ndipo ngati wina wa inu alibe mwayi woti nkukwatira mkazi wokhulupirira amene ndi mfulu, mukhoza kukwatira mwa atsikana anu wokhulupirira kuchokera kugulu la akapolo amene muli nawo, ndipo Mulungu amadziwa zonse za chikhulupiriro chanu ndipo inu ndinu amodzi. Akwatitseni ndi chilolezo cha ambuye awo ndipo muwapatse mphatso yawo ya ukwati mwa chilungamo. Iwo ayenera kudzisunga, osati a chiwerewere kapena wochita chibwenzi. Ndipo ngati akwatiwa ndipo achita chigololo, chilango chawo ndi theka la chilango chimene mfulu ya ikazi ingalandire. Ichi chikhudza iye amene aopa kupwetekeka pakati pa inu. Koma ndi kwabwino ngati inu mudziletsa ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha

❮ Previous Next ❯

ترجمة: ومن لم يستطع منكم طولا أن ينكح المحصنات المؤمنات فمن ما ملكت, باللغة نيانجا

﴿ومن لم يستطع منكم طولا أن ينكح المحصنات المؤمنات فمن ما ملكت﴾ [النِّسَاء: 25]

Khaled Ibrahim Betala
“Ndipo amene sangathe mwa inu kupeza chuma chokwatilira mkazi amene ali mfulu wokhulupirira, (akwatireni adzakazi) achisungwana okhulupirira, mwa omwe manja anu akumanja apeza, Allah akudziwa kwambiri chikhulupiliro chanu. Ndinu amodzi kuchokera kwa wina ndi mnzake (nonsenu ndinu ana a Adam). Akwatireni ndi chilolezo cha mabwana awo, ndipo apatseni chiwongo chawo mwachilamulo. (Akwatireni) omwe ali akazi odzisunga, osati achiwerewere kapena ochita zibwenzi. Ndipo akakwatiwa, kenako nkuchita chauve, chilango chawo nditheka lachilango cha mfulu. Kumeneko (kukwatira akapoloko) ndilamulo kwa yemwe mwa inu akuopa kuti angachite chiwerewere. Koma ngati mutapirira (posiya kukwatira akapolo) ndibwino kwa inu kutero. Ndipo Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek