×

Kodi ndiwo amene akhoza kugawa gawo lina la chisomo cha Ambuye wako? 43:32 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah Az-Zukhruf ⮕ (43:32) ayat 32 in Chichewa

43:32 Surah Az-Zukhruf ayat 32 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah Az-Zukhruf ayat 32 - الزُّخرُف - Page - Juz 25

﴿أَهُمۡ يَقۡسِمُونَ رَحۡمَتَ رَبِّكَۚ نَحۡنُ قَسَمۡنَا بَيۡنَهُم مَّعِيشَتَهُمۡ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَرَفَعۡنَا بَعۡضَهُمۡ فَوۡقَ بَعۡضٖ دَرَجَٰتٖ لِّيَتَّخِذَ بَعۡضُهُم بَعۡضٗا سُخۡرِيّٗاۗ وَرَحۡمَتُ رَبِّكَ خَيۡرٞ مِّمَّا يَجۡمَعُونَ ﴾
[الزُّخرُف: 32]

Kodi ndiwo amene akhoza kugawa gawo lina la chisomo cha Ambuye wako? Ndife amene timagawa pakati pawo chakudya chawo cha moyo uno ndipo tawakweza ena kukhala apamwamba kuposa anzawo kotero kuti akhoza kulemba ntchito anzawo. Koma chisoni cha Ambuye wako ndi chabwino kwambiri kuposa chuma chimene amasonkhanitsa

❮ Previous Next ❯

ترجمة: أهم يقسمون رحمة ربك نحن قسمنا بينهم معيشتهم في الحياة الدنيا ورفعنا, باللغة نيانجا

﴿أهم يقسمون رحمة ربك نحن قسمنا بينهم معيشتهم في الحياة الدنيا ورفعنا﴾ [الزُّخرُف: 32]

Khaled Ibrahim Betala
“(Choncho Allah akunena): “Kodi iwo ndi amene akugawa mtendere wa Mbuye wako (kumpatsa amene wamfuna ndi kummana amene sakumfuna? Chikhalirecho) Ife ndi Amene timagawa pakati pawo zofunika pa moyo wawo mu moyo wadziko lapansi; ndipo tawatukula ena mwa iwo pa ulemelero pamwamba pa ena, choncho ena mwa iwo akuwachita anzawo kukhala antchito awo koma mtendere wa Mbuye wako ndi wabwino kuposa zimene akusonkhanitsa.”
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek